‘Mulungu Sakhala M’nyumba Zakachisi Zomangidwa ndi Manja’
MOSAKAYIKIRA mtumwi Paulo ankadziŵa akachisi a Athena, chifukwa ankapezeka m’mizinda yambiri imene anapita pamaulendo ake aumishonale. Malinga ndi kunena kwa The Encyclopædia Britannica, Athena ankadziŵika kwambiri monga mulungu wachikazi wankhondo ndi nzeru komanso “wantchito zina zaluso zimene ankachita panthaŵi ya mtendere.”
Parthenon anali kachisi wotchuka kwambiri wa Athena ndipo anamangidwa mu mzinda wa Atene, womwe dzina lake linachokera kwa mulungu wachikaziyo. Kachisi wa Parthenon yemwe amati anali kachisi wamkulu koposa m’nthaŵi zamakedzana anali ndi fano la Athena lopangidwa ndi golide ndi minyanga, ndipo linali lalitali mamita 12. Nthaŵi imene Paulo anapita ku Atene, kachisi wopangidwa ndi miyala yoyera ya nsangalabwi ameneyu anali wotchuka mu mzindawo kwa zaka pafupifupi 500.
Kachisi wa Parthenon akuonekera poteropo, Paulo analalikira gulu la anthu a mu Atene za ‘Mulungu amene sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja.’ (Machitidwe 17:23, 24) Mwinamwake kukongola kwa akachisi a Athena kapena ulemerero wa mafano ake zinapangitsa kuti aoneke wochititsa chidwi kwambiri kwa anthu amene ankamvetsera kwa Paulo kuposa Mulungu wosaoneka amene sanali kum’dziŵa. Koma monga mmene Paulo ananenera, sitiyenera kulingalira kuti Mlengi wa munthu ‘ali wofanafana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, wolochedwa ndi . . . anthu.’—Machitidwe 17:29.
Milungu yachimuna ndi yachikazi monga Athena, imene ulemerero wawo umadalira akachisi ndi mafano, imakhalapo ndi kutha. Fano la Athena linachotsedwa mu Parthenon m’zaka za m’ma 400 C.E., ndipo masiku ano ndi mabwinja ochepa okha a akachisi ake amene alipo. Kodi ndani masiku ano amene amafuna kuti Athena awapatse nzeru ndi kuwatsogolera?
N’zosiyana kwambiri ndi Yehova, “Mulungu wosatha” amene palibe anamuonapo chikhalireni. (Aroma 16:26; 1 Yohane 4:12) Ana a Kora analemba kuti: “Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthaŵi za nthaŵi: adzatitsogolera.” (Salmo 48:14) Njira imodzi imene Yehova Mulungu angatitsogolerere ndi mwa kuphunzira Mawu ake, Baibulo, ndi kugwiritsa ntchito malangizo ake pamoyo wathu.