Kuteteza Dzina Lathu Monga Akristu
“Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova.”—YESAYA 43:10.
1. Kodi Yehova amakoka anthu otani kuti adze kwa iye?
NGATI muli pa Nyumba ya Ufumu, tayang’anani anthu amene muli nawo pafupiwo. Kodi mukuona ndani pa malo olambirirawa? Mwina mukuona achinyamata okhulupirika amene akumvetsera mwatcheru malangizo anzeru a m’Malemba. (Salmo 148:12, 13) N’zachidziwikire kuti mukuonanso mitu ya mabanja yomwe ikuyesetsa kukondweretsa Mulungu ngakhale kuti ili m’dziko limene limapeputsa moyo wa m’banja. Mwinanso mukuona achikulire okondedwa, amene akuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi kudzipatulira kwawo kwa Yehova ngakhale kuti akukumana ndi zowawa zambiri chifukwa cha ukalamba. (Miyambo 16:31) Onsewa amam’konda kwambiri Yehova. Ndipo iye waona kuti n’koyenera kuwakoka kuti akhale mabwenzi ake. Mwana wa Mulungu ananena motsimikiza kuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine am’koka iye.”—Yohane 6:37, 44, 65.
2, 3. N’chifukwa chiyani sizophweka kuchita zinthu mozindikira kuti ndife Akristu?
2 Kodi sitikusangalala kuti tili m’gulu la anthu amene Yehova akukondwera nawo ndiponso kuwadalitsa? Komatu ‘m’nthawi zowawitsa’ zino, sizophweka kuchita zinthu nthawi zonse mozindikira kuti ndife Akristu. (2 Timoteo 3:1) Izi zili choncho makamaka kwa achinyamata amene akulira m’mabanja achikristu. Wachinyamata wina anavomereza kuti: “Ngakhale kuti ndinkapezeka pa misonkhano yachikristu, ndinalibe zolinga zenizeni zauzimu, ndipo kunena zoona, sindinali wotsimikiza mtima kutumikira Yehova.”
3 Ngakhale kuti akufunitsitsa ndi mtima wonse kutumikira Yehova, ena angalephere kutero chifukwa chotengera kwambiri zochita za anzawo, zochitika za m’dzikoli, ndiponso chifukwa cha zizolowezi zoipa. Mwapang’onopang’ono zinthu zotisokoneza zingatiiwalitse kuchita zinthu mozindikira kuti ndife Akristu. Mwachitsanzo, anthu ambiri m’dzikoli masiku ano, amati miyezo ya m’Baibulo ya makhalidwe abwino ndi yachikale kapena kuti sitingakwanitse kuitsatira masiku ano. (1 Petro 4:4) Ena amaganiza kuti n’zosafunika kwenikweni kulambira Mulungu m’njira imene iyeyo akufuna. (Yohane 4:24) M’kalata imene Paulo analembera Aefeso, ananena kuti padziko lapansi pali “mzimu,” kapena kuti maganizo omwe afala kwambiri. (Aefeso 2:2) Mzimu umenewu umalimbikitsa anthu kuti maganizo awo agwirizane ndi maganizo a anthu osadziwa Yehova.
4. Kodi Yesu anatsindika motani kuti tikufunika kuteteza dzina lathu monga Akristu?
4 Komabe, monga atumiki odzipatulira kwa Yehova, tikudziwa kuti zingakhale zoopsa kwambiri ngati winawake, kaya wachinyamata kapena wachikulire, atachita zinthu zomwe zingaipitse dzina lake monga Mkristu. Munthu angadziwike ndi dzina labwino monga Mkristu, ngati akutsatira miyezo ya Yehova ndi kuchita zimene Iye amayembekezera kwa ife. Izitu n’zoyenera chifukwa tinalengedwa m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26; Mika 6:8) Baibulo limayerekezera dzina lathu labwino monga Akristu, ndi chovala chimene timavala mwakuti aliyense angathe kuchiona. Pochenjeza za nthawi yathu ino, Yesu anati: “Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.”a (Chivumbulutso 16:15) Sitiyenera kuvula makhalidwe ndi miyezo yathu yachikristu n’kulola kutengera makhalidwe a dziko la Satanali. Ngati zoterezi zitatichitikira, ndiye kuti talephera kusunga “zovala” zimenezi. Izitu zingakhale zomvetsa chisoni ndi zochititsa manyazi.
5, 6. N’chifukwa chiyani kukhala wosasunthika mwauzimu kuli kofunika?
5 Kuchita zinthu nthawi zonse mozindikira kuti ndife Akristu, kumakhudza kwambiri zimene munthu angachite m’moyo wake. Motani? Ngati wolambira Yehova ataiwala kuti ndi Mkristu angathe kusokonezeka pa zolinga zake m’moyo. Mobwerezabwereza Baibulo limachenjeza za mtima wosatsimikiza woterowo. Wophunzira Yakobo anachenjeza kuti: “Wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zake zonse.”—Yakobo 1:6-8; Aefeso 4:14; Ahebri 13:9.
6 Kodi tingateteze bwanji dzina lathu monga Akristu? N’chiyani chomwe chingatithandize kuti tizikumbukira nthawi zonse mwayi waukulu umene tili nawowu wokhala olambira a Wam’mwambamwamba? Onani njira zotsatirazi.
Dziunikeni Ngati Mulidi Mkristu Weniweni
7. N’chifukwa chiyani kuchonderera Yehova kuti atiunike kuli kopindulitsa?
7 Tsimikizirani nthawi zonse kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi wolimba. Chuma chamtengo wapatali kwambiri chimene Mkristu aliyense ali nacho ndi ubwenzi wake ndi Mulungu. (Salmo 25:14; Miyambo 3:32) Ngati tayamba kukayikira penapake za dzina lathu monga Mkristu, ndi bwino kuunika mosamala mmene ubwenzi umenewu ulili. Moyenerera, wamasalmo anachonderera kuti: “Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” (Salmo 26:2) N’chifukwa chiyani tiyenera kuunikidwa mwa njira imeneyi? Chifukwa chakuti ifeyo patokha sitingathe kudziunika modalirika pankhani ya zolinga zathu ndiponso zimene zili mumtima mwathu. Yehova yekha ndi amene angathe kuzindikira umunthu wathu, kapena kuti zolinga zathu, maganizo athu ndi mmene timamvera mumtima.—Yeremiya 17:9, 10.
8. (a) Kodi mayeso a Yehova tingapindule nawo bwanji? (b) Kodi mwathandizidwa motani kuti mupite patsogolo monga Mkristu?
8 Tikamapempha Yehova kuti atiunike, ndiye kuti tikumuuzanso kuti atiyese. Choncho iye angalole zinazake kutichitikira zomwe zingavumbule zolinga zathu zenizeni ndi mmene mtima wathu ulili. (Ahebri 4:12, 13; Yakobo 1:22-25) Mayeso oterowo tiyenera kuwalandira chifukwa amatipatsa mwayi wosonyeza kuti ndife wokhulupirika motani kwa Yehova. Mayeso amenewa angasonyeze ngati tili “angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse.” (Yakobo 1:2-4) Ndipo pamene tikuyesedwa, tingakule mwauzimu.—Aefeso 4:22-24.
9. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kudzikhutiritsa tokha kuti Baibulo limaphunzitsa choonadi? Fotokozani.
9 Chidziweni bwino choonadi cha m’Baibulo. Pang’ono ndi pang’ono tingaiwale kuti ndife atumiki a Yehova ngati utumiki wathuwo sukuyendera limodzi ndi kudziwa bwino Malemba. (Afilipi 1:9, 10) Mkristu aliyense, kaya ndi wachinyamata kapena wachikulire, ayenera kukhala ndi umboni woti iyeyo payekha azikhutira nawo wosonyeza kuti zimene amakhulupirira zilidi choonadi cha m’Baibulo. Paulo anapempha okhulupirira anzake kuti: “Yesani zonse; sungani chokomacho.” (1 Atesalonika 5:21) Akristu achinyamata omwe akuchokera m’mabanja oopa Mulungu ayenera kuzindikira kuti iwowo sangakhale Akristu oona mwa kungodalira chikhulupiriro cha makolo awo. Davide analimbikitsa Solomo, mwana wake weniweni kuti ‘am’dziwe Mulungu wa atate wake, ndi kum’tumikira ndi mtima wangwiro.’ (1 Mbiri 28:9) Sizinali zokwanira kwa Solomo wachinyamatayo kumangoonerera mmene bambo akewo akulimbitsira chikhulupiriro chawo mwa Yehova. Nayenso anafunika kum’dziwa Yehova, ndipo anachitadi zimenezo. Iye anapempha Mulungu kuti: “Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa.”—2 Mbiri 1:10.
10. N’chifukwa chiyani sipolakwika kufunsa mafunso moona mtima ndi cholinga chabwino?
10 Chikhulupiriro cholimba chimagona pa zimene munthu akudziwa. “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri,” anatero Paulo. (Aroma 10:17) Kodi anatanthauzanji pamenepa? Anatanthauza kuti tikamaphunzira Mawu a Mulungu, timalimbitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso timadalira Yehova, malonjezo ake, ndi gulu lake. Kufunsa moona mtima mafunso okhudza Baibulo kungatithandize kupeza mayankho okhutiritsa. Komanso pa Aroma 12:2, timapezapo malangizo a Paulo akuti: “Mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” Koma tingazikwanitse bwanji zimenezi? Mwa “kuchidziwa molondola choonadi.” (Tito 1:1 NW) Mzimu wa Yehova ungatithandize kumvetsa bwino nkhani zakuya zovuta kumvetsa. (1 Akorinto 2:11, 12) Ngati penapake pakutivuta kupamvetsa, tiyenera kupemphera kwa Mulungu kuti atithandize. (Salmo 119:10, 11, 27) Yehova akufuna kuti Mawu ake tiwamvetse bwino, kuwakhulupirira, ndi kuwatsatira. Iye amayankha mafunso ofunsidwa moona mtima ndiponso n’cholinga chabwino.
Tsimikizani Mtima Kukondweretsa Mulungu
11. (a) Kodi timalakalaka chiyani mwachibadwa chimene chingakhale msampha? (b) N’chiyani chingatithandize kulimba mtima kuti tisatengere zochita za anzathu?
11 Kondweretsani Mulungu, osati anthu. N’zachibadwa kufuna kudziwika kuti tili m’gulu linalake. Aliyense amafuna kukhala ndi anzake, ndipo timamva bwino kukhala pagulu la anzathu. Ana akamafika pamsinkhu wachinyamata ndiponso akakula ndithu, angatengeke kwambiri ndi zochita za anzawo. Izi zingakulitse mtima wofunitsitsa kutsanzira ena kapena kuwasangalatsa. Komatu dziwani kuti anzathu ndiponso anthu amsinkhu wathu sikuti nthawi zonse amatifunira zabwino ayi. Nthawi zina amangofuna wina woti azichita naye limodzi zoipazo. (Miyambo 1:11-19) Mkristu akagonjera anzake amene akum’kakamiza kuchita zoipa, nthawi zambiri amayesetsa kudzibisa kuti ndi Mkristu. (Salmo 26:4) Mtumwi Paulo anachenjeza kuti: “Musatengere khalidwe la dzikoli.” (Aroma 12:2, The Jerusalem Bible) Yehova amatithandiza kukhala olimba kuti tisatengeke ndi zochita za ena.—Ahebri 13:6.
12. Kodi ndi mfundo iti limodzi ndi chitsanzo chake zomwe zingatilimbikitse kusagonjera pankhani zokhudza kukhulupirika kwathu kwa Mulungu?
12 Ngati tikutengeka ndi zochita za anthu, zomwe zingaipitse dzina lathu monga Akristu, ndi bwino kukumbukira kuti kukhala wokhulupirika kwa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa maganizo a anthu kapena zochita za anthu ochuluka. Mfundo yabwino kwambiri pankhaniyi ikupezeka pa lemba la Eksodo 23:2 lomwe limati: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.” Aisrayeli ochuluka atakayikira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo Ake, molimba mtima Kalebi anakana kuyendera maganizo a anzakewo. Iye anali wotsimikiza kuti malonjezo a Mulungu ndi odalirika, ndipo anapindula kwambiri chifukwa cha kulimba mtima kwakeko. (Numeri 13:30; Yoswa 14:6-11) Kodi nanunso ndinu wotsimikiza mofananamo kukanitsitsa kuyendera maganizo amene anthu ambiri akutsatira, pofuna kuti muteteze ubwenzi wanu ndi Mulungu?
13. N’chifukwa chiyani zili nzeru kudziwitsa aliyense kuti ndinu Mkristu?
13 Dziwitsani onse kuti ndinu Mkristu. Njira yabwino yodzitchinjirizira poteteza dzina lathu monga Akristu ndiyo kuwauziratu ena kuti ndife Akristu. Aisrayeli okhulupirika m’masiku a Ezara, atakumana ndi chitsutso pamene anali kuyesetsa kuchita chifuniro cha Yehova, anati: “Ife ndife akapolo a Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi.” (Ezara 5:11) Zochita za anthu ankhanza komanso kutsutsa kwawo zingathe kutilepheretsa kuchita zinthu chifukwa cha mantha. Ngati nthawi zonse timafuna kusangalatsa aliyense, sitingachite zinthu zogwira mtima. Choncho musamaope anthu. Nthawi zonse ndi bwino kuti anthu ena muziwadziwitsa momveka bwino kuti ndinu wa Mboni za Yehova. Mwaulemu koma motsimikiza mtima, mungafotokoze kwa ena mfundo zimene mumatsatira, zikhulupiriro zanu, ndi mmene mumaonera zinthu monga Mkristu. Auzeni ena kuti inuyo munatsimikiza mtima kuti muzitsatira makhalidwe abwino amene Yehova amafuna. Atsimikizireni kuti simungasunthike pankhani ya kukhala wokhulupirika monga Mkristu. Sonyezani kuti mumanyadira makhalidwe anu abwinowo. (Salmo 64:10) Kudziwika kuti ndinu Mkristu wolimba kungakulimbikitseni, kukutetezani, ndiponso kulimbikitsa ena kufufuza za Yehova ndi anthu ake.
14. Kodi tiyenera kufooka chifukwa chakuti ena akutinyoza ndi kutitsutsa? Fotokozani.
14 N’zoona kuti ena angakunyozeni kapena kukutsutsani. (Yuda 18) Musafooke ngati ena sakukumvetsani pamene mukuyesetsa kuwafotokozera makhalidwe amene mumatsatira. (Ezekieli 3:7, 8) Ngakhale mutayesetsa chotani, simungathe kukhutiritsa anthu amene sakufuna kukhutira. Kumbukirani za Farao. Farao sanakhutire kuti Mose anali kumuuza mawu ochokera kwa Yehova, ngakhale kuti anam’dzetsera milili ndi kum’chitira zozizwitsa zosiyanasiyana. Ngakhale imfa ya mwana wake woyamba kubadwa siinamuchititse Farao kukhulupirira zimenezi. Choncho musabwerere m’mbuyo chifukwa choopa anthu. Mantha onse angathe ngati titadalira Mulungu ndi kum’khulupirira.—Miyambo 3:5, 6; 29:25.
Phunzirani pa Zam’mbuyo, Ganizirani Zam’tsogolo
15, 16. (a) Kodi cholowa chathu chauzimu n’chiyani? (b) Kodi tingapindule bwanji poganizira mwakuya za cholowa chathu chauzimu mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena?
15 Ganizirani za cholowa chanu chauzimu. Pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, Akristu angapindule poganizira mwakuya za cholowa chawo chauzimu chamtengo wapatali. Cholowa chimenechi chikuphatikizapo zinthu monga choonadi cha Mawu a Yehova, chiyembekezo cha moyo wosatha, ndi mwayi woimira Mulungu monga olengeza uthenga wabwino. Kodi mukuona udindo umene muli nawo pakati pa Mboni zake, zomwe ndi gulu lodalitsika la anthu amene apatsidwa ntchito yopulumutsa moyo, yolalikira za Ufumu? Kumbukirani kuti ndi Yehova amene akutitsimikizira kuti: “Inu ndinu mboni zanga.”—Yesaya 43:10.
16 Mungadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi kwa ineyo cholowa chauzimu chimenechi n’chamtengo wapatali motani? Kodi ndimachiona kuti ndi chofunika kwambiri mwakuti ndimayesetsa kuti chinthu choyamba pamoyo wanga chikhale kuchita chifuniro cha Mulungu? Kodi cholowa chimenechi ndimachiyamikira kwambiri moti chingandithandize kupewa zokopa zimene zinganditayitse cholowachi?’ Cholowa chathu chauzimuchi chingatichititse kumva kuti ndife otetezeka kwambiri mwauzimu, ndipo chitetezo choterechi chimapezeka m’gulu la Yehova lokha basi. (Salmo 91:1, 2) Kuwerenga nkhani zochititsa chidwi za mbiri yamakono ya gulu la Yehova, kungatithandize kusakayika n’komwe kuti palibe munthu kapena chinthu chimene chingafafanize anthu a Yehova padziko lapansi.—Yesaya 54:17; Yeremiya 1:19.
17. N’chiyaninso china chimene chikufunika kuposa kungodalira cholowa chathu chauzimu?
17 Komatu sikuti tingangodalira cholowa chathu chauzimu chokhacho. Aliyense wa ife ayenera kupanga ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Paulo atachita khama kwambiri polimbitsa chikhulupiriro cha Akristu ku Filipi, anawalembera kuti: “Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.” (Afilipi 2:12) Kuti tidzapulumuke zikudalira zochita zathu osati za wina.
18. Kodi ntchito zachikristu zingatithandize bwanji kukumbukira nthawi zonse kuti ndife Akristu?
18 Chitani khama kwambiri pa ntchito zachikristu? Ena amanena kuti “munthu amadziwika ndi ntchito imene amagwira.” Lerolino, Akristu apatsidwa ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene unakhazikitsidwa. Paulo anati: “Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga.” (Aroma 11:13) Ntchito yathu yolalikira imatisiyanitsa ndi dziko, ndipo tikamagwira nawo ntchito imeneyi timapitiriza kutchukitsa dzina lathu lakuti ndife Akristu. Kukhala wakhama kwambiri pa zochitika mu mpingo wachikristu, monga misonkhano yachikristu, ntchito yomanga malo olambirira, kuyesetsa kuthandiza osowa, ndi zina zotero, kungatithandize kukumbukira nthawi zonse kuti ndife Akristu.—Agalatiya 6:9, 10; Ahebri 10:23, 24.
Kukhala Mkristu Weniweni N’kopindulitsa
19, 20. (a) Kodi inuyo panokha mwapindula bwanji chifukwa chokhala Mkristu? (b) Kodi n’chiyani chimene chimatithandiza kukumbukira kuti ndifedi Akristu?
19 Kwa kanthawi, ganizirani za madalitso ochuluka ndiponso zabwino zina zimene tapeza chifukwa chokhala Akristu. Tili ndi mwayi waukulu chifukwa Yehova amatidziwa ifeyo patokha. Mneneri Malaki anati: “Iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.” (Malaki 3:16) Tingakhale mabwenzi a Mulungu. (Yakobo 2:23) Moyo wathu umakhala ndi zolinga zenizeni zosangalatsa ndi zopindulitsa, komanso umakhala wopindulitsa. Ndipotu tapatsidwa chiyembekezo cha tsogolo lamuyaya.—Salmo 37:9.
20 Kumbukirani kuti amene amadziwa zenizeni zokhudza kuti inuyo ndinu munthu wotani makamaka ndiponso ndinu wofunika motani ndi Mulungu, osati anthu ena ayi. Ena angamatione m’njira inayake potengera maganizo a anthu basi. Koma chikondi cha Mulungu ndi chidwi chimene ali nacho pa ife, n’zimene zimatisonyeza kuti ndife ofunika, chifukwatu ndife anthu ake. (Mateyu 10:29-31) Ndiyeno chikondi chathu pa Mulungu chingatithandize kumakumbukira nthawi zonse kuti ndife Akristu ndi kutithandiza kuona zimene tiyenera kuchita m’moyo wathu. “Ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.”—1 Akorinto 8:3.
[Mawu a M’munsi]
a N’kutheka kuti mawu amenewa akunena zimene woyang’anira malo ozungulira kachisi ku Yerusalemu ankachita. M’kati mwa usiku, iye ankayendera kachisiyo kuti aone ngati alonda achilevi, amene ankalondera malo osiyanasiyana pakachisiyo ali m’maso kapena ngati akugona. Mlonda aliyense wopezeka akugona ankamumenya ndi ndodo, ndipo zovala zake ankatha kuzitentha. Ichi chinali chilango chochititsa manyazi.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti Akristu ateteze dzina limene amadziwika nalo mwauzimu?
• Kodi tingatsimikizire motani kuti ndifedi Mkristu weniweni?
• Pamene tikufuna kusankha woti timukondweretse, ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kusankha mwanzeru?
• Kodi kukumbukira nthawi zonse kuti ndife Akristu kungakonze bwanji tsogolo lathu monga Akristu?
[Zithunzi patsamba 21]
Kukhala wakhama kwambiri pa ntchito zachikristu kungatithandize kukumbukira nthawi zonse kuti ndife Akristu