Kodi Muli ndi “Ufulu wa Kulankhula”?
ANTHU oposa sikisi miliyoni m’mayiko 235 ali ndi “ufulu wa kulankhula,” wotchulidwa m’Baibulo. Mawu amenewa amapezeka maulendo 16 m’Malemba Achigiriki Achikristu a Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures. (Afilipi 1:20; 1 Timoteo 3:13; Ahebri 3:6; 1 Yohane 3:21) Kodi kukhala ndi “ufulu wa kulankhula” kumatanthauzanji? N’chiyani chimatithandiza kukhala ndi ufulu umenewu? Kodi ndi liti pamene ufulu umenewu umatithandiza kulankhula momasuka?
Malinga ndi zimene inanena Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words, pa Chigiriki mawu omasuliridwa kuti “ufulu wa kulankhula” amatanthauza “kulankhula mosamangika, . . . kulankhula molimba mtima; motero mawu amenewa amasonyeza kusakayikira, nsangala ndi kulimba mtima, ndipo sikuti nthawi zonse amanena za kulankhula ayi.” Komatu tisasokoneze kulankhula momasuka kumeneku ndi kulankhula mosasamala kapena mwamwano. “Mawu anu akhale m’chisomo,” limatero Baibulo. (Akolose 4:6) Mwa zina, ufulu wa kulankhula umaphatikizapo kulankhula mosamala, osalola kuti zinthu monga mavuto ndi kuopa anthu zisokoneze zomwe tikulankhula.
Kodi timabadwa ndi ufulu wa kulankhula? Taonani zimene mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Efeso. Iye anati: “Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Kristu.” Paulo anapitiriza kunena kuti n’chifukwa cha Yesu Kristu kuti “tili [ndi] chokhazikika mtima [“ufulu wa kulankhula,” NW] ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.” (Aefeso 3:8-12) Ufulu wa kulankhula si wobadwa nawo koma ndi ufulu umene timaupeza chifukwa chokhala ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu popeza timakhulupirira Yesu Kristu. Tiyeni tione zimene zingatithandize kupeza ufulu umenewu ndiponso mmene tingausonyezere polalikira, pophunzitsa, ndi popemphera.
N’chiyani Chimatithandiza Kulalikira Molimba Mtima?
Yesu Kristu ndiye chitsanzo chachikulu cha munthu amene anali ndi ufulu wa kulankhula. Changu chake chinamulimbikitsa kugwiritsa ntchito mipata yolalikira imene anapeza. Popuma, pachakudya panyumba pa munthu wina, kapena paulendo, sanalekerere mwayi uliwonse wolankhula za Ufumu wa Mulungu. Yesu sanasiye kulankhula poopa kunyozedwa kapena kutsutsidwa ayi. Koma analimba mtima, n’kusonyeza poyera chinyengo cha atsogoleri a chipembedzo chonyenga m’masiku ake. (Mateyu 23:13-36) Ngakhale pamene anamangidwa n’kuyamba kuzengedwa mlandu, Yesu analankhula mopanda mantha.—Yohane 18:6, 19, 20, 37.
Nawonso atumwi a Yesu ankalankhula momasuka. Pa Pentekoste wa mu 33 C.E., Petro analankhula mwaufulu kwa anthu oposa 3,000. N’zochititsa chidwi kuti masiku ochepa chabe izi zisanachitike, Petro anachita mantha kwambiri, mtsikana wantchito atam’zindikira. (Marko 14:66-71; Machitidwe 2:14, 29, 41) Atawakokera kwa atsogoleri achipembedzo, Petro ndi Yohane sanachite mantha. Anapereka molimba mtima umboni wonena za Yesu Kristu amene anauka kwa akufa. Ndipo chifukwa chakuti Petro ndi Yohane analankhula momasuka chonchi, atsogoleriwo anazindikira kuti amunawa ankakhala ndi Yesu. (Machitidwe 4:5-13) Kodi n’chiyani chinawathandiza kulankhula molimba mtima chonchi?
Yesu anali atalonjeza atumwi ake kuti: “Pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.” (Mateyu 10:19, 20) Mzimu woyera unathandiza Petro ndi ena kusachita manyazi kapena mantha alionse amene akanapangitsa kuti asalankhule momasuka. Nafenso mphamvu imeneyi ingatithandize.
Komanso, Yesu anapatsa otsatira ake ntchito yawo yopanga ophunzira. M’pake kuti anatero, chifukwa chakuti iye ndi Amene anapatsidwa “mphamvu zonse . . . Kumwamba ndi padziko lapansi.” Ndipo ‘iye anali pamodzi ndi iwo.’ (Mateyu 28:18-20) Kudziwa kuti Yesu ali nawo, kunathandiza ophunzira oyambirirawa kukhala ndi chikhulupiriro pokumana ndi akuluakulu a boma amene anayesetsa umu ndi umu kuletsa ntchito yawo yolalikira. (Machitidwe 4:18-20; 5:28, 29) Kudziwa zimenezi kungatithandizenso ifeyo.
Pofotokoza chifukwa chinanso cholankhulira momasuka, Paulo anagwirizanitsa chiyembekezo ndi “kukhazikika mtima kwakukulu [“ufulu waukulu wa kulankhula,” NW].” (2 Akorinto 3:12; Afilipi 1:20) Popeza kuti uthenga wa chiyembekezo unali wosangalatsa kwambiri moti sakanatha kungousunga osafotokozera ena, Akristu anafunika kulalikira uthengawu. Zoonadi, chiyembekezo chathu ndi chifukwa china cholankhulira mwaufulu.—Ahebri 3:6.
Kulalikira Molimba Mtima
Kodi tingatani kuti tilalikire molimba mtima ngati tikuchita mantha? Taganizirani za chitsanzo cha mtumwi Paulo. Ali mkaidi ku Roma, iye anapempha okhulupirira anzake kuti apemphere n’cholinga choti ‘apatsidwe mawu m’kumutsegulira m’kamwa molimbika monga ayenera kulankhulira.’ (Aefeso 6:19, 20) Kodi mapemphero amenewo anayankhidwa? Inde. Ali m’ndende, Paulo anapitiriza “kulalikira Ufumu wa Mulungu, . . . ndi kulimbika konse [“mwaufulu wonse wa kulankhula,” NW], wosam’letsa munthu.”—Machitidwe 28:30, 31.
Zingakhale zovuta kulankhula mwaufulu tikapeza mwayi wolalikira kuntchito, kusukulu, kapena pamene tili paulendo. Tingalephere kulankhula chifukwa cha manyazi, kuchita mantha poganizira zimene anthu angatichitire, kapena kudzikayikira. Pamfundo imeneyinso, mtumwi Paulo anatipatsa chitsanzo chabwino. Analemba kuti: “Tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m’kutsutsana kwambiri.” (1 Atesalonika 2:2) Chifukwa choti anadalira Yehova, Paulo anatha kuchita zomwe sakanatha mwa iye yekha.
Pemphero linathandiza mayi wina, dzina lake Sherry, kuti alimbe mtima atapeza mpata wolalikira mwamwayi. Tsiku lina akudikirira mwamuna wake, iye anaona mayi wina amenenso anali kudikirira zinthu zina. Iye anati: “Chifukwa choti ndinabanika, kulephera kulankhula, ndinapemphera kwa Yehova kuti andilimbitse mtima.” Sherry atanyamuka kupita pamene panali mayi uja, panafika mbusa wa Baptist. Sherry sanayembekezere kulankhula ndi mtsogoleri wachipembedzo. Komabe, anapempheranso ndipo anatha kulalikira bwinobwino. Anam’gawira buku mayi uja ndipo anagwirizana kuti adzakumanenso. Tikamagwiritsa ntchito mipata yolalikira yomwe yapezeka, sitingakayikire kuti kudalira Yehova kudzatithandiza kulankhula momasuka.
Pophunzitsa
Pali kugwirizana kwakukulu pakati pa ufulu wa kulankhula ndi kuphunzitsa. Pofotokoza za “iwo akutumikira bwino” mu mpingo, Baibulo limati: “[Iwo] adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu [“ufulu waukulu wa kulankhula,” NW] m’chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.” (1 Timoteo 3:13) Iwo amapeza ufulu wa kulankhulawu chifukwa chakuti amatsatira zinthu zimene iwo amaphunzitsa anzawo. Akamachita zimenezi mpingo umatetezedwa ndiponso umakhala wolimba.
Tikakhala ndi ufulu wa kulankhula m’njira imeneyi, uphungu wathu umakhala wogwira mtima kwambiri ndiponso kawirikawiri anthu amautsatira. M’malo mogwa ulesi ndi chitsanzo chathu choipa, omvera amalimbikitsidwa akamaona mmene angagwiritsire ntchito zimene iwo akuphunzitsidwa. Ufulu wa kulankhula umenewu umathandiza anthu amene ali ndi ziyeneretso zauzimu ‘kubweza mbale wawo’ kapena kuti kumuwongolera, zinthu zisanafike poipa. (Agalatiya 6:1) Koma munthu wachitsanzo choipa angavutike kupereka malangizo, poona kuti alibe ufulu wa kulankhula. Kuchedwa kupereka uphungu kungakhale ndi zotsatirapo zoopsa kwambiri.
Kulankhula kwathu molimba mtima sikutanthauza kuti ndife anthu okonda kuweruza ena, kapena aliuma ayi. Paulo analimbikitsa Filemoni “mwachikondi.” (Filemoni 8, 9) Ndipo zikuoneka kuti Filemoni analabadira mawu a mtumwiyu. Inde, chikondi ndicho chiyenera kumulimbikitsa mkulu kupatsa munthu malangizo.
Kunena zoona, ufulu wa kulankhula ndi wofunika kwambiri popereka uphungu. Ufuluwu ndi wofunikanso pa zinthu zina. Paulo analembera mpingo wa ku Korinto kuti: “Ndilimbika mtima kwambiri [“ndimakhala ndi ufulu waukulu wa kulankhula,” NW] pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu n’kwakukulu.” (2 Akorinto 7:4) Paulo sankazengereza kuyamikira abale ndi alongo ake pakafunika kuti atero. Chikondi chinam’thandiza kuti aziyang’ana makhalidwe abwino a okhulupirira anzake, ngakhale kuti ankadziwa za zophophonya zawo. Nawonso mpingo wachikristu masiku ano umalimbikitsidwa, akulu akamayamikira ndi kulimbikitsa abale ndi alongo awo.
Akristu onse amafunikira kukhala ndi ufulu wa kulankhula kuti akhale ogwira mtima pophunzitsa. Sherry, amene tam’tchula kale uja, ankafuna kulimbikitsa ana ake kuti azilalikira kusukulu. Iye anati: “Ngakhale kuti ndinakulira m’choonadi, sindinkakonda kulalikira kusukulu. Ndiponso sindichita kawirikawiri umboni wamwamwayi. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuwasonyeza chitsanzo chotani ana anga?’” Izi zinam’pangitsa Sherry kuchita khama kwambiri ndi kumalalikira mwamwayi.
Zoonadi, anthu ena amaona zomwe tikuchita ndipo amadziwa tikalephera kuchita zimene timaphunzitsa. Ndiyetu tiyeni tikhale ndi ufulu waukulu wa kulankhula mwa kuchita khama kuti tizichita zomwe timanena.
Popemphera
Ufulu wa kulankhula ndi wofunika kwambiri popemphera kwa Yehova. Popanda chopinga chilichonse, tingathe kum’fotokozera Yehova zakukhosi kwathu tili ndi chikhulupiriro kuti iye akumva mapemphero athuwo ndipo atiyankha. Zikatero, timakhala paubwenzi wolimba ndi Atate wathu wakumwamba. Tisalephere kupemphera kwa Yehova chifukwa chodziona kuti ndife opanda ntchito. Koma bwanji ngati tikudziimba mlandu chifukwa cha cholakwa kapena tchimo linalake ndipo tikulephera kufotokoza zakukhosi kwathu? Kodi n’zotheka kupemphera mwaufulu kwa Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse?
Udindo wapamwamba womwe Yesu ali nawo, wokhala Mkulu wa Ansembe, ukutipatsa chifukwa china chokhulupirira pemphero. Pa Ahebri 4:15, 16 timamva kuti: “Sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima [“tilankhule mwaufulu,” NW] poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi ya kusowa.” Ili ndiye phindu la imfa ya Yesu ndiponso la udindo wake monga Mkulu wa Ansembe.
Ngati timayesetsa kumvera Yehova, tisakayikire ngakhale pang’ono kuti iye amatimvera. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa [“ufulu wa kulankhula ndi,” NW] Mulungu; ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zom’kondweretsa pamaso pake.”—1 Yohane 3:21, 22.
Kukhala omasuka kulankhula ndi Yehova m’pemphero kukutanthauza kuti tingathe kum’fotokozera chilichonse. Kaya tili ndi mantha, nkhawa, kapena madandaulo otani, tingathe kum’fotokozera Yehova, tili ndi chikhulupiriro chakuti atimvera mapemphero athu ochokera mu mtima. Ngakhale titachita tchimo lalikulu, kudziimba mlandu sikungatilepheretse kulankhula momasuka m’pemphero ngati talapa moona mtima.
Mphatso ya ufulu wa kulankhula ndi yamtengo wapatali kwambiri. Mphatsoyi ingatithandize kulemekeza Mulungu mu ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa ndipo ingatithandize kuyandikira kwambiri kwa iye m’pemphero. Tiyeni ‘tisataye kulimbika kwathu [‘ufulu wathu wa kulankhula,’ NW] kumene kuli nacho chobwezera mphoto chachikulu,’ mphoto ya moyo wosatha.—Ahebri 10:35.
[Chithunzi patsamba 13]
Mtumwi Paulo ankalankhula molimba mtima
[Zithunzi patsamba 15]
Kuti munthu aphunzitse mogwira mtima afunika ufulu wa kulankhula
[Chithunzi patsamba 16]
Ufulu wa kulankhula ndi wofunika kwambiri popemphera