-
N’chifukwa Chiyani Anthu Amavutika?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 26
N’chifukwa Chiyani Anthu Amavutika?
Zinthu zoipa zikachitika anthu amadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani zimenezi zachitika?” N’zosangalatsa kuti Baibulo limayankha funso limeneli.
1. Kodi Satana anachita chiyani kuti zoipa ziyambe kuchitika padzikoli?
Satana Mdyerekezi anapandukira Mulungu. Satana ankafuna kulamulira ena choncho anapusitsa anthu oyambirira, Adamu ndi Hava kuti nawonso apandukire Mulungu. Satana anachita zimenezi pouza Hava bodza. (Genesis 3:1-5) Anachititsa kuti Hava aziganiza kuti Yehova akumumana zinthu zinazake zabwino. Iye ankatanthauza kuti anthu akhoza kumakhala osangalala ngakhale atapanda kumvera Mulungu. Satana ananena bodza loyamba pouza Hava kuti sadzafa. N’chifukwa chake Baibulo limatchula Satana kuti “ndi wabodza komanso tate wake wabodza.”—Yohane 8:44.
2. Kodi Adamu ndi Hava anasankha kuchita chiyani?
Yehova anapatsa Adamu ndi Hava chilichonse chomwe ankafunikira. Iye anawauza kuti akhoza kudya zipatso za mtengo wina uliwonse wa m’munda wa Edeni kupatulapo umodzi wokha. (Genesis 2:15-17) Koma Adamu ndi Hava anasankha kudya zipatso za mtengo womwe anawaletsa. Hava “anathyola chipatso cha mtengowo n’kudya.” Pambuyo pake, Adamu “nayenso anadya.” (Genesis 3:6) Onse sanamvere Mulungu. Chifukwa chakuti Adamu ndi Hava anali angwiro, zinali zosavuta kuti asankhe kuchita chabwino. Koma iwo anasankha kusamvera Mulungu. Pamene anachita zimenezi anachimwa ndipo anakana kuti Mulungu aziwalamulira. Zimene anachitazi zinawabweretsera mavuto aakulu.—Genesis 3:16-19.
3. Kodi zimene Adamu ndi Hava anasankha kuchita zinatikhudza bwanji?
Adamu ndi Hava atachimwa, anapatsira uchimowo ana awo onse. Ponena za Adamu Baibulo limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse.’—Aroma 5:12.
Anthufe timavutika pa zifukwa zosiyanasiyana. Nthawi zina timavutika chifukwa chakuti sitinasankhe zinthu mwanzeru. Nthawi zinanso timavutika chifukwa chakuti anthu ena asankha zinthu molakwika. Penanso timavutika chifukwa chakuti takumana ndi zinthu zosayembekezereka.—Werengani Mlaliki 9:11.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu si amene amachititsa kuti anthu tizivutika padzikoli komanso mmene amamvera tikamavutika.
4. Ndi ndani amene amachititsa kuti tizivutika?
Anthu ambiri amakhulupilira kuti Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli. Kodi zimenezi ndi zoona? Onerani VIDIYO.
Werengani Yakobo 1:13 ndi 1 Yohane 5:19, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?
5. Kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji kungochokera pamene Satana anayamba kulamulira?
Werengani Genesis 3:1-6, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi bodza liti limene Satana ananena?—Onani vesi 4 ndi 5.
Kodi Satana anachititsa bwanji anthu kuganiza kuti Yehova amawamana zinthu zabwino?
Kodi zimene Satana ananena, zinasonyeza bwanji bodza lakuti anthu akhoza kumasangalalabe ngakhale Yehova atapanda kuwalamulira?
Werengani Mlaliki 8:9, kenako mukambirane funso ili:
Kungochokera pamene Yehova anasiya kulamulira anthu, kodi zinthu zakhala zikuyenda bwanji padzikoli?
Adamu ndi Hava anali angwiro ndipo ankakhala m’Paradaiso. Koma iwo anasankha kumvera Satana n’kupandukira Yehova
Adamu ndi Hava atapandukira Mulungu anthu onse anakhala ochimwa ndipo anayamba kuvutika komanso kumwalira
Yehova adzathetsa uchimo, kuvutika komanso imfa. Zimenezi zikadzachitika anthu adzakhala angwiro m’Paradaiso padziko lapansi
6. Anthufe tikamavutika Yehova zimamukhudza kwambiri
Kodi Mulungu zimamukhudza anthufe tikamavutika? Tiyeni tione zimene Mfumu Davide komanso mtumwi Petulo analemba. Werengani Salimo 31:7 ndi 1 Petulo 5:7, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti Yehova amaona mavuto amene timakumana nawo ndiponso amatisamalira?
7. Mulungu adzathetsa mavuto onse amene anthufe timakumana nawo
Werengani Yesaya 65:17 ndi Chivumbulutso 21:3, 4, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani n’zotonthoza kudziwa kuti Yehova adzathetsa mavuto onse amene tikukumana nawo?
Kodi mukudziwa?
Satana atanena bodza lake loyamba, anachititsa kuti anthu aziona ngati Yehova ndi woipa. Zimenezi zinawononga mbiri ya Yehova yemwe ndi wolamulira wabwino komanso wachikondi. Posachedwapa Yehova adzayeretsa dzina lake akadzathetsa mavuto onse amene anthu akukumana nawo. M’mawu ena tingati adzasonyeza kuti ulamuliro wake wokha ndiwo wabwino kwambiri. Kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi nkhani yofunika kwambiri m’chilengedwe chonse.—Mateyu 6:9, 10.
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndi cholinga cha Mulungu kuti tizivutika.”
Kodi mungayankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Satana Mdyerekezi komanso Adamu ndi Hava ndi amene anayambitsa mavuto onse amene akuchitika padzikoli. Komabe Yehova amakhudzidwa kwambiri tikamavutika ndipo posachedwapa adzathetsa mavuto onse.
Kubwereza
Kodi ndi bodza liti limene Satana Mdyerekezi anauza Hava?
Kodi kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunakhudza bwanji tonsefe?
Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amatidera nkhawa tikamakumana ndi mavuto?
ONANI ZINANSO
Onani zimene mawu oti tchimo amatanthauza m’Baibulo.
Werengani kuti mudziwe zambiri zokhudza nkhani imene Satana Mdyerekezi anayambitsa m’munda wa Edeni.
“N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2014)
Fufuzani mayankho otonthoza a funso lovuta kwambiri.
Onani mmene Baibulo linathandizira munthu wina amene anakumana ndi mavuto pa moyo wake.
-
-
Kodi Imfa ya Yesu Ingatipulumutse Bwanji?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Anthufe timachimwa, kuvutika komanso kufa chifukwa chakuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu.a Komabe Yehova anakonza njira yotipulumutsira ku uchimo ndi imfa. Iye anachita zimenezi potumiza Mwana wake Yesu Khristu. Baibulo limaphunzitsa kuti imfa ya Yesu inali ngati dipo lotiwombola. Dipo ndi malipiro amene amaperekedwa kuti munthu amasulidwe. Choncho, mtengo umene Yesu anapereka unali moyo wake wangwiro. (Werengani Mateyu 20:28.) Popeza kuti Yesu anali wangwiro anali ndi ufulu wokhala ndi moyo wosatha padzikoli. Komabe, iye analolera kupereka moyo wake, zomwe zinathandiza kuti anthufe tidzapezenso zonse zimene Adamu ndi Hava anataya. Yesu anasonyezanso mmene Yehova komanso iyeyo amatikondera. Phunziroli likuthandizani kuti muziyamikira kwambiri zimene Yesu anachita potifera.
1. Kodi imfa ya Yesu ingatithandize bwanji masiku ano?
Popeza kuti ndife ochimwa, timachita zinthu zambiri zimene zimakhumudwitsa Yehova. Komabe ngati tikumva chisoni ndi machimo amene tachita, n’kumupempha Yehova kudzera mwa Yesu Khristu kuti atikhululukire komanso tikamayesetsa kuti tisabwereze machimowo, tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (1 Yohane 2:1) Baibulo limati: “Khristu anafera machimo kamodzi kokha basi. Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu.”—1 Petulo 3:18.
2. Kodi imfa ya Yesu idzatithandiza bwanji m’tsogolo?
Yehova anatumiza Yesu kuti adzapereke moyo wake wangwiro “kuti aliyense wokhulupirira [Yesu] asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Chifukwa cha zimene Yesu anachitazi, posachedwapa Yehova adzachotsa zoipa zonse zimene zinayamba chifukwa cha kusamvera kwa Adamu. Izi zikutanthauza kuti tikamakhulupirira nsembe ya Yesu, tidzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Yesaya 65:21-23.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza chifukwa chimene Yesu anaperekera moyo wake komanso mmene imfa yakeyi ingakuthandizireni.
3. Imfa ya Yesu inatimasula ku uchimo ndi imfa
Kodi Adamu anataya mwayi wotani chifukwa chosamvera Mulungu?
Werengani Aroma 5:12, kenako mukambirane funso ili:
Kodi inuyo mukukumana ndi zotani chifukwa choti Adamu anachimwa?
Werengani Yohane 3:16, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Yehova anatumiza Mwana wake padzikoli?
Adamu anali munthu wangwiro yemwe sanamvere Mulungu. Chifukwa chakuti anachimwa, anthu onse amachimwa komanso kumwalira
Yesu anali munthu wangwiro yemwe anamvera Mulungu. Chifukwa cha zimene anachita anthu onse adzakhala angwiro ndiponso sazidzafa
4. Imfa ya Yesu ingathandize anthu onse
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Kodi imfa ya munthu mmodzi ingathandize bwanji anthu onse?
Werengani 1 Timoteyo 2:5, 6, kenako mukambirane funso ili:
Adamu anali munthu wangwiro koma chifukwa chakuti anachimwa, anthu onse amachimwa komanso kumwalira. Yesu nayenso anali munthu wangwiro. Ndiye kodi zinatheka bwanji kuti apereke “dipo lokwanira ndendende”?
5. Dipo ndi mphatso imene Yehova anakupatsani
Aliyense amene ali pa ubwenzi ndi Yehova amaona kuti dipo ndi mphatso imene Mulungu anakonzera iyeyo. Mwachitsanzo, werengani Agalatiya 2:20 kenako mukambirane funso ili:
Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti dipo inali mphatso imene Mulungu anakonzera iyeyo?
Adamu atachimwa, iyeyo ndi ana ake onse anali oyenerera kufa. Koma Yehova anatumiza Mwana wake kuti adzatifere n’cholinga choti inuyo mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale.
Mukamawerenga mavesi otsatirawa, ganizirani mmene Yehova anamvera pamene ankaona Mwana wake akuvutika. Werengani Yohane 19:1-7, 16-18, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mukumva bwanji mukaganizira zimene Yehova ndi Yesu anakuchitirani?
MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “Kodi zingatheke bwanji kuti munthu mmodzi afere anthu onse?”
Kodi mungayankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Chifukwa chakuti Yesu anatifera, Yehova amatikhululukira machimo athu komanso tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo mpaka kalekale.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
Kodi moyo wa Yesu wangwiro unakhala bwanji dipo lokwanira ndendende?
Kodi imfa ya Yesu imakuthandizani bwanji?
ONANI ZINANSO
Onani chifukwa chake timanena kuti moyo wangwiro wa Yesu ndi dipo lotiwombola.
“Kodi Nsembe ya Yesu Imawombola Bwanji ‘Anthu Ambiri’?” (Nkhani yapawebusaiti)
Dziwani zimene mungachite kuti mupulumutsidwe ku uchimo ndi imfa.
Kodi Yehova angakhululukire munthu yemwe anachitapo machimo akuluakulu?
“Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2013)
Onani mmene kuphunzira zokhudza nsembe ya Khristu kunathandizira munthu wina kusintha umunthu wake.
a Tchimo silimangotanthauza kuchita chinthu chinachake cholakwika. Koma limatanthauzanso kuti tinatalikirana ndi Mulungu chifukwa chakuti ndife ana a Adamu.
-