-
1 | Muziyesetsa Kupewa TsankhoNsanja ya Olonda (Yogawira)—2022 | Na. 1
-
-
Baibulo Limati:
“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—MACHITIDWE 10:34, 35.
Zimene Lembali Limatanthauza:
Yehovaa Mulungu samatiweruza potengera mtundu wathu, mmene khungu lathu limaonekera kapenanso chikhalidwe chathu. Mulungu amaona zinthu zofunika kwambiri monga zomwe timaganiza komanso zimene timalakalaka mumtima mwathu. Baibulo limanenanso kuti munthu amaona zooneka ndi maso “koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Samueli 16:7.
-