Chilengedwe Chimati, ‘Sangaŵiringule’
“Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuŵiringula.”—AROMA 1:20.
1, 2. (a) Kodi Yobu, moŵaŵidwa mtima, anadandaula motani kwa Yehova? (b) Kodi ndikudzibweza kotani kumene Yobu anachita potsirizira pake?
YOBU, munthu wanthaŵi zakale amene anali ndi umphumphu wosasweka kwa Yehova Mulungu, anaikidwa pachiyeso chowopsa ndi Satana. Mdyerekezi anali atachititsa Yobu kutayikiridwa chuma chake chonse chakuthupi, anadzetsa imfa pa ana ake aamuna ndi aakazi, ndipo anamkantha ndi nthenda yowopsa. Yobu analingalira kuti anali Mulungu amene anamdzetsera masoka ameneŵa, ndipo anadandaula moŵaŵidwa mtima kwa Yehova kuti: “Chikukomerani kodi kungosautsa, . . . kuti mufunsa mphulupulu yanga, ndi kulondola choipa changa; chinkana mudziŵa kuti sindili woipa.”—Yobu 1:12-19; 2:5-8; 10:3, 6, 7.
2 Nthaŵi ina pambuyo pa zimenezi, mawu a Yobu kwa Mulungu anasonyeza kusintha kwake kotheratu: “Ndinafotokozera zimene sindinazizindikira, zondidabwiza, zosazidziŵa ine. Kumva ndidamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso; chifukwa chake ndekha [ndidzibweza, NW], ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.” (Yobu 42:3, 5, 6) Kodi chinachitika nchiyani chimene chinachititsa mkhalidwe wa maganizo wa Yobu kusintha?
3. Kodi ndimfundo yotani yatsopano imene Yobu anaphunzira ponena za chilengedwe?
3 Panthaŵiyo, Yehova anali atayang’anizana ndi Yobu m’kavumvulu. (Yobu 38:1) Iye anali atafunsa Yobu mafunso ambiri. ‘Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Kodi ndani anatseka nyanja ndi zitseko ndi kuika malire a mafunde? Kodi ungachititse mitambo kugwetsa mvula yake padziko lapansi? Kodi ungameretse udzu? Kodi ungamangirire pamodzi magulu a nyenyezi ndi kuziyendetsa m’njira yake?’ M’machaputala 38 mpaka 41 a buku la Yobu, Yehova anafunsa Yobu mafunso ochuluka onga ngati amenewo ndi enanso ambiri ponena za chilengedwe Chake. Iye anachititsa Yobu kuwona mpata waukulu umene ulipo pakati pa Mulungu ndi munthu, akumakumbutsa Yobu mwamphamvu ponena za nzeru ndi mphamvu zosonyezedwa m’chilengedwe cha Mulungu, zinthu zimene zili zosatheka kuchitidwa kapena ngakhale kuzindikiridwa ndi Yobu. Yobu, pokhala atazunguzika maganizo ndi mphamvu yochititsa mantha ndi nzeru yaikulukulu ya Mulungu wamphamvuyonse yosonyezedwa m’chilengedwe Chake, anachita mantha poganiza kuti iye anali atatsutsana ndi Yehova mopanda nzeru. Chotero anati: “Kumva ndidamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso.”—Yobu 42:5.
4. Kodi tiyenera kuzindikira chiyani kuchokera ku zolengedwa za Yehova, ndipo kodi mkhalidwe wa awo amene amalephera kuziona ngwotani?
4 Zaka mazana ambiri pambuyo pake wolemba Baibulo wouziridwa anatsimikizira kuti mikhalidwe ya Yehova ingakhoze kuwonedwa m’chilengedwe chake. Mtumwi Paulo analemba pa Aroma 1:19, 20 kuti: “Chodziŵika cha Mulungu chaonekera mkati mwawo; pakuti Mulungu anachiwonetsera kwa iwo. Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuŵiringula.”
5. (a) Kodi ndichikhumbo chachibadwa chotani chimene anthu ali nacho, ndipo kodi ndimotani mmene ena amachikhutiritsira molakwa? (b) Kodi Paulo anauza Agiriki a ku Atene kuchita chiyani?
5 Munthu analengedwa ndi chikhumbo chobadwa nacho cha kulambira mphamvu ina yapamwamba. Dr. C. G. Jung, m’buku lake lakuti The Undiscovered Self, anasonyeza chikhumbo chimenechi kukhala “mkhalidwe wachibadwa wopezeka mwa munthu yekha, ndipo maumboni ake angawonedwe m’mbiri yonse ya anthu.” Mtumwi Paulo ananena za chikhumbo chobadwa nacho cha munthu cha kulambira, chimene chinapereka chifukwa chimene Agiriki a ku Atene anapangira mafano ndi maguwa operekerapo nsembe kwa milungu yambiri, yodziŵika ndi yosadziŵika. Paulo anadziŵikitsanso Mulungu wowona kwa iwo nasonyeza kuti iwo anayenera kukhutiritsa chikhumbo chachibadwa chimenechi moyenera mwa kufunafuna Yehova Mulungu wowona, “kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:22-30) Popeza kuti tili pafupi kwambiri ndi chilengedwe chake, tikhozanso kuzindikira mikhalidwe yake mosavuta.
Kayendedwe ka Madzi Kodabwitsa
6. Kodi ndimikhalidwe yotani ya Yehova yomwe timaona m’kayendedwe ka madzi?
6 Mwachitsanzo, kodi ndimikhalidwe yotani ya Yehova imene timazindikira ponena za kukhoza kwa mitambo yowoneka ngati thonje kusunga matani ambiri amadzi? Timawona chikondi chake ndi nzeru, popeza kuti mwakutero amapereka mvula kuti dziko lapansi libale zomera. Iye amachita zimenezi mwanjira ya mpangidwe wodabwitsa wophatikizidwa m’kayendedwe ka madzi, kotchulidwa pa Mlaliki 1:7 kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” Buku la m’Baibulo la Yobu limanena molunjika za mmene zimenezi zimachitikira.
7. Kodi madzi amachoka motani m’nyanja kupita kumitambo, ndipo kodi ndimotani mmene mitambo yonga thonje imasungira matani ambiri a madzi?
7 Pamene madzi a m’mitsinje ayenda kumka kunyanja, samakhala komweko. Yehova “amakweza timadontho tamadzi kumwamba kuchokera m’nyanja ndi kuvumbitsa mvula munkhungu imene wapanga.” Chifukwa chakuti madzi ali mumpangidwe wa nthunzi ndipo potsirizira pake amakhala nkhungu, “mitambo imalenjekeka pamwamba, ntchito yodabwitsa ya luso lake lachikwanekwane.” (Yobu 36:27; 37:16; The New English Bible) Mitambo imayandama kokha ngati ili mumpangidwe wa nkhungu: “Amanga madzi m’mitambo yake—nkhunguyo sing’ambika pansi pake.” Kapena monga momwe wotembenuza wina amanenera: “Asunga madzi otsekeredwa m’mitambo yaikulu yochindikala, ndipo mitamboyo sing’ambika pansi pake.”—Yobu 26:8, The Jerusalem Bible; NE.
8. Kodi ndimwanjira zosiyanasiyana zotani zimene ‘michenje ya kuthambo’ imatsanulidwira ndi kumaliza kayendedwe?
8 ‘Kodi ndani akhoza kutsanulira michenje ya kuthambo imeneyi’ kuti ichititse mvula kuvumba padziko lapansi? (Yobu 38:37) Ndiye Uyo amene ‘luso lake lachikwanekwane’ linaika zimenezi m’malo ake poyamba, amene ‘amavumbitsa mvula munkhungu imene wapanga.’ Ndipo kodi nchiyani chimene chimafunika kuvumbitsa mvula munkhungu? Payenera kukhala tinthu tolimba tating’ono kwambiri, tonga ngati fumbi kapena timibulu tamchere—toyambira pazikwizikwi kufikira zikwi mazana ambiri pa cubic sentimita imodzi iliyonse—toti tichite ngati chithima choumbirapo timadontho tamadzi. Kukuyerekezeredwa kuti kumafunikira timadontho tamumtambo miliyoni imodzi kuti dontho lamvula lodziŵika bwino lipangike. Ndipambuyo pa kuchitika kwa nzonsezi pamene mitambo imagwetsa madzi ake padziko lapansi kuti apange mitsinje imene imabwezera madziwo kunyanja. Motero ndimo mmene madzi amayendera. Ndipo kodi zonsezi zinangochitika mwangozi? Kulingalira kotero ‘nkosaŵiringulikadi’!
Magwero Amodzi a Nzeru ya Solomo
9. Kodi nchiyani chimene Solomo anawona kukhala chodabwitsa ponena za mtundu wina wa nyerere?
9 M’nthaŵi zakale, panalibe munthu amene anali ndi nzeru zofanana ndi za Solomo. Yochuluka ya nzeru imeneyo inali yonena za chilengedwe cha Yehova: “Nakamba [Solomo] za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebano kufikira hisopi wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwaŵa pansi ndi za nsomba.” (1 Mafumu 4:33) Anali Mfumu Solomo mmodzimodziyo amene analemba kuti: “Pita kunyerere, wolesi iwe, penya njira zawo nuchenjere; ziribe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe; nizituta dzinthu zawo m’masika.”—Miyambo 6:6-8.
10. Kodi fanizo la Solomo lonena za nyerere zotuta dzinthu linatsimikiziridwa motani?
10 Kodi ndani anaphunzitsa nyerere kusunga chakudya m’malimwe choti chidzafike m’dzinja? Kwazaka mazana ambiri kulondola kwa mafotokozedwe a Solomo a nyerere zimenezi zimene zinatuta mbewu ndi kuzisunga kuti zikagwiritsiridwe ntchito m’dzinja kunakayikiridwa. Palibe aliyense amene anapeza umboni uliwonse wa kukhalapo kwake. Komabe, mu 1871, wophunzira mikhalidwe ya zomera ndi zinyama wa ku Britain anatulukira nkhokwe zawo zapansi, ndipo kulondola kwa Baibulo posimba za nyererezo kunachilikizidwa. Koma kodi nyerere zimenezi zinapeza motani nzeru yowoneratu zinthu patali m’chilimwe kuti dzinja likudza ndi nzeru yodziŵa zochita? Baibulo lenilenilo limafotokoza kuti zolengedwa zambiri za Yehova zili ndi nzeru yachibadwa yozithandiza kukhala ndi moyo. Nyerere zotuta dzinthuzo zili gulu la olandira dalitso limeneli kwa Mlengi wawo. Pa Miyambo 30:24 pamanena za izo kuti: “Zipambana kukhala zanzeru.” Kunena kuti nzeru imeneyo inangokhalapo mwangozi nkopanda nzeru; ndipo kulephera kuzindikira Mlengi wanzeru amene anazichititsa kukhalapo nkosaŵiringulika.
11. (a) Kodi nchifukwa ninji mtengo waukulukuluwo wa sequoia uli wochititsa mantha kwambiri? (b) Kodi nchiyani chimene chili chodabwitsa kwambiri ponena za mchitidwe woyambirira wa photosynthesis?
11 Munthu woimirira patsinde la mtengo waukulukulu wa sequoia, wodabwa ndi ukulu wake waulemerero, momvekera bwino amadziona monga ngati nyerere yaing’ono. Ukulu wa mtengowo ngwochititsa mantha: wa mamita 90 kutalika kwake, mamita 11 thunthu lake, kuchindikala kwa khungwa lake 0.6 ya mita, mitsitsi yake ikumayala pansi mahekita 1.2 kapena 1.6. Komabe, zochititsa mantha kwambiri ndizo mmene zinthu zimapangidwira mkati mwake ndi mmene kutentha ndi kuunika kumaloŵetsedweramo m’kukula kwake. Masamba ake amatenga madzi kumitsitsi, carbon dioxide mumpweya, ndipo nyonga yopangira suga kuchokera kudzuŵa ndi kutulutsa okosijeni—mchitidwe umene zomera zimapangira chakudya wotchedwa kuti photosynthesis umene umaphatikizapo michitidwe ya makemikolo 70, imene yoŵerengeka chabe ndiyo imamvetsetseka. Modabwitsa, mchitidwe wake woyamba umadalira pakuunika kwa kudzuŵa kumene kuli ndi maonekedwe oyenera, cheza chautali woyenera; apo phuluzi sikungaloŵetsedwe ndi tizidutswa ta chlorophyll kuti kuyambitse mchitidwe wa photosynthesis.
12. (a) Kodi nchiyani chimene chili chodabwitsa ponena za kugwiritsira ntchito madzi kwa mtengo wa sequoia? (b) Kodi nchifukwa ninji nitrogen imafunika m’kukula kwa zomera, ndipo kodi kayendedwe kake kamamalizidwa motani?
12 Chodabwitsanso nchakuti mtengowo ungathe kutsopa madzi ochuluka kuchokera m’mitsitsi kuwatengera kunsonga yake ya mtengo waukulukulu umenewu wotalika mamita 90. Umatsopa madzi ochuluka kuposa ndi amene amafunikira kuchitira photosynthesis. Madzi otsalira amatayidwa kupyolera m’masamba mwakutulutsidwira mumpweya. Zimenezi zimachititsa mtengowo kukhala woziziritsidwa, monga momwe timaziziritsidwira mwakutuluka thukuta. Kuti proteni youkulitsira ipangidwe, nitrogen iyenera kuwonjezedwa ku suga, kapena zinthu zotchedwa carbohydrates. Tsamba silingathe kugwiritsira ntchito mpweya wa nitrogen wotengedwa mumpweya, koma tizilombo tokhala munthaka timasintha mpweya wa nitrogen wa m’nthaka kukhala manitrate ndi manitrite amene amasungunuka m’madzi, amenenso amayenda kuchokera kumitsitsi kukwera kumasamba. Pamene zomera ndi zinyama zimene zagwiritsira ntchito nitrogen imeneyi m’maproteni awo zifa ndi kuvunda, nitrogen imeneyo imatulukamo, ndi kumamaliza kayendedwe kake kotchedwa nitrogen cycle. Muzonsezi, kucholoŵana kolowetsedwamo nkozunguzitsa mutu, sichinthu chochitika mwangozi.
Popanda Mawu, Zimanena!
13. Kodi nchiyani chimene miyamba yodzala nyenyezi inalengeza kwa Davide, ndipo kodi imapitirizabe kunenanji kwa ife?
13 Ndikusonyezedwa kwakukulukulu kotani nanga kwa Mlengi kumene kumachokera m’thambo lodzala nyenyezi usiku limene limachititsa mantha openyerera! Pa Salmo 8:3, 4, Davide anasonyeza mantha amene anali nawo kuti: “Pakuona ine thambo lakumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” Kwa awo amene ali ndi maso owona, makutu akumva, ndi mtima wolingalira, thambo la nyenyezi limeneli limanena, monga momwe linachitira kwa Davide kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu.”—Salmo 19:1-4.
14. Kodi nchifukwa ninji mphamvu yaikulu ya imodzi ya nyenyezi ili yofunika kwambiri kwa ife?
14 Pamene tidziŵa zambiri ponena za nyenyezi, ndipamenenso zimatiuza zambiri. Pa Yesaya 40:26, tikupemphedwa kuwona mphamvu zake zazikulu koposa, kuti: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” Mphamvu yokoka ndi mphamvu yaikulu ya imodzi ya izo, dzuŵa lathu, imachititsa dziko lapansi kuzungulira m’njira yake, kukulitsa zomera, kutifunditsa, ndipo imatheketsa kukhalapo kwa chamoyo chilichonse pano padziko lapansi. Mtumwi Paulo mouziridwa anati: “Nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m’ulemerero.” (1 Akorinto 15:41) Asayansi amadziŵa za nyenyezi zachikasu zofanana ndi dzuŵa lathuli, ndiponso nyenyezi zobiriŵira, nyenyezi zazikulu zofiira, nyenyezi zoyera, nyenyezi za neutron, ndi nyenyezi zomaphulika zimene zimatulutsa mphamvu yaikulu.
15. Kodi nchiyani chimene anthu otulukira zinthu ambiri aphunzira ku chilengedwe ndi kuyesa kutsanzira?
15 Akatswiri ambiri otulukira zinthu aphunzira ku chilengedwe ndipo ayesayesa kutsanzira maluso a zolengedwa zamoyo. (Yobu 12:7-10) Onani mbali zapadera zoŵerengeka chabe za chilengedwe. Mbalame zakunyanja zokhala ndi maselo osefa madzi amchere; nsomba ndi nyesi zimene zimatulutsa magetsi; nsomba, nyongolotsi, ndi tizilombo touluka timene timatulutsa kuunika kozizira; mileme ndi nsomba za dolphin zimene zimagwiritsira ntchito namaloŵe poyenda; mavu amene amapanga mapepala; nyerere zimene zimamanga milatho; ntchenzi zimene zimamanga maiŵe; njoka zimene zili ndi thermometer (njira zopimira kutentha ndi kuzizira) mkati mwake; tizilombo ta m’maiŵe timene timagwiritsira ntchito njira zopumira ndi zoloŵera m’madzi; maoctopus amene amayenda ndi mphamvu yakutsopa ndi kutulutsa madzi; akangaude amene amamanga nyumba za mitundu isanu ndi iŵiri ndi kupanga makomo a misampha, maukonde, ndi makhwekhwe ndi amene amabala ana amene amauluka ndi mphepo, akumayenda makilomita zikwi zambiri m’mwamba kwambiri; nsomba ndi nkhanu za m’nyanja zimene zimagwiritsira ntchito matanki oziyandamitsa mofanana ndi zombo zoyenda pansi pa madzi; ndi mbalame, tizilombo, akamba a kunyanja, nsomba, ndi zolengedwa zoyamwitsa zimene zimachita zodabwitsa mwakusamuka—maluso amene sayansi singafotokoze.
16. Kodi ndichowonadi chotani cha sayansi chimene Baibulo linasunga zaka mazana ambiri asayansi asanachitulukire?
16 Baibulo linasunga cholembedwa cha chowonadi cha sayansi zaka zikwi zambiri asayansi asanachidziŵe. Chilamulo cha Mose (zaka za zana la 16 B.C.E.) chinasonyeza kuzindikiridwa kwa tizilombo topatsa matenda zaka zikwi zambiri Pasteur asanakhaleko. (Levitiko, machaputala 13, 14) M’zaka za zana la 17 B.C.E., Yobu anati: “Ayala . . . dziko pa chabe.” (Yobu 26:7) Zaka chikwi chimodzi Kristu asanafike, Solomo analemba za kayendedwe ka mwazi m’thupi; asayansi ya zamankhwala anafunikira kuyembekezera kufikira zaka za zana la 17 C.E. kuti aphunzire zimenezi. (Mlaliki 12:6) Nthaŵi imeneyo isanadze, lemba la Salmo 139:16 linasonyeza chidziŵitso cha dongosolo la majini kuti: “Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziŵalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.” M’zaka za zana la 7 B.C.E., akatswiri a zomera ndi zinyama asanazindikire za kusamuka kwa zolengedwa zina, Yeremiya analemba monga momwe kwalembedwera pa Yeremiya 8:7 kuti: “Chumba cha mlengalenga chidziŵa nyengo [yakusamuka, NE]; ndipo njiŵa ndi namzeze ndi chingalu ziyang’anira nyengo yakufika kwawo.”
“Mlengi” Amene Anthanthi ya Chisinthiko Akusankha
17. (a) Kodi nchiyani chimene lemba la Aroma 1:21-23 limanena ponena za anthu ena omwe amakana kuwona kukhalapo kwa Mlengi wanzeru wochilikiza zolengedwa zodabwitsa? (b) M’kunena kwina, kodi anthanthi ya chisinthiko akusankha chiyani kukhala “mlengi” wawo?
17 Lemba lina ponena za anthu ena amene amakana kuzindikira kukhalapo kwa Mlengi wanzeru wochilikiza zolengedwa zodabwitsa limati: “Anakhala opanda pake m’maganizo awo, ndipo unada mtima wawo wopulukira. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa; nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosawonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu wowonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwaŵa.” Iwo “anasandutsa chowonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo.” (Aroma 1:21-23, 25) Zili chimodzimodzi ndi asayansi ochilikiza chisinthiko, amene, kwenikweni, amalemekeza ntandadza wongoyerekezera woyambira pa protozoa, kudzanso nyongolotsi, nsomba, ndiyeno zamoyo zokhala m’madzi ndi pamtunda, zokwaŵa, zoyamwitsa kufikira “anthu onga nyani” monga “mlengi” wawo. Komabe, iwo amadziŵa kuti palibiretu kamoyo kosacholoŵana ka selo limodzi komwe kanayambitsa ntandadza umenewo. Kamoyo wamba kodziŵika bwino kwambiri kali ndi maatomu mamiliyoni zikwi zana limodzi, kokhala ndi michitidwe ya makemikolo zikwi zambiri yochitika mkati mwake panthaŵi imodzimodzi.
18, 19. (a) Kodi ndani amene ali Munthu woyenera kupatsidwa thamo la kuyambitsa moyo? (b) Kodi nchilengedwe chachikulu motani cha Yehova chomwe tingathe kuwona?
18 Yehova Mulungu ndiye Mlengi wa moyo. (Salmo 36:9) Iye ndiye Wochititsa Zinthu Woyamba wamkulu. Dzina lakelo, Yehova, limatanthauza kuti “Amene amachititsa kukhalako.” (NW) Zolengedwa zake sitingathe kuziŵerenga. Ndithudi pali zolengedwa mamiliyoni ambiri zimene munthu samadziŵa. Lemba la Salmo 104:24, 25 limatchula za zimenezi kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru.” Lemba la Yobu 26:14 nlolunjika pazimenezi kuti: “Tawonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong’onezo chaching’ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akuzindikiritsa ndani?” Timawona malekezero a njira zake pang’ono chabe, timamva zonong’onezedwa zochepa, koma kuzindikira ukulu wonse wa kugunda kwa mphamvu yake nkosatheka.
19 Komabe, tili ndi magwero abwino kwambiri omuwonera kuposa kupyolera m’chilengedwe chake. Magwero abwino kwambiri amenewo ndiwo Mawu ake, Baibulo. Tsopano tikutembenukira kumagwero amenewo m’nkhani yotsatirayi.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchiyani chimene Yobu anaphunzira pamene Yehova ananena naye m’kavumvulu?
◻ Kodi nchifukwa ninji Paulo ananena kuti anthu ena alibe mawu akuŵiringula?
◻ Kodi madzi amayenda motani?
◻ Kodi ndizinthu zofunika zotani zimene kuunika kwa dzuŵa kumatichitira?
◻ Kodi ndichowonadi cha sayansi chotani chimene Baibulo linavumbula asayansi asanachitulukire?