Perekani Chilengezo Chapoyera cha Chipulumutso
“Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumuka.”—AROMA 10:13.
1. M’mbiri yonse, kodi kwaperekedwa machenjezo otani?
MBIRI imasimba za ‘masiku a Yehova’ angapo. Chigumula cha m’tsiku la Nowa, kufafanizidwa kwa Sodomu ndi Gomora, ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 607 B.C.E. ndi 70 C.E. anali masiku aakulu ndiponso oopsa a Yehova. Anali masiku opereka chiweruzo pa awo amene anapandukira Yehova. (Malaki 4:5; Luka 21:22) M’masiku amenewo, ambiri anafa chifukwa cha makhalidwe awo oipa. Koma ena anapulumuka. Yehova anachititsa kuti machenjezo aperekedwe, kudziŵitsa oipa za tsoka loyandikiralo ndi kupereka mpata kwa oona mtima kuti apeze chipulumutso.
2, 3. (a) Kodi ndi chenjezo laulosi lotani limene linagwidwa mawu pa Pentekoste? (b) Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., kodi nchiyani chinafunikira poitana pa dzina la Yehova?
2 Kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E. kuli chitsanzo chabwino kwambiri cha zimenezi. Poneneratu za chochitika chimenecho zaka pafupifupi 900 pasadakhale, mneneri Yoweli analemba kuti: “Ndidzaonetsa zodabwiza kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu loopsa.” Kodi munthu akanapulumuka motani panthaŵi yoopsa imeneyi? Yoweli analemba mouziridwa kuti: “Kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m’phiri la Ziyoni ndi m’Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.”—Yoweli 2:30-32.
3 Pa Pentekoste wa 33 C.E., mtumwi Petro analankhula kwa khamu la Ayuda ndi otembenukira kuchiyuda m’Yerusalemu ndipo anagwira mawu ulosi wa Yoweli, kusonyeza kuti omvetsera ake anayenera kuyembekezera kukwaniritsidwa kwa ulosiwo m’tsiku lake: “Ndidzapatsa zodabwitsa m’thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wautsi; dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye [“Yehova,” NW], lalikulu ndi loonekera; ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumutsidwa.” (Machitidwe 2:16-21) Khamu lonse la anthu amene anali kumvetsera Petro anali m’Chilamulo cha Mose, motero dzina la Yehova anali kulidziŵa. Petro anafotokoza kuti, nchifukwa chake kuitana pa dzina la Yehova kunali kudzaphatikizapo zinanso zambiri. Mosakayika, zimenezi zinaphatikizapo kubatizidwa m’dzina la Yesu, munthu amene anaphedwa, kenako kuukitsidwira kumoyo wosakhoza kufa wakumwamba.—Machitidwe 2:37, 38.
4. Kodi Akristu anafalitsa uthenga wotani kumaiko akutali?
4 Kuyambira pa Pentekoste kumka mtsogolo, Akristu anafalitsa mawu onena za Yesu woukitsidwayo. (1 Akorinto 1:23) Iwo anaphunzitsa kuti anthu akhoza kutengedwa kukhala ana auzimu a Yehova Mulungu ndi kukhala mbali ya “Israyeli [watsopano] wa Mulungu,” mtundu wauzimu umene ‘udzalalikira zoposazo za Yehova.’ (Agalatiya 6:16; 1 Petro 2:9) Awo amene adzakhalabe okhulupirika mpaka imfa adzaloŵa moyo wosakhoza kufa kumwamba monga olamulira anzake a Yesu mu Ufumu wake wakumwamba. (Mateyu 24:13; Aroma 8:15, 16; 1 Akorinto 15:50-54) Ndiponso, Akristu ameneŵa anayenera kulalikira za kudza kwa tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Iwo anali kudzachenjeza Ayuda kuti adzakhala ndi chisautso chachikulu choposa zisautso zonse zimene zinakanthapo Yerusalemu ndi odzinenera kuti ndi anthu a Mulungu kufikira nthaŵiyo. Komabe, padzakhala opulumuka. Ati? Awo amene adzaitana pa dzina la Yehova.
“Masiku Otsiriza”
5. Kodi nkukwaniritsidwa kotani kwa ulosi kumene kwachitika lerolino?
5 M’njira zambiri, mikhalidwe yakalelo inachitira chithunzi zimene tikuona lerolino. Chiyambire mu 1914, mtundu wa anthu wakhala m’nthaŵi yapadera yotchedwa m’Baibulo kuti “nthaŵi ya chimaliziro,” “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” ndi “masiku otsiriza.” (Danieli 12:1, 4; Mateyu 24:3-8; 2 Timoteo 3:1-5, 13) M’zaka za zana lathu, nkhondo zankhanza, chiwawa chosalamulirika, ndi kuwonongeka kwa khalidwe la anthu ndi malo okhala kwakwaniritsa ulosi wa Baibulo ndendende. Zonsezi zili mbali ya chizindikiro choloseredwa ndi Yesu, chosonyeza kuti mtundu wa anthu uli pafupi kuyang’anizana ndi tsiku la Yehova lomaliza ndi loopsa. Imeneyi idzakhala nkhondo ya Armagedo, chimake cha “chisautso chachikulu chimene sichinakhaleko kuchokera pachiyambi cha dziko lapansi kufikira tsopano, ayi, ndipo sichidzakhalakonso.”—Mateyu 24:21, NW; Chivumbulutso 16:16.
6. (a) Kodi Yehova wakhala akuchitanji kuti apulumutse ofatsa? (b) Kodi nkuti kumene tingapeze uphungu wa Paulo wonena za mmene tingapulumukire?
6 Pamene tsiku losakazalo likuyandikabe, Yehova akuchitapo kanthu kuti apulumutse ofatsa. Mu “nthaŵi ya chimaliziro” ino, iye wasonkhanitsa omaliza a Israyeli wauzimu wa Mulungu, ndiponso kuyambira cha m’ma 1930 kumkabe mtsogolo, iye wachititsa atumiki ake a padziko lapansi kusumika maganizo awo pa kusonkhanitsa “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Monga gulu, ameneŵa “akutuluka m’chisautso chachikulu” ali amoyo. (Chivumbulutso 7:9, 14) Koma kodi munthu aliyense payekha angatsimikize motani kuti adzapulumuka? Mtumwi Paulo akuliyankha funso limenelo. Mu Aroma chaputala 10, iye akupereka uphungu wabwino wopulumutsa—uphungu umene unali wofunika m’tsiku lake ndipo umene uli wofunikanso m’tsiku lathu.
Pemphero la Chipulumutso
7. (a) Kodi pa Aroma 10:1, 2 tikuonapo chiyembekezo chotani? (b) Kodi nchifukwa ninji Yehova tsopano anafuna kuti “uthenga wabwino” ulalikidwe konsekonse?
7 Pamene Paulo analemba buku la Aroma, Yehova anali atausiya kale mtundu wa Israyeli. Koma mtumwiyo anavomerezabe kuti: “Kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke.” Iye anafuna kuti Ayuda ena apeze chidziŵitso cholongosoka cha chifuniro cha Mulungu, chimene chidzawachititsa kupulumuka. (Aroma 10:1, 2) Ndiponso, Yehova anafuna kuti amene ali ndi chikhulupiriro padziko lonse la mtundu wa anthu apulumuke, monga momwe Yohane 3:16 akusonyezera kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Nsembe ya dipo ya Yesu inatsegula njira ya chipulumutso chachikulu chimenecho. Monga m’tsiku la Nowa ndi masiku ena achiweruzo amene anatsatira, Yehova wachititsa kuti “Uthenga Wabwino” ulalikidwe, kusonyeza njira ya chipulumutso.—Marko 13:10, 19, 20.
8. Motsanzira Paulo, kodi Akristu oona lerolino amasonyeza kufunitsa kwawo kwa yani, ndiponso motani?
8 Posonyeza kufunitsitsa kwake kwa Myuda ndi Wakunja yemwe, Paulo analalikira nthaŵi iliyonse atapeza mpata. Iye “[a]nakopa Ayuda ndi Ahelene.” Anauza akulu a ku Efeso kuti: “Sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba, ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (Machitidwe 18:4; 20:20, 21) Mofananamo, Mboni za Yehova lerolino zimalimbikira kulalikira, osati kwa okhawo odzinenera kukhala Akristu koma kwa anthu onse, ngakhale ‘kumalekezero ake a dziko.’—Machitidwe 1:8; 18:5.
Kulengeza “Mawu a Chikhulupiriro”
9. (a) Kodi Aroma 10:8, 9 akutilimbikitsa kukhala ndi chikhulupiriro chotani? (b) Kodi ndi liti pamene tiyenera kulengeza chikhulupiriro chathu ndipo kodi tiyenera kuchilengeza motani?
9 Kuti tipulumuke tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Pogwira mawu Deuteronomo 30:14, Paulo anati: “Mawu ali pafupi ndiiwe, mkamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mawu a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira.” (Aroma 10:8) Pamene tilalikira “mawu a chikhulupiriro” amenewo, iwo amazama mwakuya m’mitima mwathu. Ndi mmene zinalili kwa Paulo, ndipo mawu ake otsatira angalimbitse chosankha chathu cha kukhala monga iye pogaŵana chikhulupiriro chimenecho ndi ena: “Ngati udzavomereza [udzalengeza, NW] mkamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.” (Aroma 10:9) Sitimangolengeza pamaso pa anthu panthaŵi yaubatizo yokha koma nthaŵi zonse tiyenera kulengeza, kupereka umboni wachangu wapoyera wa mbali zonse zazikulu za choonadi. Choonadi chimenechi chikunena za dzina limenelo lamtengo wapatali la Ambuye Mfumu Yehova; za Mfumu yathu ndi Moombolo wathu Waumesiya, Ambuye Yesu Kristu; ndi za malonjezo aakulu a Ufumu.
10. Mogwirizana ndi Aroma 10:10, 11, kodi “mawu a chikhulupiriro” ameneŵa tiyenera kuwatenga motani?
10 Alionse amene salandira “mawu a chikhulupiriro” ameneŵa ndipo sawatsatira sadzapulumuka, monga momwe mtumwiyo akupitirizira kuti: “Ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso. Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira iye, sadzachita manyazi.” (Aroma 10:10, 11) Tiyenera kupeza chidziŵitso cholongosoka cha “mawu a chikhulupiriro” ameneŵa ndi kupitiriza kuwasungabe m’mitima yathu kuti tisonkhezeredwe kuwafotokoza kwa ena. Yesu iyemwini akutikumbutsa kuti: “Yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mawu anga mumbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nawo angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.”—Marko 8:38.
11. Kodi uthenga wabwino tiyenera kuufalitsa mpaka pati, ndipo nchifukwa ninji?
11 Monga momwe mneneri Danieli ananeneratu, m’nthaŵi ino yachimaliziro, “aphunzitsi” akuoneka kuti akuwala “ngati kunyezimira kwa thambo,” pamene kuchitira umboni Ufumu kukufutukuka kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ‘akutembenuza ambiri atsate chilungamo,’ ndipo chidziŵitso choona chachulukadi, popeza Yehova akupereka kuunika kowala mowonjezereka pamaulosi onena za nthaŵi ino yachimaliziro. (Danieli 12:3, 4) Umenewu ndiwo uthenga wachipulumutso wofunika kwambiri kuti onse okonda choonadi ndi chilungamo apulumuke.
12. Kodi Aroma 10:12 akugwirizana motani ndi ntchito ya mngelo yofotokozedwa pa Chivumbulutso 14:6?
12 Mtumwi Paulo akupitiriza kuti: “Kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa iye.” (Aroma 10:12) “Uthenga Wabwino” lerolino uyenera kulalikidwa kwa anthu owonjezereka padziko lonse lapansi—kwa anthu onse, kufika kumalekezero ake a dziko lapansi. Mngelo wa pa Chivumbulutso 14:6 akuulukabe pakati pa mlengalenga, kutipatsa ‘Uthenga Wabwino wosatha, tiulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.’ Kodi zimenezi zidzawapindulitsa motani awo amene akumvetsera?
Kuitana pa Dzina la Yehova
13. (a) Kodi lemba lathu la chaka cha 1998 ndi liti? (b) Kodi nchifukwa ninji lemba limeneli nloyenera kwambiri lerolino?
13 Pogwira mawu Yoweli 2:32, Paulo akuti: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumuka.” (Aroma 10:13) Nkoyenera chotani nanga kuti mawu amenewo asankhidwa kukhala lemba la chaka cha 1998 la Mboni za Yehova! Kupita patsogolo modalira Yehova, kudziŵikitsa dzina lake ndi zifuno zake zazikulu zimene dzinalo limaimira nkofunika kwambiri tsopano kuposa kale! Monga m’zaka za zana loyamba, chiitano chomvekera chikuperekedwa m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu loipa lilipoli kuti: “Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.” (Machitidwe 2:40) Chili chiitano chomveka ngati lipenga kwa anthu onse oopa Mulungu padziko lonse lapansi kuti aitane pa Yehova kuti iye awapatse chipulumutso ndi kupatsanso awo amene amvetsera chilengezo chawo chapoyera cha uthenga wabwino.—1 Timoteo 4:16.
14. Kodi tiyenera kuitana pa Thanthwe liti kuti tipulumuke?
14 Kodi nchiyani chidzachitika pamene tsiku lalikulu la Yehova lidzaulika padziko lapansili? Ambiri sadzapempha chipulumutso kwa Yehova. Anthu ambiri ‘adzanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa.’ (Chivumbulutso 6:15, 16) Iwo adzadalira magulu ndi mabungwe onga matanthwe a m’dongosolo lino la zinthu. Komano, zikanakhala bwino chotani nanga akanadalira Thanthwe lalikulu loposa onse, Yehova Mulungu! (Deuteronomo 32:3, 4) Ponena za iye, Mfumu Davide anati: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga.” Yehova ndiye “thanthwe la chipulumutso chathu.” (Salmo 18:2; 95:1) Dzina lake ndilo “linga lolimba,” “linga” lokha lolimba limene lidzatitetezera pazovuta zimene zilinkudza. (Miyambo 18:10) Chotero, nkofunika kwambiri kuti mwa anthu pafupifupi 6,000,000,000 amene ali ndi moyo lerolino, ambiri a iwo monga momwe zingathekere aphunzitsidwe kuitana pa dzina la Yehova mokhulupirika ndi moona mtima.
15. Kodi Aroma 10:14 akusonyezanji ponena za chikhulupiriro?
15 Moyenerera, mtumwi Paulo akupitiriza mwa kufunsa kuti: “Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira?” (Aroma 10:14) Pali anthu miyandamiyanda amene angathandizidwebe kuti atenge “mawu a chikhulupiriro” kukhala awo, kuti aitane pa Yehova kaamba ka chipulumutso. Chikhulupiriro nchofunika kwambiri. M’kalata ina, Paulo akuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Mulungu]; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Komano kodi anthu enanso mamiliyoni adzafika motani pa kukhulupirira Mulungu? M’kalata yopita kwa Aroma, Paulo akufunsa kuti: “Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye?” (Aroma 10:14) Kodi Yehova amapereka njira yowathandiza kumva? Kunena zoona iye amaterodi! Tamverani mawu otsatira a Paulo: “Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?”
16. M’makonzedwe a Mulungu, kodi nchifukwa ninji alaliki ali ofunikira?
16 Malinga ndi mawu a Paulo, nzoonekeratu kuti pakufunika alaliki. Yesu anasonyeza kuti zimenezi zidzakhala choncho, “kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 24:14; 28:18-20) Kulalikira kuli mbali yofunika kwambiri ya makonzedwe a Mulungu othandiza anthu kuti aitane pa dzina la Yehova kuti apulumuke. Ngakhale m’Dziko Lachikristu ambiri sakuchitapo kanthu kuti alemekeze dzina la Mulungu lamtengo wapatali. Ambiri sadziŵa mpang’ono pomwe kusiyanitsa pakati pa Yehova ndi zinthu zina ziŵiri chifukwa cha chiphunzitso chosafotokozeka cha Utatu. Ndiponso, ambiri ali m’gulu lonenedwa pa Salmo 14:1 ndi 53:1 kuti: “Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu.” Afunikira kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu wamoyo, ndipo ayenera kumvetsa zonse zimene dzina lake limaimira ngati akufuna kupulumuka pachisautso chachikulu chimene chayandikira.
‘Mapazi Okometsetsa’ a Olalikira
17. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuti Paulo agwire mawu ulosi wa kubwezeretsedwa? (b) Kodi kukhala ndi ‘mapazi okometsetsa’ kukuphatikizaponji?
17 Mtumwi Paulo ali ndi funso linanso lofunika kwambiri: “Adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Aroma 10:15) Paulo panopo akugwira mawu Yesaya 52:7, amene ali mbali ya ulosi wonena za kubwezeretsedwa umene wakwaniritsidwa chiyambire 1919. Lerolino, kachiŵirinso, Yehova akutumiza “amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso.” Momvera, “alonda” odzozedwa a Mulungu ndi atsamwali awo akuimbabe mokondwa. (Yesaya 52:7, 8) Mapazi a awo amene akubukitsa chipulumutso lerolino angatope, ngakhale kutuwa ndi fumbi, pamene akuyenda kunyumba ndi nyumba, koma nkhope zawo zimawala ndi chimwemwe chotani nanga! Iwo akudziŵa kuti atumidwa ndi Yehova kukalalikira uthenga wabwino wa mtendere ndiponso kukatonthoza olira, kuwathandiza ameneŵa kuitana pa dzina la Yehova kuti iwo adzapulumuke.
18. Kodi Aroma 10:16-18 akuti bwanji ponena za chotsatirapo chomaliza cha kulengeza uthenga wabwino?
18 Kaya anthu ‘akhulupirira zonenedwa’ kapena asankha kusazitsatira, mawu a Paulo ngoona: “Sanamva iwo kodi! Indetu, liwu lawo linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno awo kumalekezero a dziko lokhalamo anthu.” (Aroma 10:16-18) Monga momwe “zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu,” woonekera m’zolengedwa zake, momwemonso Mboni zake padziko lapansi ziyenera kulalikira ‘chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; kutonthoza mtima wa onse amene akulira maliro.’—Salmo 19:1-4; Yesaya 61:2.
19. Kodi nchiyani chidzachitikira awo amene ‘akuitana pa dzina la Yehova’ lerolino?
19 Tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova likuyandikabe. “Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.” (Yoweli 1:15; 2:31) Tingopemphera kuti anthu enanso miyandamiyanda alabadire uthenga wabwino mwamsanga, napite ku gulu la Yehova. (Yesaya 60:8; Habakuku 2:3) Kumbukirani kuti masiku ena a Yehova anadzetsa chiwonongeko pa oipa—m’tsiku la Nowa, m’tsiku la Loti, ndi m’masiku a Israyeli ndi Yuda ampatukowo. Tsopano tili pampenupenu pa chisautso chachikulu choposa zonse, pamene mkuntho wa Yehova udzasesa kuipa pankhope ya dziko lino lapansi, kulambula njira ya paradaiso wa mtendere wosatha. Kodi inu mudzakhala mmodzi wa ‘odzaitana pa dzina la Yehova’ mokhulupirika? Ngati zili choncho, kondwerani! Mulungu iyemwini akukulonjezani kuti mudzapulumuka.—Aroma 10:13, NW.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi zinthu zatsopano ziti zimene zinafalitsidwa Pentekoste wa 33 C.E. atapita?
◻ Kodi Akristu ayenera kuwamvetsera motani “mawu a chikhulupiriro”?
◻ Kodi ‘kuitana pa dzina la Yehova’ kumatanthauzanji?
◻ Kodi amithenga a Ufumu ali ndi ‘mapazi okometsetsa’ m’lingaliro lotani?
[Zithunzi patsamba 18]
Anthu a Mulungu akulengeza zoposa zake ku Puerto Rico, Senegal, Peru, Papua New Guinea—ndithudi, kuzungulira dziko lonse