KODI MUKUDZIWA?
N’chifukwa chiyani Yosefe anayamba wameta asanakaonane ndi Farao?
Buku la Genesis limanena kuti Farao analamula zoti mkaidi wina wachiheberi amasulidwe mwamsanga. Ankafuna kuti mkaidiyo amasulire maloto ake omwe anali atamuzunguza mutu. Mkaidiyu anali Yosefe ndipo anali atakhala m’ndende kwa zaka zingapo. Ngakhale kuti Farao ankamufuna mwamsanga, Yosefe anayamba wameta kaye. (Genesis 39:20-23; 41:1, 14) Zimene anachitazi zikusonyeza kuti ankadziwa bwino chikhalidwe cha anthu a ku Iguputo.
Mitundu yambiri kuphatikizapo Aheberi, inkakonda kusunga ndevu. Koma mosiyana ndi zimenezi, buku lina limanena kuti, “ndi anthu a ku Iguputo okha omwe sankagwirizana ndi zoti munthu azisunga ndevu.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature.
Kodi anthu a ku Iguputo ankangometa ndevu zokha basi? Magazini inanso inanena kuti munthu akamapita kwa Farao ankafunika kudzikonza bwinobwino ngati kuti akupita kukachisi. (Biblical Archaeology Review) Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti Yosefe ankafunika kumeta tsitsi ndi ndevu zomwe.
Buku la Machitidwe limanena kuti bambo a Timoteyo anali Mgiriki. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti anali wochokera ku Girisi?
Ayi. Mtumwi Paulo analemba makalata ambiri mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Pamene ankalemba makalatawa ankakonda kusiyanitsa Ayuda ndi Agiriki. Mwachitsanzo, ankatchula anthu onse amene sanali Ayuda kuti Agiriki kapena Ahelene. (Aroma 1:16; 10:12) N’kutheka kuti Paulo ankanena zimenezi chifukwa anthu ambiri a m’madera amene Paulo ankalalikira ankalankhula komanso kutsatira miyambo ya Agiriki.
Koma kodi anthu a nthawi imeneyo ankaona kuti Mgiriki ndi munthu wochokera ku Girisi yekha basi? M’zaka za m’ma 300 B.C.E., munthu wina wodziwa kulankhula pagulu wa ku Atene, dzina lake Isocrates, ananena kuti chikhalidwe cha Agiriki chinkafalikira ngati moto. Anati chifukwa cha zimenezi, “anthu amene anachita maphunziro a Agiriki ndi amene ankaonedwa kuti ndi Agiriki kuposa nzika zenizeni za dziko la Girisi.” Choncho, ngakhale kuti Paulo anatchula anthu ena komanso bambo a Timoteyo kuti anali Agiriki, n’kutheka kuti sanali ochokera ku Girisi, koma ankangotsatira miyambo ya Agirikiwo.—Machitidwe 16:1