Tinamasulidwa ku Uchimo Chifukwa cha Kukoma Mtima Kwakukulu
‘Uchimo usakhale mbuye kwa inu, chifukwa muli pansi pa kukoma mtima kwakukulu.’—AROMA 6:14.
1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti lemba la Aroma 5:12 ndi lofunika kwambiri kwa a Mbonife?
TIYEREKEZE kuti mukufuna kulemba malemba amene a Mboni za Yehova amawadziwa bwino komanso amawagwiritsa ntchito kawirikawiri. Kodi lemba la Aroma 5:12 lingakhale koyambirira? Lembali limati: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.”
2 M’buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? lemba limeneli limapezeka kambirimbiri. Mukamaphunzira bukuli ndi mwana wanu kapena anthu ena, muyenera kuti mumawerenga lembali mukamakambirana mutu 3, 5 ndi 6. Mitu imeneyi imanena za cholinga cha Mulungu kwa anthu, dipo komanso zimene zimachitika munthu akamwalira. Komatu lembali lingatithandizenso tonsefe. Lingatithandize kuti tiziyamikira ubwenzi wathu ndi Yehova, tiziona zimene tingachite kuti tizimusangalatsa komanso tiziyembekezera kwambiri zimene walonjeza.
3. Kodi tonsefe tiyenera kukumbukira chiyani pa nkhani ya uchimo?
3 N’zoona kuti tonsefe ndife ochimwa ndipo tsiku lililonse timalakwitsa zinthu zina. Koma Mulungu amatichitira chifundo chifukwa amakumbukira kuti ndife fumbi. (Sal. 103:13, 14) M’pemphero la chitsanzo, Yesu ananena kuti tizipempha kuti: “Mutikhululukire machimo athu.” (Luka 11:2-4) Choncho sitiyenera kumangoganizirabe zinthu zimene Mulungu anatikhululukira. Komabe tingachite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi zimatheka bwanji kuti Mulungu atikhululukire machimo athu?’
AMATIKHULULUKIRA CHIFUKWA CHA KUKOMA MTIMA KWAKUKULU
4, 5. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kumvetsa lemba la Aroma 5:12? (b) Kodi mawu akuti ‘kukoma mtima kwakukulu’ opezeka pa Aroma 3:24 amatanthauza chiyani?
4 Buku la Aroma, makamaka chaputala 6, limatithandiza kumvetsa zimene zimachititsa kuti Yehova atikhululukire machimo athu. Komanso m’chaputala 3 timapeza mawu akuti: “Pakuti onse ndi ochimwa ndipo . . . kuyesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.” (Aroma 3:23, 24) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti ‘kukoma mtima kwakukulu’? Iye anagwiritsa ntchito mawu achigiriki omwe amatanthauza “kuchitira munthu zabwino popanda kuyembekezera kuti atibwezere kapena kukomera mtima munthu amene sakuyenera kum’komera mtima.”
5 Katswiri wina anafotokoza kuti Baibulo likamanena za kukoma mtima kwa Mulungu kapena kwa Yesu, nthawi zambiri limakhala likunena zimene iwo anachita populumutsa anthu ku uchimo ndi imfa. Koma kodi Mulungu anasonyeza bwanji kukoma mtima kwakukulu? Nanga khalidweli limakhudza bwanji ubwenzi wathu ndi iye komanso zimene tikuyembekezera? Tikambirana mafunso amenewa.
6. Kodi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kwathandiza bwanji anthu?
6 “Munthu mmodzi” wotchulidwa pa Aroma 5:12 ndi Adamu ndipo kudzera mwa iye uchimo ndi imfa ‘zinalowa m’dziko.’ Choncho “chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo imfa inalamulira monga mfumu.” Koma Paulo ananenanso kuti “kukoma mtima kwakukulu kochuluka [kwa Mulungu]” kunaoneka “kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.” (Aroma 5:12, 15, 17) Ndipo kukoma mtima kwakukulu kumeneku kwathandiza kwambiri anthu onse. Tikutero chifukwa “kudzera mwa kumvera kwa munthu mmodziyu [Yesu], ambiri adzakhala olungama.” Izi zikusonyeza kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kudzachititsa kuti “moyo wosatha ubwere kudzera mwa Yesu Khristu.”—Aroma 5:19, 21.
7. N’chifukwa chiyani dipo limene Mulungu anapereka limasonyeza kukoma mtima kwakukulu?
7 Yehova sankafunikira kutumiza Mwana wake kudzapereka dipo. Koma anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu pokonza njira yotipulumutsira ku uchimo ndi imfa. Anthu ochimwafe tinali osayenera kupatsidwa dipo ndi Mulungu komanso Yesu. Choncho timayamikira kwambiri zimene anachitazi chifukwa zimathandiza kuti machimo athu azikhululukidwa komanso kuti tidzakhale ndi moyo wosatha. Koma kodi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti timayamikiradi zomwe Mulungu anachitazi?
TIZIYAMIKIRA KUKOMA MTIMA KWAKUKULU KWA MULUNGU
8. Kodi anthu ena amakhala ndi maganizo olakwika ati?
8 Popeza ndife ana a Adamu, timachimwa. Komatu n’kulakwa kwambiri kugwiritsa ntchito mosayenera kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Tisamaganize kuti, ‘Ngakhale nditachita tchimo lalikulu, palibe vuto chifukwa Yehova angandikhululukire.’ N’zomvetsa chisoni kuti nthawi ya atumwi panalinso Akhristu ena amene anali ndi maganizo amenewa. (Werengani Yuda 4.) Ifeyo sitinganene n’komwe zimenezi. Komabe tiyenera kusamala kuti tisayambe kukhala ndi maganizo amenewa mumtima mwathu.
9, 10. Kodi Paulo ndi Akhristu ena anamasulidwa bwanji ku uchimo ndi imfa?
9 Paulo anatsindika mfundo yoti Akhristu ayenera kupewa maganizo akuti, ‘Mulungu andimvetsa ndipo andikhululukira zimene ndikuchitazi.’ Tikutero chifukwa cha zimene iye ananena zoti Akhristu ‘anafa ku uchimo.’ (Werengani Aroma 6:1, 2.) Popeza Akhistuwo anali adakali moyo, kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti iwo ‘anafa ku uchimo?’
10 Mulungu anagwiritsa ntchito dipo kuti athandize Paulo komanso a Akhristu a nthawi yake. Iye anawakhululukira machimo awo ndipo anawadzoza ndi mzimu wake woyera kuti akhale ana ake. Ankafuna kuti akakhalabe okhulupirika, adzalamulire ndi Khristu. Ndiyeno Paulo anayerekezera moyo wawo ndi wa Yesu pofuna kusonyeza kuti Akhristuwo anasintha kwambiri. Anati Yesu atafa, anaukitsidwa ndi thupi loti silingafe. N’chifukwa chake Baibulo limati, “imfa sikuchitanso ufumu pa iye.” Mofanana ndi zimenezi, Akhristuwo anafa pamene anasiya moyo wauchimo. Iwo sankalolanso kuti azichita zinthu motsatira zilakolako zoipa. Koma ankayesetsa kukhala ndi moyo wosangalatsa Mulungu. Choncho tingati ‘anafa ku uchimo koma anali amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.’—Aroma 6:9, 11.
11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti nawonso Akhristu odzakhala padzikoli ‘anafa ku uchimo’?
11 Nanga bwanji ifeyo? Tisanakhale Akhristu tinkachita machimo ambiri. Mwinanso sitinkazindikira n’komwe kuti zimene tikuchitazo n’zoipa pamaso pa Mulungu. Tinali “akapolo a zonyansa ndiponso akapolo a kusamvera malamulo.” Choncho tinali “akapolo a uchimo.” (Aroma 6:19, 20) Koma titaphunzira Baibulo, tinasintha moyo wathu, tinadzipereka kwa Mulungu ndipo kenako tinabatizidwa. Kuyambira nthawi imeneyo, timafunitsitsa kumvera Mulungu “mochokera pansi pa mtima.” Mwachidule tingati ‘tinamasulidwa ku uchimo n’kukhala akapolo a chilungamo.’ (Aroma 6:17, 18) Choncho tinganene kuti nafenso “tinafa ku uchimo.”
12. Kodi tonsefe tiyenera kusankha kuchita chiyani?
12 Taganizirani mawu a Paulo awa: “Musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo.” (Aroma 6:12) Tikamachita chilichonse chimene matupi athu ochimwawa akufuna, ndiye kuti ‘tikulola kuti uchimo uzitilamulirabe.’ Anthufe tingathe kulola kapena kukana kuti uchimo uzitilamulira. Ndiye dzifunseni kuti, ‘Kodi ndinafa ku uchimo? Kapena kodi nthawi zina ndimangotsatira mtima wanga komanso thupi lochimwali n’kumachita zinthu zoipa? Kodi ndikukhala ndi moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu?’ Ngati timayamikira kwambiri kukoma mtima kwa Mulungu, tidzayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa.
TINGAPAMBANE NKHONDO YOLIMBANA NDI UCHIMO
13. Kodi tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kusiya zoipa n’kumachita zabwino?
13 M’nthawi ya atumwi, anthu ena a ku Korinto anali akuba, achigololo, oledzera, olambira mafano ndiponso ankagonana ndi amuna kapena akazi anzawo. Koma atadziwa Mulungu n’kuyamba kumukonda, anasinthiratu ndipo ankachita manyazi akaganizira zimene ankachita poyambazo. (Aroma 6:21; 1 Akor. 6:9-11) Nawonso Akhristu a ku Roma ankafunika kusintha. Paulo anawauza kuti: “Musapereke ziwalo zanu ku uchimo kuti zikhale zida zochitira zinthu zosalungama, koma dziperekeni kwa Mulungu monga anthu amene auka kwa akufa. Ziwalo zanunso muzipereke kwa Mulungu monga zida zochitira chilungamo.” (Aroma 6:13) Paulo ankadziwa kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kukhoza kuthandiza Aromawo kukhala oyera.
14, 15. Kodi tiyenera kudzifunsa funso liti pa nkhani yomvera Mulungu “mochokera pansi pa mtima”?
14 Ndi mmene zililinso masiku ano. Abale ndi alongo ena anali ndi makhalidwe oipa ngati amene ankachitika ku Korinto. Koma nawonso anasintha moti tingati ‘anasambitsidwa n’kukhala oyera.’ Kaya inuyo poyamba zinali bwanji, funso ndi lakuti, ‘Kodi panopa muli pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu?’ Popeza Mulungu wakusonyezani kukoma mtima kwakukulu ndipo wakukhululukirani machimo anu, kodi mumapeweratu ‘kupereka thupi lanu ku uchimo?’ Kodi mumayesetsa ‘kudzipereka kwa Mulungu monga munthu amene wauka kwa akufa’?
15 Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kupewa machimo akuluakulu ngati amene ankachitika ku Korinto. Zimenezi n’zofunika kwambiri ngati tikufuna kusonyeza kuti timayamikira kukoma mtima kwa Mulungu ndipo ‘uchimo sukutilamulira.’ Koma funso lina limene tiyenera kudzifunsa ndi lakuti, ‘Kodi ndimayesetsa “kumvera mochokera pansi pa mtima” popewanso machimo ooneka ngati ang’onoang’ono?’—Aroma 6:14, 17.
16. Tikudziwa bwanji kuti Akhristu ayenera kupewanso machimo ooneka ngati aang’ono, osati akuluakulu okha?
16 Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi mtumwi Paulo. Tikudziwa kuti iye sankachita zoipa ngati zimene zatchulidwa pa 1 Akorinto 6:9-11. Koma iye anavomereza kuti anali wochimwa. Paja analemba kuti: “Ine ndine wakuthupi, wogulitsidwa ku uchimo. Sindimvetsetsa kuti n’chifukwa chiyani ndimachita zinthu motere. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita.” (Aroma 7:14, 15) Mawuwa akusonyeza kuti pali zinthu zina zimene Paulo ankachita zomwe ankaona kuti ndi machimo ndipo ankayesetsa kuti asiye. (Werengani Aroma 7:21-23.) Ifenso tiyenera kukhala ndi maganizo amenewa tikamayesetsa kumvera Mulungu “mochokera pansi pa mtima.”
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oona mtima?
17 Nkhani ina imene imavuta ndi ya kuona mtima. Tonsefe timadziwa kuti Akhristu ayenera kuchita zinthu moona mtima. (Werengani Miyambo 14:5; Aefeso 4:25.) Baibulo limati Satana ndi “tate wake wa bodza.” Tikudziwanso kuti Hananiya ndi mkazi wake anafa chifukwa cha bodza. Choncho timapewa bodza kuti tisafanane nawo. (Yoh. 8:44; Mac. 5:1-11) Koma kodi chofunika n’kupewa kunena bodza basi? Ngati timayamikira kukoma mtima kwa Mulungu, tidzayesetsa kukhala oona mtima m’njira zinanso.
18, 19. Kodi munthu woona mtima amapewanso chiyani?
18 Munthu akhoza kuchita chinyengo popanda kunena bodza. Mwachitsanzo, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Mukhale oyera, chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.” Ndiyeno pofotokoza mmene angakhalire oyera, anawauza kuti: “Musabe, musanamizane ndipo aliyense asachitire mnzake chinyengo.” (Lev. 19:2, 11) Chomvetsa chisoni n’chakuti anthu ena sanena chilungamo ngakhale kuti sanena bodza lenileni.
19 Mwachitsanzo, munthu akhoza kuuza abwana ake kapenanso anzake akuntchito kuti sapita kuntchito kapena aweruka mwamsanga chifukwa choti akukaonana ndi dokotala. Koma zoona zake zili zoti angodutsa kumalo ogulitsira mankhwala kapena angopita kuchipatala kukalipira ndalama. Chimene wachokera mwamsanga kuntchito n’choti akufuna kuti akakhale ndi nthawi yokwanira yokonzekera ulendo wopita kutchuthi kapena kunyanja ndi banja lake. N’zoona kuti akaonanadi ndi dokotala, koma kodi wachita zinthu moona mtima, kapena wachita chinyengo? Pali zitsanzo zambiri za ngati zimenezi zimene mungaziganizire. Munthu angapangitse anthu kuganiza zina pamene zimene akutanthauza kapena zolinga zake si zimenezo. Akhoza kuchita zimenezi kuti asalangidwe kapena kuti apeze zimene akufuna. Koma ngakhale atakhala kuti sananene bodza lenileni, kodi tingati akumvera lamulo la Mulungu lakuti: “Aliyense asachitire mnzake chinyengo”? Ndi bwino kuganiziranso mfundo ya pa Aroma 6:19 yakuti: ‘Perekani ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a chilungamo kuti muzichita ntchito za chiyero.’
20, 21. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati timayamikira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?
20 Munthu amene amayamikira kukoma mtima kwa Mulungu amapewa dama, kuledzera komanso machimo ena amene ankachitika ku Korinto. Koma si zokhazi. Ayenera kupewa chilichonse chimene chingakhumudwitse Yehova. Mwachitsanzo, m’malo mongopewa chiwerewere, amapewanso zosangalatsa zimene zimalimbikitsa chiwerewerecho. M’malo mopewa kuledzera amapewanso kumwa kwambiri moti n’kutsala pang’ono kuledzera. N’zoona kuti kuchita zimenezi si kophweka koma ndi nkhondo yoti tikhoza kupambana.
21 Tiyeni tiziyesetsa kupewa machimo akuluakulu komanso ang’onoang’ono. N’kutheka kuti nthawi zina tizilephera kuchita zimenezi bwinobwino. Koma tiyenera kuyesetsa ngati mmene Paulo ankachitira. Paja iye anauza Akhristu anzake kuti: “Musalole kuti uchimo uzilamulirabe monga mfumu m’matupi anu okhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo.” (Aroma 6:12; 7:18-20) Tikamayesetsa kupewa machimo a mtundu uliwonse, timasonyeza kuti timayamikira kwambiri kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu watisonyeza kudzera mwa Khristu.
22. Kodi anthu amene amayamikira kukoma mtima kwa Mulungu adzapeza mphoto iti?
22 M’nkhaniyi taona kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kumathandiza kuti azitikhululukira machimo. Tingasonyeze kuti timayamikira zimenezi popewanso kuchita machimo amene amaoneka ngati aang’ono. Paulo anatchula mphoto imene tingapeze ngati titayesetsa kuchita zimenezi. Iye anati: “Chifukwa munamasulidwa ku uchimo ndipo munakhala akapolo a Mulungu, mukukhala ndi zipatso za chiyero, ndipo pa mapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.”—Aroma 6:22.