Chitsanzo Chouziridwa cha Ntchito Yaumishonale Wachikristu
“Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu.”—1 AKORINTO 11:1.
1. Kodi ndimwanjira zina ziti zimene Yesu anaperekera chitsanzo chapadera kwa otsatira ake kuti atsanze? (Afilipi 2:5-9)
NCHITSANZO chapadera chotani nanga chimene Yesu anapereka kwa ophunzira ake! Mosangalala anasiya ulemelero wake wakumwamba kubwera padziko lapansi ndi kukhala pakati pa anthu ochimwa. Anali wofunitsitsa kuvutika kwakukulu kaamba ka chipulumutso cha anthu, chachikulu koposa, kaamba ka kuyeretsedwa kwa dzina la Atate wake wakumwamba. (Yohane 3:16; 17:4) Pozengedwa mlandu wofuna moyo wake, Yesu analengeza molimba mtima kuti: “Ndinabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi.”—Yohane 18:37.
2. Kodi nchifukwa ninji Yesu woukitsidwayo analamula ophunzira ake kupitiriza ntchito imene anaiyamba?
2 Isanafike imfa yake, Yesu anawaphunzitsa bwino koposa ophunzira ake kuti akapitirize ntchito yakupereka umboni wa chowonadi cha Ufumu. (Mateyu 10:5-23; Luka 10:1-16) Chifukwa chake, pambuyo pakuuka kwake, Yesu anakhoza kupereka lamulo lakuti: “Mukani ndi kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, mukumawabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, mukumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20, NW.
3. Kodi ntchito yakupanga ophunzira inafutukulidwa motani, koma kodi ndi m’zigawo ziti mmene inachitidwa kwakukulukulu?
3 Kwazaka zitatu ndi theka zotsatira, ophunzira a Yesu anamvera lamulo limeneli koma analekezera kupanga kwawo ophunzira kwa Ayuda, otembenuzidwira ku Chiyuda, ndi Asamariya odulidwa. Ndiyeno, mu 36 C.E., Mulungu analamula kuti mbiri yabwino ilalikidwe kwa mwamuna wosadulidwa, Korneliyo, ndi a m’nyumba yake. M’zaka khumi zotsatira, Akunja ena anabweretsedwa mumpingo. Komabe, ntchito yaikulu iwonekera kukhala itachitidwira m’madera a kummaŵa kwa Mediterranean.—Machitidwe 10:24, 44-48; 11:19-21.
4. Kodi nchochitika chapadera chotani chimene chinachitika pafupifupi 47-48 C.E.?
4 Panafunikira chinthu chosonkhezera kapena chokhozetsa Akristu kupanga ophunzira Achiyuda ndi Akunja a kumadera akutali. Chotero, pafupifupi 47-48 C.E., akulu a mpingo wa Antiokeya wa m’Suriya analandira uthenga waumulungu uwu: “Mundipatulire ine Barnaba ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.” (Machitidwe 13:2) Wonani kuti Paulo panthaŵiyo ankadziŵidwa ndi dzina lake lakale, Saulo. Wonaninso kuti, Mulungu anayamba kutchula Barnaba asanatchule Paulo, mwinamwake chifukwa chakuti panthaŵiyo Barnaba anawonedwa kukhala wamkulu pa aŵiriwo.
5. Kodi nchifukwa ninji cholembedwa cha ulendo waumishonale wa Paulo ndi Barnaba chiri chaphindu kwambiri kwa Akristu lerolino?
5 Cholembedwa chatsatanetsatane cha ulendo waumishonale wa Paulo ndi Barnaba ncholimbikitsa kwambiri kwa Mboni za Yehova, makamaka kwa amishonale ndi apainiya amene asamukira kumalo akutali kuchokera kumatauni akwawo kukatumikira Mulungu m’chitaganya chachilendo. Ndiponso, kupenda machaputala 13 ndi 14 a Machitidwe kudzasonkhezera enanso kutsanzira Paulo ndi Barnaba ndi kukulitsa phande lawo m’ntchito yofunika koposa yakupanga ophunzira.
Chisumbu cha Kupro
6. Kodi nchitsanzo chotani chimene amishonale anapereka ku Kupro?
6 Mosataya nthaŵi amishonalewo anayenda ndi ngalaŵa kuchokera ku doko la Suriya wa ku Selukeya mpaka ku chisumbu cha Kupro. Atafika mu Salami, sanacheutsidwe koma “analalikira mawu a Mulungu m’masunagoge a Ayuda.” Potsatira chitsanzo cha Kristu, sanafune kukhala pansi mumzindamo ndi kuyembekezera kuti anthu apachisumbupo abwere kwa iwo. Mmalomwake, anagwira ntchito monse mmene anapita ‘pachisumbu chonse.’ Mosakaikira konse, izi zinaphatikizapo kuyenda kwambiri ndi kusinthasintha malo ogona, popeza kuti Kupro ndichisumbu chachikulu, ndipo ulendo wawo unawayendetsa chigawo chake chachikulu koposa.—Machitidwe 13:5, 6.
7. (a) Kodi nchochitika chapadera chotani chimene chinachitika ku Pafo? (b) Kodi cholembedwachi chimatilimbikitsa kukhala ndi kaimidwe kamaganizo kotani?
7 Chakumapeto kwa nthaŵi yawo yakukhala kumeneko, amuna aŵiriwo anafupidwa ndi chokumana nacho chabwino kwambiri mumzinda wa Pafo. Wolamulira wa chisumbucho, Sergio Paulo, anamvetsera uthenga wawo ndipo “anakhulupirira.” (Machitidwe 13:7, 12) Pambuyo pake Paulo analemba kuti: “Penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iyayi.” (1 Akorinto 1:26) Komabe, pakati pa amphamvu amene analabadira panali Sergio Paulo. Chokumana nachochi chiyenera kulimbikitsa onse, makamaka amishonale, kukhala ndi kaimidwe kamaganizo kabwino ponena za kuchitira umboni kwa nduna za boma, monga momwe tikulimbikitsidwira kuchita pa 1 Timoteo 2:1-4. Amuna aulamuliro nthaŵi zina apereka chithandizo chachikulu kwa atumiki a Mulungu.—Nehemiya 2:4-8.
8. (a) Kodi ndikusintha kwa unansi kotani pakati pa Barnaba ndi Paulo kumene kukuwonekera kuyambira panthaŵiyi kumka mtsogolo? (b) Kodi Barnaba anali chitsanzo chabwino mwanjira yotani?
8 Pansi pachisonkhezero cha mzimu wa Yehova, Paulo anachita mbali yaikulu potembenuza Sergio Paulo. (Machitidwe 13:8-12) Ndiponso, kuyambira panthaŵiyi kumka mtsogolo, kukuwonekera kuti Paulo anayamba kutsogolera. (Yerekezerani ndi Machitidwe 13:7 ndi Machitidwe 13:15, 16, 43.) Izi zinali zogwirizana ndi ntchito yaumulungu imene Paulo analandira panthaŵi imene anatembenuzidwa. (Machitidwe 9:15) Mwinamwake chochitika chimenecho chinakhala chiyeso pakudzichepetsa kwa Barnaba. Komabe, mmalo mwakuwona kusintha kumeneku kukhala chitokoso kwa iye, mwachiwonekere Barnaba anachita mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, “Mwana wa Kutonthoza,” ndipo mokhulupirika anachirikiza Paulo paulendo wonse waumishonale ndi pambuyo pake pamene Akristu Achiyuda ena anatsutsa kulalikira kwawo kwa Akunja osadulidwa. (Machitidwe 15:1, 2) Nchitsanzo chabwino chotani nanga chimenechi kwa tonsefe, kuphatikizapo okhala m’nyumba za amishonale ndi za Beteli! Tiyenera kukhala ofunitsitsa nthaŵi zonse kuvomereza masinthidwe ateokratiki ndi kuchirikiza kotheratu awo oikidwa kutsogolera pakati pathu.—Ahebri 13:17.
Chitunda Chathyathyathya cha Asia Minor
9. Kodi tikuphunziranji pakufunitsitsa kwa Paulo ndi Barnaba kupita ku Antiokeya wa m’Pisidiya?
9 Kuchokera ku Kupro, Paulo ndi Barnaba anapita ndi ngalawa ku chigawo chakumpoto kwa Asiya. Pachifukwa chosatchulidwa, amishonalewo sanakhale m’chigawo chakugombe koma anayenda ulendo wautali ndi waupandu wa makilomitala pafupifupi 180 kufika ku Antiokeya wa m’Pisidiya, wokhala chapakati pa chitunda chathyathyathya cha Asia Minor. Izi zinaphatikizapo kuyenda njira zokwera mapiri ndi kutsikira m’dambo kwa mamitala pafupifupi 1,100 pamwamba pa nyanja. Katswiri wa Baibulo J. S. Howson akunena kuti: “Zizoloŵezi zakusayeruzika ndi zauchifwamba za anthu okhala m’mapiriwo olekanitsa chitunda chathyathyathya . . . ndi dambolo la ku gombe lakumwera, zinali zankhalwe m’mbiri yakale yonse.” Ndiponso, amishonalewo, anayang’anizana ndi upandu wa zovuta zachilengedwe. “Palibe chigawo mu Asia Minor,” akuwonjezera motero Howson, “chokhala chapadera kwambiri chifukwa cha ‘maliyambwe amadzi’ kuposa malo a m’mapiri a Pisidiya, kumene mitsinje imaphamuka kumatsinde a materezi aakulu, kapena kukokomokera mwamphamvu m’mipata yopapatiza.” Chidziŵitso chimenechi chimatithandiza kuwona ndi maso amaganizo mtundu wa maulendo amene amishonalewo anali ofunitsitsa kuyenda kaamba ka kufalitsa mbiri yabwino. (2 Akorinto 11:26) Mofananamo lerolino, Mboni za Yehova zambiri zimayang’anizana ndi zopinga zosiyanasiyana kuti zifikire anthu ndi kugaŵana nawo mbiri yabwino.
10, 11. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anasungira mfundo yogwirizanirapo ndi omvetsera ake? (b) Kodi nchifukwa ninji Ayuda ambiri mwachiwonekere anazizwa pakumva za kuvutika kwa Mesiya? (c) Kodi ndichipulumutso cha mtundu wanji chimene Paulo analonjeza omvetsera ake?
10 Popeza kuti munali sunagoge Wachiyuda mu Antiokeya wa m’Pisidiya, amishonalewo anamka kumeneko choyamba kuti akapatse awo ozoloŵerana kwambiri ndi Mawu a Mulungu mwaŵi wakulandira mbiri yabwino. Pamene anaitanidwa kuti alankhule, Paulo ananyamuka ndi kukamba nkhani yapoyera mwaluso kwambiri. M’nkhani yonseyo, Paulo anasunga mfundo yogwirizanirapo ndi omvetserawo Ayuda ndi otembenuzidwira ku Chiyuda. (Machitidwe 13:13-16, 26) Pambuyo pa mawu ake oyambirira, Paulo anapenda mbiri yotchuka ya Ayuda, kuwakumbutsa kuti Yehova adasankha makolo awo akale ndiyeno anawawonjola ku Igupto, limodzinso ndi mmene anawathandizira kugonjetsa nzika za Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno Paulo anagogomezera zochita za Yehova ndi Davide. Chidziŵitso choterocho chinali chofunika kwambiri kwa Ayuda m’zaka za zana loyamba chifukwa chakuti anali kuyembekezera kuti Mulungu adzaika mbadwa ya Davide kukhala mpulumutsi ndi wolamulira wosatha. Panthaŵiyi, Paulo analengeza molimba mtima kuti: “Wochokera m’mbewu yake [Davide] Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israyeli mpulumutsi, Yesu.”—Machitidwe 13:17-23.
11 Komabe, mpulumutsi amene Ayuda ambiri ankayembekezera anali ngwazi yankhondo imene ikawawonjola kuulamuliro wa Aroma ndi kukweza mtundu Wachiyuda pamwamba pa ina yonse. Chifukwa chake, iwo mosakaikira, anazizwa kumva Paulo akunena kuti Mesiyayo anaperekedwa kuti aphedwe ndi atsogoleri awo achipembedzo enieniwo. “Koma Mulungu anamuukitsa iye kwa akufa,” Paulo analengeza molimba mtima. Chakumapeto kwa nkhani yake, anafotokozera omvetsera ake kuti akakhoza kupeza mtundu wa chipulumutso wabwino koposa. “Padziŵike ndi inu,” iye anatero, “kuti mwa Iye chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo; Ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simungathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.” Paulo anamaliza nkhani yake mwakulimbikitsa omvetsera ake kusadziphatika pakati pa ambiri amene Mulungu ananeneratu kuti akanyalanyaza makonzedwe abwino koposa a chipulumutso ameneŵa.—Machitidwe 13:30-41.
12. Kodi nchiyani chinakhala chotulukapo cha nkhani ya Paulo, ndipo zimenezi ziyenera kutilimbikitsa motani?
12 Ha, inali nkhani yokambidwa bwino chotani nanga yozikidwa pa Malemba! Kodi omvetserawo analabadira motani? “Ayuda ambiri ndi akupindulika opembedza anatsata Paulo ndi Barnaba.” (Machitidwe 13:43) Nzolimbikitsa chotani nanga kwa ife lerolino! Nafenso tichitetu zoposa m’kupereka chowonadi mogwira mtima, kaya ndi muuminisitala wathu wapoyera kapena m’ndemanga ndi nkhani pamisonkhano ya mpingo wathu.—1 Timoteo 4:13-16.
13. Kodi amishonalewo anachokeranji m’Antiokeya wa m’Pisidiya, ndipo ndimafunso otani amene amabuka ponena za ophunzira atsopanowo?
13 Okondwerera atsopano mu Antiokeya wa m’Pisidiya sanaleke kuuza ena za mbiri yabwino imeneyi. Monga chotulukapo, “sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mawu a [Yehova, NW].” Ndipo posapita nthaŵi uthengawo unafalikira kunja kwa mzindawo. Kwenikweni, “mawu a [Yehova, NW] anabukitsidwa m’dziko lonse.” (Machitidwe 13:44, 49) Mmalo mwakuvomereza mfundo imeneyi, Ayuda akaduka anapambana m’kuchititsa amishonalewo kuchotsedwa mumzindawo. (Machitidwe 13:45, 50) Kodi ndimotani mmene zimenezi zinayambukirira ophunzira atsopanowo? Kodi iwo analefulidwa ndi kuleka?
14. Kodi nchifukwa ninji otsutsawo sanathe kuletsa ntchito imene amishonalewo anaiyamba, ndipo kodi timaphunziranji pazimenezi?
14 Ayi, chifukwa chakuti imeneyi inali ntchito ya Mulungu. Ndiponso, amishonalewo anali atayala maziko olimba a chikhulupiriro mwa Ambuye woukitsidwayo Yesu Kristu. Mwachiwonekere pamenepa, ophunzira atsopanowo analingalira Kristu, ndipo osati amishonalewo, monga Mtsogoleri wawo. Chifukwa chake, timaŵerenga kuti “anadzazidwa ndi chimwemwe ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 13:52) Nzolimbikitsa chotani nanga zimenezi kwa amishonale ndi opanga ophunzira ena lerolino! Ngati tichita mbali yathu modzichepetsa ndi mwachangu, Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu adzadalitsa uminisitala wathu.—1 Akorinto 3:9.
Ikoniyo, Lustra, ndi Derbe
15. Kodi ndimchitidwe wotani umene amishonalewo anatsatira m’Ikoniyo, ndi zotulukapo zotani?
15 Paulo ndi Barnaba tsopano anayenda makilomitala pafupifupi 140 kummwera chakummaŵa ku mzinda wotsatira, Ikoniyo. Kuwopa chizunzo sikunawalepheretse kutsatira mchitidwe wawo wa mu Antiokeya. Monga chotulukapo, Baibulo limati: “Khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene anakhulupirira.” (Machitidwe 14:1) Kachiŵirinso, Ayuda amene sanalandire mbiri yabwino anasonkhezera chitsutso. Koma amishonalewo anapirira ndipo anathera nthaŵi yaikulu m’Ikoniyo akumathandiza ophunzira atsopano. Ndiyeno, pamene anamva kuti Ayuda owatsutsawo anali pafupi kuwaponya miyala, Paulo ndi Barnaba mwanzeru anathaŵira ku gawo lotsatira, “Lustra, ndi Derbe, ndi dziko lozungulirapo.”—Machitidwe 14:2-6.
16, 17. (a) Kodi nchiyani chinachitikira Paulo m’Lustra? (b) Kodi ndimotani mmene zochita za Mulungu ndi mtumwiyo zinayambukirira mwamuna wachichepere wa ku Lustra?
16 Molimba mtima ‘anapitiriza kulengeza mbiri yabwino’ m’gawo lotsopano, losalalikidwapo limeneli. (Machitidwe 14:7) Pamene Ayuda a mu Antiokeya wa m’Pisidiya ndi Ikoniyo anamva zimenezi, anabwera kuchokera kutali konseko kudza ku Lustra ndi kudzasonkhezera makamuwo kuponya miyala Paulo. Posoŵa nthaŵi yakuthaŵa, Paulo anaponyedwa miyala, kotero kuti otsutsawo anakhutira kuti anali atafa. Anamguzira kunja kwa mzinda.—Machitidwe 14:19.
17 Kodi mungayerekezere mmene zimenezi zinavutitsira maganizo ophunzira atsopano. Koma modabwitsa kwambiri, pamene anazinga Paulo, ananyamuka! Baibulo silimanena kuti kaya mwamuna wachichepere wotchedwa Timoteo anali mmodzi wa ophunzira atsopanoŵa. Ndithudi zochita za Mulungu ndi Paulo m’kupita kwanthaŵi zinadziŵika kwa iye ndipo zinakhomerezedwa mozama m’maganizo ake achichepere. Paulo analemba m’kalata yake yachiŵiri kwa Timoteo kuti: “Iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, . . . zotero zonga anandichitira m’Antiokeya, m’Ikoniya, m’Lustra, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m’zonsezi Ambuye anandilanditsa.” (2 Timoteo 3:10, 11) Pafupifupi chaka chimodzi kapena ziŵiri pambuyo pakuponyedwa miyala kwa Paulo, anabwerera ku Lustra ndi kupeza kuti mwamuna wachichepere uja Timoteo anali Mkristu wachitsanzo chabwino, “anamchitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.” (Machitidwe 16:1, 2) Chotero Paulo anamsankha monga mnzake woyenda naye. Izi zinathandiza Timoteo kukula msinkhu mwauzimu, ndipo m’kupita kwa nthaŵi anayeneretsedwa kutumizidwa ndi Paulo kukachezetsa mipingo yosiyanasiyana. (Afilipi 2:19, 20; 1 Timoteo 1:3) Mofananamo, atumiki a Mulungu achangu lerolino, ali chisonkhezero chabwino koposa kwa achichepere, amene ambiri a iwo amakula ndi kukhala atumiki a Mulungu, monga Timoteo.
18. (a) Kodi nchiyani chinachitikira amishonalewo m’Derbe? (b) Kodi ndimwaŵi wotani umene tsopano unawatsegukira, koma kodi ndikachitidwe kotani kamene iwo anasankha?
18 Mmaŵa mwake pambuyo pa tsiku limene anapulumuka imfa mu Lustra, Paulo ndi Barnaba ananyamuka ndi kumapita ku Derbe. Panthaŵiyi, otsutsa sanalondole, ndipo Baibulo limati anapanga ‘ophunzira ambiri.’ (Machitidwe 14:20, 21) Pokhala atakhazikitsa mpingo m’Derbe, Paulo ndi Barnaba anafunikira kupanga chosankha. Msewu wa Aroma woyenda anthu ambiri unadzera ku Derbe mpaka ku Tariso. Kuchokera kumeneko unali ulendo wachidule kubwerera ku Antiokeya wa m’Suriya. Mothekera imeneyo ndiyo inali njira yosavuta koposa yobwerera nayo, ndipo mwina amishonalewo tsopano akafuna kuti apume. Komabe potsanzira Mbuye wawo, Paulo ndi Barnaba anawona kusoŵa kokulirapo.—Marko 6:31-34.
Kutsiriza Kotheratu Ntchito ya Mulungu
19, 20. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anadalitsira amishonalewo kaamba ka kubwerera ku Lustra, Ikoniya, ndi Antiokeya? (b) Kodi zimenezi zimapereka phunziro lanji kwa anthu a Yehova lerolino?
19 Mmalo mwakutenga njira yachidule yobwererera kwawo, amishonalewo molimba mtima anapotoloka ndi kukachezetsanso mizinda yeniyeniyo mmene miyoyo yawo inali paupandu. Kodi Yehova anawadalitsa chifukwa cha nkhaŵa yawo yopanda dyera imeneyi kaamba ka nkhosa zatsopanozo? Ndithudi anatero, popeza kuti cholembedwacho chimanena kuti iwo anakhala achipambano “kulimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m’chikhulupiriro.” Moyenerera, anawuza ophunzira atsopanowo kuti: “Tiyenera kuloŵa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.” (Machitidwe 14:21, 22) Paulo ndi Barnaba anawakumbutsanso za kuitanidwa kwawo monga oloŵa nyumba mu Ufumu wa Mulungu unalinkudzawo. Lerolino, tiyenera kupereka chilimbikitso chofananacho kwa ophunzira atsopano. Tikhoza kuwalimbikitsa kupirira mayesero mwakuwasonyeza chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi muulamuliro wa Ufumu wa Mulungu umodzimodziwo umene Paulo ndi Barnaba analalikira.
20 Asanachoke mumzinda uliwonse, Paulo ndi Barnaba anathandiza mpingo wakumaloko kukhala wolinganizidwa bwinopo. Mwachiwonekere, iwo anaphunzitsa amuna oyeneretsedwa ndi kuwaika monga otsogolera. (Machitidwe 14:23) Mosakaikira izi zinathandiza kuwonjezera kufutukukako. Mofananamo, amishonale ambiri ndi ena lerolino, atathandiza awo opanda chidziŵitso chachikulu kupita patsogolo kufikira pamene akhoza kusenza mathayo, nthaŵi zina amasamuka ndi kupitiriza ntchito yawo yabwino m’malo ena kumene kusoŵa kuli kokulirapo.
21, 22. (a) Kodi chinachitika nchiyani pamene Paulo ndi Barnaba anamaliza ulendo wawo waumishonale? (b) Kodi zimenezi zimadzutsa mafunso otani?
21 Pomalizira pake pamene amishonalewo anabwerera ku Antiokeya wa m’Suriya, anakhala ndi chikhutiro chachikulu. Ndithudi, cholembedwa cha Baibulo chimanena kuti iwo ‘adamaliza’ ntchito imene Mulungu anawaikizira. (Machitidwe 14:26) Momvekera bwino, kusimba zokumana nazo zawo ‘kunakondweretsa kwambiri abale onse.’ (Machitidwe 15:3) Koma bwanji ponena za mtsogolo? Kodi tsopano akakhala pansi ndi kungokhutira ndi chipambano chawo? Kutalitali. Pambuyo pokawonana ndi bungwe lolamulira ku Yerusalemu kukamva chosankha chawo pankhani ya mdulidwe, aŵiriwo anayambanso maulendo aumishonale. Panthaŵi ino anapita kumalo osiyana. Barnaba anatenga Yohane wotchedwa Marko napita ku Kupro, pamene Paulo anapeza mnzake watsopano, Sila, namka ku Suriya ndi Kilikiya. (Machitidwe 15:39-41) Ndipaulendo umenewu pamene Paulo anasankha Timoteo wachichepere ndi kumka naye.
22 Baibulo silimatchula zotulukapo za ulendo wachiŵiri wa Barnaba. Ponena za Paulo, anapitiriza ku gawo latsopano ndi kukhazikitsa mipingo m’mizinda isanu—Filipi, Bereya, Tesalonika, Korinto, ndi Efeso. Kodi nchiyani chinali mfungulo ya chipambano chapadera cha Paulo? Kodi njira zofananazo zimagwira ntchito kwa Akristu opanga ophunzira lerolino?
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yesu ali chitsanzo chapadera choyenera kutsanziridwa?
◻ Kodi Barnaba anali chitsanzo mwanjira yotani?
◻ Kodi timaphunziranji m’nkhani ya Paulo m’Antiokeya wa m’Pisidiya?
◻ Kodi ndimotani mmene Paulo ndi Barnaba anatsirizira kotheratu ntchito yawo?
[Chithunzi patsamba 15]
Kupirira chizunzo kwa Paulo kunakhomereza zozama m’maganizo mwa mwamuna wachichepere Timoteo