Kodi Lingaliro Lanu Laumwini Liri Lopambana?
“TCHALITCHI Chatsopano Chigawanikana Chifukwa cha Ansembe Ogonana Ofanana Ziwalo,” unatero mutu waukulu wa nkhani. Ripoti la nyuzilo linapitiriza kuvumbula kugawanika kozama m’Tchalitchi cha England pa funso la ansembe ogonana ofanana ziwalo.
“Pali malo m’tchalitchi kaamba ka ogonana ofanana ziwalo,” anadzinenera tero mtumiki woyang’anira kulembedwa kwa atsogoleri a chipembedzo a tchalitchi. M’kawonedwe kake, wogonana wofanana ziwalo yemwe ali ‘wowona mtima ndi wa thayo’ mu unansi wake ndi mwamuna wina ali ndi kuyenera kwa kuikidwa.
“Atsogoleri a chipembedzo ochita mkhalidwe wa kugonana kofanana ziwalo ali ochimwa ndipo ayenera kusiya ntchito” chinali chikhulupiriro chotsutsa cha mtsogoleri wa tchalitchi. Iye anadzimva kuti atsogoleri a chipembedzo ayenera kukhala opereka chitsanzo m’mikhalidwe yawo yonse ya makhalidwe abwino.—The Sunday Times, London, November 8, 1987.
Mosakaikira aliyense wa amunawa anali wokhutiritsidwa kuti lingaliro lake linali lolondola. Koma kodi lingaliro laumwini liyenera kukhala ulamuliro womalizira m’nkhani zodetsa nkhaŵa mokulira? Mwinamwake munganene kuti inde, mukumasungirira kuti “aliyense ali ndi kuyenera ku lingaliro lake laumwini.”
Komabe, lingalirani ndemanga zowuziridwa ziŵiri izi m’Baibulo: “Chifukwa chake, tilondole zinthu za mtendere ndi zinthu za kulimbikitsana wina ndi mnzake.” “Koma ndikudandaulirani inu, abale, . . . kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu, koma mumangike mu mtima womwewo ndi chiweruziro chomwecho.”—Aroma 14:19; 1 Akorinto 1:10.
Chotero, bwanji ngati inu, monga Mkristu, mupeza vuto m’kumvana ndi mpingo Wachikristu pa nkhani ina yofunika koposa? Ndimotani mmene mudzachitira ndi chimenecho kotero kuti mtendere ndi umodzi wofunika kwambiri wa mpingo usungiriridwe?—Mateyu 5:9; 1 Petro 3:11.
Lingalirani mkhalidwe womwe unachitika mu mpingo Wachikristu wa m’zana loyamba pamene ena anawona malingaliro awo aumwini monga opambana. Onani ku chimene ichi potsirizira pake chinatsogolera ndipo dzifunseni inu mwini: ‘Nchiyani chomwe ndikanachita ngati ndidaliko kumeneko?’
Mafunso pa Mdulidwe
Mu 36 C.E. Akunja osadulidwa analandiridwa koyamba mu mpingo Wachikristu. Ngakhale kuti Mulungu anali atakonzekeretsa mtumwi Petro kaamba ka chochitika chozizwitsachi, Petro ndi awo omwe anali naye anadabwa kuwona mzimu woyera ukutsanuliridwa pa anthu osadulidwa. (Machitidwe 10:1-16, 34-48) Akristu Achiyuda ena ambiri anachipeza ichi kukhala chovuta kuchitenga. M’chenicheni, Akristu ena Achiyuda, “[ochirikiza, NW] mdulidwe,” anasuliza Petro kaamba ka kuyanjana ndi anthu osadulidwa.—Machitidwe 11:2, 3.
Nchifukwa ninji osuliza amenewa anasokonezedwa? Chifukwa chakuti kwa chifupifupi zaka 2,000, mdulidwe unali chizindikiro cha unansi wapadera ndi Mulungu. Pamene Yehova Mulungu analamulira Abrahamu kukhala ndi amuna onse m’banja lake atadulidwa, Iye ananena kuti: “Chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa ine ndi inu . . . kosatha.” (Genesis 17:10-13) Mazana ambiri pambuyo pake, mdulidwe unali udakali wofunika kwambiri kwa Ayuda. Ambiri a iwo anadzimva kuti kusadulidwa kunatanthauza kudetsedwa. (Yesaya 52:1) Iwo anadzimva kuti anthu oyera a Mulungu sayenera kukhala ndi zochita ndi Akunja odetsedwa, osadulidwa.
Mu 49 C.E. mtumwi Paulo anayang’anizana mu Antiokeya ya ku Siriya ndi ena a “kumdulidwe” amenewa. Pamapeto pa ulendo wake woyamba wa umishonale, iye anasimba ku mpingo kumeneko mmene Mulungu “anatsegulira amitundu [osadulidwa] pa khomo la chikhulupiriro.” Chinawoneka chomvekera kwa iye kuti panalibe chifuno kaamba ka anthu amenewa a mitundu kukhala odulidwa. Anthu ena ochokera ku Yudeya, ngakhale kuli tero, anali ndi lingaliro losiyanako. “Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose,” iwo anatero, “simungathe kupulumuka.” Iwo anadzimva kuti kudulidwa kunali kofunikira kaamba ka chipulumutso ndipo kuti Akunja onse otembenuzidwira ku Chikristu anayenera kudulidwa.—Machitidwe 14:26–15:1.
Malingaliro amphamvu anaphatikizidwamo. Mosakaikira iwo anasonkhanitsa mikangano yokakamiza kuchirikiza lingaliro lawo. Ndimotani mmene mtendere ndi umodzi wa mpingo ukasungidwira? Pambuyo pa kukambitsirana kochulukira kwa nkhaniyo, mpingo mu Antiokeya “unapatula Paulo ndi Barnaba ndi ena a iwo kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.” (Machitidwe 15:2) Panalibe lingaliro lakuti mu nkhani yowopsya yoteroyo, aliyense anali woyenerera ku lingaliro lake laumwini. Akristu amenewa anali ndi kudzichepetsa ndi kukhulupirika kokwanira ku dongosolo la teokratiki kufuna chigamulo chodalirika kuchokera ku bungwe lapakati lophunzitsa.—1 Akorinto 14:33, 40; Yakobo 3:17, 18; 1 Petro 5:5, 6.
Chigamulo Chipangidwa
Atumwi ndi akulu m’Yerusalemu (mwachidziŵikire ozindikiridwa monga bungwe lolamulira mu mpingo Wachikristu woyambirira) mosamalitsa anasanthula Malemba owuziridwa ndi mzimu ndi kubwereramo mmene mzimu woyera unatsogozera zinthu mkati mwa zaka 13 zapitazo. Chigamulo chawo? Kwa Akunja otembenuzidwa, mdulidwe sunali chinthu choyenerera kaamba ka chipulumutso. (Machitidwe 15:6-29) Pano panali chitsogozo chomvekera cha kutenga malo a lingaliro laumwini.
Mipingo yomwe inalabadira chitsogozo chimenechi “inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro nachuluka m’chiŵerengero chawo tsiku ndi tsiku.” (Machitidwe 16:4, 5) Anthu ena, ngakhale ndi tero, sanalandire chigamulo cha bungwe lolamulira. Iwo anali okhutiritsidwabe kuti lingaliro lawo linali lolondola ndi kuti kugonjera ku Chilamulo cha Mose kunali kofunikira kaamba ka chipulumutso. Nchiyani chomwe mukanachita? Iwo anakhala chisonkhezero chowopsya, chogawanitsa pakati pa Akristu. Yang’anani pa uphungu woperekedwa ndi mtumwi Paulo zoposa zaka 15 zotsatirapo pamene iye anayesera kutetezera Akristu okhulupirika ku chisonkhezero cha odzilingalira owuma mutu oterowo.
Galatiya, Asia Minor, c. 50-52 C.E. Ufulu wopezedwa ndi Akristu kupyolera mwa nsembe ya Yesu Kristu unali m’ngozi. Kuwopa kwa chizunzo ndi adani Achiyuda kunapangitsa ena a Akristuwo kufuna kukakamiza mbali zochokera ku Chilamulo cha Mose pa Akristu anzawo. (Agalatiya 6:12, 13) Mtumwi Paulo anakumbutsa ophunzirawo kuti kutenga machitachita Achiyuda oterowo monga mdulidwe kukakhala kudzilola iwo eni “kukodwanso ndi goli la ukapolo.” Popeza kuti iwo anali ochimwa, palibe aliyense wa iwo yemwe akanasunga Chilamulo mwangwiro, chotero iwo akatsutsidwa ndi Chilamulo, monga mmene Ayuda analiri. Kokha nsembe ya Yesu ikawapanga iwo osadetsedwa ndi kuwapulumutsa. “Ngati mulola akuduleni [ndipo chotero kukhala ndi thayo lochita Chilamulo chonse],” Paulo ananena kuti, “Kristu simudzapindula naye kanthu.”—Agalatiya 5:1-4; Machitidwe 15:8-11.
Korinto, Grisi, c. 55 C.E. Mikangano pa mdulidwe inali kugawanitsa mipingo. Paulo anadziŵa kuti mdulidwe mwa iwo wokha sunali wolakwika. Unali mbali ya Chilamulo changwiro cha Mulungu. (Salmo 19:7; Aroma 7:12) Paulo iyemwini anali atakonza kaamba ka kusamalira kwa wachichepere wake Timoteo (amene mayi wake anali m’Yuda) kuti adulidwe. Paulo anachita tero, osati chifukwa chakuti chinali cha lamulo, koma chifukwa sanafune kupatsa Ayuda chifukwa chirichonse cha kukhumudwitsidwa pa mbiri yabwino. (Machitidwe 16:3) Iye analimbikitsa Akristu kupatuka pa kukhala olowetsedwa mu mitsutsano yosakaza. “Kodi waitanidwa wina wodulidwa?” iye anafunsa tero. “Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe [akumaganiza kuti ichi chinali chofunikira kaamba ka chipulumutso].” Chinthu chofunika chinali kumvera malamulo omvekera a Mulungu, kuphatikizapo awo obwera kupyolera mwa mpingo Wachikristu.—1 Akorinto 7:18-20; Ahebri 13:17.
Filipi, Grisi, c. 60-61 C.E. Awo omwe anadzimva kuti Akristu anali adakali omangika ndi lamulo la Chiyuda anapitiriza kunyalanyaza umboni wowonekera wakuti Yehova anali kudalitsa mpingo Wachikristu, womwe tsopano unaphatikizapo okhulupirira osadulidwa ambiri. Awo opititsa patsogolo mdulidwe anali kupangitsa kuvulaza kwauzimu kwa ena mwa kukakamiza malingaliro awo aumwini. Chotero, kalankhulidwe ka mtumwi Paulo tsopano kali kamphamvu: “Penyererani agaru [olingaliridwa mwa mwambo kukhala odetsedwa ndi Ayuda], penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula.”—Afilipi 3:2.
Krete, c. 61-64 C.E. Mtumwi Paulo anasiya Tito kuyang’anira ntchito ya Akristu mu Krete. Mosangalatsa, Tito wosakhala m’Yuda sanakakamizidwe kudulidwa. (Agalatiya 2:3) Tsopano Paulo anatsogoza Tito kuchita mwamphamvu ndi adani a chowonadi, chimene opititsa patsogolo a mdulidwe amenewa anakhala. Iwo akayenera ngakhale kuchotsedwa mu mpingo ngati iwo anawumirira m’kubukitsa malingaliro awo ogamulapo aumwini. Iye analankhula za “kusamvera mawu, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo a kumdulidwe,” ndipo anapitiriza kuti: “Amene ayenera kutsekedwa pakamwa, ndiwo amene apasula mabanja onse ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.”—Tito 1:10, 11; 3:10, 11; 1 Timoteo 1:3, 7.
Ndi zotulukapo zomvetsa chisoni zotani nanga! Amuna amenewa anali onyada ponena za malingaliro awo aumwini kotero kuti anakana chitsogozo cha mpingo Wachikristu, kupatutsa chikhulupiriro cha ena, ndi kuwononga unansi wawo wabwino ndi Mulungu.—Yerekezani ndi Numeri 16:1-3, 12-14, 31-35.
Nchiyani Chomwe Mudzachita?
Kodi tingapeŵe kupanga chophophonya chofananacho lerolino? Inde, ngati choyamba titsimikizira kuti lingaliro lathu laumwini siliwombana ndi chiphunzitso chomvekera cha Baibulo. Pa nkhani ya kugonana kwa ofanana ziwalo, mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “A chisembwere cha kugonana . . . kapena ogonana ofanana ziwalo olakwa . . . sadzalowa ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10, New International Version) Ngakhale kuli tero, pamene chitsogozo cha m’Malemba chingawoneke kwa ife kukhala chotseguka ku malingaliro osiyana, tifunikira kusonyeza kuvomereza kodzichepetsa komwe kunasonyezedwa ndi Akristu oyambirira ndi kulandira zigamulo ndi zitsogozo zochokera ku mpingo wa Mulungu. Potsirizira, ngakhale m’magawo mmene nkhani iri Mwamalemba yosakhala yolondola ndiponso osati yolakwa koma iri yosiidwira ku chigamulo chaumwini, tiyenera mokwezeka kuyamikira mtendere ndi ena, mwakutero kukhala otseguka ku kugonjera kaŵirikaŵiri.
Kodi muli ofunitsitsa kusonyeza mzimu umenewo? Ngati ndi tero, mukusonyeza lingaliro labwino la kulinganizika, kuzindikira kuti mtendere ndi umodzi ziri za mtengo wapatali kuposa lingaliro lanulanu laumwini.