Akristu ndi Dziko la Anthu
“Muyendere munzeru ndi iwo akunja.”—AKOLOSE 4:5.
1. Kodi Yesu ananenanji za otsatira ake ndi dziko lapansi?
POPEMPHERA kwa Atate wake wakumwamba, Yesu anati ponena za otsatira ake: “Dziko lapansi linadana nawo, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.” (Yohane 17:14, 15) Akristu sanafunikire kulekanitsidwa ndi dziko mwakuthupi—mwachitsanzo, mwa kukhala kwaokha m’nyumba za amonke. M’malo mwake, Kristu ‘anawatuma iwo ku dziko lapansi’ kukakhala mboni zake “kufikira malekezero ake a dziko.” (Yohane 17:18; Machitidwe 1:8) Koma anapemphabe Mulungu kuti awayang’anire chifukwa Satana, “mkulu wa dziko ili lapansi,” anali kudzasonkhezera ena kuwada chifukwa cha dzina la Kristu.—Yohane 12:31; Mateyu 24:9.
2. (a) Kodi Baibulo limawagwiritsira ntchito motani mawuwo “dziko lapansi”? (b) Kodi Yehova amasonyeza lingaliro loyenerera lotani ponena za dziko lapansi?
2 M’Baibulo mawu akuti “dziko lapansi” (Chigiriki, koʹsmos) nthaŵi zambiri amatanthauza anthu osalungama, amene ‘agona mwa woipayo.’ (1 Yohane 5:19) Popeza Akristu amatsatira malamulo a Yehova ndiponso amalabadira lamulo lakuti alalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku dziko lapansi, nthaŵi zina pakhala kusamvana pakati pa iwo ndi dziko. (2 Timoteo 3:12; 1 Yohane 3:1, 13) Komabe, liwulo koʹsmos m’Malemba limagwiranso ntchito kutanthauza banja lonse la anthu. Ponena za dziko m’lingaliro limeneli, Yesu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.” (Yohane 3:16, 17; 2 Akorinto 5:19; 1 Yohane 4:14) Choncho, pamene kuli kwakuti amada zinthu zomwe zikuchitika m’dongosolo loipa la Satana, Yehova anasonyeza chikondi chake kwa anthu mwa kutumiza Mwana wake pa dziko lapansi kuti adzapulumutse onse omwe ‘adzafika kukulapa.’ (2 Petro 3:9; Miyambo 6:16-19) Lingaliro loyenerera la Yehova ponena za dziko liyenera kutsogolera alambiri ake.
Chitsanzo cha Yesu
3, 4. (a) Kodi Yesu anatenga kaimidwe kotani ponena za ulamuliro? (b) Kodi Yesu analiona motani dziko la anthu?
3 Atatsala pang’ono kufa, Yesu anauza Pontiyo Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” (Yohane 18:36) Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, Yesu anayamba wakana kuti Satana ampatse ulamuliro pa maufumu onse a m’dziko lapansi, ndipo anali atakana kuti Ayuda ampange kukhala mfumu. (Luka 4:5-8; Yohane 6:14, 15) Komabe, Yesu anasonyeza chikondi chachikulu pa dziko la anthu. Chitsanzo cha zimenezi chinasimbidwa ndi mtumwi Mateyu kuti: “Koma iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” Chifukwa cha chikondi, analalikira kwa anthu m’mizinda ndi m’midzi yawo. Anawaphunzitsa ndi kuchiritsa matenda awo. (Mateyu 9:36) Anadziŵanso zosoŵa zakuthupi za awo amene anadza kwa iye kudzaphunzira. Timaŵerenga kuti: “Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.” (Mateyu 15:32) Ndi kusamala kwachikondi kotani nanga!
4 Ayuda anali kuwaganizira zoipa Asamariya, koma Yesu analankhula nthaŵi yaitali ndi mkazi wachisamariya nathera masiku aŵiri kupereka umboni wosamalitsa m’mudzi wachisamariya. (Yohane 4:5-42) Ngakhale kuti Mulungu anamtuma kwa “nkhosa zotayika za banja la Israyeli,” nthaŵi zina Yesu anachitapo kanthu pamene ena osakhala Ayuda anasonyeza chikhulupiriro. (Mateyu 8:5-13; 15:21-28) Inde, Yesu anasonyeza kuti nkotheka ‘kusakhala wa dziko lapansi’ komanso nthaŵi imodzimodziyo nkusonyeza chikondi pa dziko la anthu, kwa anthu. Kodi ifenso timasonyeza chifundo kwa anthu kumene timakhala, kugwira ntchito, kapena kumene timakagula zinthu? Kodi timasamala za ubwino wawo—osati kokha pa zosoŵa zawo zauzimu komanso pa zosoŵa zina ngati tingathe kupereka thandizo? Yesu anatero, ndipo mwa kuchita zimenezo, anatsegula njira yophunzitsira anthu za Ufumu. Zoona, ifeyo sitingachite zozizwitsa zenizenizo zimene Yesu anachita. Koma kaŵirikaŵiri, kusonyeza kukoma mtima, titero kunena kwake, kumachita zozizwitsa pothetsa malingaliro olakwika.
Mmene Paulo Anachitira ndi Anthu “Akunja”
5, 6. Kodi mtumwi Paulo anachita nawo motani Ayuda amene anali “akunja”?
5 M’makalata ake ambiri, mtumwi Paulo akunena za anthu “akunja,” kutanthauza anthu osakhala Akristu, kaya akhale Ayuda kapena osakhala Ayuda. (1 Akorinto 5:12; 1 Atesalonika 4:12; 1 Timoteo 3:7) Kodi anatani nawo ameneŵa? Iye ‘anakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse akapulumutse ena.’ (1 Akorinto 9:20-22) Atafika m’mudzi, choyamba anali kupita kukalalikira Ayuda amene anakhazikika mmenemo. Kodi anali kuwafikira bwanji? Mochenjera ndiponso mwaulemu anapereka maumboni okhutiritsa a m’Baibulo akuti Mesiya anafika, anafa imfa yopereka nsembe, ndipo anaukitsidwa.—Machitidwe 13:5, 14-16, 43; 17:1-3, 10.
6 Mwa njira imeneyi Paulo anagwiritsira ntchito chidziŵitso cha Ayuda chokhudza Chilamulo ndi aneneri kuti awaphunzitse za Mesiya ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo anathadi kukhutiritsa ena. (Machitidwe 14:1; 17:4) Ngakhale kuti atsogoleri achiyuda anamtsutsa, Paulo anasonyeza chikondi pa Ayuda anzake pamene analemba kuti: “Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera [Ayuda] kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke. Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso.”—Aroma 10:1, 2.
Kuthandiza Okhulupirira Osakhala Ayuda
7. Kodi otembenuka ambiri anaulabadira motani uthenga wabwino umene Paulo analalikira?
7 Otembenuka anali anthu osakhala Ayuda amene anadulidwa naloŵa chipembedzo chachiyuda. Mwachionekere, kunali otembenukira kuchiyuda ku Roma, Antiokeya wa ku Aramu, Aitiopiya, ndi Antiokeya wa ku Pisidiya—ndithudi, kulikonse kumene kunali midzi ya Ayuda. (Machitidwe 2:8-10; 6:5; 8:27; 13:14, 43; yerekezerani ndi Mateyu 23:15.) Mosiyana ndi olamulira ambiri achiyuda, otembenuka ayenera kuti sanali odzitama, ndipo sakanadzitukumula monyada kuti ndi mbadwa za Abrahamu. (Mateyu 3:9; Yohane 8:33) M’malo mwake, anasiya milungu yakunja natembenukira kwa Yehova modzichepetsa, kudziŵa zinthu zina ponena za iye ndi malamulo ake. Ndipo iwo, monga Ayuda, analandira chiyembekezo cha kudza kwa Mesiya. Pokhala atasonyeza kale kuti akufunitsitsa kusintha pofunafuna choonadi, ambiri a iwo anali okonzekera kusintha zinthu zambiri ndi kulabadira kulalikira kwa mtumwi Paulo. (Machitidwe 13:42, 43) Wotembenukira kuchiyuda amene kale anali kulambira milungu yachikunja atatembenuka kukhala Mkristu, anali kukhala wokonzekeretsedwa bwino kuchitira umboni kwa Akunja ena amene anali kulambirabe milungu yachikunjayo.
8, 9. (a) Kusiyapo otembenuka, kodi ndi anthu ena ati osakhala Ayuda amene anakopeka ndi chipembedzo chachiyuda? (b) Kodi oopa Mulungu ambiri osadulidwa anaulabadira motani uthenga wabwino?
8 Kusiyapo otembenuka odulidwa, enanso osakhala Ayuda anakopeka ndi chipembedzo chachiyuda. Woyamba wa ameneŵa kuti akhale Mkristu anali Korneliyo amene, ngakhale sanali wotembenukira kuchiyuda, anali “munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu.” (Machitidwe 10:2) Pothirira ndemanga buku la Machitidwe, Profesa F. F. Bruce analemba kuti: “Osakhala Ayuda otere mwachisawawa akutchedwa kuti ‘oopa Mulungu’; pamene kuli kwakuti limeneli sindilo dzina lawo lenileni, ndiloyenerera kuligwiritsira ntchito. Ambiri osakhala Ayuda m’masikuwo, pamene kuli kwakuti sanali ofunitsitsa kutembenukira kuchiyuda (chiyeneretso cha mdulidwe ndicho chinali chokhumudwitsa chachikulu kwa amuna), anakopeka ndi chikhulupiriro cha Mulungu mmodzi chosavuta kumva pakalambiridwe ka Ayuda m’masunagoge ndi malamulo a khalidwe labwino a moyo wachiyuda. Ena a iwo anali kupita ku sunagoge ndipo anayamba kudziŵa mapemphero ndi maphunziro a malemba, amene anali kumva akuŵerengedwa m’kope lachigiriki.”
9 Mtumwi Paulo anakumana ndi oopa Mulungu ambiri pamene anali kulalikira m’masunagoge a ku Asia Minor ndi ku Grisi. Ku Antiokeya wa ku Pisidiya anatcha awo osonkhana m’sunagoge kuti “amuna a Israyeli, ndi inu akuopa Mulungu.” (Machitidwe 13:16, 26) Luka analemba kuti Paulo atalalikira kwa Masabata atatu m’sunagoge wa ku Tesalonika, “ena a iwo [Ayuda] anakopedwa [kukhala Akristu], nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akulu osati oŵerengeka.” (Machitidwe 17:4) Mwina Ahelene ena anali oopa Mulungu osadulidwa. Pali umboni wakuti anthu ambiri osakhala Ayuda ameneŵa anadziphatika kwa Ayuda.
Kulalikira Pakati pa “Osakhulupirira”
10. Kodi Paulo anawalalikira motani Akunja osakhala Ayuda amene sanali kudziŵa kalikonse ponena za Malemba, ndipo zotsatirapo zake zinali zotani?
10 M’Malemba Achigiriki Achikristu, liwu lakuti “osakhulupirira” lingatanthauze anthu onse osakhala mumpingo wachikristu. Kaŵirikaŵiri limatanthauza anthu osalambira Mulungu. (Aroma 15:31, NW; 1 Akorinto 14:22, 23; 2 Akorinto 4:4; 6:14) Ku Atene osakhulupirira ambiri anali ataphunzira filosofi yachigiriki popanda kudziŵa kalikonse ponena za Malemba. Kodi zimenezi zinalefula Paulo kuti asawalalikire? Ayi. Koma anasintha mafikidwe ake. Analongosola malingaliro a m’Baibulo mwaluso popanda kugwira mawu Malemba Achihebri mwachindunji, amene anali osadziŵika kwa Aatene. Anasonyeza mochenjera kufanana kwa choonadi cha Baibulo ndi malingaliro ena a olemba ndakatulo akale achistoiki. Ndipo anafotokozanso lingaliro la Mulungu mmodzi woona wa anthu onse, Mulungu amene adzaweruza m’chilungamo kudzera mwa munthu amene anafa ndi kuukitsidwa. Motero Paulo mochenjera analalikira za Kristu kwa Aatene. Kodi chotsatirapo chake chinali chotani? Pamene kuli kwakuti ambiri anamtonyola poyera kapena anasonyeza kukayikira kwambiri, “ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira; mwa iwonso munali Dionisiyo Mareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nawo.”—Machitidwe 17:18, 21-34.
11. Kodi Korinto unali mzinda wotani, ndipo ntchito ya Paulo yolalikira kumeneko inabalanji?
11 Ku Korinto kunali Ayuda ambiri ndithu, choncho Paulo anakayambira kumeneko utumiki wake mwa kulalikira m’sunagoge. Koma pamene Ayuda anatsutsa, Paulo anapita kwa anthu osakhala Ayuda. (Machitidwe 18:1-6) Ndipo analitu ambiri chotani nanga! Korinto unali mzinda wapiringupiringu, wodzaza anthu akumaiko ena, ndipo wa malonda ochuluka, wotchuka kwa Ahelene ndi Aroma chifukwa cha khalidwe lake lonyansa. Ndipodi, “kukhala mwaukorinto” kunatanthauza kukhala wakhalidwe loipa. Komabe, pamene Ayuda anakana ulaliki wa Paulo mpamenenso Kristu anaonekera kwa iye ndi kumuuza kuti: “Usaope, koma nena, . . . chifukwa ndili nawo anthu ambiri m’mudzi muno.” (Machitidwe 18:9, 10) Zoonadi, Paulo anakhazikitsa mpingo ku Korinto, ngakhale kuti ena a mumpingowo kale anali ndi moyo “waukorinto.”—1 Akorinto 6:9-11.
Kuyesa Kupulumutsa “Anthu Amtundu Uliwonse” Lerolino
12, 13. (a) Kodi gawo lathu lerolino lafanana motani ndi lija la m’tsiku la Paulo? (b) Kodi timasonyeza mzimu wotani m’magawo amene zipembedzo za Dziko Lachikristu zazika mizu kuyambira kalekale kapena mmene ambiri ataya chikhulupiriro mwa magulu achipembedzo?
12 Lero, monga zinalili m’zaka za zana loyamba, ‘chisomo cha Mulungu chikupulumutsa anthu onse [“anthu amtundu uliwonse,” NW].’ (Tito 2:11) Gawo lolalikiramo uthenga wabwino lafutukuka kufika ku makontinenti onse ndi zisumbu zambiri za m’nyanja. Ndipo, monga m’tsiku la Paulo, “anthu amitundu yonse” akupezedwadi. Mwachitsanzo, enafe timalalikira m’maiko amene matchalitchi a Dziko Lachikristu azika mizu kwa zaka mazana ambiri. Monga Ayuda a m’zaka za zana loyamba, mamembala awo angakhale omangika kwambiri ndi miyambo yachipembedzo. Ngakhale zili tero, timasangalala kufunafuna awo a mkhalidwe wabwino wa mtima ndi kupezerapo mpata pa chilichonse chimene amadziŵa ponena za Baibulo. Sitimalankhula nawo motafula kapena kuwanyoza ngakhale kuti atsogoleri awo achipembedzo nthaŵi zina amatitsutsa ndi kutizunza. M’malo mwake, timadziŵa kuti ena pakati pawo angakhale nacho “changu cha kwa Mulungu” ngakhale kuti alibe chidziŵitso cholongosoka. Monga Yesu ndi Paulo, timasonyeza chikondi chenicheni kwa anthu, ndipo tili ndi chikhumbo chachikulu chakuti apulumutsidwe.—Aroma 10:2.
13 Polalikira, ambiri a ife timakumana ndi anthu amene ataya chikhulupiriro mwa magulu achipembedzo. Komabe, angakhalebe oopa Mulungu, okhulupirira mwa Mulungu pazinthu zina ndipo amene akuyesa kukhala moongoka. Mumbadwo uno wopotoka ndi wopitirizabe kusaopa Mulungu, kodi sitiyenera kukondwera titakumana ndi anthu amene ali ndi chikhulupiriro pang’ono mwa Mulungu? Ndipo kodi sitili ofunitsitsa kuwatsogoza ku malambiridwe opanda chinyengo ndi bodza?—Afilipi 2:15.
14, 15. Kodi munda waukulu wolalikiramo uthenga wabwino wakhalapo bwanji?
14 M’fanizo lake la khoka, Yesu ananeneratu kuti padzakhala gawo lalikulu la ntchito yolalikira. (Mateyu 13:47-49) Pofotokoza fanizo limeneli, Nsanja ya Olonda ya June 15, 1992, inati patsamba 20: “M’kupita kwa zaka mazana ambiri ziŵalo za [Dziko Lachikristu] zinachita mbali yaikulu kutembenuza, kukopa, ndi kufalitsa Mawu a Mulungu. Pambuyo pake matchalitchi anapanga kapena anachirikiza magulu otetezera Baibulo, amene anamasulira Baibulo m’zinenero zakumidzi. Iwo anatumizanso amishonale amene anali madokotala ndi aphunzitsi, amene anagwira ntchito yopanga Akristu m’dzina lokha. Izi zinasonkhanitsa ziŵerengero zazikulu za nsomba zosayenerera, zimene Mulungu sanavomereze. Koma zinayesa kuchititsa mamiliyoni osakhala Akristu kuona Baibulo ndi mpangidwe wa Chikristu, ngakhale kuti unali woipa.”
15 Kutembenuza anthu kwa Dziko Lachikristu kwapambana kwambiri ku South America, Afirika, ndi zisumbu zina za m’nyanja. M’tsiku lathu, ofatsa ambiri apezeka m’madera ameneŵa, ndipo tingapitirize kuchita bwino kwambiri ngati tili ndi mzimu wachiyembekezo ndi wachikondi kwa anthu odzichepetsa ameneŵa, monga momwenso Paulo analili kwa otembenukira kuchiyuda. Pakati pa ofuna thandizo lathu palinso anthu mamiliyoni amene tingawatche kuti “ogwirizana” ndi Mboni za Yehova. Nthaŵi zonse amasangalala kutiona pamene tawachezera. Ena taphunzira nawo Baibulo ndipo afika pamisonkhano yathu, makamaka Chikumbutso cha Imfa ya Kristu cha pachaka. Kodi ameneŵa si gawo lalikulu lolalikiramo uthenga wabwino wa Ufumu?
16, 17. (a) Kodi ndi anthu amtundu wanji amene timafikira ndi uthenga wabwino? (b) Kodi timamtsanzira motani Paulo mwa kulalikira kwa anthu amitundu yosiyanasiyana?
16 Ndiponso, bwanji za awo amene amachokera kumaiko osakhala a Dziko Lachikristu—kaya tikumana nawo kumaiko akwawo kapena asamukira kumaiko a Kumadzulo? Ndiponso bwanji za anthu aja mamiliyoni ambiri amene akaniratu chipembedzo, ndipo akhala okana Mulungu kapena okayikira za kukhalapo kwa Mulungu? Ndiponso, bwanji za aja amene amaona ngati chipembedzo chawo filosofi yamakono kapena ukatswiri wa zamaganizo wotchuka zimene zimafalitsidwa m’mabuku ambiri ophunzitsa zimenezi opezeka m’masitolo a mabuku? Kodi tiyenera kunyalanyaza aliyense wa ameneŵa, kumuona monga kuti sangaomboledwe? Sitingatero ngati titsanzira mtumwi Paulo.
17 Polalikira ku Atene, Paulo sanagwere mumsampha womakangana za filosofi ndi omvetsera ake. Komabe, iye anatchula mfundo zake moganizira anthu amene anali kulankhula nawo, kufotokoza choonadi cha Baibulo momvekera bwino ndipo motsatirika. Mofananamo, ifenso sitifunikira kukhala akatswiri odziŵa za zipembedzo kapena mafilosofi a anthu amene tiwalalikira. Komabe, timasintha mafikidwe athu kuti umboni wathu ukhale wogwira mtima, ndipo mwa kutero timakhala “zonse kwa anthu onse.” (1 Akorinto 9:22) Polembera Akristu a ku Kolose, Paulo anati: ‘Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthaŵi ingatayike. Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.’—Akolose 4:5, 6.
18. Kodi tili ndi ntchito yotani, ndipo sitiyenera kuiŵala chiyani?
18 Monga Yesu ndi mtumwi Paulo, tiyeni tisonyeze chikondi kwa anthu amitundu yonse. Makamaka, tiyeni tiyesetse kugaŵana uthenga wabwino wa Ufumu ndi ena. Ndiponso, tisaiŵale kuti Yesu anati ponena za ophunzira ake: “Siali a dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Tidzakambitsirana zambiri ponena za chimene mawuwa amatanthauza kwa ife m’nkhani yotsatira.
Kupenda
◻ Longosolani lingaliro loyenerera la Yesu ponena za dziko lapansi.
◻ Kodi mtumwi Paulo analalikira motani kwa Ayuda ndi otembenuka?
◻ Kodi Paulo anawafikira motani oopa Mulungu ndi osakhulupirira?
◻ Kodi tingakhale motani “zonse kwa anthu onse” m’ntchito yathu yolalikira?
[Zithunzi patsamba 10]
Mwa kusonyeza kukoma mtima kwa anansi awo, Akristu nthaŵi zambiri angathetse malingaliro olakwa