Mzimu wa Yehova Umatsogolera Anthu Ake
“Mzimu wanu ndiwokoma; unditsogolere m’njira yolungama.”—SALMO 143:10, NW.
1, 2. Kodi nchiyani chimene chingapangitse atumiki okhulupirika a Yehova kupsinjika maganizo?
‘NDIRI wopsinjika maganizo kwambiri! Kodi ndingapeze kuti chitonthozo? Kodi Mulungu wandisiya?’ Kodi mumadzimva motero nthaŵi zina? Ngati mumatero, simuli nokha. Ngakhale kuti atumiki a Yehova okhulupirika amakhala m’paradaiso wauzimu wosefukira, nthaŵi zina amayang’anizana ndi mavuto otsendereza, mayesero, ndi ziyeso zimene zimagwera anthu onse.—1 Akorinto 10:13.
2 Mwinamwake muli ndi chiyeso chanthaŵi yaitali kapena chinthu china chokupsinjani maganizo kwambiri. Mungakhale omva chisoni ndi imfa ya wokondedwa ndipo mungadziwone kukhala wotayikiridwa kwambiri. Kapena mtima wanu ungavutike ndi kudwala kwa bwenzi lanu lokondedwa. Mikhalidwe yoteroyo ingakuchotsereni chimwemwe ndi mtendere ndipo mwinamwake ngakhale kuwopseza chikhulupiriro chanu. Kodi muyenera kuchitanji?
Pemphani Mzimu wa Mulungu
3. Ngati china chake chikukuchotserani mikhalidwe yonga mtendere ndi chimwemwe, kodi nchiyani chikakhala chanzeru kuchita?
3 Ngati china chake chikukuchotserani mtendere wanu, chimwemwe, kapena mkhalidwe wina uliwonse waumulungu, kukakhala kwanzeru kupempherera mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yake yogwira ntchito. Chifukwa ninji? Chifukwa mzimu wa Yehova umatulutsa zipatso zabwino zimene zimathandiza Mkristu kuyang’anizana ndi mavuto, mayesero ndi ziyeso. Pambuyo pakuchenjeza za “ntchito za thupi,” mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.”—Agalatiya 5:19-23.
4. Pamene muyang’anizana ndi mayesero ena kapena chiyeso, kodi nchifukwa ninji kukakhala koyenerera kutchula vutolo mpemphero lanu?
4 Chifukwa cha mtundu wa chiyeso chimene mwakumana nacho, mungazindikire kuti muli m’ngozi yakutaikiridwa chifatso, kapena kudzichepetsa mtima. Pamenepa khalani wotsimikizira mwakupemphera kwa Yehova Mulungu kaamba ka chipatso cha mzimu wa chifatso. Ngati mwayang’anizana ndi chiyeso, mumafunikira kwambiri chipatso cha kudziletsa. Ndithudi, kukakhala koyenerera kupempherera chithandizo chaumulungu m’kukaniza chiyeso, kulanditsidwa kwa Satana, ndi nzeru yofunikira kupirira chiyesocho.—Mateyu 6:13; Yakobo 1:5, 6.
5. Ngati mikhalidwe iri yovutitsa maganizo kotero kuti simungadziwe chipatso cha mzimu choti mupempherere, kodi mungachitenji?
5 Komabe, panthaŵi zina, mikhalidwe ingakhale yovutitsa maganizo kapena yozunguza mutu kwakuti simungadziŵe kuti ndi chipatso chiti cha mzimu chimene mufunikira. Ndithudi, chimwemwe, mtendere, chifatso, ndi mikhalidwe ina yonse yaumulungu ingadodometsedwe. Pamenepo tingachitenji? Bwanji osapempha Mulungu mzimu woyera weniweniwo kuti upangitse zipatso zofunikirazo kuwonjezeka mwa inu? Zipatso zofunikira zingakhale chikondi kapena chimwemwe kapena mtendere kapena kuphatikiza zipatso zonse za mzimu. Ndiponso pempherani kuti Mulungu akuthandizeni kutsatira chitsogozo cha mzimu wake, chifukwa amaugwiritsira ntchito kutsogolera anthu ake.
Yehova Ali Wofunitsitsa Kuthandiza
6. Kodi Yesu anakhomereza motani mwa ophunzira ake kufunikira kwa kupemphera mosalekeza?
6 Pamene ophunzira a Yesu Kristu anafuna malangizo pa pemphero, anawachichizanso kupempherera mzimu wa Mulungu. Choyamba Yesu anagwiritsira ntchito fanizo lowasonkhezera kupemphera mosalekeza. Iye anati: “Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu; popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo, ndipo ndiribe chompatsa; ndipo iyeyu wa mkatimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa? Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye ziri zonse azisoŵa.”—Luka 11:5-8.
7. Kodi tanthauzo la mawu a Yesu pa Luka 11:11-13 nlotani, ndipo nchitsimikiziro chotani chimene amatipatsa ponena za Mulungu ndi mzimu wake?
7 Yehova ali wofunitsitsa kuthandiza aliyense wa atumiki ake odzipatulira okhulupirika, ndipo amamvetsera zopempha zawo. Koma ngati munthu woteroyo ‘apitiriza kupempha,’ monga momwe Yesu anachichizira, zimenezi zimasonyeza chikhumbo cha mumtima ndipo ndichisonyezero cha chikhulupiriro. (Luka 11:9, 10) Kristu anawonjezera kuti: “Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m’malo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye?” (Luka 11:11-13) Komabe, ngati kholo lapansi lokhala loipa chifukwa cha uchimo wa cholowa, limapatsa zinthu zabwino mwana wake, ndithudi Atate wathu wakumwamba adzapitiriza kupereka mzimu wake woyera kwa aliyense wa atumiki ake okhulupirika amene adzaupempha modzichepetsa.
8. Kodi Salmo 143:10 limagwira ntchito motani kwa Davide, Yesu, ndi atumiki amakono a Mulungu?
8 Kuti tipindule ndi mzimu woyera wa Mulungu, tiyenera kukhala ofunitsitsa kutsatira chitsogozo chake monga momwe Davide anachitira. Iye anapemphera kuti: “Mundiphunzitse chokonda inu; popeza inu ndinu Mulungu wanga; mzimu wanu ndiwokoma; [unditsogolere m’njira yolungama, NW].” (Salmo 143:10) Davide, amene anathamangitsidwa ndi mfumu ya Israyeli Sauli, anafuna mzimu wa Mulungu kumtsogolera kotero kuti akatsimikizira njira yake kukhala yolungama. M’kupita kwanthaŵi Abyatara anabwera ndi efodi wa ansembe wogwiritsiridwa ntchito potsimikizira chifuno cha Yehova. Monga woimira wansembe wa Mulungu, Abyatara analangiza Davide za njira yakuyendamo kotero kuti asangalatse Yehova. (1 Samueli 22:17–23:12; 30:6-8) Mofanana ndi Davide, Yesu anatsogozedwa ndi mzimu wa Yehova, ndipo zimenezi zakhalanso zowona kwa atsatiri odzozedwa a Kristu monga gulu. Mu 1918-19, iwo analingaliridwa kukhala otaika ndi chitaganya cha anthu, ndipo adani awo achipembedzo anaganiza kuti akawawononga. Odzozedwa anapempherera njira yotulukira mumkhalidwe wawo wa kusagwira ntchito, ndipo mu 1919, Mulungu anayankha mapemphero awo, nawapulumutsa, nawayambitsanso utumiki wake. (Salmo 143:7-9) Ndithudi, mzimu wa Yehova panthaŵiyo unali kuthandiza ndi kutsogolera anthu ake, monga momwe ukuchitira lerolino.
Mmene Mzimu Umathandizira
9. (a) Kodi mzimu woyera umagwira ntchito motani monga “mthandizi”? (b) Kodi timadziŵa motani kuti mzimu woyera simunthu? (Wonani mawu amtsinde.)
9 Yesu Kristu anatcha mzimu woyera “mthandizi.” Mwachitsanzo, anauza otsatira ake kuti: “Ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu [mthandizi, NW], kuti akhale ndi inu kunthaŵi yonse, ndiye mzimu wa chowonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuwona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu.” Pakati pa zinthu zina, “mthandizi” ameneyo akakhala mphunzitsi, pakuti Kristu analonjeza kuti: “Koma [mthandiziyo, NW], mzimu woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.” Mzimuwo ukachitiranso umboni za Kristu, ndipo anatsimikiziritsa ophunzira ake kuti: “Kuyenera kwa inu kuti ndichoke ine. Pakuti ngati sindichoka, [mthandiziyo, NW] sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita, ndidzamtuma iye kwa inu.”—Yohane 14:16, 17, 26; 15:26; 16:7.a
10. Kodi ndimnjira zotani zimene mzimu woyera wakhalira mthandizi?
10 Kuchokera kumwamba, Yesu anatsanulira mzimu woyera wolonjezedwa pa otsatira ake pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E. (Machitidwe 1:4, 5; 2:1-11) Monga mthandizi, mzimu unawapatsa chidziŵitso chowonjezereka cha chifuno ndi cholinga cha Mulungu ndi kumasulira Mawu aulosi kwa iwo. (1 Akorinto 2:10-16; Akolose 1:9, 10; Ahebri 9:8-10) Mthandizi ameneyo anapatsanso mphamvu ophunzira a Yesu kukhala mboni m’dziko lonse lapansi. (Luka 24:49; Machitidwe 1:8; Aefeso 3:5, 6) Lerolino, mzimu woyera ungathandize Mkristu wodzipatulira kukula m’chidziŵitso ngati amagwiritsira ntchito zogaŵira zonse zauzimu zoperekedwa ndi Mulungu mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Mzimu wa Mulungu ungapereke chithandizo mwakugaŵira chilimbikitso ndi mphamvu zofunikira kuchitira umboni monga mmodzi wa atumiki a Yehova. (Mateyu 10:19, 20; Machitidwe 4:29-31) Komabe, mzimu woyera umathandizanso anthu a Mulungu m’njira zina.
“Zobuula Zosatheka Kuneneka”
11. Ngati chiyeso chikuwonekera kukhala chosalakika, kodi Mkristu ayenera kuchitanji?
11 Ngati Mkristu akuvutitsidwa ndi chiyeso chimene chiwonekera kukhala chosalakika, kodi ayenera kuchitanji? Eya, pemphererani mzimu woyera, ndipo uloleni uchite ntchito yake! “Momwemonso mzimu athandiza kufooka kwathu” anatero Paulo, “pakuti chimene tizipempha monga chiyenera sitidziŵa; koma mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo iye amene asanthula m’mitima adziŵa chimene achisamalira mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.”—Aroma 8:26, 27.
12, 13. (a) Kodi Aroma 8:26, 27 amagwira ntchito motani pamapemphero operekedwa makamaka m’mikhalidwe yoyesa? (b) Kodi Paulo ndi anzake anachitanji pamene anali pansi pa chitsenderezo chowopsa m’chigawo cha Asiya?
12 Awo oyera mtima amene mzimu wa Mulungu umawapempherera ali otsatira odzozedwa a Yesu, okhala ndi chiyembekezo cha kumwamba. Koma kaya muli ndi chiyembekezo cha kumwamba kapena chapansi, monga Mkristu mungathe kukhala ndi chithandizo cha mzimu woyera wa Mulungu. Nthaŵi zina Yehova amapereka yankho lachindunji ku mapemphero ena. Komabe, panthaŵi zina, mungakhale otsenderezeka kwambiri kwakuti simungathe kufotokoza zovuta zanu ndi mawu ndipo mungangochonderera kwa Yehova ndi zobuula zosaneneka. Kwenikweni, mwina simungadziŵe chofunikira koposa kwa inu ndipo mungapemphe chinthu chosayenera pokhapokha mutapempherera mzimu woyera. Mulungu amadziŵa kuti mumafuna kuti chifuniro chake chichitike, ndipo amazindikira zimene mumafunikira kwenikweni. Ndiponso, mwa mzimu wake woyera, anapangitsa mapemphero ambiri kulembedwa m’Mawu ake, ndipo ameneŵa amanena za mikhalidwe yoyesa. (2 Timoteo 3:16, 17; 2 Petro 1:21) Chifukwa chake, Yehova angawone malingaliro ena ofotokozedwa m’mapemphero ouziridwa oterowo kukhala monga mawu anu amene mungafune kutchula monga mmodzi wa atumiki ake, ndipo angayankhe mapempherowo mmalo mwanu.
13 Mwina Paulo ndi anzake sanadziŵe chimene anayenera kupempherera pamene anakumana ndi mazunzo m’chigawo cha Asiya. Pokhala ‘atathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yawo, koma okha anakhala nacho chitsutso cha imfa mwa iwo okha.’ Koma iwo anafuna mapembedzero a ena ndi kudalira mwa Mulungu, amene angadzutse akufa, ndipo anawapulumutsa. (2 Akorinto 1:8-11) Nkotonthoza chotani nanga kuti Yehova amamva ndi kuchitapo kanthu pa mapemphero a autumiki ake okhulupirika!
14. Kodi ndiubwino wotani umene ungakhalepo ngati Yehova alola chiyeso kupitiriza kwa kanthaŵi?
14 Anthu a Mulungu kaŵirikaŵiri amakumana ndi ziyeso monga gulu. Monga momwe tawonera poyambirirapo, anazunzidwa mkati mwa Nkhondo Yadziko I. Ngakhale kuti panthaŵiyo anali asanamvetsetse bwino lomwe kaimidwe kawo ndipo chotero sanadziŵe chimene anayenera kupempherera, Mawu a Yehova anali ndi mapemphero aulosi amene iye anawayankha kwa iwo. (Salmo 69, 102, 126; Yesaya, chaputala 12) Koma bwanji ngati Yehova walola chiyeso kupitirira kwa kanthaŵi? Zimenezi zingachitire umboni, zingasonkhezere ena kulandira chowonadi, ndipo zimapatsa Akristu mwaŵi wakusonyeza chikondi cha pa abale mwakupempherera ena kapena kuthandiza okhulupirira anzathu amene akuvutika. (Yohane 13:34, 35; 2 Akorinto 1:11) Kumbukirani kuti Yehova amatsogolera anthu ake ndi mzimu wake woyera, amachita zimene ziri zabwino kwa iwo, ndipo nthaŵi zonse amachita zinthu m’njira imene idzalemekeza ndi kuyeretsa dzina lake loyera.—Eksodo 9:16; Mateyu 6:9.
Musamvetse Chisoni Mzimu
15. Kodi Akristu angadalire pa mzimu wa Yehova kuwachitira chiyani?
15 Chotero, ngati muli mtumiki wa Yehova, pemphererani mzimu woyera mkati mwa mayesero ndi pa nthaŵi zina. Ndiyeno khalani wotsimikizira kutsatira chitsogozo chake, popeza Paulo analemba kuti: “Musamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa iye, kufikira tsiku la mawomboledwe.” (Aefeso 4:30) Mzimu wa Mulungu unali ndipo uli chisindikizo, kapena ‘chikole cha zimene zinali nkudza,’ kaamba ka Akristu odzozedwa okhulupirika—ndicho, moyo wakusafa kumwamba. (2 Akorinto 1:22; Aroma 8:15; 1 Akorinto 15:50-57; Chivumbulutso 2:10) Ponse paŵiri Akristu odzozedwa ndi awo okhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi angadalire pa mzimu wa Yehova kuwachitira zambiri. Ungawatsogolere kumoyo wa kukhulupirika ndi kuwathandiza kupeŵa ntchito za kuchimwa zimene zingawatayitse chivomerezo cha Mulungu, kutayikiridwa mzimu wake woyera, ndi kulephera kupeza moyo wosatha.—Agalatiya 5:19-21.
16, 17. Kodi Mkristu angamvetse chisoni motani mzimu?
16 Kodi ndimotani mmene Mkristu, kaya modziŵa kapena mosadziŵa, angamvetsere chisoni mzimu? Eya, Yehova amagwiritsira ntchito mzimu wake kukhazikitsa umodzi ndi kuika amuna oyenera mumpingo. Chifukwa chake, ngati wina mum’mpingo ang’ung’udza za kuikidwa kwa akulu, kufalitsa bodza lamkunkhuniza, ndi zina zotero, akakhala wosatsatira chitsogozo cha mzimu wa Mulungu wa mtendere ndi umodzi. Kwenikweni, akakhala akumvetsa chisoni mzimu.—1 Akorinto 1:10; 3:1-4, 16, 17; 1 Atesalonika 5:12, 13; Yuda 16.
17 Polembera Akristu ku Efeso, Paulo anawachenjeza za zizoloŵezi za bodza, mkwiyo wopitirira, kuba, malankhulidwe oipa, kukondwerera dama, chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake. Ngati Mkristu adzilola kudziphatika m’zinthu zotero, akakhala akupikisana ndi uphungu wa Baibulo wouziridwa ndi mzimu. (Aefeso 4:17-29; 5:1-5) Inde, ndipo kumlingo wakutiwakuti akakhala akumvetsa chisoni mzimu wa Mulungu.
18. Kodi chingachitike nchiyani kwa Mkristu aliyense amene ayamba kunyalanyaza uphungu wa Mawu a Mulungu ouziridwa ndi mzimu?
18 Kwenikweni, Mkristu aliyense amene ayamba kunyalanyaza uphungu wa Mawu a Yehova ouziridwa ndi mzimu akayamba kukulitsa kaimidwe kamaganizo kamene kakatulukira m’tchimo ladala ndi kutaikiridwa chiyanjo chaumulungu. Ngakhale kuti angakhale sakuchita tchimo tsopano, angakhale ali panjira imeneyo. Mkristu woteroyo wochita zosiyana ndi chitsogozo cha mzimu adzakhala akuumvetsa chisoni. Motero adzakhala akukana ndi kumvetsanso chisoni Yehova, Magwero a mzimu woyera. Wokonda Mulungu aliyense sangafune kutero!
Pitirizani Kupempherera Mzimu Woyera
19. Kodi nchifukwa ninji anthu a Yehova lerolino afunikira kwambiri mzimu wake?
19 Ngati muli mtumiki wa Yehova, pitirizani kupempherera mzimu woyera. Makamaka “m’masiku otsiriza” ano, okhala ndi nthaŵi zowawitsa zovuta kuchita nazo, Akristu afunikira chithandizo cha mzimu wa Mulungu. (2 Timoteo 3:1-5) Mdyerekezi ndi ziŵanda zake, ochotsedwa kumwamba ndipo tsopano ali m’mabwalo a dziko lapansi, ali aukali ndi gulu la Yehova. Chifukwa chake, tsopano koposa ndi kale lonse, anthu a Mulungu afunikira mzimu woyera kuwatsogolera, kapena kuwatsogoza, ndi kuwathandiza kupirira zovuta ndi chizunzo.—Chivumbulutso 12:7-12.
20, 21. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kutsatira chitsogozo cha Mawu, mzimu, ndi gulu la Yehova?
20 Sonyezani chiyamikiro nthaŵi zonse kaamba ka chithandizo chimene Yehova Mulungu amagaŵira mwa mzimu wake woyera. Tsatirani chitsogozo cha Mawu ake ouziridwa ndi mzimu, Baibulo. Gwirizanani kotheratu ndi gulu la Mulungu la padziko lapansi lotsogozedwa ndi mzimu. Musadzilole kutembenukira ku njira yosakhala yamalemba imene ikamvetsa chisoni mzimu woyera, pakuti zimenezi pomalizira zikachititsa kuti uchotsedwe ndipo motero kukhala m’ngozi yauzimu.—Salmo 51:11.
21 Kutsogozedwa ndi mzimu wa Yehova ndiyo njira yokha yomsangalatsira ndi kukhala ndi mtendere, ndi umoyo wachimwemwe. Kumbukiraninso, kuti Yesu anatcha mzimu woyera “mthandizi,” kapena “wotonthoza.” (Yohane 14:16, NW, mawu amtsinde) Mulungu amatonthoza Akristu ndi mzimu woyera, ndi kuwapatsa mphamvu kuyang’anizana ndi ziyeso. (2 Akorinto 1:3, 4) Mzimuwo umapatsa mphamvu anthu a Yehova yakulalikira mbiri yabwino ndi kuwathandiza kukumbukira mfundo za Malemba zofunika kupereka umboni wabwino. (Luka 12:11, 12; Yohane 14:25, 26; Machitidwe 1:4-8; 5:32) Mwapemphero ndi chitsogozo cha mzimu, Akristu angayang’anizane ndi ziyeso za chikhulupiriro ali ndi nzeru yakumwamba. Chifukwa chake, m’mikhalidwe yonse ya moyo amapitiriza kupempherera mzimu woyera wa Mulungu. Monga chotulukapo, mzimu wa Yehova umatsogolera anthu ake.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti mzimu woyera watchedwa “mthandizi” monga ngati kuti ndimunthu, uwo suli munthu, chifukwa mloŵa mmalo wa dzina Wachigiriki wosonya ku chinthu (womasuliridwa “iye”) wagwiritsiridwa ntchito pa mzimu. Aloŵa mmalo a dzina achikazi a Chihebri mofananamo amagwiritsiridwa ntchito kutchula nzeru monga munthu. (Miyambo 1:20-33; 8:1-36) Ndiponso, mzimu woyera “unatsanuliridwa,” zimene sizingachitidwe ndi munthu.—Machitidwe 2:33.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupempherera mzimu woyera wa Yehova?
◻ Kodi mzimu woyera ndimthandizi motani?
◻ Kodi zimatanthauza chiyani kumvetsa chisoni mzimu, ndipo kodi tingapewe motani kuchita motero?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupitiriza kupempherera mzimu woyera ndi kutsatira chitsogozo chake?
[Chithunzi patsamba 15]
Monga atate wachikondi amapatsa zinthu zabwino mwana wake, momwemo Yehova amapatsa mzimu woyera atumiki ake amene amaupempherera
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi mumadziŵa mmene mzimu wa Yehova umapembedzerera Akristu opemphera?