-
Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa MulunguMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
6. Buku la anthu onse
Baibulo ndi buku limene lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. Werengani Machitidwe 10:34, 35, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani Mulungu amafuna kuti Mawu ake amasuliridwe ndi kufalitsidwa m’zinenero zambiri?
Kodi ndi zinthu ziti zokhudza Baibulo zimene zimakusangalatsani?
Pafupifupi
munthu aliyense
padzikoli
akhoza kupeza Baibulo m’chinenero chimene amamva
Baibulo likupezeka m’zinenero zoposa
3,000
lathunthu kapena mbali zake zina
Mabaibulo
5,000,000,000
afalitsidwa
ndipo nambala imeneyi ikuposa buku lina lililonse
-
-
Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana MumpingoMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
4. Yesetsani kuthetsa mtima watsankho
Tonsefe timafuna kumakonda abale ndi alongo athu onse. Komabe tingavutike kugwirizana ndi munthu yemwe amaoneka wosiyana ndi ife. Ndiye n’chiyani chimene chingatithandize? Werengani Machitidwe 10:34, 35, kenako mukambirane mafunso awa:
Yehova amalandira anthu amitundu yonse kuti akhale Mboni zake. Ndiye kodi mungatengere bwanji chitsanzo cha Yehova pa nkhani ya mmene mumaonera anthu omwe ndi osiyana ndi inu?
Kodi inuyo mukufuna kupewa zinthu ziti zomwe anthu ambiri m’dera lanu amachita posonyeza tsankho?
Werengani 2 Akorinto 6:11-13, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mukuganiza kuti muyenera kuchita chiyani kuti muzikonda kwambiri abale ndi alongo omwe mumasiyana nawo zinthu zina?
-