Kodi Tingavomereze Motani Chikondi cha Mulungu Mopanda Dyera?
‘Ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.’—1 YOHANE 4:11.
1, 2. Kodi chimafunikira nchiyani kwa ife kuti tivomereze zisonyezero za chikondi cha Mulungu mopanda dyera?
YEHOVA mwiniyo ngwaumunthu wachikondi. Ndithudi, m’nkhani yapitayo, tinawona kuchuluka kwa zisonyezero zenizeni za chikondi chake. Tinazindikiranso mmene Mose, Davide, ndi Yesu Kristu anavomerezera zisonyezero za chikondi zimenezo mopanda dyera. Kodi mmodzi ndi mmodzi wa Mboni za Yehova sayenera kufuna kuchita zofananazo? Ndithudi ayenera!
2 Kodi chofunikira nchiyani kuti tivomereze mopanda dyera zisonyezero za chikondi cha Mulungu? Choyamba, tiyenera kumpatsa malo oyamba m’moyo wathu, kumkonda ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi nyonga. (Marko 12:29, 30) Zimenezo zikutanthauza kukhala wokhoterera kwa Mulungu, kukhala ndi unansi waumwini wathithithi ndi Yehova. Kodi timakhumba kulankhuzana ndi Atate wathu wakumwamba m’pemphero? Kodi timapemphera mosaleka ndikulimbikira m’pemphero? Kapena kodi timangotchula zinthu m’mangum’mangu m’mapemphero athu, nthaŵi zina tikumakhaladi otanganitsidwa kwambiri osakhoza kupemphera? (Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Kodi timalunjikitsa chidwi kwa Yehova, kumpatsa iye ndi gulu lake ulemu kaamba ka zimene tingakhale takwaniritsa? (1 Akorinto 3:7; 4:7) Ndithudi, kodi timalingalira monga mmene anachitira wamasalmo? Ponena za Mulungu, iye anati: “Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi.”—Salmo 119:164.
3. Pamene tikumana pamodzi kuyanjana, kodi tingasonyeze motani kuti tikuvomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera?
3 Kaya tikuvomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera kapena ayi iko kungavumbulidwe bwino pamene tikumana pamodzi kaamba ka mayanjano. Kodi makambitsirano athu amasumika pa zinthu zakuthupi kapena zauzimu? Ichi sichikutanthauza kuti nthaŵi iriyonse titakumana pamodzi ndi Akristu anzathu tiyenera kukhala ndi phunziro la Baibulo losamalitsa. Koma motsimikizirikadi tingapeze zinthu zokondweretsa zauzimu zofunikira kuphatikizidwa m’makambitsirano athu. Bwanji osasimba zokumana nazo zakumunda, kufotokozerana malemba apamtima pathu a m’Baibulo, kusimba mmene tinaphunzirira chowonadi, kapena kutchula umboni wa chisamaliro chachikondi ndi dalitso la Mulungu?
4. Kodi tiyenera kuzilingalira bwanji nkhani ngati tagwiritsidwa mwala ponena za mwaŵi wakutiwakuti wautumiki?
4 Mkhalidwe wina umene ungavumbule kuya kwa kuyamikira kwathu chikondi cha Mulungu ndiwo pamene tamanidwa mwaŵi wakutiwakuti wautumiki m’gulu la Yehova. Kodi timachita motani? Ngati tiri kwakukulukulu odera nkhaŵa kulemekeza Yehova, ndiko kuti tidzavomereza kuti Mulungu mwachiwonekere adzalemekezedwa ndendende ndi munthu wokhala ndi mwaŵi uliwonse wautumiki. (Yerekezerani ndi Luka 9:48.) Koma ngati tiri odera nkhaŵa ndi mwaŵi kapena kutchuka kwathu mopambanitsa, kumanidwako kudzatitsendereza, monga mmene tingaganizire. Tiyenera kukumbukira kuti Yehova amatikonda ndipo angakhale akudziŵadi kuti pakali pano sitingasamalire kulemera kwa mathayo akutiakuti ateokratiki. Iye angakhale akutidalitsa molemerera m’njira zinanso, ndipo chisonyezero choterocho cha chikondi chake chiyenera kutithandiza kusungabe kulinganizika kwathu kwauzimu.—Miyambo 10:22.
Kukonda Chilungamo, Ndikudana Nako Kusayeruzika
5. Kodi zisonyezero za chikondi cha Mulungu ziyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pamkhalidwe wathu?
5 Kusonyezedwa kwa chikondi cha Mulungu pa ife kuyenera kutisonkhezera kutsanzira Kristu m’kukonda chilungamo ndikudana nako kusayeruzika. (Ahebri 1:9) Zowonadi, sitingachite zimenezi mwangwiro, monga mmene anachitira Yesu. Komabe, tingachipange kukhala chonulirapo chathu kukhala oyera, owona mtima, ndi osunga malamulo monga mmene kungathekere mumkhalidwe wathu wopanda ungwirowu. Kuti tichite tero, sitiyenera kokha kukulitsa kukonda zinthu zolungama ndi zabwino komanso kukulitsa chidani, kuipidwa, kunyansidwa, ndi chinthu choipa. Monga mmene mtumwi Paulo anafotokozera kuti: ‘Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.’ (Aroma 12:9) Liwu lakuti ‘kuda’ nlamphamvu kwambiri, limatathauza “kuchiwona chinthu kukhala chonyansa kwambiri.”—Webster’s New Collegiate Dictionary.
6. Kodi nchiyani chidzatithandiza kuchenjera ndi ziyeso zoikidwa m’njira yathu ndi dziko, thupi lathu lochimwa, ndi Mdyerekezi?
6 Kodi chidzatithandiza nchiyani kuchenjera ndi ziyeso zoikidwa m’njira yathu ndi dzikoli, thupi lathu lochimwa, ndi Mdyerekezi? Kukhala wokhulupirika kwa Yehova Mulungu. Iye akutichonderera kuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Inde, kukhala wokhulupirika kwa Yehova kudzatisonkhezera kutenga njira yanzeru ya kudana ndi zimene iye amazida. Kuwonjezerapo, mosasamala kanthu ndikuti kuswa limodzi la malamulo a Mulungu kukuwoneka kosangulutsa ndi kokondweretsa chotani, tiyenera kupitirizabe kudzikumbutsa tokha kuti kuchita tero sikulidi kwaphindu. (Agalatiya 6:7, 8) Mtima wa munthu ngwodwala, wauchiwanda, wachinyengo, mongadi mmene tikukumbutsidwira pa Yeremiya 17:9. Mtima Wamkristu umakonda zinthu zabwino, zokongola, ndizoyera. Koma nthaŵi zina zikhoterero zauchimo zimaukhotetsa kukhumbanso zinthu zoipa. Mofanana ndi mitima ya Aisrayeli amene analambira Yehova komano nasungabe “misanje” yawo yamafano, choteronso mtima wathu ungakhale wadyera ndi wachinyengo. (1 Mafumu 22:43; Deuteronomo 12:2) Mtima wathu wopanda ungwiro ungayese kupeza chodzikhululukira kuti utiloŵetse m’njira yachiyeso. Iwo ungayambe kunyalanyaza kuipa kwa choipacho chomwe tayesedwa nacho. Kapenatu mtima wathu ungayese kutikhutiritsa kuti chilango choperekedwa chirichonse chidzangokhala kwakanthaŵi kochepa.
7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuchenjera ndi kukhumbira zoipa?
7 M’kuyamikira kwathu chikondi cha Mulungu, tiyenera kuchenjera ndikukhumbira zoipa, monga ngati kulakalaka chisembwere cha kugonana, kaya ndife mbeta kapena okwatira. Kaŵirikaŵiri, maseŵera omwe anayamba ndikutyasira kosavulaza atulukapo kukhumbirana kwa Akristu aŵiriwo mwakuti achita tchimo ndikuchotsedwa. Ngakhale akulu, amene ayenera kukhala chitsanzo chopanda banga ku nkhosa, achititsidwa chisoni ndinkhanizi!—Yerekezerani ndi 1 Mafumu 15:4, 5.
8. Kodi mtumwi Paulo akutipatsa chitsanzo chotani cha chenjezo, ndipo kodi vuto loterolo lingachitiridwe fanizo motani?
8 Lingalirani mtumwi Paulo, amene anadalitsidwa kukhala ndi masomphenya osakhala aumunthu ndi mphamvu ndi mphatso za kuuziridwa kwaumulungu. Kuti apambane m’nkhondo yake yolimbana ndi zikhoterero zauchimo, iye anafunikira kupumphuntha—inde, kulimenya mwamphamvu—thupi lake. Kodi tidzakhutiritsidwa ndikuchita kwathu pang’ono? (Aroma 7:15-25; 1 Akorinto 9:27) Kuli ngati kuti tinali m’bwato laling’ono lopalasa patsinje wamadzi oyenda mwamphamvu ndipo tikukokedwera kumathithi ake. Kuti tipeŵe tsokali, tiyenera kupalasira komwe kukuchokera madzi molimbana ndi madzi amphamvuwo. Tingaone ngati sitikusendera mpang’ono pomwe, koma malinga ngati tipitirizabe kulimbikira mwamphamvu, sitidzagwera m’mathithiwo ndikuwonongedwa. Motsimikizirika, kusonyezedwa kwa chikondi cha Yehova Mulungu kwa ife kuyenera kutichititsa kulimbikira mwamphamvu kukhala okhulupirika kwa iye mwa kuda kusayeruzika ndi kukonda chilungamo.
Sonyezani Chikondi cha Paubale
9. Kodi ndiuphungu wotani umene mtumwi Yohane akupereka ponena za kukonda abale athu?
9 Kusonyezedwa kwa chikondi cha Mulungu kuyenera kutisonkhezeranso kukonda abale athu monga mmene Yesu Kristu amakondera ophunzira ake. (Yohane 13:1) Mtumwi Yohane moyenera kwenikweni, akuti: ‘Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu. Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.’ (1 Yohane 4:10, 11) Kwenikweni, Yesu anati njira imene ikazindikiritsa atsatiri ake ndiyo kukondana kwawo.—Yohane 13:34, 35.
10, 11. Kodi ndiziti zomwe ziri njira zina m’zimene tingasonyezere chikondi cha paubale?
10 Ife tidziŵa kuti Akristu ayenera kusonyeza chikondi cha paubale. Koma sikuli kopanda pake kudzikumbutsa njira zosiyanasiyana zimene tingasonyezere nazo kukondana konga kwa Kristu kumeneku. Chikondi choterocho chidzatithandiza kusasamala nako kusiyana kochititsidwa ndi fuko, utundu, maphunziro, mwambo, ndi mkhalidwe wachuma. Kuwonjezera apa, chikondi cha paubale chidzatisonkhezera kukumana pamodzi pamisonkhano. Ngati timakondadi abale athu, sitidzavomereza kusacha bwino kwa kunja kapena kusamva bwino pang’ono kwathupi kutilanda chisangalalo cha kusonkhana nawo ndi kugawana nawo chilimbikitso. (Aroma 1:11, 12) Kuposa apa, chikondi cha paubale chidzatipangitsa kukonzekera bwino misonkhano yathu ndikukhalamo ndi phande mokangalika kotero kuti tidandaulirane kuchikondano ndi ntchito zabwino.—Ahebri 10:23-25.
11 Bwanji nanga ponena za kuthandiza abale athu muuminisitala wakumunda? Kwaonedwa kuti akulu ndi atumiki otumikira kaŵirikaŵiri amatulukira muuminisitala wakunyumba ndi nyumba ndi enawo kapena ali okha atakhoza kutero, popanda kulingalira za kuitana ofalitsa Aufumu ofunikira thandizo muuminisitala kuti apite nawo. Kusonyeza chikondi mwanjirayi kudzapangitsa utumiki wakumunda wa akulu ndi atumiki otumikira kukhala ndi mphotho yowirikiza kaŵiri. Ndipo bwanji osapita ndi wofalitsa watsopano kuphunziro la Baibulo lapanyumba?—Aroma 15:1, 2.
12. Kodi 1 Yohane 3:16-18 tidzaimvetsetsa bwanji?
12 Chikondi chidzatichititsanso kuthandiza abale athu amene angakhale nako kusoŵa kwenikweni kwa zinthu zakuthupi. Mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale. Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pomana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’chowonadi.’ (1 Yohane 3:16-18) Sitingapemphedwe pali pano kupereka miyoyo yathu mmalo mwawo, koma nthaŵi zina timakhala ndi mwaŵi wa kuwasonyeza chikondi m’njira zinanso, osati m’mawu okha kapena ndi lilime komanso ndintchito. Palibe cholakwa kufotokoza mawu a kukonda abale athu, koma sitimafuna kuchilekezera apa chikondi chathu pamene iwo ali osoŵa zinthu zakuthupi. Ndemanga ya Yesu yakuti “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira” imagwiranso ntchito pankhani ya kupereka thandizo lakuthupi.—Machitidwe 20:35.
13. (a) Kodi ndiziti zomwe ziri zowonadi zina zoyambirira zimene tinaphunzira mothandizidwa ndi gulu lowoneka ndi maso la Yehova? (b) Kodi ndimfundo yamphamvu yotani imene Charles Taze Russell anaipanga?
13 Tiri nawo mwaŵi wa kusonyeza chikondi kwa abale athu amene amatsogolera mumpingo kapena m’chigwirizano ndi gulu lowoneka ndi maso la Yehova padziko lonse. Ichi chimaphatikizapo kukhala okhulupirika kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Tiyeni tiyang’anizane nayo mfundo yakuti mosasamala kanthu ndi kubwerezabwereza kochuluka kumene tingakhale tinaliŵerenga Baibulo, sitikadakhoza kuphunzira chowonadi patokha. Sitikadachipeza chowonadi chonena za Yehova, zifuno zake ndi mikhalidwe, tanthauzo ndi kufunika kwa dzina lake, Ufumu, dipo la Yesu, kusiyana pakati pa gulu la Mulungu ndi la Satana, kapena chifukwa chimene Mulungu walolera kuipa. Nzofananadi ndi zimene pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, Charles Taze Russell, analemba mu 1914 kuti: “Kodi ife sitiri anthu odalitsidwa, achimwemwe? Kodi Mulungu wathu siwokhulupirika? Ngati pali munthu amene amadziŵa zabwino, avomereze ichi. Ngati aliyense wa inu adzapeza chinthu chirichonse chabwinopo, tiyembekezera kuti adzatiwuza. Ife sitikuchidziŵa chinthu nchimodzi chomwe chimene chiri chabwinopo kuposa zomwe tazipeza m’Mawu a Mulungu. . . . Palibe lirime kapena pensulo limene lingatisimbire mtendere, chisangalalo ndi dalitso limene chidziŵitso choyera cha Mulungu wowona chatibweretsera m’mitima ndi m’moyo wathu. Mbiri ya Nzeru za Mulungu, Chiweruzo Chachilungamo, Mphamvu ndi Chikondi zimakhutiritsa mokwanira zikhumbo za ponse paŵiri nzeru ndi mtima wathu. Sitikufunafunanso chinthu china. Palibe chomwe chingakhumbidwenso kuposa kumvetsetsa Mbiri yodabwitsayi m’maganizo mwathu.” (The Watch Tower, December 15, 1914, masamba 377-8) Mawu olembedwa bwinowa ngwowona chotani nanga!
Kutumikira Omwe Ali Kunja
14. Kodi ndimotani mmene zisonyezero za chikondi cha Mulungu ziyenera kutisonkhezerera kuchita ndi okhala kunja?
14 Kusonyezedwa kwa chikondi cha Mulungu kumene tasangalala nako kuyenera kutisonkhezera kusonyeza chikondi chapamnansi kwa anthu okhala kunja kwa mpingo. Kodi ichi tingachichite motani? Mikhalidwe njomwe ingatisonyeze kuti tingafunikire kuthandiza anansi athu ndi zinthu zakuthupi. Koma, chofunika kwenikweni nchakuti, tingasonyeze chikondi cha pamnansi mwa kubweretsera ena mbiri yabwino Yaufumu wa Mulungu ndi kuthandiza okonda chilungamo kukhala ophunzira a Yesu Kristu. Kodi timalowa mokhazikika muuminisitala wapoyera umenewu, kapena kodi tikuwunyalanyaza? Kodi wangokhala njira yobwerezabwereza kapena utumiki wamba? Kapena kodi tasonkhezeredwadi ndi chikondi cha pamnansi? Kodi timasonyeza chifundo? Kodi ndife oleza mtima, kuyembekezera anthu kuyankha? Kodi timawalimbikitsa eninyumba kulongosola malingaliro awo? Inde, mmalo mwa kungolankhula tokha, tiyeni tilole chikondi cha pamnansi kutisonkhezera kumvetsera ndikukhala ndi makambitsirano ofupa a Baibulo ndi anthu amene timakumana nawo muuminisitala wathu.
15. (a) Kodi nchifukwa ninji mawu akuti “umboni wamwamwaŵi” ali abwinopo kuposa akuti “umboni wamwadzidzidzi”? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuwugwira mwaŵi wa kuchitira umboni mwamwaŵi?
15 Kodi ndife atcheru monga mmene tifunikira kukhalira kugwira mwaŵi wa kuchitira umboni mwamwaŵi? Kuyenera kudziŵidwa kuti uku sikuli kuchitira umboni wamwadzidzidzi, kuganizira kuti ndintchito yosakonzekeredwa kapena yosafunika kwenikweni. Umboni wamwamwaŵi ngwofunika kwabasi, ndipo kukonda anthu anzathu kudzatipangitsa kufunitsitsa kupanga mwaŵi wa kukhalamo ndi phande. Kuchitira umboni koteroku kumakhala kobala zipatso chotani nanga! Mwachitsanzo, pamene ankapezeka ku msonkhano wa Mboni za Yehova kumpoto kwa Italy, mbale wina anapita ku garaji kuti akabwezereko magetsi a galimoto lake. Pamene ankayembekezera, iye anachitira umboni kwa omwe anali pafupi naye naŵagawira mahandibilu oŵaitanira ku nkhani yapoyera ya Baibulo pa Sande. Chaka chimodzi pambuyo pake pamsonkhano wa mitundu yonse mu Rome, mbale wina amene iye sanamzindikire anampatsa moni mosangalala. Kodi mbaleyu anali yani? Eya, anali mmodzi wa amuna aja omwe anawagaŵira mahandibilu pagaraji chaka chimodzi chapitacho! Mwamuna uja adapita kukamvetsera nkhani yapoyera ndipo anapereka dzina lake kuti achititsidwe phunziro la Baibulo. Tsopano onse aŵiri iyeyu ndi mkazi wake ndi Mboni zodzipereka za Yehova. Palibe kukaikira kuti kuchitira umboni wamwamwaŵi kungakhale kofupa kwenikweni!
Pitirizanibe Kuvomereza Chikondi cha Mulungu
16. Kodi ndimafunso ati omwe tingachite bwino kudzifunsa tokha?
16 Yehova wachulukadi m’kusonyeza chikondi kwa zolengedwa zake. Monga momwe tawonera, Malemba amatipatsa zitsanzo zabwino za anthu omwe avomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera. Moyenerera kwenikweni, wamasalmo wouziridwa anadzuma kuti: ‘Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!’ (Salmo 107:8, 15, 21, 31) Kodi tiyenera kuvomereza chisomo cha Mulungu kwachabe? Zimenezo zisachitike konse! (2 Akorinto 6:1) Chotero lekani aliyense wa ife payekha adzifunse kuti: ‘Kodi ndimayamikiradi kusonyezedwa kwa chikondi cha Mulungu kumene ndasangalala nako kale ndipo ndikukuyembekezera mwachidaliro kusangalala nako mtsogolomu? Kodi kukundisonkhezera kukonda Yehova ndimtima wanga, moyo, malingaliro, ndi nyonga yanga yonse? Kodi ndiridi wokhoterera kwa Mulungu? Kodi ndimakonda chilungamo ndikuda kusayeruzika? Kodi ndikuchisonyeza chikondi cha paubale? Ndipo kodi ndikuyesera mosamalitsa chotani kuyenda m’mapazi a Yesu muuminisitala wanga?’
17. Kodi chidzatulukapo nchiyani titavomereza mopanda dyera zisonyezero za chikondi cha Yehova Mulungu?
17 Zowonadi, pali njira zambiri zimene tingasonyezeremo chiyamikiro chathu chochokera mumtima kaamba ka zisonyezero zonse za chikondi cha Mulungu zimene takumana nazo. Mwa kuwugwira mokwanira mwaŵi wa kusonyeza chiyamikiro choterocho, tidzachititsa mtima wa Atate wathu wakumwamba kusangalala, ndikukhala dalitso kwa ena, ndikulandira chisangalalo, mtendere, ndi chikhutiro. Chotero lekani tipitirizebe kuvomereza kusonyezedwa kwa chikondi cha Mulungu mopanda dyera.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi chimafunikira nchiyani kuti tivomereze chikondi cha Mulungu mopanda dyera?
◻ Kodi tingachenjere motani ndi ziyeso?
◻ Kodi ndiziti zimene ziri njira zina zosonyezera chikondi cha paubale?
◻ Kodi ndimotani mmene kusonyezedwa kwa chikondi cha Yehova kuyenera kutisonkhezerera kuchita ndi anansi athu?
[Chithunzi patsamba 17]
Tiyenera kulimbana ndi zikhoterero zauchimo kuti tipeŵe tsoka
[Chithunzi patsamba 18]
Akulu amasonyeza chikondi cha paubale mwa kutsagana ndi ena muuminisitala Waufumu
[Chithunzi patsamba 19]
Charles Taze Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, anapereka chisamaliro ku mtendere, chisangalalo, ndi dalitso zimene Mulungu yekha ndiye angapereke