Zochitika m’Mbiri ya Ufulu wa Kulankhula
M’MBIRI yonse anthu amenyera nkhondo ufulu wa kulankhula. Apanga malamulo, amenya nkhondo, ndipo miyoyo yatayika pankhani ya kuyenera kwa kufotokoza poyera lingaliro la munthu.
Kodi nchifukwa ninji kuyenera kwachibadwa kwachionekere kumeneko kwasonkhezera mkangano, kufikiradi pa kukhetsa mwazi? Kodi nchifukwa ninji zitaganya za anthu, zakale ndi zamakono zomwe, zimapeza kukhala koyenera kuika malire kapena ngakhale kuletseratu kukhalapo kwa kuyenera kumeneku?
Malingaliro a anthu pa nkhani ya ufulu wa kulankhula akhala akumasinthasintha kwambiri. Nthaŵi zina ufulu wa kulankhula waonedwa ngati mwaŵi wofunikira kukhala nawo. Panthaŵi zina walingaliridwa monga vuto lofunikira kuthetsedwa ndi maboma kapena zipembedzo.
Popeza mbiri njodzala ndi nkhani za awo amene anamenyera nkhondo kuyenera kwa kufotokoza poyera lingaliro la munthu, kumene kaŵirikaŵiri kunawachititsa kuzunzidwa kapena kuphedwa mwankhanza, kupenda zina za zochitika zimenezi kuyenera kutipatsa mpata wa kudziŵa za vutolo.
Ophunzira mbiri angakumbukire bwino za wafilosofi wachigiriki Socrates (470-399 B.C.E.), amene malingaliro ake ndi ziphunzitso zinaonedwa kukhala zisonkhezero zoipitsa makhalidwe a achichepere ku Athens. Zimenezi zinachititsa nkhaŵa yaikulu pakati pa atsogoleri andale ndi achipembedzo a ulamuliro wachigiriki ndi kuchititsa imfa yake. Pempho lake pamaso pa oweruza amene anamuimba mlandu likali kudzitetezera kwamphamvu la ufulu wa kulankhula: “Ngati mungalole kundichotsera mlandu panthaŵi ino kuti ndisalankhulenso za malingaliro anga pofunafuna nzeru kumeneku, ndi kuti ngati ndipezedwanso ndikuchita zimenezi ndidzafa, ndiyenera kukuuzani kuti, ‘Amuna inu a mu Atene, ndidzamvera Mulungu koposa inu. Pamene ndikali moyo ndi nyonga sindidzasiya kutsatira nthanthi ndi kulimbikitsa ndiponso kukopa aliyense wa inu amene ndidzakumana naye. Pa zimenezi, ndithudi ndidzatsata malamulo a Mulungu . . .’ Ndipo, inu Aatene, ndikupitiriza kunena kuti, ‘Kaya mundichotsera mlanduwu kapena ayi; koma dziŵani kuti sindidzachitira mwina, ngakhale ngati nditi ndifere zimenezi nthaŵi zambiri.’”
Pamene nthaŵi inali kupita, Roma anali ndi kusintha m’mbiri yake yoyambirira moyanja ziletso zochepa, akumasinthanso kuyanja ziletso zambiri pamene ufumuwo unali kufutukuka. Zimenezi zinayambitsa nyengo yoipitsitsa koposa pa ufulu wa kulankhula. Mkati mwa ulamuliro wa Tiberiyo (14-37 C.E.), sanalekerere konse awo amene anatsutsa boma kapena njira zake. Ndipo sanali Roma yekha amene anatsutsa ufulu wa kulankhula; inali nthaŵiyi pamene atsogoleri achiyuda anaumiriza Pontiyo Pilato kupha Yesu chifukwa cha ziphunzitso zake ndi kulamulanso mwamphamvu kuti atumwi ake aleke kulalikira. Ameneŵanso anali okonzekera kufa koposa kuleka.—Machitidwe 5:28, 29.
Mkati mwa nyengo zochuluka za mbiri, zoyenera za munthu zovomerezedwa ndi maboma kaŵirikaŵiri zinasinthidwa kapena zinalandidwa monga momwe anafunira, zimene zinachititsa kumenyera nkhondo kopitiriza ufulu wa kulankhula. Kuyambira mu Nyengo za Pakati, anthu ena anafuna chikalata cholembedwapo mawu a zoyenera zawo, chokhala ndi ziletso pa ulamuliro wa boma pa zoyenera zimenezo. Chotero, mipambo yambiri ya zoyenera inayamba kupangidwa. Pakati pa imeneyi panali Magna Carta, chinthu chimene chinasintha zinthu m’zoyenera za munthu. Pambuyo pake panadza English Bill of Rights (1689), Virginia Declaration of Rights (1776), French Declaration of the Rights of Man (1789), ndi United States Bill of Rights (1791).
M’zaka za zana la 17, 18 ndi la 19 munali anthu amene anatsogolera m’mbiri ya kulankhula mosabisa za ufulu wa kulankhula. Mu 1644 wolemba ndakatulo wachingelezi John Milton, amene angakumbukiridwe bwino chifukwa cha Paradise Lost, analemba kabuku kotchuka kakuti Areopagitica monga kutsutsa kwake ziletso pa ufulu wa kufalitsa nkhani.
M’zaka za zana la 18 munali chifutukuko cha ufulu wa kulankhula ku England, ngakhale kuti ziletso zinali zikalipo. Ku America maboma ake anali kufuna moumirira ufulu wa kulankhula, mawu apakamwa ndi osindikizidwa omwe. Mwachitsanzo, Constitution of the Commonwealth of Pennsylvania, ya September 28, 1776, mwapang’ono inati: “Kuti anthu ali ndi ufulu wa kulankhula, ndi wa kulemba, ndi wa kufalitsa malingaliro awo, chotero ufulu wa kufalitsa nkhani suyenera kuletsedwa.”
Mawu ameneŵa anasonkhezera kupangidwa kwa First Amendment ku United States. Konsichushoni ya mu 1791, imene inalengeza za maganizo a oyambitsa American Constitution pa zoyenera za anthu zokondedwa inati: “Nyumba ya Malamulo sidzapanga lamulo lililonse pa gulu lachipembedzo, kapena kuletsa ufulu wake wa kulankhula; kapena kuchepetsa ufulu wa kulankhula, kapena wa kufalitsa nkhani; kapena kuyenera kwa anthu kusonkhana mwamtendere, ndi kupempha Boma kupereka thandizo pa madandaulo awo.”
Wafilosofi wa m’zaka za zana la 19 wachingelezi John Stuart Mill anafalitsa nkhani yake yakuti “On Liberty” mu 1859. Imagwidwa mawu kaŵirikaŵiri ndi imene yasonyezedwa kukhala amodzi a mawu aakulu koposa potsata ufulu wa kulankhula.
Komabe, kumenyera nkhondo ufulu wa kulankhula poyera sikunathere pa kufika kwa zaka zonenedwa kukhala zopereka chidziŵitso za zana lino la 20. Mwachitsanzo, chifukwa cha zoyesayesa za kuchepetsa ufulu wa kulankhula ku America, zilengezo zotetezera ufuluwo zamveka m’mabwalo a milandu, m’mabwalo aang’ono ndi m’Bwalo Lapamwamba la United States.
Woweruza Oliver Wendell Holmes, Jr., wa Bwalo Lapamwamba la United States, anafotokoza za chikhulupiriro chake pa ufulu wa kulankhula m’zigamulo zambiri za bwalo la milandu. Pofotokoza njira yodziŵira ufulu wa kulankhula, anati: “Ngati pali lamulo lililonse la Konsichushoni limene limafuna kulitsatira kwambiri kuposa lina lililonse ndilo lamulo lakuti munthu ayenera kulankhula mwaufulu malingaliro ake—osati kulola awo amene akuvomerezana nafe kulankhula mwaufulu malingaliro awo koma ufulu wa kulankhula malingaliro amene tikudana nawo.”—United States v. Schwimmer, 1928.
Kusalabadira lamulo limeneli nkumene kwasonkhezera nkhondo za m’mabwalo a milandu zimene zimachititsa nkhaniyi kusinthasinthabe pakati pa ufulu ndi kuumiriza. Kaŵirikaŵiri pamakhala lingaliro lakuti, “Ufulu wa kulankhula n’ngwanga—osati wako.” M’buku la dzina limeneli Nat Hentoff akutchula zochitika pamene otetezera mwamphamvu First Amendment anasintha malingaliro awo malingana ndi kuganiza kwawo. Akutchula za milandu imene Bwalo Lapamwamba la United States linabweza zigamulo zake, kuphatikizapo zina zokhudza Mboni za Yehova ndi zaka zawo zambiri za kumenyera nkhondo ufulu wa kulankhula momasuka ponena za zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Ponena za izo, iyeyo analemba kuti: “Ziŵalo za chipembedzo chimenecho zathandiza kwambiri m’zaka zonsezi kufutukula ufulu wa chikumbumtima kupyolera m’milandu yokhudza konsichushoni.”
Openda milandu ambiri ndi olemba mbiri amakono alemba zambiri ponena za nkhondo za m’mabwalo a milandu ambiri zomenyedwa kutetezera ufulu wa kulankhula kumapeto kwa zaka za zana lino la 20, osati ku America kokha komanso kumaiko ena. Ufulu wa kulankhula ngwosatsimikizirika. Ngakhale kuti maboma angadzitamirire za kukhala ndi ufulu umene amapatsa anthu awo, ukhoza kutayika pamene boma kapena oweruza milandu asintha, monga momwe zochitika zasonyezera. Mboni za Yehova zakhala zotsogolera mu nkhondo ya ufulu wofunika umenewu.
M’buku lake lakuti These Also Believe, Profesa C. S. Braden akulemba kuti: “Izo [Mboni za Yehova] zachita utumiki wapadera pa demokrase mwa nkhondo zawo za kusungitsa zoyenera za munthu, pakuti m’nkhondo yawo achita zambiri potetezera zoyenera zimenezo kaamba ka kagulu kalikonse mu America. Pamene zoyenera za munthu za kagulu kalikonse ziponderezedwa, zoyenera za magulu ena zimakhala zosatetezereka. Motero iwo achirikiza kwambiri kusungitsa zina za zinthu zofunika kwambiri mu demokrase yathu.”
Anthu okonda ufulu amavutika mtima kuti adziŵe chifukwa chake maboma ena ndi zipembedzo zimamana anthu awo ufulu umenewu. Ndiko kumana choyenera chofunika kwa munthu, ndipo anthu ambiri padziko lonse amavutika ndi kuponderezedwa kwa ufulu umenewu. Kodi maganizo a anthu kulinga ku ufulu wa kulankhula, ngakhale m’maiko amene ali ndi kuyenera kofunika kumeneku, adzapitiriza kumasinthasintha? Kodi lingaliro la ufulu wa kulankhula lidzagwiritsiridwa ntchito kulungamitsira makhalidwe oipa kapena kutukwana? Mabwalo a milandu ayamba kale kulimbana ndi mkanganowo.
[Chithunzi patsamba 3]
Socrates anachirikiza ufulu wa kulankhula
[Mawu a Chithunzi]
Musei Capitolini, Roma