“Musabwezere Choipa pa Choipa”
“Musabwezere choipa pa choipa. Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.”—AROMA 12:17.
1. Kodi anthu ambiri amakonda kuchita chiyani?
NTHAWI zambiri mwana akakankhidwa ndi m’bale wake, iye amafunanso kuchita chimodzimodzi. N’zomvetsa chisoni kuti si ana okha amene ali ndi mtima wobwezera. Achikulire ambiri nawonso amachita zimenezi. Munthu wina akawalakwira amafuna kubwezera. N’zoona kuti achikulire ambiri sangachite kukankha mnzawo, koma ambiri amabwezera m’njira zina zosaonetsera. Mwina amadyera miseche munthu yemwe wawalakwirayo kapena amapeza njira zoti amulepheretse kuchita bwino pazinthu zina. Kaya agwiritsa ntchito njira yotani koma cholinga chake n’kubwezera.
2. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu oona amapewa mtima wobwezera? (b) Kodi tikambirana mafunso ati ndiponso chaputala chiti cha m’Baibulo?
2 Akhristu oona amapewa mtima wobwezera, ngakhale kuti n’zovuta kutero. Iwo amayesetsa kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Musabwezere choipa pa choipa.” (Aroma 12:17) N’chiyani chimene chingatilimbikitse kutsatira malangizo abwino amenewa? Kodi ndani makamaka amene sitiyenera kum’bwezera choipa? Kodi tingapindule motani ngati tipewa kubwezera? Kuti tiyankhe mafunsowa, tiyeni tione chifukwa chimene Paulo ananenera mawu amenewa. Tionenso mmene chaputala 12 cha Aroma chimasonyezera kuti kusabwezera ndi njira yoyenera, yachikondi ndiponso yosonyeza kudzichepetsa imene tiyenera kutsatira. Motero, tikambirana zinthu zitatu zimenezi chilichonse pachokha.
“Chotero Ndikukudandaulirani”
3, 4. (a) Kodi Paulo anafotokoza chiyani kuyambira m’chaputala 12 cha Aroma, ndipo n’chifukwa chiyani anagwiritsa ntchito mawu akuti “chotero”? (b) Kodi Akhristu a ku Roma anayenera kukhudzidwa motani ndi chifundo cha Mulungu?
3 Kuyambira m’chaputala 12, Paulo anafotokoza nkhani zinayi zogwirizana zimene zimakhudza moyo wa Akhristu. Iye anafotokoza mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi Yehova, okhulupirira anzathu, anthu osakhulupirira ndiponso olamulira. Paulo anasonyeza kuti pali chifukwa chachikulu chopewera mtima wochita zinthu zolakwika ndiponso wobwezera, pamene anati: “Chotero ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu, abale.” (Aroma 12:1) Mawu akuti “chotero,” ndi ofanana ndi mawu akuti “chifukwa cha zimene zatchulidwa kale.” Paulo kwenikweni ankanena kuti, ‘chifukwa cha zimene ndangofotokozazi, ndikukudandaulirani kuti muchite zimene nditi ndikuuzeni.’ Kodi Paulo anali atawafotokozera chiyani Akhristu a ku Roma?
4 M’machaputala 11 oyambirira a kalata yake, Paulo anafotokoza mwayi wapadera kwambiri umene Ayuda ndi anthu a mitundu ina anali nawo wodzalamulira pamodzi ndi Khristu mu Ufumu wa Mulungu, chiyembekezo chimene mtundu wa Isiraeli unakana. (Aroma 11:13-36) Iwo anatha kukhala ndi mwayi wapadera kwambiri umenewu “mwa chifundo chachikulu cha Mulungu.” Kodi Akhristu anayenera kutani, Mulungu atawasonyeza chisomo chachikuluchi? Iwo anafunikira kukhudzidwa kwambiri ndiponso kuyamikira mochokera pansi pa mtima moti n’kuchita zimene Paulo ananena. Iye anati: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kulingalira.” (Aroma 12:1) Koma kodi Akhristu amenewo akanadzipereka motani “nsembe” kwa Mulungu?
5. (a) Kodi munthu angadzipereke motani “nsembe” kwa Mulungu? (b) Kodi Akhristu amafunikira kutsatira mfundo iti pamoyo wawo?
5 Paulo anapitiriza kufotokoza kuti: “Musamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) M’malo motengera mzimu wa dziko, iwo anafunikira kusintha maganizo awo kuti akhale ofanana ndi a Khristu. (1 Akorinto 2:16; Afilipi 2:5) Akhristu onse oona, ngakhale ifenso masiku ano, amafunikira kutsatira mfundo imeneyi pamoyo wawo.
6. Mogwirizana ndi mawu a Paulo a pa Aroma 12:1, 2, kodi n’chiyani chimene chimatilimbikitsa kuti tisabwezere?
6 Kodi mawu a Paulo a pa Aroma 12:1, 2 angatithandize bwanji? Mofanana ndi Akhristu odzozedwa a ku Roma amenewo, timayamikira kwambiri kuti Mulungu wakhala akutisonyeza chifundo m’njira zosiyanasiyana ndipo akupitirizabe kutero tsiku lililonse. Chotero, mtima wathu woyamikira umatilimbikitsa kutumikira Mulungu ndi mphamvu zathu, chuma chathu, ndi luso lathu lonse. Umatilimbikitsanso kuyesetsa kuti tiziganiza ngati Khristu osati mofanana ndi dziko. Ndipo kukhala ndi maganizo ofanana ndi a Khristu kumatithandiza pochita zinthu ndi okhulupirira anzathu komanso anthu osakhulupirira. (Agalatiya 5:25) Mwachitsanzo, tikamaganiza mofanana ndi Khristu, timapewa mtima wofuna kubwezera.—1 Petulo 2:21-23.
“Chikondi Chanu Chisakhale cha Chiphamaso”
7. Kodi n’chikondi chotani chomwe chikufotokozedwa m’chaputala 12 cha Aroma?
7 Timapewa kubwezera choipa pa choipa osati chabe chifukwa ndi njira yoyenera komanso chifukwa ndi njira yachikondi. Taonani zimene mtumwi Paulo anafotokoza ponena za chikondi. M’buku la Aroma, Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti “chikondi” (m’Chigiriki a·gaʹpe) kambirimbiri ponena za chikondi cha Mulungu ndi cha Khristu. (Aroma 5:5, 8; 8:35, 39) Koma m’chaputala 12, Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti a·gaʹpe polankhula za chikondi chimene anthu ayenera kusonyezana. Atafotokoza kuti Akhristu ena ali ndi mphatso zauzimu zosiyanasiyana, Paulo anatchula khalidwe limene Akhristu onse ayenera kukhala nalo. Iye anati: “Chikondi chanu chisakhale cha chiphamaso.” (Aroma 12:4-9) Kusonyeza ena chikondi ndi chizindikiro chofunika cha Akhristu oona. (Maliko 12:28-31) N’chifukwa chake, Paulo akulangiza Akhristufe kuti tizisonyeza chikondi chenicheni.
8. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi chosakhala cha chiphamaso?
8 Paulo anafotokozanso mmene tingasonyezere chikondi chosakhala cha chiphamaso, iye anati: “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.” (Aroma 12:9) Mawu akuti ‘kunyansidwa’ ndi ‘kugwiritsitsa’ ndi amphamvu kwambiri. Mawu akuti ‘kunyansidwa’ angamasuliridwe kuti ‘kudana kwambiri ndi chinthu.’ Tiyenera kudana kwambiri ndi zinthu zoipa osati chabe zotsatirapo zake zokha. (Salmo 97:10) Mawu akuti ‘kugwiritsitsa’ amachokera ku mawu a Chigiriki omwe amatanthauza ‘kumata.’ Motero, Mkhristu yemwe ali ndi chikondi chenicheni amamamatira kwambiri khalidwe lochita chabwino moti limakhala umunthu wake.
9. Kodi ndi malangizo otani omwe Paulo anatchula mobwerezabwereza?
9 Paulo anatchula mobwerezabwereza njira imodzi yosonyezera chikondi. Iye anati: “Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani; muzidalitsa, osatemberera.” “Musabwezere choipa pa choipa.” “Okondedwa, musabwezere choipa.” “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:14, 17-19, 21) Mawu a Paulo akusonyeza bwino kwambiri mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu osakhulupirira, ngakhale amene amatitsutsa.
“Pitirizani Kudalitsa Anthu Amene Amakuzunzani”
10. Kodi tingadalitse motani anthu omwe akutizunza?
10 Kodi tingatsatire motani malangizo a Paulo akuti: “Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani”? (Aroma 12:14) Yesu anauza otsatira ake kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyo 5:44; Luka 6:27, 28) Motero, njira imodzi imene timadalitsira anthu omwe akutizunza ndiyo kuwapempherera. Ngati ena akutitsutsa chifukwa chosadziwa, tingapemphe Yehova kuwatsegula maso kuti azindikire choonadi. (2 Akorinto 4:4) N’zoona kuti zingaoneke zachilendo kupempha Mulungu kuti adalitse amene akutizunza. Koma maganizo athu akafanana kwambiri ndi a Khristu m’pamene ifenso tingathe kusonyeza kwambiri chikondi kwa adani athu. (Luka 23:34) Kodi pangakhale zotsatirapo zotani tikamasonyeza chikondi chotero?
11. (a) Kodi chitsanzo cha Sitefano chimatiphunzitsa chiyani? (b) Mofanana ndi zimene zinachitikira Paulo, kodi anthu ena ozunza angasinthe motani?
11 Sitefano ndi mmodzi mwa anthu amene anapempherera om’zunza, ndipo pemphero lake linayankhidwa. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pa Pentekoste mu 33 C.E., Sitefano anamangidwa ndi anthu omwe ankatsutsa mpingo wachikhristu. Iwo anam’duduluzira kunja kwa Yerusalemu ndi kum’ponya miyala. Iye asanamwalire, anafuula kuti: “Yehova, musawaimbe mlandu wa tchimo ili.” (Machitidwe 7:58–8:1) Mmodzi mwa anthu omwe Sitefano anawapempherera tsiku limenelo anali Saulo, yemwe anaonerera ndi kuvomereza kuphedwa kwa Sitefanoyo. M’kupita kwa nthawi, Yesu yemwe anali ataukitsidwa anaonekera kwa Saulo. Iyeyu yemwe kale anali wozunza anakhala wotsatira wa Khristu, ndipo anatchedwa mtumwi Paulo, amene analemba kalata yopita kwa Aroma. (Machitidwe 26:12-18) Mogwirizana ndi pemphero la Sitefano, zikuoneka kuti Yehova anakhululukira Paulo chifukwa chozunza Akhristu. (1 Timoteyo 1:12-16) N’zomveka kuti Paulo analimbikitsa Akhristu kuti: “Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani.” Chifukwa cha zimene zinam’chitikira, iye ankadziwa kuti anthu ena ozunza angadzakhale atumiki a Mulungu. Masiku anonso, anthu ena omwe anali ozunza ndi Akhristu chifukwa choti atumiki a Yehova amakhala mwamtendere.
“Khalani mwa Mtendere ndi Anthu Onse”
12. Kodi malangizo opezeka pa vesi 9 la Aroma chaputala 12 akugwirizana bwanji ndi omwe ali pa vesi 17?
12 Malangizo a Paulo otsatira, onena za mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu okhulupirira ndiponso osakhulupirira amati: “Musabwezere choipa pa choipa.” Mawu a Paulo amenewa akugwirizana ndi zimene iye ananena poyamba kuti: “Nyansidwani ndi choipa.” Kodi munthu anganene bwanji kuti amanyansidwadi ndi choipa pamene iyeyo akubwezera ena choipa? Kuchita zimenezi n’kosemphana kwambiri ndi kusonyeza ‘chikondi chosakhala chachiphamaso.’ Ndiyeno Paulo anati: “Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino.” (Aroma 12:9, 17) Kodi mawuwa tingawagwiritse ntchito motani?
13. Kodi timachita zinthu motani pamaso pa “anthu onse”?
13 M’kalata yake kwa Akorinto, Paulo analembamo za chizunzo chimene atumwi anakumana nacho. Iye anati: “Takhala ngati choonetsedwa m’bwalo la masewero ku dziko, kwa angelo, ndi kwa anthu. . . . Pamene akutinenera zachipongwe, timadalitsa; pozunzidwa, timapirira; ponyozedwa, timayankha mofatsa.” (1 Akorinto 4:9-13) Masiku anonso, Akhristu oona akuonetsedwa kwa anthu m’dzikoli. Pamene anthu amaona zinthu zabwino zimene tikuchita ngakhale ena akutichitira zinthu mopanda chilungamo, angayambe kumvetsera uthenga wathu wachikhristu.—1 Petulo 2:12.
14. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale mwamtendere ndi anthu ena?
14 Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale mwamtendere ndi anthu ena? Tichite zonse zimene tingathe. Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” (Aroma 12:18) Mawu akuti “ngati ndi kotheka” ndiponso “monga mmene mungathere” akusonyeza kuti si nthawi zonse pamene kukhala mwamtendere ndi anthu ena kumatheka. Mwachitsanzo, sitingaphwanye lamulo la Mulungu chifukwa chongofuna kukhala mwamtendere ndi munthu. (Mateyo 10:34-36; Aheberi 12:14) Koma popanda kusemphana ndi mfundo zolungama, timachita zonse zimene tingathe kuti tikhale mwamtendere “ndi anthu onse.”
“Musabwezere Choipa”
15. Kodi lemba la Aroma 12:19 limanena chifukwa chotani chimene sitiyenera kubwezera?
15 Chifukwa china chomveka chimene sitiyenera kubwezera, chomwe Paulo anafotokoza n’choti timasonyeza kudzichepetsa. Iye anati: “Musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Aroma 12:19) Mkhristu amene amabwezera ndi wodzikuza chifukwa amachita zimene Mulungu yekha ayenera kuchita. (Mateyo 7:1) Ndipo Mkhristuyo akabwezera, amasonyeza kuti sakhulupirira mawu a Yehova akuti: “Ndidzawabwezera ndine.” Mosiyana ndi zimenezi, Akhristu oona amakhulupirira kuti Yehova ‘adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhika ake.’ (Luka 18:7, 8; 2 Atesalonika 1:6-8) Iwo modzichepetsa amasiyira Mulungu kuti abwezere choipa.—Yeremiya 30:23, 24; Aroma 1:18.
16, 17. (a) Kodi ‘kuunjika makala amoto’ pamutu pa munthu wina kumatanthauzanji? (b) Kodi inuyo munaonapo mmene kuchitira munthu wosakhulupirira zinthu zabwino kunafewetsera mtima wake? Ngati n’choncho, perekani chitsanzo.
16 Kubwezera mdani kungaumitse mtima wake koma kum’chitira zabwino kungaufewetse. Chifukwa chiyani tikutero? Taonani mawu a Paulo kwa Akhristu a ku Roma akuti: “Ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse chakudya; ngati ali ndi ludzu, m’patse chakumwa; pakuti mwakutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.” (Aroma 12:20; Miyambo 25:21, 22) Kodi zimenezi zikutanthauzanji?
17 ‘Kumuunjikira makala a moto pamutu pake’ ndi mawu okuluwika amene anayamba chifukwa cha mmene ankayengera zitsulo m’nthawi za m’Baibulo. Miyala yopangira zitsulo ankaiika m’ng’anjo, ndiyeno ankaika makala amoto pamwamba ndi pansi pa miyalayo. Makala amoto omwe anali pamwamba ankatenthetsa kwambiri miyala yolimbayo moti inkasungunuka kenako n’kusiyana ndi zinthu zosafunika za m’miyalayo. N’chimodzimodzi ndi ifeyo, tikamachitira anthu otitsutsa zinthu zabwino tingafewetse mtima wawo kuti iwonso ayambe kusonyeza makhalidwe abwino. (2 Mafumu 6:14-23) Ndipotu, anthu ambiri mumpingo wachikhristu anayamba kuphunzira choonadi chifukwa cha zinthu zabwino zimene atumiki a Yehova ankawachitira.
Chifukwa Chake Sitibwezera
18. N’chifukwa chiyani kusabwezera ndi njira yoyenera, yachikondi ndiponso yosonyeza kudzichepetsa?
18 M’nkhani yofotokoza mwachidule chaputala 12 cha Aroma imeneyi, taona zifukwa zingapo zofunika ‘zosabwezera choipa pa choipa.’ Choyamba, kupewa kubwezera ndi njira yoyenera kutsatira. Chifukwa cha chifundo chimene Yehova watisonyeza, n’koyenera ndiponso kwanzeru kudzipereka kwa iye ndi kutsatira malamulo ake, kuphatikizapo lamulo loti tizikonda adani athu. Chachiwiri, kupewa kubwezera choipa pa choipa ndi njira yachikondi. Ngati sitibwezera koma tikhala mwamtendere ndi anthu, mwina tingathandize ngakhale anthu ena omwe ndi otsutsa kwambiri kuti ayambe kulambira Yehova. Chachitatu, kupewa kubwezera choipa ndi njira yosonyeza kudzichepetsa. Kubwezera ena kumasonyeza kudzikuza chifukwa Yehova amati: “Kubwezera ndi kwanga.” Ndipo Mawu a Mulungu amachenjezanso kuti: “Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Mwanzeru, tikasiyira Mulungu kubwezera timasonyeza kuti ndife odzichepetsa.
19. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
19 Paulo anafotokoza mwachidule nkhani yake ya mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu ena. Iye analimbikitsa Akhristu kuti: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:21) Kodi masiku ano ndi mphamvu zoipa zotani zomwe tikulimbana nazo? Kodi tingazigonjetse motani? Mafunso awa ndi enanso ayankhidwa m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungafotokoze?
• Kodi ndi malangizo otani omwe amapezeka mobwerezabwereza mu chaputala 12 cha Aroma?
• Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kusabwezera?
• Ngati ‘sitibwezera choipa pa choipa,’ kodi ifeyo ndiponso anthu ena tingapindule bwanji?
[Bokosi patsamba 22]
Chaputala 12 cha Aroma chimafotokoza mmene Mkhristu ayenera kuchitira zinthu ndi
• Yehova
• okhulupirira anzake
• anthu osakhulupirira
[Chithunzi patsamba 23]
Kalata ya Paulo kwa Aroma imapereka malangizo othandiza kwa Akhristu
[Chithunzi patsamba 25]
Kodi chitsanzo cha Sitefano chimatiphunzitsa chiyani?