Lingaliro Lachikristu la Ulamuliro
“Palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu.”—AROMA 13:1.
1. Kodi liwu lakuti “authority” (ulamuliro) nlogwirizana ndi chiyani, chotero nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Yehova ndiye Wolamulira Wamkulukulu?
ULAMULIRO umagwirizanitsidwa ndi kulenga. Liwulo “authority” (ulamuliro) nlogwirizana ndi liwu lakuti “author,” limene limatanthauza “amene amayambitsa, kupanga, kapena kuchititsa kukhalako.” Uyo Wamkulu amene anachititsa zolengedwa zonse kukhalako, zamoyo ndi zopanda moyo, ndi Yehova Mulungu. Mosakayikira iye ndiye Wolamulira Wamkulukulu. Akristu oona amagwirizana ndi malingaliro a zolengedwa zakumwamba zimene zimalengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11.
2. Kodi ndimotani mmene olamulira aumunthu oyambirira m’lingaliro lina anavomerezera kuti analibe kuyenera kwachibadwa kwa kulamulira anthu anzawo, ndipo kodi nchiyani chimene Yesu anauza Pontiyo Pilato?
2 Kuyesa kuyeneretsa mwalamulo ulamuliro wawo kochitidwa ndi ambiri a olamulira aumunthu oyambirira mwa kunena kuti anali mulungu kapena oimira mulungu kunali kungozindikira m’lingaliro lina kuti palibe munthu amene ali ndi kuyenera kwachibadwa kwa kulamulira anthu ena.a (Yeremiya 10:23) Magwero okha alamulo a ulamuliro ndi Yehova Mulungu. Kristu anauza Pontiyo Pilato, bwanamkubwa Wachiroma wa Yudeya kuti: “Simukadakhala nawo ulamuliro uli wonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba.”—Yohane 19:11.
“Palibe Ulamuliro Wina Koma Wochokera kwa Mulungu”
3. Kodi mtumwi Paulo ananena chiyani ponena za “maulamuliro aakulu,” ndipo kodi ndi funso lotani limene ndemanga za Yesu ndi Paulo zimadzutsa?
3 Mtumwi Paulo analembera Akristu okhala muulamuliro wa Ufumu wa Roma kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa [m’malo awo aang’ono, NW] ndi Mulungu.” (Aroma 13:1) Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti ulamuliro wa Pilato unapatsidwa kwa iye “kuchokera Kumwamba”? Ndipo kodi ndi mwanjira yotani imene Paulo analingalirira kuti maulamuliro andale a m’tsiku lake anaikidwa m’malo awo ndi Mulungu? Kodi iwo anatanthauza kuti Yehova mwiniyo ndiye ali ndi thayo la kuika wolamulira mmodzi ndi mmodzi aliyense wa dziko ili?
4. Kodi Yesu ndi Paulo anatcha Satana kukhala yani, ndipo kodi ndi kudzinenera kotani kwa Satana kumene Yesu sanakane?
4 Kodi zimenezi zingakhale choncho motani, popeza kuti Yesu anatcha Satana “mkulu wa dziko ili lapansi,” ndipo mtumwi Paulo anamutcha “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano”? (Yohane 12:31; 16:11; 2 Akorinto 4:4) Ndiponso, pamene anali kuyesa Yesu, Satana anampatsa “ulamuliro” pa “maufumu onse a dziko lokhalamo anthu,” akumanena kuti ulamuliro umenewu unapatsidwa kwa iye. Yesu anakana zimene anampatsa, koma sanakane kuti ulamuliro wotero unali woyenera kupatsidwa ndi Satana.—Luka 4:5-8.
5. (a) Kodi ndimotani mmene tiyenera kumvera mawu a Yesu ndi Paulo onena za ulamuliro waumunthu? (b) Kodi maulamuliro aakulu ali ‘oikidwa [m’malo awo aang’ono,] ndi Mulungu’ m’lingaliro lotani?
5 Yehova anapereka ulamuliro wa dziko ili kwa Satana mwa kumlola kukhala ndi moyo pambuyo pa kupanduka kwake ndi pambuyo poyesa Adamu ndi Hava ndi kuwachititsa kupandukira uchifumu Wake. (Genesis 3:1-6; yerekezerani ndi Eksodo 9:15, 16.) Chotero mawu a Yesu ndi Paulo ayenera kutanthauza kuti anthu aŵiri oyamba m’Edene atakana teokrase, kapena ulamuliro wa Mulungu, Yehova analola anthu opatuka kuyambitsa madongosolo a ulamuliro amene akawalola kukhala m’chitaganya chadongosolo. Nthaŵi zina, kuti akwaniritse chifuno chake, Yehova wachititsa olamulira kapena maboma ena kugwa. (Danieli 2:19-21) Ena wawalola kulamulirabe. Ponena za olamulira amene kukhalako kwawo kwaloledwa ndi Yehova, kunganenedwe kuti iwo “aikidwa [m’malo awo aang’ono, NW] ndi Mulungu.”
Akristu Oyambirira ndi Maulamuliro a Aroma
6. Kodi Akristu oyambirira anawaona motani maulamuliro a Roma, ndipo nchifukwa ninji?
6 Akristu oyambirira sanagwirizane ndi timagulu tampatuko Tachiyuda timene tinachita chiŵembu ndi kulimbana ndi Aroma amene anali m’Israyeli. Malinga ngati maulamuliro a Roma, ndi mpambo wawo wa malamulo wadongosolo, anasungitsa bata kumtunda ndi panyanja; kumanga ngalande zamadzi zambiri zothandiza, misewu, ndi maulalo; ndipo kaŵirikaŵiri kuchitira onse zabwino, Akristu anawaona kukhala ‘mtumiki [kapena, “wantchito,” NW, mawu amtsinde] wa Mulungu kuchitira iwo zabwino.’ (Aroma 13:3, 4) Kulemekeza ndi kumvera lamulo kunadzetsa mkhalidwe umene unakhozetsa Akristu kulalikira mbiri yabwino ponseponse, monga momwe Yesu analamulira. (Mateyu 28:19, 20) Ndi chikumbumtima chabwino, anali kulipira misonkho yolamulidwa ndi Aroma, ngakhale ngati ndalama zina zinagwiritsiridwa ntchito pazifuno zina zosavomerezedwa ndi Mulungu.—Aroma 13:5-7.
7, 8. (a) Kodi kuŵerenga mosamalitsa Aroma 13:1-7 kumavumbulanji, ndipo kodi nkhani yake yonse imasonyezanji? (b) Kodi ndi m’mikhalidwe yotani imene maulamuliro a Roma sanatumikire monga “mtumiki wa Mulungu,” ndipo zimenezi zitachitika ndi mkhalidwe wamaganizo wotani umene Akristu oyambirira anali nawo?
7 Kuŵerenga mosamalitsa mavesi asanu ndi aŵiri oyambirira a Aroma chaputala 13 kumavumbula kuti “maulamuliro aakulu” andale anali “mtumiki wa Mulungu” wotama awo ochita zabwino ndi kulanga awo ochita zoipa. Nkhani yonse imasonyeza kuti Mulungu, osati maulamuliro aakulu, ndiye amanena chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa. Chotero, ngati mfumu Yachiroma kapena wolamulira aliyense wandale anafuna zinthu zimene Mulungu analetsa kapena, mwanjira ina, analetsa zinthu zimene Mulungu anafuna, sanatumikirenso monga mtumiki wa Mulungu. Yesu ananena kuti: “Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Ngati Boma la Roma linafuna zinthu za Mulungu, zonga ngati kulambira kapena moyo wa munthu, Akristu oona anatsatira uphungu wa atumwi wakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
8 Kukana kwa Akristu oyambirira kulambira mfumu ndi kulambira mafano, kusiya misonkhano yawo Yachikristu, ndi kuleka kulalikira mbiri yabwino kunadzetsa chizunzo. Ambiri amakhulupirira kuti mtumwi Paulo ananyongedwa Mfumu Nero italamula zimenezo. Mafumu ena, makamaka Domitian, Marcus Aurelius, Septimius Severus, Decius, ndi Diocletian, nawonso anazunza Akristu oyambirira. Pamene mafumu ameneŵa ndi maulamuliro awo aang’ono anazunza Akristu, sanali kutumikira monga “mtumiki wa Mulungu” ayi.
9. (a) Kodi nziti zimene zikali zoona ponena za maulamuliro aakulu, ndipo kodi nkwayani kumene chilombo chandale chimalandira mphamvu ndi ulamuliro? (b) Kodi nchiyani chimene moyenerera chinganenedwe pa kugonjera Kwachikristu ku maulamuliro aakulu?
9 Zonsezi zikuthandiza kusonyeza kuti pamene kuli kwakuti maulamuliro aakulu andale amatumikira m’mbali zina monga “choikika ndi Mulungu” kusungitsa chitaganya chaumunthu chadongosolo, amakhalabe mbali ya dongosolo la zinthu ladziko limene Satana ndiye mulungu wake. (1 Yohane 5:19) Ali mbali ya gulu landale lapadaziko lonse lophiphiritsiridwa ndi “chilombo” cha pa Chivumbulutso 13:1, 2. Chilombocho chimalandira mphamvu ndi ulamuliro kwa “chinjoka chachikulu,” Satana Mdyerekezi. (Chivumbulutso 12:9) Chotero, moyenerera, kugonjera Kwachikristu ku maulamuliro otero kuli ndi malire, sikotheratu.—Yerekezerani ndi Danieli 3:16-18.
Ulemu Woyenera Kaamba ka Ulamuliro
10, 11. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anasonyezera kuti tiyenera kukhala aulemu kwa anthu amene ali ndi ulamuliro? (b) Kodi nchifukwa ninji ndipo ndimotani mmene mapemphero angaperekedwere “chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro”?
10 Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Akristu ayenera kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wachipongwe ndi wamwano kulinga ku maulamuliro aakulu andale. Zoona, ambiri mwa anthu ameneŵa sayenerera ulemu makamaka m’miyoyo yawo yamtseri kapena ngakhale yapoyera. Komabe, atumwi, mwa chitsanzo chawo ndi uphungu wawo, anasonyeza kuti anthu amene ali ndi ulamuliro ayenera kuchitiridwa ulemu. Pamene Paulo anaima pamaso pa Mfumu Herode Agrippa II amene anali kugonana ndi wachibale wake, analankhula naye ndi ulemu woyenera.—Machitidwe 26:2, 3, 25.
11 Ndipotu Paulo ananena kuti nkoyenera kutchula maulamuliro adziko m’mapemphero athu, makamaka pamene apemphedwa kupanga zosankha zimene zimayambukira miyoyo yathu ndi ntchito Zachikristu. Iye analemba kuti: “Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekeza monse. Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:1-4) Mkhalidwe wathu wamaganizo waulemu kulinga kwa maulamuliro otero ungawachititse kutilola kuchita ntchito yathu momasukirapo ya kuyesa kupulumutsa “anthu onse.”
12, 13. (a) Kodi ndi uphungu wachikatikati wotani wonena za ulamuliro umene Petro anapereka? (b) Kodi ndimotani mmene tingaletsere “chipulukiro cha anthu opusa” amene amayambitsa malingaliro olakwa ponena za Mboni za Yehova?
12 Mtumwi Petro analemba kuti: “Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa; monga mfulu, koma osakhala nawo ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu. Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.” (1 Petro 2:13-17) Umenewu ndi uphungu wachikatikati chotani nanga! Tiyenera kugonjera kotheratu kwa Mulungu monga akapolo ake, kugonjera kokhala ndi malire ndi kwaulemu ku maulamuliro aakulu andale otumidwa kulanga oipa.
13 Kwapezeka kuti maulamuliro adziko ambiri ali ndi malingaliro olakwa kwambiri ponena za Mboni za Yehova. Kaŵirikaŵiri zimenezi zili chifukwa chakuti anyengezedwa ndi adani anjiru a anthu a Mulungu. Kapena kungakhale kwakuti zonse zimene adziŵa ponena za ife anazimva m’zoulutsira nkhani, zimene nthaŵi zina sizimakhala zopanda tsankho m’nkhani zake. Nthaŵi zina tingathetse malingaliro olakwa ameneŵa mwa mkhalidwe wathu wamaganizo waulemu ndipo, ngati kutheka, mwa kupereka kwa olamulirawo chithunzi cholongosoka cha ntchito ndi zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Kwa nduna zotanganitsidwa, brosha lakuti Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century lingapereke mafotokozedwe achidule. Kuti apeze chidziŵitso chochulukirapo, angagaŵiridwe buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, chiŵiya chabwino chimene chiyenera kukhala ndi malo pa mashelufu a malaibulale a onse akumaloko ndi amtunduwo.
Ulamuliro m’Mabanja Achikristu
14, 15. (a) Kodi nchiyani chimene chili maziko a ulamuliro m’banja Lachikristu? (b) Kodi mkhalidwe wamaganizo wa akazi uyenera kukhala wotani kulinga kwa amuna awo, ndipo nchifukwa ninji?
14 Nkwachionekere kuti ngati Mulungu amafuna Akristu kusonyeza ulemu woyenerera ku maulamuliro adziko, iwo ayeneranso kulemekeza dongosolo laulamuliro lokhazikitsidwa ndi Mulungu m’mabanja Achikristu. Mtumwi Paulo analongosola mwachidule lamulo la mkhalidwe la umutu limene limafunga pakati pa anthu a Yehova. Iye analemba kuti: “Ndifuna kuti mudziŵe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Limeneli ndi lamulo la mkhalidwe la teokrase, kapena ulamuliro wa Mulungu. Kodi limaphatikizapo chiyani?
15 Ulemu kaamba ka teokrase umayambira m’banja. Mkazi Wachikristu amene samasonyeza ulemu woyenerera pa ulamuliro wa mwamuna wake—kaya akhale wokhulupirira mnzake kapena ayi—sali wateokratiki. Paulo anapereka uphungu kwa Akristu kuti: ‘[Gonjerani kwa, NW] wina ndi mnzake m’kuwopa Kristu. Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa [mpingo, NW], ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. Komatu monga [mpingo, NW] umvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse.’ (Aefeso 5:21-24) Monga momwe amuna Achikristu ayenera kugonjera ku umutu wa Kristu, akazi Achikristu ayenera kuzindikira nzeru ya kugonjera ku ulamuliro wa amuna awo woperekedwa ndi Mulungu. Zimenezi zidzawadzetsera chikhutiro chakuya cha mumtima ndipo, chofunika koposa, dalitso la Yehova.
16, 17. (a) Kodi ndimotani mmene ana oleredwa m’mabanja Achikristu angadzisiyanitsire ndi achichepere ambiri lerolino, ndipo kodi ali ndi chifukwa chotani? (b) Kodi Yesu anali chitsanzo chabwino motani kwa achichepere lerolino, ndipo kodi iwo akulimbikitsidwa kuchitanji?
16 Ana ateokratiki amakonda kusonyeza ulemu woyenera kwa makolo awo. Ponena za mbadwo wa achichepere m’masiku otsiriza, kunaloseredwa kuti iwo akakhala “osamvera akuwabala.” (2 Timoteo 3:1, 2) Koma kwa ana Achikristu Mawu ouziridwa a Mulungu amati: “Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:20) Ulemu kaamba ka ulamuliro wa makolo umakondweretsa Yehova ndi kudzetsa dalitso lake.
17 Zimenezi zikusonyezedwa ndi chochitika cha Yesu. Cholembedwa cha Luka chimati: “Ndipo anatsika nawo pamodzi [makolo ake] nadza ku Nazarete; [ndipo anapitiriza kuwagonjera, NW] iwo: . . . Ndipo Yesu anakulabe m’nzeru ndi mumsinkhu, ndi m’chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.” (Luka 2:51, 52) Yesu anali ndi zaka 12 panthaŵiyo, ndipo mtundu wa mneni Wachigiriki wogwiritsiridwa ntchito panopo umagogomezera kuti “anapitiriza kuwagonjera” makolo ake. Chotero kugonjera kwake sikunathe pamene analoŵa muunyamata. Ngati achicheperenu mufuna kukula mu uzimu ndi m’chisomo cha Yehova ndi cha anthu opembedza, muyenera kusonyeza ulemu kaamba ka ulamuliro m’banja lanu ndi kunja kwake.
Ulamuliro mu Mpingo
18. Kodi Mutu wa mpingo Wachikristu ndani, ndipo kodi wapereka kwa yani ulamuliro?
18 Polankhula za kufunika kwa dongosolo mu mpingo Wachikristu, Paulo analemba kuti: “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; . . . Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka [kapena, “monga mwa dongosolo,” NW, mawu amtsinde].” (1 Akorinto 14:33, 40) Kuti zinthu zonse zichitike m’njira yadongosolo, Kristu, Mutu wa mpingo Wachikristu, wapereka ulamuliro kwa amuna okhulupirika. Timaŵerenga kuti: “Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki . . . koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Kristu.”—Aefeso 4:11, 12, 15.
19. (a) Kodi Yesu waika yani kuti ayang’anire zinthu zake zonse zapadziko lapansi, ndipo nkwayani kumene wapereka ulamuliro wapadera? (b) Kodi ndi kuperekedwa kwa ulamuliro kotani kumene kumachitika mu mpingo Wachikristu, ndipo kodi kumeneku kumafunanji kwa ife?
19 M’nthaŵi ino ya mapeto, Kristu waika kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuyang’anira “zinthu zake zonse,” kapena zabwino za Ufumu pa dziko lapansi. (Mateyu 24:45-47) Mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, kapolo ameneyu amaimiridwa ndi bungwe lolamulira la amuna Achikristu odzozedwa amene Kristu wapatsa ulamuliro wakupanga zosankha ndi kuika oyang’anira ena. (Machitidwe 6:2, 3; 15:2) Nalonso, Bungwe Lolamulira limapereka ulamuliro ku Makomiti Anthambi, oyang’anira zigawo ndi madera, ndi akulu mu uliwonse wa mipingo yoposa 73,000 ya Mboni za Yehova kuzungulira dziko lapansi. Amuna onseŵa Achikristu odzipereka ayenerera chichirikizo ndi ulemu wathu.—1 Timoteo 5:17.
20. Kodi nchitsanzo chotani chimene chikusonyeza kuti Yehova sakondwera ndi awo amene alibe ulemu kaamba ka Akristu anzawo amene ali ndi ulamuliro?
20 Ponena za ulemu umene tiyenera kupatsa awo okhala ndi ulamuliro mu mpingo Wachikristu, kuyerekezera kokondweretsa kwa zimenezo ndi kugonjera kwathu ku maulamuliro adziko kungapangidwe. Pamene munthu aswa lamulo laumunthu limene Mulungu amavomereza, chilango choperekedwa ndi “mafumu” chili, kwenikweni, chisonyezero mwanjira ina cha mkwiyo wa Mulungu kwa “wochita zoipa.” (Aroma 13:3, 4) Ngati Yehova amakwiya pamene munthu aswa malamulo aumunthu ndipo asoŵa ulemu woyenera kaamba ka maulamuliro adziko, ayenera kukhala wosakondwa kwambiri chotani nanga ngati Mkristu wodzipatulira anyalanyaza malamulo a mkhalidwe a Baibulo ndi kusonyeza kupanda ulemu kwa Akristu anzake amene ali ndi ulamuliro!
21. Kodi ndi uphungu uti wa m’Malemba umene tidzakhala ofunitsitsa kutsatira, ndipo kodi nchiyani chimene chidzapendedwa m’nkhani yotsatira?
21 Mmalo mwa kukhala wosayanjidwa ndi Mulungu chifukwa cha kukhala ndi mkhalidwe wamaganizo wachipanduko kapena wakudziimira, tidzatsatira uphungu wa Paulo kwa Akristu a ku Filipi wakuti: “Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthaŵi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m’dziko lapansi.” (Afilipi 2:12-15) Mosiyana ndi mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka wamakono umene wadzidzetsera tsoka la ulamuliro, anthu a Yehova amagonjera mofunitsitsa ku ulamuliro. Motero amapeza mapindu ochuluka, monga momwe tidzaonera m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yapitayo.
Mwa Kupenda
◻ Kodi Wolamulira Wamkulukulu ndani, ndipo nchifukwa ninji ulamuliro wake uli walamulo?
◻ Kodi maulamuliro aakulu ali ‘oikidwa [m’malo awo aang’ono,] ndi Mulungu’ m’lingaliro lotani?
◻ Kodi ndiliti pamene maulamuliro aakulu amasiya kukhala “mtumiki wa Mulungu”?
◻ Kodi ndi dongosolo lotani laulamuliro limene lili m’mabanja Achikristu?
◻ Kodi ndi kuperekedwa kwa ulamuliro kotani kumene kuli mu mpingo Wachikristu?
[Zithunzi patsamba 18]
Yesu anati: “Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara”