-
‘Funafunani Mulungu ndi Kumupezadi’‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
13. Kodi Paulo anafotokoza kuti zinthu zonse zinakhalapo bwanji, nanga zimene ananenazo zimatanthauza chiyani?
13 Mulungu analenga zinthu zonse. Paulo ananena kuti: “Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja. Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.”d (Mac. 17:24) Zinthu zonse zam’chilengedwe sizinakhalepo mwangozi koma zinachita kulengedwa ndi Mulungu woona. (Sal. 146:6) Mosiyana ndi milungu yabodza, monga Atena, yomwe inkalemekezedwa kwambiri chifukwa cha akachisi ndi maguwa ake ansembe, Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi, yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa, sangakhale mu akachisi omangidwa ndi manja a anthu. (1 Maf. 8:27) Zimene Paulo ankatanthauza zinali zoonekeratu. Iye ankatanthauza kuti Mulungu woona ndi wamkulu kuposa mafano opangidwa ndi anthu amene ankapezeka mu akachisi omangidwa ndi anthu.—Yes. 40:18-26.
-
-
‘Funafunani Mulungu ndi Kumupezadi’‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
d Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti ‘dziko’ ndi koʹsmos, ndipo Agiriki ankagwiritsa ntchito mawuwa kutanthauza zolengedwa zonse zakuthambo ndi zapadziko lapansi. N’kutheka kuti Paulo, amene ankayesetsa kunena mfundo zimene Agirikiwo angagwirizane nazo, anagwiritsa ntchito mawu amenewa ndi tanthauzo limeneli.
-