Lidiya—Wopembedza Mulungu Ndiponso Wochereza Alendo
KUYAMBIRA kale, atumiki a Mulungu woona adzidziŵikitsa mwa kuchereza kwawo alendo. (Genesis 18:1-8; 19:1-3) Kuchereza alendo, komasuliridwa kuti “chikondi, kufuna, kapena kukomera mtima alendo,” kochokera mumtima woona kuli chizindikiro cha Chikristu choona ngakhale lerolino. Kwenikweni, ndiko chofunika kwa onse ofuna kulambira Mulungu movomerezeka.—Ahebri 13:2; 1 Petro 4:9.
Munthu wina amene anasonyeza kuchereza alendo m’njira yabwino anali Lidiya. ‘Anaumiriza’ amishonale achikristu amene anafika ku Filipi kugona m’nyumba yake. (Machitidwe 16:15) Ngakhale kuti Lidiya akutchulidwa mwachidule m’Malemba, zochepa zonenedwa pa iye zingakhale zolimbikitsa kwa ife. Motani? Kodi Lidiya anali yani? Kodi timadziŵanji za iye?
“Wakugulitsa Chibakuwa”
Lidiya anali kukhala ku Filipi, mzinda waukulu wa Makedoniya. Komabe, anali wa ku Tiyatira, mzinda wa chigawo cha Lidiya, kumadzulo kwa Asia Minor. Chifukwa cha zimenezi, ena amanena kuti “Lidiya” linali dzina losemerera lopatsidwa kwa iye ku Filipi. M’mawu ena, iye anali “Mlidiya,” monga momwedi mkazi amene Yesu Kristu anachitirako umboni anatchedwera “mkazi Msamariya.” (Yohane 4:9) Lidiya ankagulitsa “chibakuwa” kapena zinthu zonika ndi mtundu umenewo. (Machitidwe 16:12, 14) Zolembedwa zofukulidwa ndi akatswiri ofukula mabwinja zimachitira umboni kuti ku Tiyatira ndi ku Filipi kunali onika zinthu. Nkotheka kuti Lidiya anasamukirako chifukwa cha ntchito yake, kaya kuti akachite malonda ake kapena monga woimira kampani ya onika a ku Tiyatira.
Chibakuwa chinali kupangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. Chokwera mtengo koposa chinali chochokera ku nkhono zina za m’madzi. Malinga ndi kunena kwa Martial, wolemba ndakatulo wachiroma wa m’zaka za zana loyamba, chofunda cha chibakuwa chabwino koposa cha ku Turo (malo ena kumene zimenezi zinali kupangidwa) chinali kugulidwa ndi ndalama zofika 10,000 sesterces, kapena madinari 2,500, ndalama zolingana ndi malipiro a wantchito a masiku 2,500. Mwachionekere, zovala zotero zinali zinthu zambambande zimene oŵerengeka okha ndiwo anali kukhala nazo. Chotero Lidiya angakhale anali wopeza bwino kwambiri m’zachuma. Mulimonse mmene zinalili, iye anakhoza kuchereza mtumwi Paulo ndi anzake—Luka, Sila, Timoteo, ndipo mwinamwake ndi enanso.
Kulalikira kwa Paulo ku Filipi
Pafupifupi chaka cha 50 C.E., Paulo kwanthaŵi yoyamba anafika ku Ulaya nayamba kulalikira ku Filipi.a Pamene anafika mumzinda watsopanowo, chinali chizoloŵezi cha Paulo kupita ku sunagoge kukalalikira choyamba kwa Ayuda ndi otembenuka amene anali kusonkhana komweko. (Yerekezerani ndi Machitidwe 13:4, 5, 13, 14; 14:1.) Komabe, malinga ndi kunena kwa ena, lamulo la Roma linaletsa Ayuda kutsata chipembedzo chawo mu “malo opatulika” a Filipi. Chifukwa chake, atagona momwemo “masiku ena,” patsiku la Sabata amishonalewo anapeza malo m’mbali mwa mtsinje kunja kwa mzindawo kumene ‘anaganizira kuti amapempherako.’ (Machitidwe 16:12, 13) Mwachionekere umenewu unali Mtsinje wa Gangites. Kumeneko amishonalewo anangopezako akazi, mmodzi wa iwo anali Lidiya.
“Anapembedza Mulungu”
Lidiya “anapembedza Mulungu,” koma mwina iyeyo anali wotembenukira ku Chiyuda wofunafuna choonadi chachipembedzo. Ngakhale kuti anali ndi ntchito yabwino, Lidiya anali wosakonda chuma. M’malo mwake, anapatula nthaŵi ya zinthu zauzimu. “[Yehova anatsegula mtima wake, NW], kuti amvere zimene anazinena Paulo,” ndipo Lidiya analandira choonadi. Kwenikweni, ‘iye ndi a pabanja pake anabatizidwa.’—Machitidwe 16:14, 15.
Baibulo silimatchula enawo amene anali a pabanja la Lidiya. Popeza kuti mwamuna sakutchulidwa, iye angakhale anali mbeta kapena mkazi wamasiye. Mwinamwake ‘banja lake’ linapangidwa ndi achibale, koma liwulo lingatanthauzenso akapolo kapena antchito. Mulimonse mmene zinalili, Lidiya mwachangu anauza aja amene anali kukhala nawo zinthu zimene anaphunzira. Ndipo ayenera kuti anali wachimwemwe chachikulu chotani nanga pamene iwo anakhulupirira ndi kulandira chikhulupiriro choona!
“Anatiumiriza Ife”
Asanakumane ndi Lidiya, mwinamwake amishonalewo anakhutira ndi malo ogona omwe iwo anali kudzilipirira okha. Koma iye anafunitsitsa kuwapatsa malo ena ogona. Komabe, kuumirira kwake kumasonyeza kuti Paulo ndi anzake anali atayesa kukana. Chifukwa ninji? Paulo anafuna kuti ‘uthenga wabwino ukhale waulere, kuti asaipse ulamuliro wake’ ndi kuti asakhale wosautsa kwa aliyense. (1 Akorinto 9:18; 2 Akorinto 12:14) Koma Luka akuwonjezera kuti: “Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa [Yehova, NW], muloŵe m’nyumba yanga, mugone mmenemo. Ndipo anatiumiriza ife.” (Machitidwe 16:15) Nkhaŵa yaikulu ya Lidiya inali pa kukhala wokhulupirika kwa Yehova, ndipo kuchereza alendo mwachionekere kunali umboni wa chikhulupiriro chake. (Yerekezerani ndi 1 Petro 4:9.) Ndi chitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga! Kodi nafenso timagwiritsira ntchito chuma chathu kuchirikiza zinthu za uthenga wabwino?
Abale ku Filipi
Pamene Paulo ndi Sila anamasulidwa m’ndende pambuyo pa chochitika chokhudza namwali wogwidwa ndi ziŵanda, anabwerera kunyumba ya Lidiya, kumene anapeza abale ena. (Machitidwe 16:40) Okhulupirira mumpingo wopangidwa chatsopano wa Filipi angakhale atagwiritsira ntchito nyumba ya Lidiya monga malo osonkhanako nthaŵi zonse. Kuli koyenera kuganiza kuti nyumba yake inapitiriza kukhala malo a ntchito yateokrase mumzindawo.
Kuchereza alendo kwabwino kumene Lidiya anasonyeza poyamba kunakhala mkhalidwe wa mpingo wonse. Ngakhale kuti anali osauka, Afilipi nthaŵi zingapo anatumizira Paulo zinthu zimene anafunikira, ndipo mtumwiyo anayamikira.—2 Akorinto 8:1, 2; 11:9; Afilipi 4:10, 15, 16.
Lidiya sakutchulidwa m’kalata imene Paulo anatumizira Afilipi pafupifupi 60-61 C.E. Malemba samanena zimene zinachitika kwa iye pambuyo pa zochitika zosimbidwa m’Machitidwe chaputala 16. Ngakhale zili choncho, kutchulidwa mwachidule kwa mkazi wolimba ameneyu kumatichititsa kufuna ‘kuchereza alendo.’ (Aroma 12:13) Tikuthokoza chotani nanga kukhala ndi Akristu onga Lidiya pakati pathu! Mzimu wawo umathandiza kwambiri kuchititsa mipingo kukhala yachikondi ndi yaubwenzi, Yehova Mulungu nalemekezedwa.
[Mawu a M’munsi]
a Pakati pa mizinda yofunika koposa ya Makedoniya, Filipi anali mudzi wotukuka wa asilikali wolamuliridwa ndi jus italicum (Lamulo Lachitaliyana). Lamulo limeneli linapatsa Afilipi zoyenera zolingana ndi zija zimene nzika za Roma zinali nazo.—Machitidwe 16:9, 12, 21.
[Bokosi patsamba 28]
Moyo wa Ayuda ku Filipi
Moyo wa Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda uyenera kuti unali wovuta ku Filipi. Pangakhale panali malingaliro otsutsa Chiyuda, pakuti kutatsala pang’ono kuti Paulo afike, Mfumu Klaudiyo anali atapitikitsa Ayuda ku Roma.—Yerekezerani ndi Machitidwe 18:2.
Kwenikweni, Paulo ndi Sila anamka nawo kwa oweruza atachiritsa namwali amene anali ndi mzimu wambwebwe. Ambuye ake, pokhala atalandidwa magwero aphindu la ndalama, anagwiritsira ntchito tsankhu la nzika zinzawo mwa kunena kuti: ‘Anthu awa avuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda, ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma.’ Chotero, Paulo ndi Sila anakwapulidwa ndi ndodo naponyedwa m’ndende. (Machitidwe 16:16-24) M’malo otero, kulambira Yehova, Mulungu wa Ayuda poyera, kunafuna kulimba mtima. Koma umboni ukusonyeza kuti Lidiya sanavutike maganizo pokhala wosiyana ndi ena.
[Zithunzi patsamba 27]
Mabwinja ku Filipi