Lingaliro la Baibulo
Kugonana kwa Ofanana Ziŵalo—Nkulekeranji?
“Sindiganiza kuti Mulungu amasamala kwenikweni ponena za kukhoterera kwa za kugonana kwa munthu. Iye amasamala za mmene timatsogolera miyoyo yathu. Ndipo kugonana sikuli kanthu.”—Chiŵalo cha gulu la ogonana ofanana ziŵalo lophunzira Baibulo.
CHIŴERENGERO chomakula cha anthu akulandira kugonana kwa ofanana ziŵalo monga njira yongosiyanako ya moyo. Kodi Mulungu amavomereza?
Pamene kuli kwakuti anthu ambiri asintha kawonedwe kawo ndipo ena ake ali osagamulapo, lingaliro la Baibulo liri lomvekera bwino kotheratu: “Sudzagonana ndi mwamuna monga mmene ungachitire ndi mkazi. Ichi ndi chinthu chodedwa,” limalongosola tero Baibulo. (Levitiko 18:22, The New Jerusalem Bible) Palibe zodzikhululukira, palibe zilolezo, palibe chikaikiro—kugonana kwa ofanana ziwalo kuli konyansa m’maso mwa Mulungu.a Kwa Aisrayeli akale okhala pansi pa Chilamulo cha Mose, chilango chinali imfa. (Levitiko 20:13) Ndipo ndi kufika kwa Chikristu, kutsutsa kwa Mulungu kwa kugonana kwa ofanana ziŵalo kunapitirizabe.—1 Akorinto 6:9, 10.
Mulungu Ali Wotsutsa—Nchifukwa Ninji?
Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu ali wotsutsa mowuma khosi chotero kulinga ku iko? Chifukwa chimodzi chalongosoledwa pa Yesaya 48:17: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, Amene ndikuphunzitsa kupindula, Amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” Mawu amenewo amabwera kuchokera kwa Mkonzi wa malamulo a chibadwa a chilengedwe chaponseponse. Iye amadziŵa kapangidwe kathu ka kuthupi, maganizo, malingaliro, ndi uzimu. Iye amatsutsa kugonana kwa ofanana ziŵalo chifukwa chakuti, pakati pa zinthu zina, iko sikumapindulitsa munthuyo. Kubwereramo m’kalata ya mtumwi Paulo kwa Akristu okhala mu Roma kumatsimikizira chimenechi. Iye analemba kuti:
“Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi awo anasandutsa machitidwe awo achibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chawo wina ndi mnzake, amuna okha okha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwawo. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m’chidziŵitso chawo, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera.”—Aroma 1:26-28.
Dziŵani kuti, kugonana kwa ofanana ziŵalo kumatchedwa osati kokha “za manyazi,” “chamanyazi,” ndi “chosayenera” komanso “chosalingana ndi chibadwidwe.” Ponena za mavesi amenewa, ripoti lochokera ku Church of England limanena kuti: “Chimene Paulo akutanthauza ndi kunena kuti ‘chosakhala chachibadwidwe’ chiri ‘chosakhala chachibadidwe’ kwa mtundu wa anthu mkapangidwe ka chilengedwe cha Mulungu. M’chitidwe wonse wa kugonana kwa ofanana ziŵalo uli kupatuka kuchoka ku kakhazikitsidwe ka chilengedwe ka Mulungu.” Katswiri wa makhalidwe a anthu Weston LaBarre anakutcha iko kukhala “kukhumudwitsa kwa munthu mwini ndi mkhalidwe wofunika wachibadwa wathupi la anthu ena.” Chimenechi chimagwirizana ndi tanthauzo la liwu la Chigriki logwiritsiridwa ntchito m’Baibulo ndipo lotembenuzidwa “chibadwa” kapena, “molingana ndi chibadwa.”
Sichiri chodabwitsa kuti “kupatuka [kulikonse] kuchoka ku kakhazikitsidwe ka chilengedwe cha Mulungu” kumatuta zotulukapo zoipa (monga mmene mbiri yoipa ya munthu ndi malo ozungulira zasonyezera). Ogonana ofanana ziŵalo ‘amalandira mwa iwo eni mphotho ya kuyenera kulakwa kwawo.’ M’mawu ena, moyo wawo umakhala moyo wa kusokera kwa kugonana kosakhala kwachibadwidwe; chotero, moyo wopanda chivomerezo cha Mulungu. M’kuwonjezerapo, iwo angavutike ndi kuvulala kwakuthupi chifukwa cha zilakolako zawo.b
Zipatso Zoipa
Paulo akunenanso kuti ogonana ofanana ziŵalo “akatenthetsana [m’lingaliro lenileni, kutenthedwa] ndi chilakolako chawo ndi wina ndi mnzake.” Pamene kuli kwakuti kulingalira kolakwika kungasonkhezere zikhumbo zolakwika ngakhale m’kugonana kwa osiyana ziŵalo, chikuwoneka kuti ndi kuyembekezera maunansi a kugonana oipa, chilakolako chosalamulirika chimatentha ngakhale molimbirako. “Moyo Wachikondi Chapaŵiri cha Ngozi,” nkhani yofalitsiwa m’magazini ya Newsweek, inanena kuti: “Amuna ndi akazi ochita kugonana kwa a ziŵalo zonse mofananamo kaŵirikaŵiri amalankhula za kudzutsidwa ‘kwamphamvu’, ‘nyonga yosiyanako’ yomwe amakhala nayo ndi chiŵalo chawo chogonanira. James akukumbukira iko kukhala monga ‘kuwuluka mumlengalenga. Kunali komwerekeretsa, kwakuya.’” Pokhala otenthedwa motero, ogonana ofanana ziŵalo ambiri ali ndi ogonana nawo ochuluka (ena ali ndi mazana angapo), ndipo kwa ena chilakolako chawo chimawakakamiza kuchita kugonana nthaŵi zambiri pa tsiku, ngakhale ndi alendo kotheratu. Kachitidwe kopanda lamulo kameneka sikamatsogolera kokha ku nthenda zopatsirana, zonga ngati nthenda ya chiwindi, koma kamabweretsa nsanje, kupanda chisungiko, ndi kupanda chimwemwe, mongadi mmene chimachitikira m’maunansi opanda lamulo a kugonana kwa osiyana ziŵalo.
Pamene munthu agonjera ku “chilakolako chonyansa,” iye angamangidwe ukapolo. (1 Atesalonika 4:5) Ku utali wotani? Kulozera ku AIDS, wogonana wofanana ziŵalo mmodzi anavomereza kuti: “Ngakhale utayang’anizidwa ndi imfa yoipa, yochititsa mantha, chisonkhezero cha kugonanacho chiri chisonkhezero champhamvu.” Chimenecho chimakumbutsa chenjezo la Baibulo lakuti: “Musamalola uchimo uchite ufumu m’thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake.”—Aroma 6:12.
Popeza kuti mkhalidwe woipa wa chisembwere uli wozikidwa kwakukulukulu pa kudzikondweretsa, iko kaŵirikaŵiri kumatsogolera ku machitidwe omwerekera owonjezereka. Ndipo chibadwa chochimwa cha munthu pokhala chimene chiri, pamene kachitidweko kakhala kofala, kusangalatsa kwake kumayamba kuchepekera. Chotero, ogonana ofanana ziŵalo ena afikira ku sadomasochism ndi machitachita ena oipa.c Kuchitira ndemanga pa Baibulo kwina kumanena kuti “chiyambukiro cha maziko oterowo ndi zilakolako zosakhala zachibadwa . . . zinakhoterera kumwereketsa maganizo; kutsitsa munthu kufika ku mlingo wa nkhalwe; kuwononga nzeru ya kuzindikira.” Wophunzira Baibulo anagwirizanitsa kugonana kwa ofanana ziŵalo ndi “ziwawa, zimene zinali zosiyana kotheratu ndi lingaliro, chibadwa, ndi eni ake ndi ubwino wa wina ndi mnzake.”
Miyezo ya Baibulo Imabweretsa Mtendere
Tingakhale achiyamikiro kuti Mulungu samasintha miyezo yake kokha kuti akhutiritse zosangalatsa zomapita kapena zikhumbo zomwerekeretsa za anthu. Mongadi mmene iye samavomerezera kuipitsa dziko lapansi kapena kunama kokha chifukwa chakuti anthu ambiri amafuna kutero, chotero samalekerera kugonana kwa ofanana ziŵalo ngakhale kuti ambiri amakuchirikiza iko ndi changu. Mosasamala kanthu za njira imene anthu amachilikiza, Yehova amafuna ife kumulemekeza iye ndi kudzipindulitsa ife eni.
Mwachiyamikiro, ena akana machitachita oterowo ndipo alondola “chiphunzitso cholamitsa” chopezeka m’Mawu a Mulungu. (1 Timoteo 1:10; 1 Akorinto 6:9-11) Monga mmene yemwe kale anali wochita kugonana kwa ofanana ziŵalo analongosolera kuti: “Chomwe chimandibweretsera chisangalalo chiri chakuti tsopano ndiri ndi chikumbumtima choyera, ndipo ndimadziŵa kuti ndikukhala moyo umene uli wosangalatsa kwa Mulungu Wamphamvuyonse.”
[Mawu a M’munsi]
a Kugonana kwa ofanana ziŵalo kuli kachitidwe ka kugonana ndi munthu wa chiŵalo chofanana.
b “Amuna ogonana ofanana ziŵalo ali ndi unyinji wa mavuto a zamankhwala osiyanasiyana apadera ogwirizanitsidwa choyambirira ku njira yawo ya kugonana.” (Providing Health Care for Gay Men) Pakati pa mavuto a matenda oterowo pali kutaikiridwa kwa chilakolako chakudya, chinzonono cha ku chiŵalo chogonanira ndi kotulutsira zonyansa, kutupa ndi zironda m’malo a m’seri, kulephera kwa ziŵalo zogonanira, ndi nthenda ya Bowen.
c Sadomasochism yamasuliridwa ndi New Collegiate Dictionary ya Webster skukhala “kupeza chisangalalo kuchokera m’kupereka kuwawitsa kwakuthupi kapena kwa maganizo kaya pa anthu ena kapena pa iwemwini.”