Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Yesu anayenda m’dziko lonse la Isiraeli pa ntchito yake yolalikira. Ndiye kodi n’chifukwa chiyani mtumwi Petulo ananena kuti pankhani ya kuphedwa kwa Yesu, Ayuda komanso atsogoleri awo ‘anachita zinthu mosadziwa’?—Mac. 3:17.
Polankhula ndi gulu la Ayuda limene linachititsa kuti Mesiya aphedwe, Petulo ananena kuti: “Ndikudziwa kuti munachita zinthu mosadziwa, monganso anachitira olamulira anu.” (Mac. 3:14-17) N’kutheka kuti Ayuda ena sanamvetse bwinobwino kuti Yesu anali Mesiya ndipo sanamvetse ziphunzitso zake. Koma ena chinali chifukwa choti analibe mtima wofuna kukondweretsa Mulungu, ankadana ndi Yesuyo komanso ankamuchitira nsanje.
Taganizirani mmene mtima wosafuna kukondweretsa Yehova unalepheretsera anthu ena kumvetsera zimene Yesu ankaphunzitsa. Pophunzitsa, nthawi zambiri Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo ndipo ankafotokoza matanthauzo ake kwa anthu ofuna kumvetsetsa. Koma ena ankangochokapo basi, osakhala ndi chidwi chofuna kumvetsetsa. Pa nthawi ina, ngakhale ena mwa ophunzira ake anakhumudwa ndi mawu okuluwika amene Yesu analankhula. (Yoh. 6:52-66) Ophunzira amenewo analephera kuzindikira kuti mafanizo a Yesu akanawathandiza kusonyeza ngati analidi okonzeka kusintha maganizo ndiponso zochita zawo. (Yes. 6:9, 10; 44:18; Mat. 13:10-15) Analepheranso kuganizira ulosi umene unanena kuti Mesiya adzagwiritsira ntchito mafanizo pophunzitsa.—Sal. 78:2.
Anthu ena sankamvera zimene Yesu ankaphunzitsa chifukwa chodana naye. Iye ataphunzitsa m’sunagoge wa kwawo ku Nazareti, anthu “anazizwa.” Koma m’malo movomereza kuti Yesu ndi Mesiya, iwo anam’kayikira n’kumafunsana kuti: “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zinthu zimenezi? . . . Kodi iyeyu si mmisiri wa matabwa, mwana wa Mariya, komanso m’bale wa Yakobe ndi Yosefe ndi Yudasi ndi Simoni? Ndipo alongo ake si awa omwe tili nawo pompano?” (Maliko 6:1-3) Anthu a ku Nazareti ankaona kuti zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zopanda phindu chifukwa choti iye sankachokera m’banja lapamwamba.
Nanga bwanji atsogoleri achipembedzo a panthawiyo? Ambiri sankasamalako n’komwe za Yesu pa zifukwa zomwezo. (Yoh. 7:47-52) Nawonso sankavomereza zimene Yesu ankaphunzitsa chifukwa chomuchitira nsanje, poti anthu ambiri ankakonda kumumvetsera. (Maliko 15:10) Ndipo n’zosakayikitsa kuti anthu ambiri otchuka sanasangalale ngakhale pang’ono kumva Yesu akuwadzudzula chifukwa cha chinyengo chawo. (Mat. 23:13-36) Mpake kuti Yesu anawadzudzula chifuwa cha umbuli wawo wadalawo. Iye anati: “Tsoka inu odziwa Chilamulo, chifukwa munalanda anthu kiyi yodziwira zinthu. Inuyo simunalowemo [mu Ufumu], ndipo ofuna kulowamo munawatsekereza!”—Luka 11:37-52.
Kwa zaka zitatu ndi theka, Yesu analalikira uthenga wabwino m’dziko la Isiraeli. Iye anaphunzitsanso anthu ambiri kugwira nawo ntchitoyo. (Luka 9:1, 2; 10:1, 16, 17) Yesu ndi ophunzira ake anachita bwino kwambiri ntchito yawoyi moti Afarisi anadandaula kuti: “Onani! Dziko lonse lakhamukira kwa iye.” (Yoh. 12:19) Motero pafupifupi Ayuda onse ankadziwa zinazake ndithu zokhudza uthenga wabwino. Komabe, pa nkhani yakuti Yesu ndi Mesiya tingati iwo kwenikweni anali ‘osadziwa.’ Akanafuna akanatha kumudziwa bwino Mesiya n’kuyamba kumukonda kwambiri, koma sanatero ayi. Moti ena anathandiza nawo kuti Yesu aphedwe. N’chifukwa chake mtumwi Petulo analimbikitsa ambiri mwa anthuwa kuti: “Chotero lapani, ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe. Ndi kutinso nyengo za chitsitsimutso zibwere kuchokera kwa Yehova mwiniyo. Komanso kuti atumize Yesu, amene ndiye Khristu woikidwa chifukwa cha inu.” (Mac. 3:19, 20) N’zochititsa chidwi kuti Ayuda ambiri komanso “ansembe ambirimbiri” anayamba kumvetsera. Iwowa sankachitanso zinthu mosadziwa. M’malomwake, iwo analapa ndipo Yehova anayamba kuwakonda.—Mac. 2:41; 4:4; 5:14; 6:7.