Aliyense Adzakhala Paufulu
“Ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu waulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.”—AROMA 8:18-22.
MTUMWI Paulo m’ndime iyi ya m’kalata yake yopita kwa Akristu a ku Roma ananena mwachidule chifukwa chake miyoyo sili paufulu weniweni ndiponso chifukwa chake kaŵirikaŵiri ili yopanda chifuno komanso yopweteka. Anafotokozanso mmene tingapezere ufulu weniweni.
“Masauko a Nyengo Yatsopano”
Paulo ponena kuti “sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife,” sanali kuchepetsa “masauko a nyengo yatsopano.” M’nthaŵi ya Paulo komanso pambuyo pake, Akristu anazunzika kwambiri mu ulamuliro wankhanza wa Aroma, omwe sanali kusamala za ufulu wachibadwidwe. Pamene Aroma anaona kuti Akristu anali kudana ndi Boma, anawazunza koopsa. Wolemba mbiri J. M. Roberts anati: “Akristu ambiri okhala kulikulu [Roma] anaphedwa mozunzika pabwalo la maseŵero kapena kuwotchedwa amoyo.” (Shorter History of the World) Ponena za anthu amene anazunzidwa ndi Nero ameneŵa, lipoti lina linati: “Ena anali kuphedwa mowapachika pamtengo, ena anali kuwasokerera m’zikopa zanyama ndipo anali kusakidwa ndi agalu, ena anali kuwapaka phula ndipo anali kuwayatsa kuti akhale ngati nyali zounikira usiku.”—New Testament History, yolembedwa ndi F. F. Bruce.
Mosakayikira Akristu akale ameneŵa anali kufuna ufulu kuti alekane ndi chiponderezo chimenecho, koma sankafuna kuswa ziphunzitso za Yesu Kristu kuti aupeze. Mwachitsanzo, pakulimbana kwa olamulira achiroma ndi omenyera ufulu achiyuda monga Azelote, iwo anasunga uchete kotheratu. (Yohane 17:16; 18:36) Kwa Azelote, “kudikirira nthaŵi yabwino ya Mulungu imene adzabweretsa mtendere zinali zosagwirizana ndi vuto lomwe linalipolo.” Iwo ankati chomwe chinali kufunika chinali “kulimbana” ndi mdani wawo Roma. (New Testament History) Akristu oyambirira anali kuganiza mosiyana ndi zimenezi. Kwa iwo “kudikira nthaŵi yabwino ya Mulungu” ndicho chinali chosankha chokha chanzeru. Anali ndi chikhulupiriro kuti palibe china chilichonse chimene chingathetseretu “masauko a nyengo yatsopano” ndi kubweretsa ufulu weniweni komanso wopanda mapeto kusiyapo ngati Mulungu achitapo kanthu. (Mika 7:7; Habakuku 2:3) Komabe, tisanapende mmene zimenezi zidzachitikire, tiyeni tipende kaye chifukwa chake “cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru.”
“Chagonjetsedwa Kuutsiru”
Benjamin Wilson m’Baibulo lotchedwa The Emphatic Diaglott akuti, apa liwulo “cholengedwa,” silitanthauza “zolengedwa zopanda moyo ndi zinyama” monga mmene ena amaganizira, komano limatanthauza “anthu onse.” (Yerekezerani ndi Akolose 1:23.) Limatanthauza mtundu wonse wa anthu—tonse amene timalakalaka ufulu. Chifukwa cha zimene makolo athu oyamba anachita ‘tinagonjetsedwa kuutsiru.’ Chinali ‘chosafuna enife’ kapena chifukwa cha zimene aliyense anasankha kuti zimenezi zichitike. Tinachita kubadwa nazo. Malinga ndi zimene Malemba amanena, Rousseau analakwitsa ponena kuti “munthu anabadwa ndi ufulu.” Tonsefe tinabadwa ndi ukapolo wa uchimo ndi kupanda ungwiro, akapolo titero kunena kwake, a dziko lodzaza ndi zokhumudwitsa ndi zinthu zopanda pake.—Aroma 3:23.
Chifukwa chiyani zili chonchi? Chifukwa chakuti makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, ankafuna kukhala “ngati Mulungu,” odziimira paokha, ndiponso odzisankhira chabwino ndi choipa. (Genesis 3:5) Anaiwala mfundo ina yofunika yonena zaufulu. Mlengi yekha ndiye amene ali ndi ufulu wonse. Iye ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse. (Yesaya 33:22; Chivumbulutso 4:11) Ufulu wa anthu uli ndi polekezera. N’chifukwa chake wophunzira Yakobo analimbikitsa Akristu a m’tsiku lake kuti azitsatira “m’lamulo langwiro, ndilo laufulu.”—Yakobo 1:25.
Yehova anachotsa Adamu ndi Hava m’banja lake lachilengedwe chonse potsirizira pake anamwalira. (Genesis 3:19) Nanga ana awo? Ngakhale kuti tsopano anali kudzapatsira ana awo kupanda ungwiro, uchimo, ndi imfa, Yehova mwachifundo anawalola kubereka ana. Chotero “imfa inafikira anthu onse.” (Aroma 5:12) Mulingaliro limeneli Mulungu ‘anagonjetsa [cholengedwa] kuutsiru.’
“Vumbulutso la ana a Mulungu”
Yehova anagonjetsa chilengedwe kuutsiru “ndi chiyembekezo” chakuti tsiku lina mtundu wa anthu udzakhalanso paufulu kupyolera muntchito ya “ana a Mulungu.” Kodi “ana a Mulungu” ameneŵa ndi ayani? Ndi ophunzira a Yesu Kristu amene, monga anthu ena onse ‘obadwa mwa [munthu],’ amabadwa ndi uchimo komanso opanda ungwiro. Pobadwa amakhala opanda malo m’banja loyera ndi langwiro lachilengedwe chonse cha Mulungu. Komabe, Yehova amawachitira chinthu china chapadera. Kupyolera mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, Iye amawamasula kuukapolo womwe anabadwa nawo wa uchimo ndipo amawayesa “olungama,” kapena oyera mwauzimu. (1 Akorinto 6:11) Ndiyeno amawatenga monga “ana a Mulungu,” ndi kuwabwezeranso m’banja lake lachilengedwe chonse.—Aroma 8:14-17.
Monga ana otengedwa a Yehova, adzakhala ndi mwayi waulemerero. Adzakhala “ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko” pamodzi ndi Yesu Kristu monga mbali ya Ufumu kapena Boma lakumwamba la Mulungu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4) Limeneli ndi boma lokhazikitsidwa zolimba pa malamulo aufulu ndi achilungamo—osati otsendereza ndi ankhanza. (Yesaya 9:6, 7; 61:1-4) Mtumwi Paulo ananena kuti ana a Mulungu ameneŵa ali anzake a Yesu, ‘mbewu ya Abrahamu’ yolonjezedwa kalekale. (Agalatiya 3:16, 26, 29) Chotero, iwonso, ali ofunika kwambiri pokwaniritsa lonjezo limene Mulungu analonjeza bwenzi lake Abrahamu. Mbali ya lonjezo limenelo inali yakuti kupyolera mwa mbewu ya Abrahamu (kapena, mwana), “mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.”—Genesis 22:18.
Kodi adzabweretsa madalitso otani kumtundu wa anthu? Ana a Mulungu adzagwira nawo ntchito yomasula mtundu wonse wa anthu ku zinthu zopweteka zimene uchimo wa Adamu unabweretsa ndi kubwezera mtundu wa anthu ku ungwiro. Anthu “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu” angadzidalitse mwakusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu ndi mwa kugonjera ku Ufumu wake wachikondi. (Chivumbulutso 7:9, 14-17; 21:1-4; 22:1, 2; Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Mwanjira imeneyi “cholengedwa chonse” chidzasangalalanso ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” Koma uwu sudzakhala ufulu winawake wochepa wandale wa kanthaŵi kochepa. M’malo mwake, udzakhala ufulu pachilichonse chimene chadzetsa zowawa ndi mavuto ku mtundu wa anthu kuyambira pamene Adamu ndi Hava anakana uchifumu wa Mulungu. N’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena kuti “masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa” ndi utumiki waulemerero umene anthu okhulupirika adzachita!
Kodi “vumbulutso la ana a Mulungu” lidzayamba liti? Posachedwapa tsopano, pamene Yehova adziŵikitsa anthu onse amene ali ana a Mulungu. Izi zidzachitika pamene “ana” ameneŵa, oukitsidwira kumwamba, pamodzi ndi Yesu Kristu adzayeretsa dziko loipa ndi lopondereza lino pankhondo ya Mulungu ya Harmagedo. (Danieli 2:44; 7:13, 14, 27; Chivumbulutso 2:26, 27; 16:16; 17:14; 19:11-21) Tikuona umboni wochuluka paliponse wakuti tili mkati mwenimweni mwa “masiku otsiriza,” pamene Mulungu sadzalekereranso chipanduko ndi kuipa kumene chinabweretsa monga mmene wachitira kwanthaŵi yaitali.—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-31.
Inde, ndi zoona, zimene mtumwi Paulo ananena, kuti “cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zoŵaŵa pamodzi kufikira tsopano.”—koma osati kwanthaŵi yaitali. Anthu mamiliyoni amene ali ndi moyo pakalipano adzaona ‘kukonzedwanso kwa zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo mkamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire,’ kuphatikizapo kubwezeretsedwa kwa mtendere, ufulu, ndi chilungamo kumtundu wonse wa anthu.—Machitidwe 3:21.
Pomalizira Pake—Ufulu Weniweni
Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mudzasangalale ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu”? Yesu Kristu anati: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:31, 32) Kuphunzira komanso kumvera malamulo ndi ziphunzitso za Kristu ndiyo njira yopezera ufulu. Ngakhale tsopano zimenezi zimabweretsa ufulu pamlingo wina wake. Posachedwapa, mu ulamuliro wa Kristu Yesu zidzabweretsa ufulu weniweni. Njira yoyenera kutsata ndiyo kudziŵa “mawu” a Yesu mwa kuphunzira Baibulo. (Yohane 17:3) Monga Akristu oyambirira, yanjanani ndi mpingo wa ophunzira oona a Kristu. Mwa kuchita zimenezi, mungapindule ndi choonadi chomasula chimene Yehova akupereka lerolino kupyolera m’gulu lake.—Ahebri 10:24, 25.
Pamene ‘mukulindira vumbulutso la ana a Mulungu,’ muyenera kukulitsa chidaliro chimene mtumwi Paulo anali nacho mu chisamaliro ndi chichirikizo cha Kristu, ngakhale pamene mavuto ndi chisalungamo zikuoneka kukhala zosapiririka. Atakambirana za kuvumbulutsidwa kwa ana a Mulungu, Paulo anafunsa kuti: “Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?” (Aroma 8:35) Inde, kugwira mawu a Rousseau, Akristu a m’tsiku la Paulo anali adakali “paukapolo” chifukwa cha kuponderezedwa. Anali “kuphedwa dzuŵa lonse” monga “nkhosa zakupha.” (Aroma 8:36) Kodi zimenezi zinawafooketsa?
“Koma,” Paulo analemba motere, “m’zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda.” (Aroma 8:37) analaka mosasamala kanthu za zonse zimene Akristu oyambirira anapirira? Motani? “Ndakopeka mtima,” anatero poyankha, “kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:38, 39) Inunso ‘mungalake nsautso kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza’ zomwe mwina mukupirira pakalipano. Chikondi cha Mulungu chimatitsimikiza kuti posachedwapa—nthaŵi iliyonse kuyambira lero—‘tidzamasulidwa ku ukapolo [wonse] . . . ndi kuloŵa mu ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’
[Zithunzi patsamba 6]
“Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano”
[Chithunzi patsamba 7]
‘Cholengedwa chidzamasulidwa ku ukapolo ndi kuloŵa mu ufulu waulemerero wa ana a Mulungu’