Anapeza Mesiya
“Ifetu tapeza Mesiya.”—YOH. 1:41.
1. N’chiyani chinachititsa Andireya kunena kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”?
TSIKU lina Yohane M’batizi anaima ndi ophunzira ake awiri ndipo anaona Yesu akubwera. Atayandikira, Yohane anafuula kuti, “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu!” Nthawi yomweyo, Andireya ndi wophunzira winayo anatsatira Yesu ndipo anakhala naye tsiku lonse. Pa nthawi ina, Andireya anapeza m’bale wake dzina lake Simoni Petulo n’kupita naye kwa Yesu. Anachita zimenezi pambuyo pomuuza nkhani yosangalatsa kwambiri yakuti: “Ifetu tapeza Mesiya.”—Yoh. 1:35-41.
2. Kodi kuona maulosi ena onena za Mesiya kutithandiza bwanji?
2 Patapita nthawi, Andireya, Petulo ndi ophunzira ena anali ndi mwayi wokwanira wofufuza m’Malemba ndipo ananena mosakayikira kuti Yesu wa ku Nazareti ndiye Mesiya amene Mulungu analonjeza. Tiyeni tipitirize kuona maulosi ena onena za Mesiya. Zimenezi zitithandiza kukhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu ndiponso Wodzozedwa wake.
“Taona! Mfumu Yako Ikubwera”
3. Kodi Yesu anakwaniritsa maulosi ati pamene analowa mu Yerusalemu monga mfumu?
3 Mesiya adzalowa mu Yerusalemu monga mfumu. Zekariya analosera kuti: “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni sangalala kwambiri. Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe. Mfumuyo ndi yolungama ndipo yapambana. Iyo ndi yodzichepetsa ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera nyama yokhwima, imene ndi mwana wamphongo wa bulu.” (Zek. 9:9) Wamasalimo analemba kuti: “Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.” (Sal. 118:26) Khamu la anthu linafuula mosangalala kwambiri pamene Yesu analowa mu Yerusalemu. N’zoonekeratu kuti Yesu sanachite kuuza anthuwo kuti afuule choncho. Koma zimene anthuwo anachita zinakwaniritsa ulosiwu ndendende. Pamene mukuwerenga nkhaniyi, yerekezani kuti mukuona zochitikazo ndipo mukumva anthu akufuula mosangalala.—Werengani Mateyu 21:4-9.
4. Kodi lemba la Salimo 118:22, 23 linakwaniritsidwa bwanji?
4 Yesu ndi wamtengo wapatali kwa Mulungu ngakhale kuti ambiri adzakana zoti iye ndi Mesiya. Mogwirizana ndi ulosi, Yesu “ananyozedwa” ndipo anthu amene samamukhulupirira ‘ankamuona ngati wopanda pake.’ (Yes. 53:3; Maliko 9:12) Koma Mulungu anauzira wamasalimo kulemba kuti: “Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona. Umenewu wachokera kwa Yehova.” (Sal. 118:22, 23) Pa nthawi ina, Yesu anatchula ulosi umenewu polankhula ndi atsogoleri achipembedzo amene ankadana naye. Petulo nayenso ananena kuti ulosiwu unakwaniritsidwa pa Khristu. (Maliko 12:10, 11; Mac. 4:8-11) Yesu anadzakhala mwala “wapakona pa maziko” a mpingo wachikhristu. Ngakhale kuti anthu osaopa Mulungu anamukana, ‘Mulungu anamusankha’ ndipo ndi “wamtengo wapatali kwa iye.”—1 Pet. 2:4-6.
Wophunzira Wina Anamupereka Ndipo Ena Anamuthawa
5, 6. Kodi maulosi ananena zotani pa nkhani ya kuperekedwa kwa Mesiya ndipo zinakwaniritsidwa bwanji?
5 Ulosi unanena kuti Mesiya adzaperekedwa ndi mnzake wosakhulupirika. Davide analosera kuti: “Munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira, munthu amene anali kudya chakudya changa, wakweza chidendene chake kundiukira.” (Sal. 41:9) Kale, anthu ankaona kuti kudyera limodzi ndi chizindikiro chakuti anthuwo ndi ogwirizana kwambiri. (Gen. 31:54) Choncho zimene Yudasi Isikariyoti anachita popereka Yesu kunali kusakhulupirika kwakukulu. Pofotokozera atumwi ake za munthu amene adzamupereke, Yesu anasonyeza kuti ulosi wa Davide umenewu udzakwaniritsidwa. Iye anati: “Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha. Koma zili choncho kuti Malemba akwaniritsidwe, paja amati, ‘Munthu amene anali kudya chakudya changa wanyamula chidendene chake kundiukira.’”—Yoh. 13:18.
6 Munthu amene adzapereke Mesiya adzapatsidwa ndalama 30 zasiliva, zomwe ndi mtengo wogulira kapolo. Mateyu ananena kuti Yudasi anapatsidwa ndalama 30 zokha zasiliva kuti apereke Yesu ndipo izi zinakwaniritsa ulosi wa pa Zekariya 11:12, 13. Koma n’chifukwa chiyani Mateyu ananena kuti ulosi umenewu unanenedwa ndi “mneneri Yeremiya”? Mu ‘buku la aneneri’ munali buku la Yeremiya, la Zekariya komanso mabuku ena. Zikuoneka kuti pamene Mateyu ankalemba zimenezi, buku la Yeremiya linkaikidwa kumayambiriro kwa bukuli. Choncho pamene Mateyu anatchula “Yeremiya” anali kunena za buku lonse la aneneri. (Yerekezerani ndi Luka 24:44.) Yudasi sanagwiritse ntchito ndalama zimenezi m’malomwake anakaziponya m’kachisi n’kupita kukadzimangirira.—Mat. 26:14-16; 27:3-10.
7. Kodi ulosi wa pa Zekariya 13:7 unakwaniritsidwa bwanji?
7 Ngakhale ophunzira a Mesiya adzamusiya n’kubalalika. Zekariya analemba kuti: “Ipha m’busa ndipo nkhosa zake zibalalike.” (Zek. 13:7) Pa Nisani 14 mu 33 C.E., Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno, pakuti Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa, ndipo nkhosa za m’gululo zidzabalalika.’” Izi ndi zimene zinachitikadi chifukwa Mateyu analemba kuti “ophunzira ake onse anamuthawa [Yesu], n’kumusiya yekha.”—Mat. 26:31, 56.
Ananenezedwa Ndiponso Kumenyedwa
8. Kodi lemba la Yesaya 53:8 linakwaniritsidwa bwanji?
8 Mesiya adzazengedwa mlandu n’kuweruzidwa kuti aphedwe. (Werengani Yesaya 53:8.) M’bandakucha pa Nisani 14, Khoti lonse Lalikulu la Ayuda linasonkhana, linamanga Yesu n’kumupereka kwa Pontiyo Pilato, yemwe anali bwanamkubwa wachiroma. Pilato anamufunsa Yesu ndipo anamupeza wopanda mlandu uliwonse. Koma iye atafunsa khamu la anthu ngati likufuna kuti amasule Yesu, khamulo linafuula kuti: “M’pachikeni!” Ndiyeno linapempha kuti amasule chigawenga china dzina lake Baraba. Pofuna kusangalatsa khamulo, Pilato anamasula Baraba, analamula kuti Yesu akwapulidwe ndipo kenako anamupereka kuti akamupachike.—Maliko 15:1-15.
9. Kodi n’chiyani chinachitika m’nthawi ya Yesu pokwaniritsa ulosi wa pa Salimo 35:11?
9 Mboni zonama zidzaneneza Mesiya. Davide analemba kuti: “Mboni zachiwawa zimaimirira. Zimandifunsa zinthu zimene sindikudziwa.” (Sal. 35:11) Mogwirizana ndi ulosiwu, “ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda anali kufunafuna umboni wonama kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha.” (Mat. 26:59) “Ndipo anthu ambiri anali kupereka umboni wonama kutsutsana naye, koma maumboni awowo anali kutsutsana.” (Maliko 14:56) Adani a Yesu olusawo sanasamale zoti maumboni amene ankaperekedwawo anali abodza. Chomwe ankafuna ndi chakuti Yesu aphedwe basi.
10. Kodi lemba la Yesaya 53:7 linakwaniritsidwa bwanji?
10 Mesiya sadzayankha anthu omuneneza. Yesaya analosera kuti: “Iye anapanikizidwa ndipo analola kuti asautsidwe, koma sanatsegule pakamwa pake. Anatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa, ndipo mofanana ndi nkhosa yaikazi imene imakhala chete akamaimeta ubweya, nayenso sanatsegule pakamwa pake.” (Yes. 53:7) “Pamene ansembe aakulu komanso akulu anali kumuneneza, [Yesu] sanayankhe chilichonse.” Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zonse zimene akukunenezazi?” Koma Yesu “anangokhala duu, osanena kanthu, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambiri.” (Mat. 27:12-14) Yesu sananyoze anthu omuneneza.—Aroma 12:17-21; 1 Pet. 2:23.
11. Kodi chinachitika n’chiyani pokwaniritsa Yesaya 50:6 ndi Mika 5:1?
11 Yesaya analosera kuti Mesiya adzamenyedwa. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.” (Yes. 50:6) Nayenso Mika analosera kuti: “Iwo adzamenya woweruza wa Isiraeli patsaya ndi ndodo.” (Mika 5:1) Posonyeza kuti ulosiwu unakwaniritsidwa, Maliko analemba kuti: “Ena anayamba kumulavulira [Yesu], kumuphimba nkhope ndi kumukhoma nkhonya. Iwo anali kunena kuti: ‘Losera!’ Atamuwomba mbama, asilikali a pakhoti anamutenga.” Maliko ananenanso kuti asilikali “anali kum’menya m’mutu ndi bango ndi kumulavulira, ndipo anali kugwada ndi kumuweramira” momunyoza. (Maliko 14:65; 15:19) Anthuwa ankachitira Yesu zonsezi ngakhale kuti iye sanawalakwire chilichonse.
Anakhala Wokhulupirika Mpaka Imfa
12. Kodi lemba la Salimo 22:16 ndi Yesaya 53:12 linakwaniritsidwa bwanji pa Yesu?
12 Ulosi unanena zinthu zina zokhudza kupachikidwa kwa Mesiya. Davide ananena kuti: “Khamu la anthu ochita zoipa landizinga. Iwo akuluma manja ndi mapazi anga ngati mkango.” (Sal. 22:16) Maliko analemba za kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu ndipo zinthu zimene analemba ndi zoti anthu ambiri amene amawerenga Baibulo amazidziwa bwino. Iye anati: “Tsopano nthawi ili cha m’ma 9 koloko m’mawa, iwo anam’pachika.” (Maliko 15:25) Anakhomera manja ndi mapazi ake kumtengo. Ulosi unanenanso kuti Mesiya adzaphedwa limodzi ndi ochimwa. Yesaya analemba kuti: “Anakhuthula moyo wake mu imfa ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ochimwa.” (Yes. 53:12) Ndiyeno zinachitika kuti “achifwamba awiri anapachikidwa limodzi ndi [Yesu], mmodzi kudzanja lake lamanja, wina kumanzere kwake.”—Mat. 27:38.
13. Kodi ulosi wa pa Salimo 22:7, 8 unakwaniritsidwa bwanji pa Yesu?
13 Davide analosera kuti Mesiya adzanyozedwa. (Werengani Salimo 22:7, 8.) Yesu atapachikidwa pamtengo wozunzikirapo ananyozedwa. Mateyu analemba kuti: “Tsopano anthu odutsa anayamba kunena mawu onyoza Yesu. Anali kupukusa mitu yawo n’kumanena kuti: ‘Iwe wogwetsa kachisi ndi kum’manga m’masiku atatu, dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!’” Nawonso ansembe aakulu, alembi komanso akulu anayamba kumuchita chipongwe ndi kunena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ameneyutu ndi Mfumu ya Isiraeli, atsiketu pamtengo wozunzikirapowo kuti ife timukhulupirire. Suja amakhulupirira Mulungu? Mulunguyo am’pulumutse tsopano ngati akumufunadi. Ndi ujatu anali kunena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’” (Mat. 27:39-43) Yesu anapirira zonsezi popanda kupsa mtima kapena kubwezera. Iye ndiye chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.
14, 15. Kodi maulosi okhudza zovala za Mesiya ndiponso kumupatsa vinyo wowawasa anakwaniritsidwa bwanji?
14 Adzachita maere pazovala za Mesiya. Wamasalimo analemba kuti: “Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo, ndipo akuchita maere pazovala zanga.” (Sal. 22:18) Zimenezi zinachitikadi. Baibulo limanena kuti asilikali achiroma “atam’pachika [Yesu] anagawana malaya ake akunja mwa kuchita maere.”—Mat. 27:35; werengani Yohane 19:23, 24.
15 Mesiya adzapatsidwa vinyo wowawasa wosakaniza ndi ndulu. Wamasalimo analemba kuti: “Anandipatsa chomera chakupha kuti ndidye, ndipo anayesa kundimwetsa vinyo wowawasa pamene ndinali ndi ludzu.” (Sal. 69:21) Mateyu analemba kuti: “Anapatsa Yesu vinyo wosakaniza ndi ndulu kuti amwe, koma iye atalawa, anakana kumwa.” Kenako, “mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga chinkhupule ndi kuchiviika m’vinyo wowawasa ndipo anachiika kubango ndi kum’patsa kuti amwe.”—Mat. 27:34, 48.
16. Kodi ulosi wa pa Salimo 22:1 unakwaniritsidwa bwanji?
16 Mesiya adzaoneka ngati wasiyidwa ndi Mulungu. (Werengani Salimo 22:1.) Maliko ananena kuti cha m’ma 3 koloko, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “‘Eli, Eli, lama sabachthani?’ Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: ‘Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?’” (Maliko 15:34) Ponena zimenezi, sikuti Yesu anali atasiya kukhulupirira Atate wake wakumwamba. Iye anadziwa kuti Mulungu sadzamuteteza kwa adani ake pa nthawi ya imfa yake. Unali mwayi woti Yesu asonyeze kuti adzakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ngakhale pamene akuyesedwa. Kufuula kwa Yesu kumeneku kunakwaniritsa ulosi wa pa Salimo 22:1.
17. Kodi lemba la Zekariya 12:10 ndi Salimo 34:20 linakwaniritsidwa bwanji?
17 Mesiya adzalasidwa, koma mafupa ake sadzathyoledwa. Anthu okhala mu Yerusalemu “adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.” (Zek. 12:10) Lemba la Salimo 34:20 limanena kuti: “[Mulungu] amateteza mafupa onse a wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.” Mtumwi Yohane ananena kuti ulosiwu unakwaniritsidwa. Iye analemba kuti: “Mmodzi wa asilikaliwo anamulasa [Yesu] ndi mkondo m’mbalimu cham’mimba, ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi. Munthu amene anaona zimenezo [Yohane] akuchitira umboni, ndipo umboni wakewo ndi woona. . . . Izi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, pamene linati: ‘Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.’ Ndiponso lemba lina limati: ‘Iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.’”—Yoh. 19:33-37.
18. Kodi zinatheka bwanji kuti Yesu aikidwe m’manda limodzi ndi anthu olemera?
18 Mesiya adzaikidwa m’manda limodzi ndi anthu olemera. (Werengani Yesaya 53:5, 8, 9.) Madzulo a pa Nisani 14, “munthu wina wachuma wa ku Arimateya, wotchedwa Yosefe,” anapempha Pilato kuti atenge mtembo wa Yesu ndipo Pilato analoleza. Mateyu analemba kuti: “Yosefe anatenga mtembowo ndi kuukulunga munsalu yoyera yabwino kwambiri, ndipo anakauika m’manda ake achikumbutso atsopano, amene anawasema m’thanthwe. Kenako anagubuduza chimwala chachikulu ndi kutseka pakhomo la manda achikumbutsowo, n’kuchoka.”—Mat. 27:57-60.
Tamandani Mesiya, Mfumu Yathu
19. Kodi chinachitika n’chiyani pokwaniritsa ulosi wa pa Salimo 16:10?
19 Mesiya adzaukitsidwa. Davide analemba kuti: “[Yehova] simudzasiya moyo wanga m’Manda.” (Sal. 16:10) Azimayi ena anapita kumanda kumene Yesu anaikidwa. Taganizirani mmene anadabwira ataona mngelo ali m’mandamo. Mngeloyu anawauza kuti: “Musadabwe choncho. Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, amene anapachikidwa. Iyetu wauka kwa akufa, salinso muno ayi. Taonani! Si apa pamene anamugoneka.” (Maliko 16:6) Mtumwi Petulo anauza khamu la anthu limene linasonkhana ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E. kuti: “[Davide] anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka kwa Khristu. Ananeneratu kuti iye sanasiyidwe m’Manda, komanso kuti thupi lake silinavunde.” (Mac. 2:29-31) Mulungu sanalole kuti thupi la Mwana wake wokondedwa livunde. Koma iye anachita chinthu china chozizwitsa kwambiri. Anaukitsa Yesu kuti akakhale ndi moyo wauzimu kumwamba.—1 Pet. 3:18.
20. Kodi maulosi amanena chiyani za ulamuliro wa Mesiya?
20 Ulosi umanena kuti Mulungu adzalengeza kuti Yesu ndi Mwana wake. (Werengani Salimo 2:7; Mateyu 3:17.) Khamu la anthu linatamanda Yesu ndiponso Ufumu umene unali kubwera. Ifenso timamutamanda mosangalala polankhula za iye ndi Ufumu wake. (Maliko 11:7-10) Posachedwapa, Khristu adzawononga adani ake pamene ‘adzakwera pahatchi yake chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo.’ (Sal. 2:8, 9; 45:1-6) Nthawi imeneyo, Ufumu wake udzabweretsa mtendere padziko lonse lapansi ndipo aliyense sadzasowa kanthu. (Sal. 72:1, 3, 12, 16; Yes. 9:6, 7) Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Yehova, wayamba kale kulamulira monga Mfumu kumwamba. Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala Mboni za Yehova ndi kuuza anthu ena mfundo za choonadi zimenezi.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ulosi wonena za kuperekedwa ndiponso kusiyidwa kwa Yesu unakwaniritsidwa bwanji?
• Kodi ndi zinthu ziti zokhudza kupachikidwa kwa Yesu Khristu zimene zinaloseredwa?
• Kodi n’chiyani chimakuchititsani kukhulupirira kuti Yesu ndiye Mesiya?
[Chithunzi patsamba 13]
Kodi zimene Yesu anachita polowa mu Yerusalemu monga mfumu zinakwaniritsa maulosi ati?
[Zithunzi patsamba 15]
Yesu anafa chifukwa cha machimo athu koma panopa ndi Mfumu