-
Tizisangalala ndi Chiyembekezo ChathuNsanja ya Olonda—2012 | March 15
-
-
10, 11. (a) Kodi nkhosa zina zili ndi chiyembekezo chotani? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chodzakhala kosatha padziko lapansi kukugwirizana bwanji ndi Khristu ndiponso ‘kuonekera kwa ana a Mulungu’?
10 Mtumwi Paulo analemba za chiyembekezo chosangalatsa chimene “ana a Mulungu” obadwa ndi mzimu amakhala nacho monga “olandira cholowa anzake” a Khristu. Kenako analemba za chiyembekezo chosangalatsa chimene Yehova wasungira anthu osawerengeka a nkhosa zina. Iye anati: “Pakuti chilengedwe [anthu] chikudikira mwachidwi nthawi imene ulemelero wa ana a Mulungu [odzozedwa] udzaonekere. Popeza chilengedwe chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake, osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa iye amene anachipereka, pa maziko a chiyembekezo chakuti chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:14-21.
-
-
Tizisangalala ndi Chiyembekezo ChathuNsanja ya Olonda—2012 | March 15
-
-
12. Kodi kuonekera kwa Akhristu odzozedwa kudzathandiza bwanji anthu?
12 Koma kunena zoona, “chilengedwe” chidzapumuladi mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Pa nthawi imeneyi, “ana a Mulungu” aulemerero adzaonekeranso pamene adzagwiranso ntchito monga ansembe limodzi ndi Khristu ndipo adzathandiza anthu kupindula ndi nsembe ya dipo ya Yesu. Monga nzika za Ufumu wa Mulungu, anthu adzamasulidwa ku uchimo ndi imfa. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono, anthu omvera ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda.’ Ngati adzakhalabe okhulupirika kwa Yehova mkati mwa zaka 1,000 mpaka pamapeto pa mayesero omaliza, mayina awo adzalembedwa mu “mpukutu wa moyo.” Iwo adzalowa mu “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Chiv. 20:7, 8, 11, 12) Chimenechitu ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri.
-