PHUNZIRO 54
Kodi “Kapolo Wokhulupirika Ndi Wanzeru” Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?
Yesu ndiye Mutu wampingo wa Chikhristu. (Aefeso 5:23) Popeza kuti Yesu ali kumwamba, masiku ano amatsogolera otsatira ake padziko lapansi pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Werengani Mateyu 24:45.) Yesu Khristu ndi amene anasankha ‘kapoloyu’ ndipo anamupatsa zochita mumpingo wa Chikhristu. Komabe, kapoloyu amayenera kumvera Khristu ndipo amatumikira abale a Khristu. Kodi kapoloyu ndi ndani? Nanga kodi amatisamalira bwanji?
1. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi ndani?
Yehova wakhala akugwiritsa ntchito munthu kapena kagulu ka anthu popereka malangizo kwa anthu ake. (Malaki 2:7; Aheberi 1:1) Yesu ataphedwa, atumwi komanso akulu a ku Yerusalemu ndi amene ankatsogolera mpingo wa Chikhristu. (Machitidwe 15:2) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, lomwe ndi kagulu ka akulu, limapereka chakudya chauzimu ndiponso kutsogolera pa ntchito yolalikira. Kagulu kameneka ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene [Yesu] anamuika” kuti azichita zimenezi. (Mateyu 24:45a) Abale onse a m’Bungwe Lolamulira ndi Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera ndipo amayembekezera kuti akadzamwalira adzapita kumwamba kukalamulira limodzi ndi Khristu.
2. Kodi ndi chakudya chauzimu chiti chimene kapolo wokhulupirika amapereka?
Yesu ananena kuti kapolo wokhulupirika azidzapereka “chakudya [kwa Akhristu anzawo] pa nthawi yoyenera.” (Mateyu 24:45b) Mofanana ndi chakudya chimene chimatithandiza kuti tikhale amphamvu ndiponso athanzi, chakudya chauzimu chomwe ndi malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu chimatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova komanso kuti tizigwira ntchito yomwe Yesu anatipatsa. (1 Timoteyo 4:6) Timalandira chakudya chauzimuchi kudzera m’misonkhano yampingo, misonkhano yadera komanso misonkhano yachigawo. Timalandiranso malangizo kudzera m’mabuku ofotokoza Baibulo komanso mavidiyo omwe amatithandiza kuti tizichita zimene Mulungu amafuna n’cholinga choti tilimbitse ubwenzi wathu ndi iye.
FUFUZANI MOZAMA
Onani chifukwa chake timafunikira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” yemwe ndi Bungwe Lolamulira.
3. Anthu a Yehova ayenera kumachita zinthu mwadongosolo
Motsogoleredwa ndi Yesu, Bungwe Lolamulira limatsogolera ntchito ya Mboni za Yehova kuti iziyenda mwadongosolo. Yesu ankatsogoleranso Akhristu amunthawi ya atumwi m’njira yofanana ndi imeneyi. Onerani VIDIYO.
Werengani 1 Akorinto 14:33, 40, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mavesiwa akusonyeza bwanji kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azichita zinthu mwadongosolo?
4. Kapolo wokhulupirika amatsogolera ntchito yolalikira
Ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri kwa Akhristu amunthawi ya atumwi. Werengani Machitidwe 8:14, 25, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi ndani amene ankatsogolera ntchito yolalikira munthawi ya atumwi?
Kodi Petulo ndi Yohane anachita chiyani atapatsidwa malangizo ndi atumwi anzawo?
Ntchito yofunika kwambiri imene Bungwe Lolamulira limatsogolera ndi yolalikira. Onerani VIDIYO.
Yesu ananena kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri. Werengani Maliko 13:10, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani Bungwe Lolamulira limaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri?
N’chifukwa chiyani timafunikira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti aziyendetsa ntchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse?
5. Kapolo wokhulupirika amapereka malangizo
Abale a m’Bungwe Lolamulira amapereka malangizo kwa Akhristu padziko lonse. Kodi amadziwa bwanji malangizo amene akuyenera kupereka? Onani mmene bungwe lolamulira lamunthawi ya atumwi linachitira zimenezi. Werengani Machitidwe 15:1, 2, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Akhristu amunthawi ya atumwi ankavutika kugwirizana pa nkhani iti?
Kodi Paulo, Baranaba ndi anthu ena anapita kwa ndani kuti akawapatse malangizo othetsera nkhaniyo?
Werengani Machitidwe 15:12-18, 23-29, kenako mukambirane funso ili:
Lisanasankhe zochita, kodi bungwe lolamulira lamunthawi ya atumwi linachita zotani kuti lidziwe maganizo a Mulungu pa nkhaniyi?—Onani mavesi 12, 15 ndi 28.
Werengani Machitidwe 15:30, 31 ndi 16:4, 5, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Akhristu amunthawi ya atumwi anachita zotani atalandira malangizo ochokera ku bungwe lolamulira?
Kodi Yehova anawadalitsa bwanji chifukwa chomvera malangizowo?
Werengani 2 Timoteyo 3:16 ndi Yakobo 1:5, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Bungwe Lolamulira la masiku ano limatani kuti lipeze malangizo likamafuna kusankha zochita?
ZIMENE ENA AMANENA: “Mukamamvera Bungwe Lolamulira mumakhala mukungotsatira maganizo a anthu.”
Kodi n’chiyani chimene chimakutsimikizirani kuti Yesu ndi amene amatsogolera Bungwe Lolamulira?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Bungwe Lolamulira ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene anaikidwa ndi Khristu. Kapoloyu amapereka malangizo komanso chakudya chauzimu kwa Akhristu padziko lonse.
Kubwereza
kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anaikidwa ndi ndani?
Kodi Bungwe Lolamulira limatisamalira bwanji?
Kodi inuyo mukukhulupirira kuti Bungwe Lolamulira ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?
ONANI ZINANSO
Onani mmene Bungwe Lolamulira limagwirira ntchito zake.
“Kodi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova Limachita Zotani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani zimene Bungwe Lolamulira limachita poonetsetsa kuti tikulandira chakudya chauzimu chabwino.
Kodi abale a m’Bungwe Lolamulira amaiona bwanji ntchito yomwe Yesu anawapatsa?
Kodi misonkhano yampingo komanso misonkhano ikuluikulu imasonyeza bwanji kuti Yehova akutsogolera Bungwe Lolamulira?