PHUNZIRO 49
Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?—Mbali Yoyamba
Anthu akakwatirana kumene, amayembekezera kuti azikhala mosangalala ngati mmene zinalili pa tsiku la ukwati wawo. Ndipo zimenezi n’zotheka. Akhristu omwe akhala m’banja kwa nthawi yaitali n’kumayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo, amadziwa kuti zimenezi n’zotheka.
1. Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa amuna okwatira?
Yehova anapatsa mwamuna wokwatira udindo wokhala mutu wa banja lake. (Werengani Aefeso 5:23.) Choncho Yehova amayembekezera kuti mwamuna azisankha zinthu zimene zingathandize banja lake. Baibulo limalangiza amuna okwatira kuti: “Pitirizani kukonda akazi anu.” (Aefeso 5:25) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Mwamuna wachikondi amachita zinthu mokomera mtima mkazi wake akakhala kwaokha kapena akakhala ndi anthu ena. Amaonetsetsa kuti mkazi wake ndi wotetezeka komanso akusangalala ndipo amamupatsa zinthu zonse zimene amafunikira. (1 Timoteyo 5:8) Koma chofunika kwambiri ndi choti amathandiza mkazi wake kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Mateyu 4:4) Mwachitsanzo, amapemphera ndiponso kuwerenga Baibulo limodzi ndi mkazi wake. Mwamuna akamakonda ndi kusamalira mkazi wake, amakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.—Werengani 1 Petulo 3:7.
2. Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa akazi okwatiwa?
Mawu a Mulungu amanena kuti mkazi wokwatiwa “azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Kodi angapange bwanji zimenezi? Angaganizire makhalidwe abwino amene mwamuna wake ali nawo ndiponso khama limene amachita pomusamalira komanso kusamalira ana awo. Angasonyezenso kuti amalemekeza mwamuna wake akamagwirizana ndi zimene mwamuna wake wasankha, akamamulankhula mwaulemu ndiponso akamalankhula zinthu zabwino zokhudza mwamunayo ngakhale mwamuna wake atakhala kuti satumikira Yehova.
3. Kodi anthu okwatirana angalimbitse bwanji banja lawo?
Ponena za anthu okwatirana, Baibulo limati: “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.” (Mateyu 19:5) Zimenezi zikutanthauza kuti ayenera kuyesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti chikondi chawo chisayambe kuchepa. Iwo angachite zimenezi akamayesetsa nthawi zonse kupeza nthawi yochezera limodzi, kuuzana zakukhosi ndiponso kuuzana maganizo awo momasuka komanso mwachikondi. Kupatulapo Yehova, iwo amaona kuti mwamuna kapena mkazi wawo ndi wofunika kwambiri kuposa chinthu kapena munthu wina aliyense. Komanso amayesetsa kupewa kuzolowerana kapena kucheza kwambiri ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wawo.
FUFUZANI MOZAMA
Onani mfundo za m’Baibulo zomwe zingathandize kuti banja lanu likhale lolimba.
4. Amuna, muzikonda komanso kusamalira bwino akazi anu
Baibulo limanena kuti: “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo.” (Aefeso 5:28, 29) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amakonda ndi kusamalira mkazi wake?
Werengani Akolose 3:12, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mwamuna angamusonyeze bwanji mkazi wake makhalidwe amenewa?
5. Akazi, muzikonda ndi kulemekeza amuna anu
Baibulo limalimbikitsa akazi kuti azilemekeza amuna awo kaya amatumikira Yehova kapena ayi. Ngati mwamuna wanu salambira Yehova, n’zosakayikitsa kuti mumafuna atayamba kumutumikira. Werengani 1 Petulo 3:1, 2, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi njira yabwino yothandizira mwamuna wanu kuti ayambe kutumikira Yehova, ndi kumulalikira nthawi zonse kapena kumulemekeza kwambiri komanso kumusonyeza makhalidwe abwino? N’chifukwa chiyani mukutero?
Zimakhala bwino kwambiri mwamuna ndi mkazi wake akamasankha zochita limodzi. Komabe nthawi zina, mkazi sangagwirizane ndi zimene mwamuna wake wasankha. Zikatere, mkaziyo ayenera kufotokoza maganizo ake modekha ndiponso mwaulemu ndipo ayenera kuzindikira kuti Yehova anapereka udindo kwa mwamuna wake wosankha zinthu zokhudza banja lawo. Choncho, ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti zimene mwamunayo wasankha ziyende bwino. Akamachita zimenezi, amakhala akuthandizira kuti banja lake likhale losangalala. Werengani 1 Petulo 3:3-5, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yehova amamva bwanji mkazi akamalemekeza mwamuna wake?
6. N’zotheka kuthana ndi mavuto am’banja lanu
Palibe banja lopanda mavuto. Choncho, anthu okwatirana ayenera kuchita zinthu mogwirizana kuti athane ndi mavuto awo. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, n’chiyani chikusonyeza kuti mwamuna ndi mkazi wake uja anasiya kukondana ngati kale?
Kodi anachita chiyani kuti alimbitse banja lawo?
Werengani 1 Akorinto 10:24 ndi Akolose 3:13. Pambuyo powerenga lemba lililonse, mukambirane funso ili:
Kodi kutsatira malangizo amenewa kungathandize bwanji kuti banja likhale lolimba?
Baibulo limanena kuti tiyenera kumalemekezana. Kulemekezana kumaphatikizapo kuchitirana zinthu mokoma mtima ndiponso mwaulemu. Werengani Aroma 12:10, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi anthu okwatirana ayenera kudikirira kuti mwamuna kapena mkazi wawo ndi amene ayenera kuyamba kuwalemekeza kuti nawonso azimulemekeza? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZIMENE ENA AMANENA: “Banja lathu silikuyenda bwino chifukwa sitigwirizananso ngati kale.”
Kodi mungawathandize bwanji kudziwa kuti Baibulo likhoza kuwathandiza kuti banja lawo liziyenda bwino?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Mwamuna ndi mkazi wake angamasangalale ngati amakondana, kulemekezana ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo.
Kubwereza
Kodi mwamuna angachite chiyani kuti banja lake likhale losangalala?
Kodi mkazi angachite chiyani kuti banja lake likhale losangalala?
Ngati muli pabanja, kodi ndi mfundo ya m’Baibulo iti yomwe ingathandize kuti banja lanu likhale lolimba?
ONANI ZINANSO
Onani zimene zingakuthandizeni kuti muzisangalala m’banja lanu.
Onerani nyimbo yomwe ikusonyeza ubwino wogwiritsa ntchito malangizo a Mulungu m’banja lanu.
Onani zimene kugonjera mwamuna monga mutu wa banja kumatanthauza.
“Akazi, N’chifukwa Chiyani Muyenera Kugonjera Amuna Monga Mutu?” (Nsanja ya Olonda, May 15, 2010)
N’chiyani chinathandiza banja lina kulimbana ndi mavuto aakulu kuphatikizapo kutha kwa banja lawo?