Lingaliro la Baibulo
Kukhululukira ndi Kuiŵala—Kodi Nkotheka Motani?
“NDIDZAKHULULUKIRA MPHULUPULU YAWO, NDIPO SINDIDZAKUMBIKIRA TCHIMO LAWO.”—YEREMIYA 31:34.
MAWU amenewo olembedwa ndi mneneri Yeremiya amavumbula za kanthu kena kapadera ponena za chifundo cha Yehova: Pamene akhululukira, amaiŵala. (Yesaya 43:25) Baibulo limanenanso kuti: “Monganso [ Yehova, NW ] anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Chotero ife monga Akristu tiyenera kutsanzira kukhululukira kwa Yehova.
Komabe, pakubuka mafunso ena ofunika. Pamene Yehova akhululukira, kodi iye kwenikweni samakumbukiranso machimo athu? Ndipo pamene tikhululukira, kodi tiyenera kuiŵala m’lingaliro la kukhala osakhoza kukumbukira? Kodi kunganenedwe kuti ngati sitiiŵala mwanjira imeneyo, ndiye kuti sitinakhululukiredi munthu?
Mmene Yehova Amakhululukira
Kukhululukira kumaphatikizapo kuleka mkwiyo. Pamene Yehova akhululukira, iye amachita zimenezo mokwanira.a Wamasalmo Davide analemba kuti: “[Yehova] sadzatsutsana nawo nthaŵi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha. Monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa iye.”—Salmo 103:9, 12, 13.
Kukwanira kwa chikhululukiro cha Mulungu kukufotokozedwa mowonjezereka pa Machitidwe 3:19: “Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu.” Mawu akuti ‘fafaniza’ akuchokera ku verebu Yachigiriki (e·xa·leiʹpho) imene imataenthauza kuti “pukuta, chotsa.” (Onani Chivumbulutso 7:17; 21:4.) The New International Dictionary of New Testament Theology imalongosola kuti: “Lingaliro losonyezedwa ndi verebuyo pano ndipo mwinamwake kwinanso ndilo mwina la kukulunga paphale lolembapo la phula kuti ligwiritsiridwenso ntchito ([yerekezerani ndi] ‘kupukuta sileti kukhala loyera’).” Pamene tilapa machimo, Yehova amapukuta cholembedwacho kukhala palibenso. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti samakumbukiranso machimo athu? Tiyeni tilingalire za chitsanzo china cholembedwa m’Baibulo.
Pamene Mfumu Davide anachita chigololo ndi Bateseba ndipo nayesa kuchibisa pambuyo pake mwa kulinganiza imfa ya mwamuna wake, Yehova anatumiza mneneri Natani kukadzudzula Davide. (2 Samueli 11:1-17; 12:1-12) Ndi chotulukapo chotani? Davide analapa moona mtima, ndipo Yehova anamkhululukira. (2 Samueli 12:13; Salmo 32:1-5) Kodi Yehova anaiŵala machimo a Davide? Kutalitali! Olemba Baibulo Gadi ndi Natani pambuyo pake analemba nkhani yonseyo m’buku la 2 Samueli (lomalizidwa pafupifupi 1040 B.C.E.) Davide ali pafupi kumwalira.
Chotero cholembedwacho, kapena chikumbukiro cha machimo a Davide—ndiponso cholembedwa cha kulapa kwake ndi chikhululukiro cha Yehova chimene chinatsatirapo—zimakumbukikabe, kuti oŵerenga Baibulo a lerolino apindule nazo. (Aroma 15:4; 1 Akorinto 10:11) Kwenikweni, popeza kuti “Mawu a [ Yehova, NW ] [monga momwe alili m’Baibulo] akhala chikhalire,” cholembedwa cha machimo a Davide sichidzaiŵalika!—1 Petro 1:25.
Nangano kodi kunganenedwe motani kuti Yehova amapukuta sileti kuliyeretsa pamene tilapa machimo moona mtima? Kodi mawu a Yehova akuti: “Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo,” tingawamve motani?—Yeremiya 31:34.
Mmene Yehova Amaiŵalira
Verebu Yachihebri yotembenuzidwa kuti “ndidzakumbukira” (mpangidwe wa za·kharʹ) simatanthauza kungokumbukira zakale. Malinga ndi kunena kwa Theological Wordbook of the Old Testament, ingatanthauzenso “kutchula, kulengeza, kufotokoza, kulalikira, kupemphera, kukumbutsa, kuimba mlandu, kuulula.” Theological Dictionary of the Old Testament imawonjezera kuti: “Kaŵirikaŵiri, [za·kharʹ] kwenikweni amapereka lingaliro la kuchitapo kanthu kapena amaphatikizidwa ndi maverebu a kuchitapo kanthu.” Motero, pamene Yehova akunena za mtundu wake wopulupudzawo kuti “adzakumbukira choipa chawo,” iye akutanthauza kuti adzachitapo kanthu motsutsana nawo chifukwa cha kusalapa kwawo. (Yeremiya 14:10) Komanso, pamene Yehova anena kuti, “sindidzakumbukira tchimo lawo,” akutitsimikizira kuti pamene akhululukira machimo athu, sadzawakumbutsanso kuti atiimbe mlandu, kutitsutsa, kapena kutilanga.
Kupyolera mwa mneneri Ezekieli, Yehova analongosola lingaliro la mmene amakhululukira ndi kuiŵala: “Koma woipayo akabwerera kusiya machimo ake onse adawachita nakasunga malemba anga onse, ndi kuchita chiweruzo ndi chilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa. Nnena chimodzi chonse cha zolakwa zake zonse adazichita chidzakumbukika chimtsutse; m’chilungamo chake adachichita ad[z]akhala ndi moyo.” (Ezekieli 18:21, 22; 33:14-16) Inde, pamene Yehova akhululukira wochimwa wolapa, amapukuta sileti naliyeretsa ndi kuiŵala m’lingaliro lakuti sadzachitapo kanthu motsutsana naye pa machimo amenewo mtsogolo.—Aroma 4:7, 8.
Pokhala opanda ungwiro, sitingathe kukhululukira m’lingaliro langwiro monga mmene Yehova amachitira; maganizo ake ndi njira zake zili zapamwamba kwambiri kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Nangano kodi ife tiyenera kukhululukira ndi kuiŵala kufikira pamlingo wotani pamene ena atichimwira?
Mmene Tingakhululukire ndi Kuiŵala
Khalani “akukhululukirana [mwaufulu, NW ],” amalimbikitsa motero Aefeso 4:32. Malinga ndi kunena kwa wolemba dikishonale W. E. Vine, liwu Lachigiriki lotembenunzidwa kuti ‘kukhululukira mwaufulu’ (kha·riʹzo·mai) limatanthauza “kusonyeza chiyanjo momasuka.” Pamene kulakwiridwa kwathu kuli kwakung’ono, sitimavutika kwambiri kusonyeza chikhululukiro. Kukumbukira kuti nafenso tili opanda ungwiro kumatikhozetsa kukhululukira zophophonya za ena. (Akolose 3:13) Pamene tikhululukira ena, timaleka kukwiya, ndipo unansi wathu ndi wotilakwirayo sumaipa kwanthaŵi yaitali. M’kupita kwa nthaŵi, zolakwa zazing’ono zimenezo zimazimiririka m’chikumbukiro.
Komabe, bwanji nanga ngati ena atichimwira motivulaza kwambiri? M’zochitika zazikulu zonga kugonedwa ndi wachibale, kugwiriridwa chigololo, ndi kufuna kuchita mbanda, chikhululukiro chingaloŵetsemo zambiri. Makamaka zimenezi zingakhale choncho pamene wochimwayo savomereza tchimo, salapa, ndipo sapepesa.b (Miyambo 28:13) Yehova mwiniyo samakhululukira ochimwa amene ali okakala mtima ndi osalapa. (Ahebri 6:4-6; 10:26) Pamene kuvulazika mtima kuli kwakukulu, sitingathe kuiŵaliratu m’maganizo zimene zinachitika. Komabe, tingatonthozedwe ndi chitsimikiziro chakuti m’dziko latsopano limene likudzalo, “zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” (Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4) Pamenepo chilichonse chimene tidzakumbukira sichidzatipweteketsa mtima kumene tingakhale nako tsopano.
M’zochitika zina tingafunikire kuyamba kuchitapo kanthu kuthetsa nkhaniyo, mwinamwake mwa kukambitsirana ndi wotichimwirayo, tisanakhululukire. (Aefeso 4:26) Mwa njira imeneyi kumvana molakwa kulikonse kungathetsedwe, kupepesa koyenera kukumachitidwa, ndipo chikhululukiro chikumaperekedwa. Bwanji nanga za kuiŵala? Sitingaiŵaliretu zimene zinachitidwa, koma tingaiŵale m’njira yakuti sitikusungiranso nkhaniyo kukhosi wotichimwirayo kapena kuzadzutsanso nkhaniyo mtsogolo. Sitifunikira kuchita miseche pa nkhaniyo, ndiponso sitifunikira kupeŵa kotheratu wotichimwirayo. Komabe, pangatenge nthaŵi yaitali kuti unansi wathu ndi wotichimwirayo ubwerere m’malo, ndipo mwina sitidzakhala ndi kukondana konga kwapoyamba.
Talingalirani za chitsanzo ichi: Tinene kuti munaululira nkhani ina ya kukhosi kwanu bwenzi limene mumalikhulupirira, ndiyeno pambuyo pake mudziŵa kuti ilolo laululira kwa ena nkhaniyo mokuchititsani manyazi ndi kukukwiyitsani kwambiri. Mumfikira ndi kukambitsirana naye za nkhaniyo, ndipo iye amva chisoni kwambiri; apepesa napempha chikhululukiro. Inuyo pomva kupepesa kwake, musonkhezeredwa kumkhululukira. Kodi mudzaiŵala zimene zinachitikazo? Kutalitali; mosakayikira inu mudzakhala wosamala kwambiri kuti mumuululire za kukhosi mtsogolo. Komabe inu munamkhululukira; simudzapitiriza kudzutsanso nkhaniyo ndi iye. Simudzamsungira kanthu kukhosi, ndiponso simudzachita miseche za iyo ndi ena. Mungakhale wosafuna kuyanjana naye kwambiri monga poyamba, komabe inu mumamkonda monga mbale wanu Wachikristu.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:19.
Komabe, bwanji ngati ngakhale ndi zoyesayesa zanu za kuthetsa nkhaniyo, wokuchimwiraniyo sakuvomereza cholakwa chake ndi kupepesa? Kodi mungakhululukire m’lingaliro la kusasunga kanthu kukhosi? Kukhululukira ena sikumatanthauza kuti tiyenera kulekerera kapena kuchepetsa zimene achita. Mkwiyo ndiwo katundu wothodwetsa kunyamula; ukhoza kudzaza m’maganizo mwathu, ukumatilanda mtendere. Poyembekezera kupepesa kumene sikudzachitika konse, tidzangogwiritsidwa mwala mowonjezereka. Kwenikweni, mwakutero timalola munthu wotichimwirayo kulamulira malingaliro athu. Motero, tifunikira kukhululukira ena, kapena kuleka kukwiya, osati kaamba ka phindu lawo lokha komanso lathu kuti tipitirizebe ndi moyo wathu.
Kukhululukira ena nkovuta nthaŵi zina. Koma pamene munthu asonyeza kulapa koona, tingayese kutsanzira kukhululukira kwa Yehova. Pamene iye akhululukira olakwa olapa, amaleka kukwiya—amapukuta sileti kuliyeretsa ndi kuiŵala m’njira yakuti sadzawaimbanso mlandu pa machimo amenewo mtsogolo. Nafenso tingamenyere nkhondo pa kusasunga kanthu kukhosi pamene wotilakwirayo ali wolapa. Komabe, pangakhale nthaŵi zina pamene sitiyenera kukhululukira. Palibe munthu wochitiridwa nkhalwe zoipitsitsa amene ayenera kuumirizidwa kukhululukira womlakwira wosalapa. (Yerekezerani ndi Salmo 139:21, 22.) Koma m’zochitika zambiri pamene ena atichimwira, tingathe kukhululukira m’lingaliro la kuleka kukwiya, ndipo tingaiŵale m’lingaliro la kusadzaimbanso mlandu mbale wathu pa nkhaniyo mtsogolo.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Kodi Chikhululukiro cha Mulungu Nchotheratu Motani?” m’kope la Galamukani! wa December 8, 1993, masamba 29-30.
b Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 862, imati: “Akristu samafunikira kukhululukira awo amene amachita tchimo dala mwanjiru, mosalapa. Oterowo amakhala adani a Mulungu.”—Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 9]
Yosefe ndi abale ake