Sonyezani Kufunitsitsa ku Kulalikira Mbiri Yabwino
“[Pali kufunitsitsa ku mbali yanga, NW] kuti ndilalikire mbiri yabwino kwa inunso.”—AROMA 1:15.
1, 2. Kodi ndi motani mmene anthu amachitira mu nthawi yangozi?
“IWO anabwera kuchokera kuzungulira konseko . . . mazana a odzipereka anakhuthukira mu theka lagawo la kumaloko, akumafika ndi malole odzaza ndi zakudya ndi zovala, akumamanga malo othawirapo, ena akumagwira ntchito maora 18 mpaka 20 pa tsiku, ena osagona ndi komwe masiku oyambirira pambuyo pa kusweka kochititsa mantha kwachochinjiriza. ”
2 Mmenemo ndi mmene anthu anachitira pamene kusefukira kwa madzi kwa mwamsanga kunamenya dera lapakati mu California m’ngululu yapita, kupangitsa anthu 24,000 kuthawa kaamba ka chisungiko. Inde, pamene ngozi—kuchokera ku kusefukira kwa madzi kupita ku zivomezi ndi ngozi za nyukiliya—zichitika, anthu kawirikawiri amavomereza modzipereka ndipo amakhala chapafupi kupereka thandizo. Iwo anapinda malaya awo, kulimba mtima mu zowopsya zambiri ndi kusakwanira, ndipo mofunitsitsa anabwera kudzathandiza anzawo—angakhale alendo.
Nthawi Yakuchita Changu
3. Kodi ndi ngozi yaikulu kwambiri yotani imene mtundu wa anthu ukuyang’anizana nayo lerolino?
3 Lerolino, mtundu wa munthu ukuyang’anizana mwachindunji ndi tsoka lalikulu kwambiri m’mbiri. Sichiri chifukwa cha kuwononga kumene munthu akuchita pa dziko, chiwopsyezo cha nkhondo ya nyukiliya, kapena kuwonjezeka kwa upandu ndi chiwawa, mosasamala kanthu kuti zinthuzi ziri zovuta chotani. M’malo mwake, mtundu wa munthu ukuyang’anizana ndi chimene Yesu Kristu anatchula kuti “Masauko aakulu monga sipandakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko kufikira tsopano inde sipadzakhalanso.” Kusonyeza kuti ndi kuwononga kotani kumene “chisautso chachikulu” chidzachita, Yesu anapitiriza kunena kuti: “Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense.”—Mateyu 24:21, 22.
4. M’chiyang’aniro changozi imeneyo, kodi ndi motani mmene tiyenera kuchitira?
4 Kodi mukanachita chiyani ngati mukanadziwa kuti anthu ambiri, kuphatikizapo ena omwe amakhala pafupi ndi inu, akawonongeka posachedwapa mu chisautso chimenecho? Kodi mungakhale ofuna kuthandiza? Kumbukirani masomphenya olosera a Ezekieli a mwamuna wokhala ndi zolembera. Iye anauzidwa kuti kokha awo omwe alandira chizindikiro pmphumi pawo ayenera kupulumuka kuwonongedwa kwa Yerusalemu, ndipo iye anali amene anayenera kupereka chizindikiro chopulumutsa moyocho. Ndi motani mmene iye anavomerezera? “Ndachita monga munandilamulira ine,” iye anatero.—Ezekieli 9:1-11.
5. Kodi ndi ntchito yotani imene tinalamulidwa kuchita, ndipo kodi iyo iri yofulumira motani?
5 Kodi mukusonyeza kuvomereza kumodzimodziko ndi kufunitsitsa monga munthu wovala bafutayo, kumachita monga mmene Yehova walamulira? Kodi nchiyani chimene Yehova walamula? Kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, iye wapereka lamulo: “Chifukwa chache mukani phunzitsani anthu amitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndina kulamulirani inu.” (Mateyu 28: 19, 20) Iyi iri ntchito yakusunga moyo monga momwe chinaliri chizindikiro chophiphiritsira cha pamphumi mu nthawi ya Ezekieli. Aliyense amene savomereza ndi kukhala wophunzira wa Yesu Kristu adzavutika ndi chiwonongeko pamanja a Wowononga Wamkulu wa Mulungu. (2 Atesalonika 1:6-8) Kodi mukuzindikira kufulumiza kwake? Kodi mukusonyeza iko mwakusonyeza kufunitsitsa kwa kulalikira mbiri yabwino?
Kufunitsitsa—Kumasonyezedwa Motani?
6. Kodi “kufunitsitsa” kumatanthauzanji?
6 Anthu a Yehova, kuli konse, amazindikira kufulumira kwa nthawi. Tonse a ife timafuna kuwona anthu ambiri monga momwe kungathekere ali kumapulumutsidwa kuchokera ku “chisautso chachikulu” chomayandikiracho. Malinga ndi kunena kwa dikishonale, kufunitsitsa kuli “chikondwerero kapena chikhumbo chofunitsitsa cha kutsatira kapena kupeza china chake.” Yemwe ali wofunitsitsa ponena za china chake amalunjikitsa ponse pawiri maganizo ndi kachitidwe kuloza ku kupeza icho. Iye adzachita chiri chonse chomwe chiri mumphamvu yake ndi cholinga chofuna kulaka zokhumudwitsa ndi zolepheretsa, ndipo iye adzapitiriza kuchita tero mpaka atafikira chonulirapo chake. Mmenemo ndi mmene mtumwi Paulo anamverera ponena za utumiki wake, ndipo tidzachita bwino kumutsanzira iye.—1 Akorinto 4:16.
7. Kodi nchifukwa ninji Paulo anafuna kupita ku Roma?
7 Talingalirani, mwachitsanzo, mawu a Paulo ku Akristu a ku Roma, pa Aroma 1:13-16. “Kawiri Kawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu,” iye anauza iwo. Chifukwa ninji? “Kuti ndikaone zobala zina mwa inunso,” iye analongosola. Ponena zimenezi, kodi Paulo anali kokha kulingalira za kuwachezera abalewo mu Roma ndipo mwina mwake kuwalimbikitsa iwo kukulitsa mokulira “zipatso za mzimu,” monga mmene opereka ndemanga ena amanenera? (Agalatiya 5:22, 23) Ayi, popeza mawu ake owonjezera, “monga mwa anthu amitundu” amachipangitsa icho kumvekera bwino kuti anali wofunitsitsa kupeza zipatso za Ufumu pakati pa anthu osakhulupirira omwe anali mu Roma. Iye anafuna kubweretsa mbiri yabwino ku Roma ndipo mwina mwake kuchokera pamenepo kupita ku malo ena.—Aroma 15:23, 24.
8. Kodi ndi motani mmene Paulo “analetsedwera” kupita ku Roma?
8 “Koma ndaletsedwa kufikira lero,” anatero Paulo. Kuletsedwa ndi chiyani? Kodi iye anali wotanganitsidwa kwambiri ndi zinthu zaumwini zomwe anafuna kuzifikira? Chabwino, Paulo anali munthu wotanganitsidwa koma osati ndi zikondwerero zaumwini. Panthawi imene analembera ku Aroma (chifupifupi 56 C.E. ), iye anali atamaliza kale maulendo aakulu a umishonale awiri ndipo anali wotanganitsidwa kwambiri mu ulendo wachitatu. Kawirikawiri, pa maulendo amenewa anali kutsogozedwa ndi mzimu woyera ku malo enieni. (Onani Machitidwe 16:6-9. ) Monga momwe analembera mu kalata yake, makonzedwe anali atapangidwa kale kaamba ka iye kupita ku Yerusalemu “kukatumikira oyera mtima” kumeneko. (Aroma 15:25, 26) Ndipo anali atakumana ndi ‘zitsenderezo’ zochulukira zonga ngati zimenezi.—Onani 2 Akorinto 11:23-28.
9. Kodi ndi motani mmene Paulo anasonyezera kufunitsitsa kwa kulalikira mbiri yabwino?
9 Angakhale kunali tero, Paulo sanadzimve kuti anali ndi zochita zokwanira, ndiponso sanalingalire kuti anali ndi ntchito yake ndipo imeneyo inali yokwanira. Iye anafuna kuchita zowonjezereka. Mu chenicheni, iye anati: “Pali kufunitsitsa kumbali yanga kuti ndilalikire mbiri yabwino kwa inunso ku Roma.” Chimenecho ndicho chimene kufunitsitsa kuli! Moyenerera, profesa F. F. Bruce mu bukhu lake The Epistle of Paul to the Romans ananena izi ponena za mtumwiyo: “Kulalikira kwa uthenga wabwino kuli mu mwazi wake, ndipo iye sangathe kuchoka ku iwo; iye sakhala konse ‘wopuma ku ntchito’ koma ayenera kukhala mokhazikika pa iyo, ali kumachotsako mangawa owonjezereka omwe ali nawo pa mtundu wonse wa anthu—mangawa amene iye sadzakwaniritsa kubwezera ngati akali ndi moyo.” Kodi mmenemo ndi mmene munauonera utumiki wanu?
10. Kodi ndi ‘ziletso’ zotani zimene zingakhale mu njira yathu, koma kodi ndi motani mmene tingachitire ndi izo?
10 Lerolino, anthu onse a Yehova ali otanganitsidwa ndi mathayo ambiri. Ena ali ndi mabanja oti awasamalire, ena ali ndi mathayo m’mbali zina. Ena ali ndi malire mu zimene angachite chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Ndipo komabe ena ali ndi mathayo olemera mu mpingo Wachikristu. Komabe, timazindikiranso kuti nthawi iri kutha kaamba ka dongosolo la zinthu liripoli, ndipo umboni wa Ufumu uyenera kuperekedwa. (Marko 13:10) Mwakutero, monga Paulo, tiyenera kusonyeza kufunitsitsa kufikira mu ntchito ya kulalikira mosasamala kanthu za ‘zoletsa’ zomwe zingakhale mu njira yathu. Sitiyenera kudzimva kukhala okhutiritsidwa, kulingalira kuti tiri ndi zambiri zoti tichite monga momwe kunaliri.—1 Akorinto 15:58.
“Wamangawa” kwa Onse
11. Kodi mawu akuti “ndiri wamangawa,” amatanthauzanji?
11 Panali mphamvu ina yofulumiza pambuyo pa kuyesayesa kosatopa kwa Paulo mu kulalikira mbiri yabwino. “Ine ndiri wamangawa wa Ahelene ndi wa Akunja, kwa anzeru ndi wa opusa,” anatero Paulo. (Aroma 1:14) Ndi mwanjira yotani mmene Paulo anali “wamangawa”? Otembenuza ena amagwiritsira ntchito kalongosoledwe aka “Ndiri pansi pa thayo” (New English Bible), “Ndiri ndi thayo” (Today’s English Version), kapena “Ndiri ndi mangawa a thayo” (Jerusalem Bible). Kodi pamenepo, iye anali kunena kuti, ntchito yolalikira inali ntchito yotopetsa kapena thayo limene iye anafunikira kulipereka pamaso pa Mulungu? Chiri chapafupi kukulitsa kapenyedwe kameneko ngati ife titaleka kupenya kofulumira kapena takokedwa ndi zokopa za dziko. Koma chimenecho sindicho chimene Paulo anali nacho m’maganizo.
12. Ndi kwa ayani kumene Paulo anali “wamangawa,” ndipo nchifukwa ninji?
12 Monga “chotengera chosankhika” ndiponso monga “mtumwi wa anthu amitundu,” Paulo anali ndi thayo lolemera kwambiri pamaso pa Mulungu. (Machitidwe 9:15; Aroma 11:13) Komabe lingaliro lake lathayo silinali kokha kwa Mulungu. Iye ananena kuti anali “wamangawa” kwa ‘Ahelene (Agiriki), Akunja, anzeru ndi opusa.’ Kaamba ka chifundo ndi mwawi woperekedwa kwa iye, iye analiwona kukhala thayo lake la kulalikira kotero kuti onse amve mbiri yabwino. Iye anazindikira, kuti chinali chifuniro cha Mulungu chakuti “anthu onse ayenera kupulumutsidwa ndi kubwera ku chidziwitso cha chowonadi.” (1 Timoteo 1:12-16; 2:3, 4) Chimenecho ndicho chifukwa chake iye anagwirira ntchito mosalekeza, osati kokha kuti akhale ku thayo lake kulinga kwa Mulungu komanso kubwezera mangawa ake kwa anthu anzake. Kodi mumadzimva kukhala wamangawa mwa umwini chotero kulinga kwa anthu amene ali mugawo lanu? Kodi mumadzimva kukhala wamangawa kwa iwo
“Osachita Manyazi ndi Mbiri Yabwino”
13. Kodi nchiyani chimene chinali chiyerekezo cha Paulo ponena za mbiri yabwino?
13 Paulo kwenikwenidi anali chitsanzo chowonekera mu kusonyeza kufunitsitsa kwa kulalikira mbiri yabwino. Iye mozama anayamikira chikondi chopambana chomwe chinasonyezedwa kwa iye ndi Mulungu, ndipo iye sanachifune icho kukhala chopanda phindu. (1 Akorinto 15:9, 10) Ndicho chifukwa chake iye anapitiriza kunena kuti: “Pakuti sindichita manyazi ndi [mbiri yabwino, NW]” (Aroma 1: 16) Kuchokera pakayang’anidwe ka munthu, Akristu sanali kokha achilendo komanso ananyazitsidwa. “Takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse,” anatero Paulo. (1 Akorinto 4:13) Komabe iye sanali wa manyazi kuitengera mbiri yabwino ku Roma, pakati pa dziko lophunzira ndi pa maziko a Ufumu wa Chiroma. Pamene tiyang’anizana ndi kupanda chikondwerero, kunyozedwa, kapena ngakhale chitsutso ku ntchito yathu yolalikira, tikukumbukira chitsanzo cholimbikitsa cha Paulo.
14. Kodi nchifukwa ninji Paulo “sanachite manyazi ndi mbiri yabwino”?
14 “Osachita manyazi ndi mbiri yabwino” iridi njira ina ya kunena kuti “onyadira ndi mbiri yabwino,” ndipo mmenemo ndi mmene tiyenera kukhalira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti “iridi, kwenikweni, mphamvu ya Mulungu kaamba ka chipulumutso kwa aliyense wokhala ndi chikhulupiriro,” analongosola motero Paulo. Iye anali ndi chokumana nacho chaumwini chokwanira chochirikizira mawu ake. Ndi mbiri yabwino, Paulo anati, “tikugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse la kumvera kwa Kristu.” (2 Akorinto 10:5) Kaya chinali chotsutsana ndi miyambo ya Ayuda, nthanthi za Agriki, kapena mphamvu ya Aroma, mbiri yabwino inatsimikizira kukhala yachipambano.
15. Ndi motani mmene kufunitsitsa kunali mphamvu yofulumiza mu moyo wa Paulo?
15 Chiri chabwino kwambiri chotani nanga kuti mmalo mwa kuumva uwo kukhala wolemetsa, Paulo anali ‘wofuna’ kukwaniritsa thayo lake lopatsidwa ndi Mulungu! Monga mmene iye mwini analongosolera: “Pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira [mbiri yabwino, NW]!” (1 Akorinto 9:16) Kufunitsitsa kumeneku kunamuthandiza iye kupitirizabe kwa zaka zambiri za utumiki wosatopetsa, kotero kuti pomalizira iye akananena kuti: “Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.”—2 Timoteo 4:7.
Kukhutiritsa Kumawonjezera ku Zotulukapo
16. Kodi ndi zitokoso zothekera zotani zomwe mukuganiza kuti zinakumanizana ndi mwamuna wokhala ndi zolembera m’masomphenya a Ezekieli?
16 Monga Paulo, munthu wokhala ndi zolembera mu masomphenya a Ezekieli anali mosakaikira wofuna ponena za ntchito yake. Iye anabweretsa ripoti labwino: Ntchito inakwaniritsidwa! Nkhaniyo siimatiuza kuti ndi motani mmene iye anapitira kupeza awo onse amene anali “kuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zinachitidwa pakati pache.” (Ezekieli 9:4) Angakhale kuti palibe chimene chinanenedwa ponena za ndi motani mmene kuika chizindikiro kumeneku kunakwaniritsidwira, mwachiwonekere sinali ntchito yokhweka.
17. (a) Kodi ndi zitokoso zotani zimene mumakumanizana nazo mu ntchito ya kupanga ophunzira, ndipo ndi motani mmene mumachitira nazo? (b) Kodi kuyesetsa kofunikako kuli koyenereradi?
17 Mofananamo lerolino, ntchito yathu siiri yokhweka. Funso, chotero, liri lakuti: Kodi tiri okhutiritsa motani ku ntchito yopulumutsa moyo imeneyi? Kuti tipange ophunzira ambiri a anthu monga mmene kungathekere, tiyenera kukhala mu ntchito imeneyi mokhazikika ndipo mwadongosolo, osalola mwawi uli wonse wakugawana mbiri yabwino kutipitirira. Monga ife, anthu a mdera lathu ali otanganitsidwa; mwina mwake angakhale osakhazikika ku nyumba pamene tiwafikira, ndipo angakhale ngati iwo alipo, iwo kawirikawiri amakhala ndi zina zochita. Kodi ndi chiyani chomwe tingachite? Chabwino, tikafunikira kusunga zolembera zolongosoka ndi kubwererako panthawi zosiyanasiyana, kawirikawiri, ndi chiyembekezo chakuti tidzapezako wina wake woti tilankhule naye. Kodi zoyesayesa zimenezo ziri zoyenereradi? Lolani nkhani zachidule zotsatirazi kuchokera kwa eni nyumba awiri zipereke yankho:
“Ndingakonde kulongosola chiyamikiro changa kwa Mboni za Yehova kaamba ka maulendo awo ambirimbiri omwe anapanga ku nyumba yanga. Ndikudziwa kuti panthawi zina ntchito yanu simawonedwa ndi awo omwe ali kunja kwa tchalitchi chanu kukhala molemerera yotenthetsa maganizo monga mmene iliri. Chotero ndinaganiza zakugawana nanu chokumana nacho changa ndi kunena kuti zikomo!”
“Pali ambiri a ife amene tiri ndi njala kaamba ka chowonadi, chotero ambiri a ife timakhulupirira kuti njira zonse zimatsogoza ku chipulumutso. Inu amene mumayesera kufufuzafufuza kaamba ka wina wake kuti mumulalikireko, musakhumudwitsidwe pa ife! Sitiri anthu oipa kwenikweni, angakhale kuti timakutukwanani, kukuchititsani manyazi, ndi kukukanani. Musakhumudwitsidwe, chifukwa chakuti taphunzitsidwa mabodza ambiri, kuuzidwa nkhani zambiri zoopsya, ndi kuphunzitsidwa kukudani inu kuika patali uthenga wa Ufumu wa Yehova kuchoka kwa ife.”
18. (a) Ndi motani mmene mungathandizire ena kupeza lingaliro la mbiri yabwino? (b) Kodi ndi motani mmene wofalitsa wina analakira kupanda chikondwerero kowonekera?
18 Kuti tifikire mtima wa mmodzi ndi mmodzi ndi kuwathandiza kupeza chidziwitso chenicheni cha mbiri yabwino chimatenga kuposa chigwirizano chakunja, kupereka uthenga wokonzekeredwa, kapena kusiya mabukhu ena a Baibulo. Tiyenera kukalamira kuzindikira zofuna zawo ndi zodera nkhawa zawo, zokonda zawo ndi zimene sakonda, mantha awo ndi kunyada kwawo. Zonse zimenezi zimafunikira kulingalira kokulira ndi kuyesayesa—ndi kufunitsitsa kumbali yathu. Lingalirani pa zokumana nazo zotsatirazi:
Wofalitsa analankhula kwa mayi wina pakhomo loyandikana nalo, sanapeze chivomerezo chokulira. Kuzindikira kuti panali ana ambiri, iye anafunsa ndi ana angati anali nawo. Iye anayankha kuti onsewa sanali ana ake koma anali ana a mulamu wake, omwe anali atafika kumene kuchokera ku dziko lina. Kukambitsiranako kenaka kunafika ku mutu wa kuperewera kwa nyumba. Wofalitsa anavomereza kuti nyumba zabwino zinali zovuta kuzipeza mu mizinda yaikulu, popeza analinso kuyembekezera anansi ena omwe anayenera kubwera, ndipo anadzipereka kuti athandize. Mayiyo anakondwera kwambiri ndipo anamuitana mulamu wake. Kukambitsirana kunapitirira, ndipo anasinthana manambala a telefoni. Osaiwala cholinga cha kuitanako, wofalitsayo mwaluntha anatsegula pa tsamba 157 la bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha ndi kulongosola kuti m’dongosolo latsopano la zinthu lolonjezedwalo, mavuto anyumba ndi ntchito adzakhala atapita. Mwamunayo anasangalatsidwa kwambiri ndipo mwachangu analilandira bukhulo. Pambuyo pake, wofalitsayo anabwereranso ndi mawu onena za nyumba ya renti; iye anayambitsanso kukambitsirana kwake kwa Baibulo.
19. Iri nthawi kaamba ka ife tsopano yakuchita chiyani? Ndipo kodi nchiyani chomwe tikafunikira kukambitsirana mopitirirapo?
19 Nthawi ya kulalikira mbiri yabwino ikutha mofulumira. Kuti ndi kuutali wotani wowonjezera kumene “angelo anayi” adzapitiriza “kugwira mphepo zinayi za dziko” sitikudziwa. (Chivumbulutso 7:1) Mu njira iriyonse, “chisautso chachikulu” chidakali kutsogolo, ndipo anthu owona mtima akusokhanitsidwa. Ndithudi, “minda iri yoyera kaamba ka kututa.” (Mateyu 24:21, 22; Yohane 4:35) Tsopano iri nthawi kaamba ka ife yakudzikanikiza ife eni mwamphamvu mu ntchito yosadzabwerezedwanso iyi. Kodi ndi motani mmene tingagwiritsire ntchito bwino kwambiri nthawi yotsalira? Kodi ndi motani mmene tingakhalire ndi kugawanamo kokulirapo mu ntchito yopulumutsa moyo imeneyi? Ndipo kodi nchiyani chingatithandize ife kupitirizabe kusonyeza mtima wa kufunitsitsa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu? Mafunso amenewa adzakambitsiridwa mu nkhani yotsatira.
Lingalirani Chitsanzo cha Paulo Malinga ndi Aroma 1:13-16—
◻ Nchifukwa ninji anafuna kupita ku Roma?
◻ Kodi nchiyani chomwe chinamuletsa iye kupita?
◻ Koma kodi ndi motani mmene iye anachitira?
◻ Ndi kwa ayani ndipo nchifukwa ninji anali “wamangawa”?
◻ Kodi ndi motani mmene iye anadzimverera ponena za mbiri yabwino? Chifukwa ninji?
◻ Monga Paulo, kodi nchiyani chomwe tingachite kuti tikhale wokhutiritsa mu kulalikira mbiri yabwino?