-
‘Funafunani Mulungu ndi Kumupezadi’‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
17, 18. N’chifukwa chiyani anthu ayenera kukhala ndi mtima wofuna kudziwa Mulungu, ndipo tikuphunzira chiyani kwa Paulo amene analankhula ndi anthu mowafika pamtima?
17 Anthu ayenera kukhala ndi mtima wofuna kudziwa Mulungu. Paulo ananena kuti, chifukwa cha Mulungu, “tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” Akatswiri ena amanena kuti Paulo ankanena mawu amene ananenedwa ndi munthu wina (dzina lake Epimenides) wolemba ndakatulo wa ku Kerete amene anakhalapo m’zaka za m’ma 500 B.C.E., amene anali “wotchuka kwambiri pa nkhani zokhudza miyambo ya chipembedzo cha ku Atene.” Paulo anapereka chifukwa chinanso chimene anthu ayenera kukondera Mulungu ponena kuti: ‘Andakatulo anu ena ananena kuti, “Paja ndife ana ake.”’ (Mac. 17:28) Anthu ayenera kuona kuti pali ubale wapadera pakati pa iwowo ndi Mulungu chifukwa chakuti anali Atate wa munthu woyamba amene ndi kholo la anthu onse. Pofuna kuwafika pamtima omvera akewo, mwanzeru Paulo anagwira mawu ochokera m’nkhani za Chigiriki zimene mwina anthuwo ankazikonda kwambiri.e Potengera chitsanzo cha Paulo, ifenso nthawi zina tingagwire mawu mabuku a mbiri yakale kapena mabuku ena amene anthu amagwiritsa ntchito. Mwachitsanzo, mawu oyenerera amene tawatenga m’buku limene anthu amalikonda, angathandize munthu amene si wa Mboni kumvetsa mmene miyambo ndi zinthu zina zimene anthu azipembedzo zabodza amachita zinayambira.
-
-
‘Funafunani Mulungu ndi Kumupezadi’‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
e Paulo anagwira mawu a ndakatulo ina (yotchedwa Phaenomena) ya zinthu zakuthambo yolembedwa ndi Aratus, wolemba ndakatulo wa m’gulu la Sitoiki. Mawu ofanana ndi amenewa amapezeka m’nkhani zina za Chigiriki, ndiponso mu nyimbo zotamanda Zeu zolembedwa ndi Cleanthes, wolemba mabuku wa m’gulu la Sitoiki.
-