Ulamuliro wa Anthu Ochepa Udzabweretsa Madalitso kwa Anthu Ambiri
KUYAMBIRA m’nthawi ya atumwi, Mulungu wakhala akusankha Akhristu okhulupirika owerengeka kukhala ana ake. Akhristu amenewa amachokera m’mitundu yonse ya anthu. Ana amenewa amasintha kwambiri moti Mawu a Mulungu amafotokoza kuti kusinthaku ndi kubadwa mwatsopano. Cholinga cha kubadwa mwatsopano n’chakuti ana amenewa akonzekere kukalamulira kumwamba. (2 Timoteyo 2:12) Kuti adzakhale olamulira, iwo akamwalira amaukitsidwa n’kupita kumwamba. (Aroma 6:3-5) Ali kumwambako, “adzalamulira dziko lapansi monga mafumu” pamodzi ndi Khristu.—Chivumbulutso 5:10; 11:15.
Komabe, Mawu a Mulungu amanenanso kuti pali anthu ena omwe si obadwanso amene adzapulumitsidwe. Baibulo (m’Malemba a Chiheberi ndiponso Achigiriki Achikhristu) limafotokoza kuti Mulungu anakonza zoti anthu odzapulumuka adzakhale magulu awiri. Gulu lina ndi la anthu ochepa ndipo lidzapita kumwamba komanso gulu lina ndi lalikulu kwambiri ndipo lidzakhala padziko lapansi. Mwachitsanzo, taonani zimene mtumwi Yohane analembera okhulupirira anzake amene anali atabadwa mwatsopano. Ponena za Yesu, Yohane anati: “Iye ndiye nsembe yachiyanjanitso yophimba machimo athu. Osati athu okha [kutanthauza kagulu kochepa], komanso a dziko lonse [kutanthauza gulu lalikulu].”—1 Yohane 2:2.
Mofanana ndi zimenezi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti chilengedwe [kutanthauza gulu lalikulu] chikudikira mwachidwi kuti ana a Mulungu [kutanthauza gulu laling’ono] aonetsedwe.” (Aroma 8:19-21) Kodi mawu a mtumwi Yohane ndi mtumwi Paulo amenewa akutanthauza chiyani? Akutanthauza kuti anthu obadwanso adzakhala mbali ya boma lakumwamba kuti abweretse madalitso osatha kwa anthu mamiliyoni ambiri okhala padziko lapansi, amene azidzalamulidwa ndi boma la Mulungu. N’chifukwa chake Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”—Mateyo 6:10.
Mfundo yonena za magulu awiri amene adzapulumutsidwe imapezekanso m’Malemba a Chiheberi. Mwachitsanzo, Yehova anauza Abulahamu, yemwe anali kholo la Yesu kuti: “M’mbewu zako [kutanthauza gulu laling’ono] mitundu yonse ya dziko lapansi [kutanthauza gulu lalikulu] idzadalitsidwa.” (Genesis 22:18) Ndithudi, mitundu yonse ya anthu idzapeza madalitso kudzera “m’mbewu” ya Abulahamu.
Kodi “mbewu” imeneyo ikuimira ndani? Ikuimira Yesu Khristu pamodzi ndi ana a Mulungu obadwa mwatsopano. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Ngati muli a Khristu, mulidi mbewu ya Abulahamu.” (Agalatiya 3:16, 29) Nanga kodi ndi madalitso otani amene anthu a mitundu yonse adzapeze kudzera mwa “mbewu” imeneyi? Madalitso ake ndiwo mwayi wokhalanso paubwenzi ndi Mulungu ndiponso kudzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Wamasalmo Davide analosera kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29; Yesaya 45:18; Chivumbulutso 21:1-5.
N’zoona kuti pali anthu ochepa okha amene akalamulire kumwamba. Koma ndi anthu ambiri amene adzalandire moyo wosatha padziko lapansi, n’kupindula ndi madalitso a ulamuliro wakumwamba umenewo. Choncho, yesetsani kuti inuyo pamodzi ndi banja lanu mudzakhale m’gulu la anthu amene adzalandire madalitso osatha mu Ufumu wa Mulungu.
[Chithunzi patsamba 12]
Pali anthu ambiri amene adzalandire moyo wosatha padziko lapansi pano. Kodi inuyo mudzalandira nawo madalitso amenewa?