Kodi Muyenera Kukhoma Misonkho?
“M’bwezereni aliyense amene munamukongola: ngati inu muli ndi ngongole ya msonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira; ngati ndi kuopa kwa oyenera kuwaopa, ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu.”—Aroma 13:7, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
POONA mmene misonkho ikukwerera, langizo limene lili pamwambali lingaoneke ngati lovuta kulitsatira. Komabe, amenewo ndi mawu a mtumwi Paulo ndipo anawalemba m’Baibulo. Mosakayika, mumalemekeza Baibulo. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Akristu ayeneradi kukhoma misonkho yonse, kuphatikizapo misonkho imene ena angaione kuti ndi yopitirira muyezo kapena yopanda chilungamo?’
Taganizirani zimene Yesu analangiza ophunzira ake. Iye ankadziŵa kuti Ayuda anzake ankadana kwambiri ndi misonkho imene Aroma anakhazikitsa. Ngakhale zinali choncho, Yesu anawalimbikitsa kuti: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) N’zochititsa chidwi kuti Yesu analimbikitsa kupereka msonkho ku boma limene linali litatsala pang’ono kumupha.
Patatha zaka zochepa, Paulo anapereka langizo limene taligwira mawu pachiyambi pa nkhani ino. Iye analimbikitsa kupereka misonkho ngakhale kuti ndalama zambiri za misonkhoyo anali kuzigwiritsa ntchito kulipirira asilikali ndi zida za nkhondo za Aroma ndiponso kulipirira moyo wa makhalidwe oipa ndiponso wowononga zinthu wa mafumu a Aroma. N’chifukwa chiyani Paulo anali ndi maganizo otereŵa, amene anthu ambiri sanali kuwakonda?
Maulamuliro Aakulu
Onani nkhani yonse imene muli mawu a Paulo ameneŵa. Pa Aroma 13:1, iye analemba kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.” Nthaŵi imene mtundu wa Israyeli unali ndi olamulira oopa Mulungu, zinali zosavuta kuti anthu aone kupereka ndalama pothandiza dziko lawolo kukhala udindo wa nzika iliyonse ndiponso udindo wawo wachipembedzo. Koma kodi Akristu anali ndi udindo wofananawu pamene olamulira anali anthu osakhulupirira, olambira mafano? Inde, anali nawo. Mawu a Paulo anasonyeza kuti Mulungu anawapatsa mafumu “ulamuliro.”
Maboma amagwira ntchito yaikulu kuti akhazikitse bata. Zimenezi zimathandiza kuti Akristu apitirize kugwira ntchito zawo zosiyanasiyana zauzimu. (Mateyu 24:14; Ahebri 10:24, 25) Motero, pofotokoza za maboma amene akulamulira, Paulo anati: “Ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino.” (Aroma 13:4) Paulo mwiniyo anapezerapo mwayi pa chitetezo chimene boma la Aroma linkapereka. Mwachitsanzo, pamene gulu la anthu linamuukira, asilikali a Aroma ndi amene anam’pulumutsa. Patapita nthaŵi iye anachita apilo ku khoti la Aroma kuti apitirizebe kutumikira monga mmishonale.—Machitidwe 22:22-29; 25:11, 12.
Motero, Paulo anapereka zifukwa zitatu zokhomera msonkho. Choyamba, iye analankhula za ‘mkwiyo’ wa maboma polanga anthu ophwanya malamulo. Chachiŵiri, anafotokoza kuti chikumbumtima cha munthu woopa Mulungu, chidzawonongeka ngati achita chinyengo pankhani yokhoma msonkho. Chomaliza, anasonyeza kuti kukhoma misonkho n’kubwezera chabe zimene boma limachita monga “atumiki.”—Aroma 13:1-6.
Kodi Akristu anzake a Paulo anamvera zimene iye ananena? Umboni ukusonyeza kuti anatero, chifukwa munthu wina wodzitcha Mkristu wa m’zaka za m’ma 100 yemwe anali wolemba mabuku, dzina lake Justin Martyr (cha m’ma 110 mpaka 165 C.E.) anati, Akristu ankakhoma misonkho “mosavuta kuposa anthu ena onse.” Masiku ano, maboma akafuna malipiro, kaya akhale oti anthu agwiritse ntchito nthaŵi yawo kuthandiza bomalo kapena kupereka ndalama, Akristu amapitiriza kumvera lamulolo mosanyinyirika.—Mateyu 5:41.a
Komabe, Akristu ali ndi ufulu wopezerapo mwayi pa malamulo ochotsera msonkho. Nthaŵi zina angagwiritse ntchito mwayi wowachepetsera msonkho kapena kusakhoma msonkho, womwe amapatsidwa anthu amene amapereka zopereka ku gulu la chipembedzo. Komabe, pomvera Mawu a Mulungu, Akristu oona sazemba misonkho. Amakhoma misonkho, n’kusiya m’manja mwa olamulirawo udindo wonse wa mmene ndalamazo adzazigwiritsira ntchito.
Misonkho yokwera kwambiri yangokhala njira ina imene “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Mboni za Yehova zimalimbikitsidwa ndi lonjezo la m’Baibulo lakuti posachedwapa, anthu onse adzachitiridwa chilungamo pamene boma la Mulungu lidzalamulira, boma limene silidzalemetsa anthu ndi misonkho yopanda chilungamo.—Salmo 72:12, 13; Yesaya 9:7.
[Mawu a M’munsi]
a Langizo la Yesu lopereka “kwa Kaisara zake za Kaisara” silinangonena za msonkho wokha ayi. (Mateyu 22:21) Buku lakuti Critical and Exegetical Hand-Book to the Gospel of Matthew, lomwe analemba ndi Heinrich Meyer, limafotokoza kuti: “Mawu akuti [zake za Kaisara] . . . sakutanthauza misonkho ya boma yokha ayi, koma chilichonse chimene Kaisara anayenera kupatsidwa chifukwa chakuti anali wolamulira.”
[Mawu Otsindika patsamba 11]
Akristu oyambirira ankakhoma misonkho “mosavuta kuposa anthu ena onse.”—ANATERO JUSTIN MARTYR
[Chithunzi patsamba 10]
Akristu oona amamvera malamulo a msonkho
[Chithunzi patsamba 11]
Yesu anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara”
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
© European Monetary Institute