Chipiriro Chimene Chimapeza Chilakiko
‘Pakuti chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.’—AHEBRI 10:36.
1. Kodi nchifukwa ninji chipiriro chiri chofunika kwa aliyense amene akutumikira Yehova Mulungu lerolino?
DZIKO lonseli likugona m’mphamvu ya mulungu wachinyengo. Wolamulira wake wosawoneka, Satana Mdyerekezi, akusumika zoyesayesa zake zonse pakutsutsa Yehova ndi kulimbana motsutsa kulemekezedwa kwa uchifumu wa chilengedwe chonse wa Yehova woimiridwa ndi Ufumu Waumesiya. Ichi chimakupanga kukhala kosatheka kuti aliyense amene amadzipereka kwa Mulungu ndi kukhala ku mbali Yake m’nkhani ya ufumu wake apeŵe kutsutsidwa kopitirizabe ndi dziko lino. (Yohane 15:18-20; 1 Yohane 5:19) Chifukwa chake, aliyense wa ife ayenera kudzikonzekeretsa kupirira kufikira dzikoli litagonjetsedwa kotheratu pa Armagedo. Kuti tikhale pakati pa olakika a Mulungu amene apambana dziko ndi chikhulupiriro chawo ndi umphumphu, tiyenera kunonomera mpaka mapeto. (1 Yohane 5:4) Kodi tingachite motani chimenechi?
2, 3. Kodi ndimotani mmene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu aliri zitsanzo zazikulu koposa za chipiriro?
2 Choyamba, tingapeze chilimbikitso ku zitsanzo zapadera ziŵiri za chipiriro. Kodi iwo ndani? Mmodzi ndi Yesu Kristu, ‘wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse,’ amene wapirira mokhulupirika muutumiki wa Mulungu chiyambire pamene analengedwa kalekale panthaŵi yosadziŵika. Mwakuumirira kwake kutumikira Mulungu mokhulupirika, Yesu anakhala chitsanzo kwa zolengedwa zonse zaluntha zimene zinalengedwa pambuyo pake kumwamba ndi padziko lapansi. (Akolose 1:15, 16) Komabe, chitsanzo chachikulu koposa cha chipiriro ali Yehova Mulungu, amene wapirira kwanthaŵi yaitali chipanduko chotsutsa uchifumu wake wachilengedwe chonse ndipo adzapitirizabe kuchita tero kufikira pamene adzachitapo kanthu kuthetseratu nkhani ya uchifumu.
3 Yehova wapirira mwa njira yopereka chitsanzo m’nkhani zoloŵetsamo ulemu wake ndi malingaliro ake aumwini. Iye wagwira mtima pamene ayang’anizana ndi kuputidwa kwakukulu ndipo wadziletsa kusachitapo kanthu motsutsana ndi amene amamtonza—kuphatikizapo Satana Mdyerekezi. Tikuyamikira chipiriro cha Mulungu ndi chifundo chake. Popanda zimenezi, sitikanasangalala ndi moyo ngakhale waufupi wokha. Ndithudi, Yehova Mulungu wadzisonyeza kukhala wosayerekezereka m’chipiriro chake.
4, 5. (a) Kodi ndimotani mmene fanizo la Paulo la woumba mbiya limasonyezera chipiriro cha Mulungu ndi chifundo chake? (b) Kodi ndimotani mmene chifundo cha Mulungu sichidzapitira pachabe?
4 Mtumwi Paulo akuloza ponse paŵiri ku chipiriro ndi chifundo cha Mulungu pamene akunena kuti: ‘Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi? Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuwonetsa mkwiyo wake, ndi kudziŵitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko? ndikuti iye akadziŵitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okha okha, komanso a mwa anthu amitundu?’—Aroma 9:21-24.
5 Monga momwe mawuwa akusonyezera, mkati mwa nyengo ino ya chipiriro chake, Yehova akupitirizabe ndi cholinga chake chaulemerero ndi kusonyeza chifundo pa zotengera zinazake zaumunthu. Iye akukonzekeretsa zotengera zimenezi kaamba ka ulemerero wosatha ndipo motero akulepheretsa zolinga zoipa za mdani wake wamkulu, Satana Mdyerekezi, ndi magulu onse a Satana. Sianthu onse amene akhala zotengera za mkwiyo, ofunikira chiwonongeko. Chimenechi chimamveketsa bwino chipiriro choleza mtima cha Mulungu Wamphamvuyonse. Chifundo chake sichidzapita pachabe. Chidzatulukapo (1) banja laulemerero la Ufumu kumwamba pansi pa Mwana wokondedwa wa Yehova, Yesu Kristu, ndi (2) fuko la anthu lochiritsidwa ndi langwiro pa dziko lapansi laparadaiso, onse olandira moyo wosatha.
Kupirira Kufikira Mapeto
6. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu sangapeŵe chiyeso cha chipiriro? (b) Kodi liwu Lachigiriki lotembenuzidwa ‘chipiriro’ kaŵirikaŵiri limapereka lingaliro lotani?
6 Pokhala ndi chiyembekezo chabwino koposa choterocho patsogolo, mawu a Yesu otonthoza otsatirawa ayenera kukhala m’malingaliro mwathu nthaŵi zonse: ‘Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumuka.’ (Mateyu 24:13) Kuli kofunika kuyamba bwinobwino pa njira yakukhala wophunzira Wachikristu. Koma chimene chiri kanthu kwenikweni ndimmene timapiririra, mmene timamalizira bwino njirayo. Mtumwi Paulo anagogomezera chimenechi pamene ananena kuti: ‘Pakuti chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.’ (Ahebri 10:36) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa ‘chipiriro’ panopa ndilo hy·po·mo·neʹ. Kaŵirikaŵiri liwuli limapereka lingaliro la kulimbika mtima, kuchirimika, kapena chipiriro choleza mtima chimene sichimataya chiyembekezo poyang’anizana ndi zopinga, mazunzo, mayesero, ndi ziyeso. Ngati tikufuna kupeza chipulumutso pomalizira pake, tiyenera kuchilandira chiyeso cha chipiriro monga mbali ya kukonzekera kofunika kaamba ka chipulumutso chimenecho.
7. Kodi nchinyengo chotani chimene tiyenera kupeŵa, ndipo nchitsanzo chayani chimene chidzatithandiza kupirira?
7 Sitiyenera kudzinyenga ndi lingaliro lodzikondweretsa tokha lakuti tikhoza kuchilaka chiyeso mofulumira. Kuti nkhani za ufumu wa chilengedwe chonse ndi umphumphu wa munthu ziyankhidwe motsimikizirika, Yehova sanachite mosiyako. Iye wapirira zinthu zosakondweretsa ngakhale kuti akanazichotsapo mwakamphindi. Yesu Kristu nayenso anali chitsanzo cha chipiriro. (1 Petro 2:21; yerekezerani ndi Aroma 15:3-5.) Pokhala ndi zitsanzo zabwino zimenezi, ndithudi nafenso timakhala ofunitsitsa kupirira kufikira mapeto.—Ahebri 12:2, 3.
Chiyeneretso Chofunikira
8. Kodi ndimkhalidwe wotani umene tonsefe timaufunikira umene mtumwi Paulo anausonyeza?
8 Palibe mtumiki wa Mulungu, ngakhale m’nthaŵi zakale, amene sanafunikire kutsimikizira umphumphu wake mwa chipiriro. Anthu otchuka kwambiri a m’mbiri ya Baibulo omwe anakhalabe okhulupirika kufikira imfa ndipo anayeneretsedwa kulandira moyo wosatha kumwamba anafunikira kutsimikizira kuchirimika kwawo. Mwachitsanzo, yemwe anali Mfarisi, Saulo wa ku Tariso, anati kwa Akorinto: ‘Sindipereŵera ndi atumwi oposatu m’kanthu konse, ndingakhale ndiri chabe. Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m’chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.’ (2 Akorinto 12:11, 12) Mosasamala kanthu za kuvuta kwa ntchitoyo, Paulo analemekeza kwambiri uminisitala wake kwakuti anapirira zambiri ndipo anayesayesa mwakhama kusabweretsa chitonzo chirichonse.—2 Akorinto 6:3, 4, 9.
9. (a) Kodi ndimotani mmene otsalira odzozedwa asonyezera chipiriro, ndipo ndi chotulukapo chotani? (b) Kodi nchiyani chimene chimatumikira monga chotisonkhezera kuti tipitirizebe mokhulupirika muutumiki waumulungu?
9 M’masiku amakono, Akristu odzozedwa omwe anali kutumikira Mulungu nkhondo yadziko yoyamba isanachitike anadziŵa kuti 1914 ikazindikiritsa mapeto a Nthaŵi za Akunja, ndipo ambiri a iwo anayembekezera kulandira mphotho yawo yakumwamba m’chaka chosaiŵalika chimenecho. Koma chimenechi sichinachitike. Monga momwe zenizeni zikusonyezera tsopano, iwo anali adakali ndi zaka makumi owonjezeredwa kwa iwo. Mkati mwa nyengo yotalikitsidwa yosayembekezeredwa imeneyi ya moyo wawo wapadziko lapansi, iwo anayengedwa ndi Yehova Mulungu. (Zekariya 13:9; Malaki 3:2, 3) Chipiriro chopitirizabe chinawadzetsera zabwino. Monga atumiki a Yehova, iwo anasangalala potchedwa anthu a dzina lake. (Yesaya 43:10-12; Machitidwe 15:14) Lerolino, pokhala atapyola nkhondo zadziko ziŵiri ndi nkhondo zazing’ono zosaŵerengeka, amasangalala kuthandizidwa m’kufalitsidwa kwa mbiri yabwino ndi khamu lalikulu lomakula la nkhosa zina, tsopano lofika chiŵerengero choposa mamiliyoni anayi. Paradaiso wauzimu amene amasangalala naye wafutukukira padziko lonse, ngakhale ku zisumbu zapanyanja zakutali kwenikweni. Chiyanjo chimenechi, chimene tikuyamikira mowonjezerekawonjezereka pamene tikukhalabe ndi moyo, chatumikira monga chotisonkhezera kupitirizabe mokhulupirika muutumiki waumulungu kufikira pamene chifuniro ndi cholinga cha Yehova zikwaniritsidwa kotheratu.
10. Kuti pasakhale kufooka kulikonse mwa ife, kodi nchiyani chimene chimafunikira nthaŵi zonse?
10 Popeza kuti mphotho yathu imadalira pa kuchirimika kwathu, nthaŵi zonse timafunikira kufulumizidwa pankhani yofunika imeneyi. (1 Akorinto 15:58; Akolose 1:23) Kuti pasakhale kufooka pakati pa anthu a Yehova, tiyenera kumalimbikitsidwa nthaŵi zonse kuti tigwiritse chowonadi ndi mwaŵi wamtengo wapatali wakuchifalitsa, monga momwe mipingo yopangidwa chatsopano inaliri m’zaka za zana loyamba mwa maulendo obwereza opangidwa ndi Paulo ndi Barnaba. (Machitidwe 14:21, 22) Lolani kuti chikhale cholinga chathu chotsimikiza mtima chakuti, monga momwe ananenera mtumwi Yohane, chowonadi chidzakhalabe mwa ife, ‘ndipo chidzakhala ndi ife ku nthaŵi yosatha.’—2 Yohane 2.
Kuyembekezera ndi Chipiriro Chosagwedera
11. Kodi nchiyani chimene chikuwonekera kukhala kachitidwe ka Mulungu kulinga kwa anthu ake, ndipo kodi ichi chinasonyezedwa motani m’nkhani ya Yosefe?
11 Zimatenga nthaŵi kuti chiyeso chotigwera chilakidwe. (Yakobo 1:2-4) Kuti Yembekeza! Yembekeza! Yembekeza! kukuwoneka kuti ndiko kunali kachitidwe ka Mulungu kwa atumiki ake akale pamene cholinga chawo cha kupitiriza m’chikhulupiriro chinayesedwa. Koma yembekeza ameneyo, pomalizira pake, nthaŵi zonse anakhaladi mphotho kwa atumiki okhulupirika amenewo. Mwachitsanzo, Yosefe, anayembekezera kwa zaka 13 monga kapolo ndi mkaidi, koma chokumana nachocho chinayenga umunthu wake.—Salmo 105:17-19.
12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene Abrahamu analiri chitsanzo cha chipiriro chokhulupirika? (b) Kodi ndimwanjira yotani imene chikhulupiriro ndi chipiriro cha Abrahamu zimasonyezedwera kukhala chitsanzo kwa ife?
12 Abrahamu anali kale ndi zaka 75 pamene Mulungu anamuitana kutuluka mu Uri wa kwa Akaldayo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. Iye anali wazaka pafupifupi 125 pamene analandira chitsimikizo cha lumbiro la lonjezo la Mulungu—chimene chinachitika mwamsanga Abrahamu atasonyeza nyonga ya chikhulupiriro chake mwakufika pamlingo wakupereka nsembe mwana wake wokondedwa, Isake, nangoimitsidwa pamene mngelo wa Yehova analetsa dzanja lake ndi kutsekereza nsembeyo. (Genesis 22:1-18) Zaka makumi asanu zinali nthaŵi yaitali kwa Abrahamu kuyembekezera monga wapaulendo m’dziko lachilendo, koma iye anayembekezerabe kwa zaka zina 50 kufikira pamene anamwalira ali ndi zaka zakubadwa 175. M’nthaŵi yonseyo, Abrahamu anali mboni yokhulupirika ndi mneneri wa Yehova Mulungu.—Salmo 105:9-15.
13 Chikhulupiriro ndi chipiriro za Abrahamu zikuperekedwa monga chitsanzo kwa atumiki onse a Mulungu amene akufuna kulandira madalitso olonjezedwa kupyolera mwa Yesu Kristu, Mbewu ya Abrahamu. (Ahebri 11:8-10, 17-19) Ponena za iye, timaŵerenga pa Ahebri 6:11-15 kuti: ‘Koma tikhumba kuti yense wa inu awonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima. Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa iye yekha, nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.’
14. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza kuti chiyeso cha chipiriro chiri chosatha ndipo mphotho yake njogwiritsa mwala?
14 Otsalira odzozedwa awona kale zaka 77 zikupita kuchokera pamapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914, pamene ena a iwo anayembekezera kuti mpingo wowona Wachikristu udzapatsidwa ulemerero kumwamba. Utali umene otsalirawo adzayenera kuyembekezerabe sitikuudziŵa. Pamenepo kodi tiyenera kugwedezeka ndi kuganiza kuti kuyembekezako kuli kosatha ndikuti mphothoyo njogwiritsa mwala? Ayi! Kutero sikukakweza uchifumu wa Mulungu kapena kulemekeza dzina lake. Iye sakalungamitsidwa pamaso pa dziko potipatsa chilakiko ndi mphotho yotulukapo ya moyo wosatha. Mosasamala kanthu za utali wa nthaŵi, otsalirawo, pamodzi ndi anzawo onga nkhosa okhulupirika, ali otsimikiza mtima kuyembekezera pa Yehova kuti achitepo kanthu panthaŵi yake. Posonyeza chipiriro chopereka chitsanzo choterocho, iwo amatsanzira njira ya Abrahamu.—Aroma 8:23-25.
15. (a) Kodi mfuu yathu ndiyotani, ndipo kodi Mulungu watiwombola mwachilakiko kupyola m’zokumana nazo zotani? (b) Kodi nchisonkhezero chotani cha Paulo chimene chikukhalabe choyenerera m’tsiku lathu?
15 Choncho, mfuu yathu ndiyo, chipiriro chosagwedera m’kuchita chifuniro cha Mulungu. (Aroma 2:6, 7) M’nthaŵi zapita, iye watichirikiza m’mavuto owopsa, kuphatikizapo kuponyedwa m’ndende ndi m’misasa yachibalo, ndipo iye watiwonjola mwachilakiko ndi ulemerero kaamba ka dzina lake ndi chifuniro chake.a M’nthaŵi yotsalabe ya kumalizidwa kwa chiyeso chathu, Yehova adzapitirizabe kuchita chimodzimodzi. Chilimbikitso cha Paulo chikhalabe choyenerera m’tsiku lathu: “Popeza kuti mufunikira kuleza mtima ndi chipiriro, kuti muchite ndi kukwaniritsa chifuniro cha Mulungu, ndipo motero kulandira ndi kupeza chisangalalo ndi kukondwa nacho mokwanira cholonjezedwacho.”—Ahebri 10:36, The Amplified Bible; Aroma 8:37.
16. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuwona kudzipereka kwathu kwa Yehova m’njira yochepa kapena yosiyako?
16 Malinga ngati Yehova ali ndi ntchito yoti tichite m’dziko lino loipa, pamenepo, potsatira chitsanzo cha Yesu, tifuna kudziloŵetsa m’ntchito imeneyo kufikira itamalizidwa. (Yohane 17:4) Kudzipereka kwathu kwa Yehova sikunali kwakuti tidzamtumikira kokha kwa kanthaŵi kochepa ndiyeno Armagedo idzabwera. Kudzipereka kwathu kunali kosatha. Ntchito ya Mulungu kwa ife siidzathera pa nkhondo ya Armagedo. Komabe, ndikokha pambuyo pakuti taikwaniritsa ntchito imene iyenera kumalizidwa Armagedo isanakanthe ndipamene tidzawona zinthu zazikulu zobwera pambuyo pa nkhondo yaikulu imeneyo. Ndiyeno, kuwonjezera pa mwaŵi wosangalatsa wa kupitirizabe kuchita ntchito yake, tidzafupidwa ndi madalitso oyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali amene anawalonjeza.—Aroma 8:32.
Kukonda Mulungu Kumatithandiza Kupirira
17, 18. (a) M’nthaŵi zovuta, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupirira tikukhala ndi chivomerezo cha Mulungu? (b) Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupeza chilakiko, ndipo kodi nchiyani chimene sitimanena pa nthaŵi imene yatsalako?
17 Mwinamwake, pamene nthaŵi zikhala zovuta, tingafunse kuti: ‘Kodi tingapirirebe motani?’ Yankho? Mwakumkonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, maganizo, moyo ndi nyonga. ‘Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza. Chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthaŵi zonse.’ (1 Akorinto 13:4, 7, 8) Tiyenera kupirira chifukwa cha kukonda Mulungu, apo phuluzi chipiriro chathu chidzakhala chabe. Koma ngati tilimbika m’zovuta chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Yehova, pamenepo chipiriro chathu chimazamitsa chikondi chathu kwa iye. Kukonda Mulungu, Atate wake, kunakhozetsa Yesu kupirira. (Yohane 14:30, 31; Ahebri 12:2) Ngati chisonkhezero chathu chenicheni ndicho kukonda Mulungu, Atate wathu, kodi nchiyani chimene tingalephere kupirira?
18 Ndichikondi chathu chosagwedera kwa Yehova Mulungu chimene chatikhozetsa kukhalabe olilaka dziko m’nthaŵi ino yovuta kwenikweni yopereka chiyeso. Ndipo Yehova, kupyolera mwa Yesu Kristu, adzapitirizabe kutipatsa chithandizo chimene timachifunikira mosasamala kanthu za utali umene dongosolo la zinthu lakaleli lidzaloledwa kukhalapobe. (1 Petro 5:10) Ndithudi, sitikulosera utali wa nthaŵi imene yatsalako, ndipo sitikukhazikitsa deti lirilonse. Timasiya zimenezo kwa Wosunga Nthaŵi Wamkulu, Yehova Mulungu.—Salmo 31:15.
19, 20. (a) Kodi ndimotani mmene tiyenera kuwonera tsiku lirilonse lomapita limene talipirira? (b) Kodi ndikupusa kotani kumene tifuna kukupeŵa, ndipo chifukwa ninji?
19 Komabe, mbadwo umene unanenedweratu kuti udzawona ndi kukumana ndi “mapeto a dongosolo la zinthu” (NW) tsopano wakalamba m’zaka. (Mateyu 24:3, 32-35) Choncho tiyeni tisaiŵale konse kuti tsiku lirilonse limene talipirira liri tsiku limodzi limene lachotsedwa ku nthaŵi ya Satana ndi ziŵanda zake yakuipitsa chilengedwe mwakukhalapo kwawo kwenikweniko ndiponso nditsiku limodzi lotiyandikiritsa ku nthaŵi imene Yehova sadzapiriranso kukhalapo kwa ‘zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko.’ (Aroma 9:22) Posachedwapa, pamene kuleza mtima kwa Yehova kufika kumapeto, iye adzasanulira mkwiyo wake pa amuna ndi akazi osapembedza. Motero, iye adzasonyeza kusakondwera kwake kwaumulungu ndi njira yawo yochitiramo zinthu, ngakhale kuti iye anawalola kupitirizabe kwa nyengo yonseyi ya nthaŵi.
20 Kukakhala kupusa kwenikweni ngati ife tileka zoyesayesa zathu zachikondi zakupeza mphotho yolemekezeka imene yaperekedwa kwa ife kupyolera mwa Yesu Kristu. Mmalo mwake, ndife otsimikiza mtima kupitirizabe mokhulupirika monga Mboni za Yehova m’nthaŵi ino yofunika kwambiri pamene Yehova ali pafupi kudzilemekeza monga Mfumu Yachilengedwe Chonse.
[Mawu a M’munsi]
a Mwachitsanzo, Christine Elizabeth King analemba kuti: “Boma [la Chinazi] linalephera kokha kwa Mboni, poti ngakhale kuti anazipha zikwizikwi, ntchitoyo inapitirizabe ndipo mu May 1945 gulu la Mboni za Yehova lidalipobe, pamene kuli kwakuti National Socialism panalibenso. Ziŵerengero za Mboni zinawonjezereka ndipo sizinalolere molakwa. Gululo linakhala ndi ofera chikhulupiriro ochuluka ndipo linamenyanso mwachipambano nkhondo ya Yehova Mulungu.”—The Nazi State and the New Religions: Five Case Studies in Non-Conformity, tsamba 193.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitingapeŵe kuyesedwa kwa chipiriro chathu?
◻ Kodi nchinyengo chotani chimene tifuna kupeŵa?
◻ Kuti tipeŵe kufooka kulikonse mwa ife, kodi tifunikira chiyani?
◻ Kodi mfuu yathu njotani?
◻ M’nthaŵi zovuta, kodi nchiyani chimene chidzatithandiza?
[Chithunzi patsamba 11]
Anthu a Mulungu, monga Mboni izi mu Port of Spain, Trinidad, nthaŵi zonse akhala ofunitsitsa kuyembekezera pa Yehova