-
Mulungu Akuonetsa Chikondi Chake kwa IfeNsanja ya Olonda—2011 | June 15
-
-
7, 8. Kodi zochita za anthu awiri angwiro zinali ndi zotsatira zosiyana ziti?
7 Chifukwa cha chikondi, Yehova anakonza njira yoti anthu amasuke ku uchimo umene anatengera. Paulo anafotokoza kuti zimenezi n’zotheka ndi munthu wina wangwiro amene anadzakhala ngati Adamu wachiwiri. (1 Akor. 15:45) Koma zochita za munthu wangwiro ameneyu zinali ndi zotsatira zosiyana kwambiri ndi za Adamu woyamba, yemwe analinso wangwiro. Kodi zinasiyana bwanji?—Werengani Aroma 5:15, 16.
8 Paulo analemba kuti: “Mmene zilili ndi mphatsoyi si mmene zinalili ndi uchimowo.” Adamu anachimwa ndipo analandira chilango choyenera, chomwe chinali imfa. Koma imfa sinangokhudza iye yekha. Paulo anati: “Mwa uchimo wa munthu mmodzi [ameneyu] ambiri anafa.” Choncho ana onse a Adamu, kuphatikizapo ifeyo, ayenera kufa chifukwa nawonso ndi ochimwa. Komabe n’zolimbikitsa kudziwa kuti zochita za munthu wangwiro, yemwe ndi Yesu, zinali ndi zotsatira zosiyana kwambiri ndi za Adamu. Kodi zotsatira zake n’zotani? Paulo anayankha ponena kuti: “Anthu kaya akhale amtundu wotani akuyesedwa olungama kuti akhale ndi moyo.”—Aroma 5:18.
9. Kodi mawu a pa Aroma 5:16, 18 onena kuti anthu akuyesedwa kapena kuti akutchedwa olungama akutanthauza kuti Mulungu anachita chiyani?
9 Kodi mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “atchedwe olungama” ndiponso akuti “akuyesedwa olungama” akutanthauza chiyani? Munthu wina womasulira Baibulo anati: “Mawu amenewa akufotokoza zinthu ngati zikuchitika m’khoti motsatira malamulo. Mawuwa akusonyeza kuti Mulungu wasintha mmene akuonera munthu osati kuti munthuyo wasintha . . . Zili ngati kuti munthu akuimbidwa mlandu wakuti ndi wosalungama ndipo Mulungu ndi woweruza yemwe wagamula kuti munthuyu amasulidwe.”
-
-
Mulungu Akuonetsa Chikondi Chake kwa IfeNsanja ya Olonda—2011 | June 15
-
-
14, 15. Kodi anthu amene amatchedwa olungama ndi Mulungu amakhala ndi chiyembekezo chotani koma iwo amayenerabe kuchita chiyani?
14 Kukhululukidwa uchimo umene tinatengera komanso machimo amene tachita ndi mphatso yaikulu kwambiri yochokera kwa Wamphamvuyonse. Munthu asanakhale Mkhristu amachita machimo osawerengeka, koma Mulungu amatha kukhululukira machimo onsewa chifukwa cha dipo. Paulo analemba kuti: “Mphatso imene inatsatira machimo ambiri, inachititsa kuti anthu atchedwe olungama.” (Aroma 5:16) Atumwi ndiponso anthu ena amene alandira mphatso imeneyi (ya kutchedwa olungama) ayenera kukhalabe ndi chikhulupiriro polambira Mulungu woona. Kodi iwo ali ndi chiyembekezo chotani? Anthu “amene alandira kukoma mtima kwakukulu kochuluka ndiponso mphatso yaulere yaikuluyo ya chilungamo, adzakhala ndi moyo ndi kulamulira monga mafumu kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.” Mphatso ya chilungamo imachita zosiyana kwambiri ndi uchimo. Zotsatira za mphatsoyi ndi moyo.—Aroma 5:17; werengani Luka 22:28-30.
-