Mmene Mungaphunzitsire Chikumbumtima Chanu
“CHIKUMBUMTIMA choyera ndi msamiro wabwino koposa.” Mwambi wakalewu ukugogomezera mfundo yofunika kwambiri: Pamene tilabadira chikumbumtima chathu, timakhala ndi mtendere wamaganizo.
Komabe, si onse amene amasankha kutero. Adolf Hitler analengeza kuti anali pantchito yomasula anthu ku chinthu chonyazitsa, kapena chinyengo, chotchedwa chikumbumtima. Ulamuliro wake wankhanza umapereka chithunzi choopsa cha nkhanza yoipitsitsa imene anthu angakhale nayo ngati achita zinthu mosemphana ndi chikumbumtima chawo. Nkhanza zotero zimasonyezedwanso lerolino ndi anthu apandu achiwawa—awo amene amagona akazi mokakamiza ndi kupha anzawo mopanda chisoni. Ambiri amene amachita zotere ndi anyamata ang’onoang’ono. Buku lina lofotokoza zimenezi linali ndi kamutu kakang’ono kakuti Children Without a Conscience [Ana Opanda Chikumbumtima].
Ngakhale kuti anthu ambiri sangaganize nkomwe zochita upandu wachiwawa, ambiri sadera nkhaŵa za kuchita chisembwere, kunena bodza, kapena chinyengo. Kuzungulira dziko lonse lapansi, makhalidwe akuipiraipira. Ponena za mpatuko waukulu wakuchoka pakulambira koona, mtumwi Paulo analemba kuti Akristu ena adzagonja ku zisonkhezero za dziko nadzakhala “olochedwa m’chikumbumtima mwawo monga ndi chitsulo chamoto.” (1 Timoteo 4:2) Ukatangale wafika poipa kwambiri ‘m’masiku otsiriza ano.’ (2 Timoteo 3:1) Choncho, Akristu ayenera kuyesayesa zolimba kuti asungebe chikumbumtima chawo. Tingatero mwa kuchiphunzitsa ndi kuchikulitsa.
Maganizo, Mtima, ndi Chikumbumtima Chanu
Mtumwi Paulo anati: “Ndinena zoona mwa Kristu, sindinama ayi, chikumbumtima changa chichita umboni pamodzi ndi ine mwa Mzimu Woyera.” (Aroma 9:1) Choncho, chikumbumtima chingachitire umboni. Chingayang’anire makhalidwe ndipo chingawavomereze kapena kuwatsutsa. Nzeru yaikulu yakudziŵa chabwino ndi choipa inaikidwa mwa ife ndi Mlengi wathu. Komabe, chikumbumtima chathu chingathe kusinthidwa ndi kuphunzitsidwa. Motani? Mwakukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chochokera m’Mawu a Mulungu. “Koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro,” akutero mtumwi Paulo. (Aroma 12:2) Pamene mudzaza malingaliro a Mulungu ndi zofuna zake m’maganizo mwanu, chikumbumtima chanu chimayamba kugwira ntchito mwaumulungu.
Mboni za Yehova zathandiza anthu mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi ‘kukhala ndi chidziŵitso chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu.’ (Yohane 17:3) Kupyolera m’makonzedwe a phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, izo zimaphunzitsa anthu amaganizo abwino malamulo a Yehova Mulungu ponena za kugonana, zakumwa zoledzeretsa, ukwati, kuchita bizinesi, ndi nkhani zina zambiri.a (Miyambo 11:1; Marko 10:6-12; 1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 5:28-33) Kukhala ndi ‘chidziŵitso cholongosoka’ chimenechi ndi chiyambi chofunika pa kukulitsa chikumbumtima chaumulungu. (Afilipi 1:9 NW) Komabe, ngakhale Mkristu amene amalidziŵa bwino Baibulo ayenera kupitirizabe kudzaza maganizo ake ndi Mawu a Mulungu kuti chikumbumtima chake chikhalebe chathanzi.—Salmo 1:1-3.
Baibulo limagwirizanitsanso chikumbumtima ndi mtima wophiphiritsira, umene umaphatikizapo zikhumbo zathu ndi nkhaŵa zathu. (Aroma 2:15) Kuti chikumbumtima chigwire ntchito yake bwino, maganizo ndi mtima ziyenera kugwirira ntchito pamodzi mogwirizana. Izi zikutanthauza kuti kungokhala ndi chidziŵitso m’maganizo mwanu sikokwanira. Muyenera kusinthanso mtima wanu—zolingalira, zikhumbo, ndi zolakalaka zanu. Ndicho chifukwa chake buku la Miyambo limagwiritsira ntchito mawu monga “kulozetsa mtima wako,” “ulunjikitse mtima wako,” ndi “ika mtima wako.” (Miyambo 2:2; 23:19; 27:23, NW) Njira ina yochitira zimenezo ndiyo kusinkhasinkha ndi kuŵerenga Malemba. “Ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu,” limatero Salmo 77:12. Kusinkhasinkha kumatithandiza kuzindikira bwino malingaliro athu ndi zolinga zathu.
Mwachitsanzo, talingalirani kuti muli ndi chizoloŵezi choipa monga kumwerekera ndi fodya. Mofanana ndi anthu ambiri, inu mosakayikira konse mumadziŵa ngozi zake pathanzi lanu. Komabe, mosasamala kanthu za machenjezo ochokera kwa mabwenzi ndi a m’banja lanu, mukulephera kusiya mchitidwewu. Kodi kusinkhasinkha za uthenga wa m’Baibulo kungalimbitse motani chikumbumtima chanu pa nkhani imeneyi?
Mwachitsanzo, tayesani kusinkhasinkha za mawu a mtumwi Paulo opezeka pa 2 Akorinto 7:1: “Pokhala nawo tsono malonjezano ameneŵa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuopa Mulungu.” Pezani tanthauzo la mawu amenewa. Dzifunseni kuti, ‘Kodi “malonjezano” amene Paulo akunenawa nchiyani?’ Mutaŵerenga nkhani yonseyo, mudzapeza kuti mavesi oyambirira akunena motere: “‘“Tulukani pakati pawo, ndipo patukani,” ati Ambuye, “ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka”’; ‘“Ndipo Ine ndidzalandira inu.”’ ‘“Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa ine ana aamuna ndi aakazi,” anena Ambuye Wamphamvuyonse.’”—2 Akorinto 6:17, 18.
Pempho la Paulo lakuti ‘tidzikonzere tokha kuleka chodetsa,’ tsopano mphamvu yake yawonjezereka! Monga chotisonkhezera kuchita zimenezo, Mulungu akulonjeza ‘kutilandira,’ kutiika m’chisamaliro chake. ‘Kodi ndingakhale ndi ubwenzi wathithithi ndi iye—wofanana ndi wa mwana wamwamuna kapena wamkazi ndi atate ake?’ mungadzifunse motero. Kodi lingaliro ‘lolandiridwa’ kapena lokondedwa ndi Mulungu wanzeru ndi wachikondi nlosasangalatsa? Ngati lingaliro limenelo likuoneka lachilendo kwa inu, yang’anirani mmene atate achikondi amasonyezera chikondi ndi kuyanjana ndi ana awo. Tsopano tangolingalirani za mgwirizano wotero pakati pa inuyo ndi Yehova! Pamene musinkhasinkha zimenezi, mpamenenso chikhumbo chokhala ndi unansi umenewo chimakula.
Koma dziŵani izi: Kuyandikana ndi Mulungu nkotheka kokha ngati ‘simukhudza kanthu kosakonzeka.’ Dzifunseni kuti: ‘Kodi kumwerekera ndi fodya sikuli m’gulu la “zinthu zosakonzeka,”(NW) zimene Mulungu amadana nazo? Kodi kuchita zimenezi ndiko “chodetsa . . . thupi” ndi kuika thanzi langa pangozi zosiyanasiyana? Popeza kuti Yehova ndi Mulungu wangwiro, kapena kuti “woyera,” kodi angavomereze kudzidetsa dala kotereku?’ (1 Petro 1:15, 16) Onani kuti Paulo akuchenjezanso za ‘chodetsa cha mzimu’ kapena kuti zikhoterero za maganizo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi kumwerekera kumeneku kumalamulira maganizo anga? Kodi ndidzachita zonse zotheka kungoti ndikhutiritse chikhumbo changa, mwinamwake ndi kuika pangozi thanzi langa, banja langa, inde ngakhale unansi wanga ndi Mulungu? Kodi ndalola kumwerekera ndi fodya kuwononga moyo wanga pamlingo wotani?’ Mutaganizira za mafunso opweteka m’maganizowa mungalimbe mtima ndi kusiya mchitidwewo!
Inde, mungafunikire chithandizo ndi chichirikizo cha ena kuti muleke fodya. Komabe, kusinkhasinkha za malangizo opezeka m’Baibulo kungathandize kwambiri kuphunzitsa ndi kulimbitsa chikumbumtima chanu kuti mudzimasule ku chizoloŵezichi.
Pamene Tichita Choipa
Mosasamala kanthu zakuyesayesa kwathu kuchita chimene chili chabwino, nthaŵi zina zikhoterero zathu zauchimo zingatigonjetse ndipo tingachimwe. Pamenepo chikumbumtima chathu chidzativutitsa, koma tingayese kuchinyalanyaza. Kapena tingalefuke kwambiri mpaka kufuna kusiya kudzipereka kwathu m’kutumikira Mulungu. Komabe, talingalirani za Mfumu Davide. Pamene anachita chigololo ndi Bateseba, chikumbumtima chake chinamuvutitsa. Iye akufotokoza nsautso imene anapeza motere: “Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; Uŵisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.” (Salmo 32:4) Zopweteka? Inde! Komatu chisoni chaumulungu chotere chinapangitsa Davide kuti alape ndi kupezanso chiyanjo cha Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 7:10.) Kuchonderera kwa Davide kuti akhululukidwe kumapereka umboni waukulu wosonyeza kulapa kwake kochokera pansi pa mtima. Popeza kuti analabadira chikumbumtima chake, Davide anathandizidwa kuti asinthe ndipo pomalizira pake anapezanso chimwemwe.—Salmo 51.
Zofananazo zingachitike lerolino. Ena anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kumbuyoku koma anasiya atazindikira kuti zochita zawo zinali zosemphana ndi miyezo yapamwamba ya Mulungu. Mwinamwake ankakhala pamodzi ndi mwamuna kapena mkazi amene sanakwatirane naye kapena anali akapolo a zizoloŵezi zoipa. Chikumbumtima chawo chinawapweteka!
Ngati muli m’mkhalidwe woterowo, lingalirani za mawu a mtumwi Petro patsiku la Pentekoste. Pamene anavumbula machimo a Ayuda anzake, iwo “analaswa mtima.” Iwo sananyozere, koma anamvera uphungu wa Petro ndipo analapa napeza chiyanjo cha Mulungu. (Machitidwe 2:37-41) Inunso mungachite chimodzimodzi! M’malo mosiya choonadi kaamba kakuti chikumbumtima chanu chikukupwetekani, chikumbumtima chanu chikusonkhezereni ‘kulapa ndi kubwerera.’ (Machitidwe 3:19) Mwa kutsimikiza mtima ndi khama, mungapange masinthidwe oyenera ndi kupezanso chiyanjo cha Mulungu.
“Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino”
Kaya mwayamba kumene kuphunzira za makhalidwe a Yehova kapena mwakhala zaka zambiri ndipo ndinu Mkristu wokhwima m’maganizo, uphungu wa Petro wotsatirawu ngwofunika: ‘Khalani ndi chikumbumtima chabwino.’ (1 Petro 3:16) Ndi chinthu chofunika, si mtolo ayi. Chiphunzitseni mwakudzaza maganizo ndi mtima wanu ndi nzeru zopezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Labadirani pamene chikumbumtima chanu chikuchenjezani. Sangalalani ndi mtendere wa m’maganizo umene umadza chifukwa chomvera chikumbumtima.
Zoonadi, kuphunzitsa ndi kusintha chikumbumtima chanu nkovuta. Komabe, mungapemphere kwa Yehova Mulungu kuti akuthandizeni. Ndi chithandizo chake, mudzakhoza kutumikira Mulungu “m’chikumbumtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga.”—1 Timoteo 1:5.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, khalani omasuka kufika ku mpingo wapafupi ndi kwanuko wa Mboni za Yehova kapena lemberani ofalitsa magazini ano.
[Chithunzi patsamba 6]
Kuŵerenga Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha kumathandiza kuphunzitsa chikumbumtima chathu