-
Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a YesuNsanja ya Olonda—2012 | January 15
-
-
11, 12. Kodi Herode anazunza bwanji Akhristu kuphatikizapo Petulo ndipo n’chifukwa chiyani ankachita zimenezo?
11 Petulo amene analipo pa nthawiyo anaona mmene mapemphero ochokera pansi pa mtima amathandizira. (Werengani Machitidwe 12:1-6.) Mavesi oyambirira a nkhaniyi amatiuza zimene Herode anachita pozunza Akhristu n’cholinga choti Ayuda azimukonda. Iye ankadziwa bwino kuti Yakobo anali mtumwi amene ankachitira limodzi zinthu ndi Yesu. Choncho iye anamupha “ndi lupanga.” (Vesi 2) Izi zinachititsa kuti mpingo utaye mtumwi wokondedwa ndipo chimenechi chinali chiyeso chachikulu.
-
-
Phunzirani Kukhala Maso Kuchokera kwa Atumwi a YesuNsanja ya Olonda—2012 | January 15
-
-
13, 14. (a) Kodi mpingo unachita chiyani Petulo atamangidwa? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Akhristu anzake a Petulo anachita pa nkhani ya pemphero?
13 Mpingo unadziwa zoyenera kuchita. Vesi 5 limati: “Petulo anakhala akusungidwa m’ndendemo, koma mpingo unali kumupempherera mosalekeza kwa Mulungu ndi mtima wonse.” Iwo anapemphera ndi mtima wonse kuti m’bale wawo wokondedwa athandizidwe ndi Mulungu. Iwo sanataye mtima chifukwa choti Yakobo anaphedwa kapena kuganiza kuti mapemphero awo sangayankhidwe. Iwo ankadziwa kuti mapemphero a anthu okhulupirika ndi amtengo wapatali kwa Yehova. Iye amayankha mapemphero ngati ali ogwirizana ndi chifuniro chake.—Aheb. 13:18, 19; Yak. 5:16.
14 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Akhristu anzake a Petulo anachita? Munthu amene ali maso samangopempherera nkhani zokhudza iyeyo koma amapemphereranso abale ndi alongo ena. (Aef. 6:18) Kodi mukudziwa za abale ndi alongo amene akukumana ndi mayesero? Ena akuzunzidwa, ena saloledwa ndi boma kuti azilalikira ndipo m’madera ena mukuchitika masoka achilengedwe. Ndi bwino kuwatchula anthu oterewa m’mapemphero. Mwinanso mukudziwa anthu ena amene akukumana ndi mavuto osaonekera kwambiri. Mwina angakumane ndi mavuto a m’banja, kukhumudwitsidwa kapena matenda. Mungachite bwino kuganizira za anthu amene mungawatchule mwachindunji m’mapemphero anu kwa Yehova, yemwe ndi “Wakumva mapemphero.”—Sal. 65:2.
-