‘Nzeru za Mulungu N’zozama’ Kwambiri
“Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?”—AROMA 11:33.
1. Kodi mwayi waukulu kwambiri kwa Akhristu obatizidwa ndi uti?
KODI mwayi waukulu kwambiri umene mwalandira ndi uti? Poyamba, mungaganize za ntchito ina imene mwapatsidwa kapena ulemu winawake umene mwalandira. Koma kwa Akhristu obatizidwafe, kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi Mulungu woona, ndi mwayi waukulu kwambiri. Chifukwa cha zimenezi timakhalanso ndi mwayi ‘wodziwidwa ndi Mulungu.’—Agal. 4:9; 1 Akor. 8:3.
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kudziwa Yehova ndiponso kudziwidwa ndi iye ndi mwayi waukulu kwambiri?
2 Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti kudziwa Yehova ndiponso kudziwidwa ndi iye ndi mwayi waukulu kwambiri? Chifukwa chakuti iye ndi Wamkulu m’chilengedwe chonse komanso amateteza anthu amene amawakonda. Mneneri Nahumu anauziridwa kulemba kuti: “Yehova ndi wabwino ndipo ndi malo achitetezo pa tsiku la nsautso. Amadziwa amene amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.” (Nah. 1:7; Sal. 1:6) Chiyembekezo chathu chodzakhala ndi moyo wosatha chimadalira kwambiri pa kudziwa kwathu Mulungu woona ndi Mwana wake Yesu Khristu.—Yoh. 17:3.
3. Kodi kudziwa bwino Mulungu kumatanthauza chiyani?
3 Kudziwa Mulungu sikumangotanthauza kudziwa dzina lake basi. Iye ayenera kukhala Mnzathu ndipo tiyenera kudziwa zimene amakonda ndi zimene amadana nazo. Kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezi kumasonyeza kuti timamudziwa bwino Mulungu. (1 Yoh. 2:4) Koma pali zinthu zinanso zimene zingatithandize ngati tikufunadi kudziwa Yehova. Sitiyenera kungodziwa zimene wachita, koma tiyeneranso kudziwa mmene wazichitira ndiponso chifukwa chimene wachitira zinthuzo. Tikamadziwa bwino zolinga za Yehova m’pamenenso timagoma kwambiri ndi ‘nzeru zake zozama.’—Aroma 11:33.
Yehova Ndi Mulungu Wokhala ndi Cholinga
4, 5. (a) Kodi m’Baibulo mawu akuti “cholinga” amatanthauza chiyani? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu akhoza kukwaniritsa cholinga chake pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana.
4 Yehova ndi Mulungu wokhala ndi cholinga ndipo Baibulo limanena kuti ali ndi “cholinga chamuyaya.” (Aef. 3:10, 11) Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? Mawu akuti “cholinga” m’Baibulo amatanthauza chinthu chimene munthu akufuna kuchita koma akhoza kuchikwaniritsa pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana.
5 Mwachitsanzo, munthu akhoza kukhala ndi cholinga chopita kumalo enaake. Pangakhale misewu yosiyanasiyana imene angadutse ndiponso akhoza kuyenda pa njinga kapena pa galimoto. Pamene akuyenda mumsewu umene wasankha akhoza kukumana ndi mavuto ena ngati mvula, kuchuluka kwa magalimoto ndiponso kutsekedwa kwa misewu. Zinthu zimenezi zingamuchititse kusintha njira. Koma ngakhale atasintha msewu kapena kayendedwe, adzakhala atakwaniritsa cholinga chake akafika kumaloko.
6. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amatha kusintha njira yokwaniritsira cholinga chake?
6 Nayenso Yehova wasonyeza kuti amatha kusintha njira yokwaniritsira cholinga chake chamuyaya. Podziwa kuti angelo komanso anthu ali ndi ufulu wosankha zochita, Iye amakhala wokonzeka kusintha njira yokwaniritsira cholinga chake. Mwachitsanzo, tiyeni tione mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake chokhudza Mbewu imene analonjeza. Poyamba penipeni, Yehova anauza banja loyamba kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Gen. 1:28) Kodi cholinga chakechi chinalephereka anthu atamupandukira m’munda wa Edeni? Ayi sichinalephereke. Nthawi yomweyo Yehova anapeza njira ina yokwaniritsira cholinga chakecho. Iye ananeneratu za “mbewu” imene idzathetse mavuto onse amene opandukawo anayambitsa.—Gen. 3:15; Aheb. 2:14-17; 1 Yoh. 3:8.
7. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu amene Yehova anagwiritsa ntchito podzifotokoza pa Ekisodo 3:14?
7 Mmene Yehova amasinthira njira yokwaniritsira cholinga chake pakachitika zinazake, n’zogwirizana ndi mawu amene anagwiritsa ntchito podzifotokoza. Mose atauza Yehova zifukwa zimene ankaona kuti zingamulepheretse kuchita ntchito imene anamupatsa, Yehova anamutsimikizira kuti: “‘Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.’ Ndiyeno anawonjezera kuti: ‘Ana a Isiraeli ukawauze kuti, “Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala ndiye wandituma kwa inu.”’” (Eks. 3:14) Yehova amatha kukhala aliyense amene akufuna kuti akwaniritse bwinobwino cholinga chake. M’buku la Aroma chaputala 11, Paulo anapereka fanizo lofotokoza bwino mfundo imeneyi. M’chaputala chimenechi ananena za mtengo wa maolivi wophiphiritsira. Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, kukambirana fanizo limeneli kutithandiza kumvetsa kuzama kwa nzeru za Yehova.
Cholinga cha Yehova Chokhudza Mbewu Imene Analonjeza
8, 9. (a) Kodi ndi mfundo zinayi ziti zimene zingatithandize kumvetsa fanizo la mtengo wa maolivi? (b) Kodi ndi yankho la funso liti limene limasonyeza kuti Yehova amatha kusintha njira yokwaniritsira cholinga chake?
8 Kuti timvetse fanizo la mtengo wa maolivi tiyenera kudziwa mfundo zinayi zosonyeza mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake chokhudza mbewu imene analonjeza. Choyamba, Yehova analonjeza Abulahamu kuti kudzera mwa mbewu, kapena kuti mbadwa zake, “mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso.” (Gen. 22:17, 18) Chachiwiri, mtundu wa Isiraeli, womwe unali mbadwa za Abulahamu, unapatsidwa mwayi wopanga ‘ufumu wa ansembe.’ (Eks. 19:5, 6) Chachitatu, Aisiraeli ambiri atakana Mesiya, Yehova anapeza njira ina yopangira ‘ufumu wa ansembe.’ (Mat. 21:43; Aroma 9:27-29) Pomaliza, ngakhale kuti Yesu ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu, anthu enanso amapatsidwa mwayi wokhala mbali ya mbewu imeneyi.—Agal. 3:16, 29.
9 Buku la Chivumbulutso limanena zinthu zina zokhudza mfundo zinayizi. Limanena kuti anthu okwanira 144,000 adzalamulira ndi Yesu monga mafumu ndi ansembe kumwamba. (Chiv. 14:1-4) Anthu amenewa amatchedwanso “ana a Isiraeli.” (Chiv. 7:4-8) Koma kodi anthu 144,000 amenewa amachokera mu mtundu wa Aisiraeli enieni kapena kuti Ayuda? Yankho la funso limeneli litithandiza kudziwa kuti Yehova amatha kusintha njira yokwaniritsira cholinga chake. Tiyeni tsopano tipeze yankho la funso limeneli m’kalata ya mtumwi Paulo yopita kwa Aroma.
‘Ufumu wa Ansembe’
10. Kodi mtundu wa Isiraeli unali ndi mwayi wapadera uti?
10 Monga tanenera kale, mtundu wa Isiraeli unali ndi mwayi wopanga ‘ufumu wa ansembe ndi mtundu woyera.’ (Werengani Aroma 9:4, 5.) Koma kodi n’chiyani chinachitika Mbewu imene Mulungu analonjeza itafika? Kodi zinathekadi kuti Aisiraeli auzimu okwana 144,000, omwe ndi mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu, achokere mu mtundu wa Isiraeli?
11, 12. (a) Kodi kusankha anthu opanga Ufumu wakumwamba kunayamba liti, ndipo Ayuda ambiri anachita chiyani pa nthawi imeneyo? (b) Kodi Yehova anatani kuti pakhale ‘chiwerengero chokwanira’ cha anthu opanga mbewu ya Abulahamu?
11 Werengani Aroma 11:7-10. Ayuda ambiri anakana Yesu. Choncho mwayi wokhala mbewu ya Abulahamu unaperekedwanso ku mitundu ina. Koma pamene kusankha anthu opanga ‘ufumu wa ansembe’ kumwamba kunayamba pa Pentekosite 33 C.E., panali Ayuda ena amtima wabwino amene analandira mwayiwu. Popeza anali masauzande owerengeka okha, tinganene kuti anali “ochepa” poyerekeza ndi mtundu wonse wa Ayuda.—Aroma 11:5.
12 Koma kodi Yehova anatani kuti pakhale ‘chiwerengero chokwanira’ cha anthu opanga mbewu ya Abulahamu? (Aroma 11:12, 25) Taonani yankho limene mtumwi Paulo anapereka. Iye anati: “Komabe, sizili ngati kuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse ochokera kwa Isiraeli [weniweni] amene alidi ‘Aisiraeli.’ Ndiponso si onse amene ali ana [mbali ya mbewu ya Abulahamu] chifukwa chongokhala mbewu ya [mbadwa za] Abulahamu . . . Izi zikutanthauza kuti, si ana akuthupi amene alidi ana a Mulungu, koma ana a lonjezo ndiwo amayesedwa mbewu.” (Aroma 9:6-8) Choncho sikuti munthu ayenera kukhala mbadwa yeniyeni ya Abulahamu kuti ayenerere kukhala mbali ya mbewu imene Yehova analonjeza.
Mtengo wa Maolivi Wophiphiritsira
13. Kodi zinthu izi zimaimira chiyani? (a) mtengo wa maolivi, (b) muzu wake, (c) thunthu lake ndiponso (d) nthambi zake.
13 Paulo anayerekeza anthu opanga mbewu ya Abulahamu ndi nthambi za mtengo wa maolivi wophiphiritsira.a (Aroma 11:21) Mtengo wa maolivi wobzalidwa umaimira kukwaniritsidwa kwa cholinga chimene Mulungu anali nacho pamene anachita pangano ndi Abulahamu. Muzu wa mtengowu ndi woyera ndipo umaimira Yehova chifukwa ndi amene amapereka moyo kwa Aisiraeli auzimu. (Yes. 10:20; Aroma 11:16) Thunthu la mtengowu limaimira Yesu chifukwa chakuti iye ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu. Nthambi zonse pamodzi zimaimira ‘chiwerengero chokwanira’ cha anthu opanga mbali yachiwiri ya mbewu ya Abulahamu.
14, 15. Kodi ndani ‘anadulidwa’ pamtengo wa maolivi wobzalidwa, nanga ndani analumikizidwa kumtengowu?
14 M’fanizo la mtengo wa maolivi, Ayuda amene anakana Yesu akuyerekezedwa ndi nthambi za mtengo wa maolivi zimene “zinadulidwa.” (Aroma 11:17) Choncho anataya mwayi wokhala mbali ya mbewu ya Abulahamu. Koma ndani anawalowa m’malo? Ayuda ankadzitama chifukwa chokhala mbadwa za Abulahamu ndipo ayenera kuti ankaona kuti n’zosatheka kulowedwa m’malo ndi anthu a mitundu ina. Koma Yohane Mbatizi anali atawachenjeza kale kuti ngati Yehova atafuna akhoza kuutsira Abulahamu ana kuchokera ku miyala.—Luka 3:8.
15 Ndiyeno kodi Yehova anakwaniritsa bwanji cholinga chake? Paulo anafotokoza kuti nthambi za mtengo wa maolivi wam’tchire zinalumikizidwa kumtengo wa maolivi wobzalidwa kuti zilowe m’malo mwa zimene zinadulidwa. (Werengani Aroma 11:17, 18.) Choncho Akhristu odzozedwa ndi mzimu ochokera ku mitundu ina, ngati amene anali mu mpingo wa ku Roma, analumikizidwa mophiphiritsira kumtengo wa maolivi. Izi zinachititsa kuti akhale mbali ya mbewu ya Abulahamu. Poyamba iwo anali ngati nthambi za mtengo wa maolivi wam’tchire ndipo analibe mwayi uliwonse wokhala m’pangano lapaderali. Koma Yehova anawapatsa mwayi wokhala Ayuda auzimu.—Aroma 2:28, 29.
16. Kodi mtumwi Petulo anafotokoza bwanji kupangidwa kwa mtundu watsopano wauzimu?
16 Mtumwi Petulo anafotokoza zimenezi ponena kuti: “Choncho iye [Yesu Khristu] ndi wamtengo wapatali kwa inu [Aisiraeli auzimu, kuphatikizapo Akhristu a mitundu ina] chifukwa ndinu okhulupirira, koma kwa osakhulupirira, ‘mwala umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri,’ komanso ‘mwala wopunthwitsa ndi thanthwe lokhumudwitsa.’ . . . Koma inu ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri’ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa. Pakuti kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu. Munali anthu amene sanakuchitireni chifundo, koma tsopano ndinu amene mwachitiridwa chifundo.”—1 Pet. 2:7-10.
17. Kodi zimene Yehova anachita zinali ‘zosemphana ndi chilengedwe’ m’njira iti?
17 Yehova anachita zinthu zimene anthu ambiri angaone kuti sizingachitike. Paulo ananena kuti zimene zinachitikazi ndi ‘zosemphana ndi chilengedwe.’ (Aroma 11:24) N’chifukwa chiyani anatero? Zingaoneke zachilendo ndiponso zosemphana ndi chilengedwe kuti munthu alumikize nthambi ya mtengo wam’tchire kumtengo wobzalidwa. Koma izi ndi zimene alimi ena ankachita nthawi ya atumwi.b Nayenso Yehova anachita zinthu zodabwitsa. Ayuda ankaona kuti anthu a mitundu ina sangabale zipatso zabwino. Koma Yehova anachititsa anthu a mitundu inayo kukhala mbali ya “mtundu” wobala zipatso za Ufumu. (Mat. 21:43) Mwayi woti anthu osadulidwa a mitundu ina alumikizidwe kumtengo wa maolivi wophiphiritsirawu unayamba mu 36 C.E. pamene Koneliyo anadzozedwa ndi mzimu. Mwa anthu osadulidwa a mitundu ina, Koneliyo anali woyamba kulowa Chikhristu.—Mac. 10:44-48.c
18. Kodi Ayuda enieni anali ndi mwayi uti ngakhale pambuyo pa 36 C.E.?
18 Kodi izi zikutanthauza kuti mwayi woti Ayuda enieni akhale mbali ya mbewu ya Abulahamu unatha mu 36 C.E.? Ayi. Paulo ananena kuti: “Iwonso [Ayuda enieni] ngati angayambe kukhala ndi chikhulupiriro, adzalumikizidwa kumtengowo, pakuti Mulungu akhoza kuwalumikizanso. Ngati iweyo unadulidwa kumtengo wa maolivi umene mwachilengedwe umamera m’tchire, ndipo mosemphana ndi chilengedwe, unalumikizidwa kumtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si kwapafupi kulumikiza nthambi izi kumtengo wawo umene zinadulidwako?”d—Aroma 11:23, 24.
“Aisiraeli Onse Adzapulumuka”
19, 20. Kodi mtengo wa maolivi wophiphiritsira ukuimira zinthu ziti zimene Yehova akukwaniritsa?
19 Cholinga cha Yehova chokhudza “Isiraeli wa Mulungu” chikukwaniritsidwa m’njira yochititsa chidwi kwambiri. (Agal. 6:16) Malinga ndi zimene Paulo ananena, “Aisiraeli onse adzapulumuka.” (Aroma 11:26) Pa nthawi imene Yehova wasankha, “Aisiraeli onse,” kapena kuti chiwerengero chokwanira cha Aisiraeli auzimu, adzatumikira monga mafumu ndi ansembe kumwamba. Palibe chimene chingalepheretse cholinga cha Yehova.
20 Mogwirizana ndi ulosi, mbewu ya Abulahamu, yomwe ndi Yesu Khristu limodzi ndi Akhristu odzozedwa 144,000, idzabweretsa madalitso kwa “anthu a mitundu ina.” (Aroma 11:12; Gen. 22:18) Chifukwa cha zimenezi, anthu onse a Mulungu adzapindula ndi cholinga chake chokhudza mbewu. Tikamaganizira mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake chamuyaya, m’pamene timazindikira kwambiri kuti “madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.”—Aroma 11:33.
[Mawu a M’munsi]
a Sikuti mtengo wa maoliviwu poyamba unkaimira mtundu wa Isiraeli. Tikunena choncho chifukwa chakuti mtunduwu sunakhale ufumu wa ansembe, ngakhale kuti Aisiraeli ena anakhala mafumu ndipo ena anali ansembe. Mu Isiraeli, lamulo silinkalola mafumu kukhala ansembe. Choncho mtengo wa maoliviwu sunaimire mtundu wa Isiraeli. Paulo anagwiritsa ntchito fanizoli posonyeza kuti cholinga cha Mulungu choti apange ‘ufumu wa ansembe’ chidzakwaniritsidwa ndi Aisiraeli auzimu. Mfundo imeneyi ikusintha zimene zinalembedwa mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya August 15, 1983, tsamba 14 mpaka 19.
b Onani bokosi lakuti, “N’chifukwa Chiyani Ankalumikiza Nthambi za Mtengo wa Maolivi Wam’tchire?”
c Izi zinachitika pambuyo poti Ayuda enieni apatsidwa mpata wa zaka zitatu ndi hafu woti akhale mbali ya mtundu wauzimu watsopano. Zimene zinachitikazi zinatchulidwa mu ulosi wa milungu 70 ya zaka.—Dan. 9:27.
d Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “wolimidwa” pa Aroma 11:24 anachokera ku mawu otanthauza “wabwino kwambiri” kapena “wogwirizana ndi cholinga chake.” Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za zinthu zimene zimakwaniritsa bwino cholinga chimene anazipangira.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova tikamaona mmene akukwaniritsira cholinga chake?
• Pa Aroma chaputala 11 kodi zinthu izi zikuimira chiyani?
Mtengo wa maolivi
Muzu wake
Thunthu lake
Nthambi zake
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti nthambi zinalumikizidwa kumtengo “mosemphana ndi chilengedwe”?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]
N’chifukwa Chiyani Ankalumikiza Nthambi za Mtengo wa Maolivi Wam’tchire?
▪ M’nthawi ya atumwi panali munthu wina amene anali msilikali wachiroma ndiponso mlimi ndipo dzina lake linali Lucius Junius Moderatus Columella. Iye ndi wodziwika chifukwa cholemba mabuku 12 okhudza moyo wakumudzi ndiponso ulimi.
M’buku lake lachisanu, analembamo mwambi wakale kwambiri wakuti: “Munthu amene amalima munda wa maolivi amapempha zipatso, amene amathira manyowa amapempha zipatso mochonderera koma amene amatengulira mitengo yake amakakamiza mundawo kubala zipatso.”
Pambuyo pofotokoza mitengo imene inkakula bwino koma osabala zipatso, iye ananena zoyenera kuchita. Iye anati: “Ndi bwino kuiboola n’kulumikiza nthambi zanthete za mtengo wa maolivi wam’tchire. Mukatero, mtengowo umakhala ngati watenga pathupi ndipo umabala zipatso zambiri.”
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi mukudziwa tanthauzo la fanizo la mtengo wa maolivi wophiphiritsira?