-
Kodi Yehova Ndi Wotani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
3. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amatikonda?
Khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova ndi chikondi. Ndipo Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Timaona umboni wakuti Yehova amatikonda tikamawerenga Baibulo komanso tikamaona zimene analenga. (Werengani Machitidwe 14:17.) Chitsanzo ndi mmene anatilengera. Mwachitsanzo, anatilenga kuti tizitha kuona kukongola kwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu, kumva nyimbo zabwino, ndiponso kumva kukoma kwa chakudya. Zimenezi zikusonyeza kuti amafuna kuti tizisangalala ndi moyo.
-
-
Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo WapataliMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa chotipatsa moyo?
Moyo ndi mphatso yochokera kwa Atate wathu wachikondi, Yehova. Choncho tiyenera kumamuyamikira chifukwa cha mphatso imeneyi. Baibulo limati iye ndi “kasupe wa moyo” kutanthauza kuti ndi amene analenga zamoyo zonse. (Salimo 36:9) Limanenanso kuti: “Ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25, 28) Yehova amatipatsa zinthu zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo. Kuwonjezera pamenepa, Yehova amatipatsa zinthu zina zosiyanasiyana kuti tizisangalala ndi moyo.—Werengani Machitidwe 14:17.
-