Kugonjera Kwathu Kochepa ku Maulamuliro Aakulu
‘Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera.’—AROMA 13:5.
1. Kodi ndi zokumana nazo zovuta zotani zimene Mboni za Yehova zinakhala nazo pamanja a maulamuliro aakulu a Nazi, ndipo kodi izi zinachitika chifukwa cha ‘kuchita zoipa’?
PA JANUARY 7, 1940, Franz Reiter ndi achichepere ena asanu a ku Austria anaphedwa pa makina onyongera. Iwo anali a Bibelforscher, Mboni za Yehova, ndipo anafa chifukwa chakuti anakana mwachikumbumtima kumenyera nkhondo Ufumu wa Hitler. Reiter anali mmodzi wa Mboni zikwi zambiri zimene zinafera chikhulupiriro chawo m’nkhondo yadziko yachiŵiri. Ena ambiri anapirira kwa zaka zambiri m’misasa yachibalo. Kodi onsewa anavutika ndi “lupanga” la maulamuliro aakulu a Nazi chifukwa chakuti ‘ankachita choipa’? (Aroma 13:4) Kutalitali! Mawu otsatira a Paulo akusonyeza kuti Akristu ameneŵa anamvera malamulo a Mulungu m’Aroma mutu 13, ngakhale kuti iwo anavutika pamanja a ulamuliro.
2. Kodi nchiti chomwe chiri chifukwa chachikulu chokhalira wogonjera ku maulamuliro aakulu?
2 Pa Aroma 13:5, mtumwiyo analemba motere: ‘Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbumtima.’ Koyambirirako, Paulo adanena kuti kugwira “lupanga” kwa ulamuliro kunali chifukwa chabwino chokhalira wogonjera kwa iwo. Komabe, iye tsopano akupereka chifukwa champhamvu: chikumbumtima. Timakalamira kutumikira Mulungu ndi ‘chikumbumtima choyera.’ (2 Timoteo 1:3) Baibulo limatiuza kuti tiyenera kukhala ogonjera ku maulamuliro aakulu, ndipo timamvera chifukwa chakuti timafuna kuchita chabwino pamaso pa Mulungu. (Ahebri 5:14) Ndithudi, chikumbumtima chathu chophunzitsidwa ndi Baibulo chiyenera kutisonkhezera kumvera ulamuliro ngakhale pamene palibe munthu wotiyang’anira.—Yerekezerani ndi Mlaliki 10:20.
‘Chifukwa cha Ichi Mupatsanso Msonkho’
3, 4. Kodi ndi mbiri yabwino yotani imene Mboni za Yehova ziri nayo, ndipo nchifukwa ninji Akristu ayenera kukhoma misonkho?
3 Zaka zingapo zapitazo, mu Nigeria mudali zipoloŵe chifukwa cha kukhoma misonkho. Anthu ambiri anafa, ndipo maulamuliro anaitana gulu lankhondo. Asilikaliwo analoŵa m’Nyumba Yaufumu m’mene msonkhano unkachitika ndipo anafunsa cholinga cha kusonkhanako. Pamene anapeza kuti unali msonkhano wa phunziro la Baibulo wa Mboni za Yehova, ofisala wamkulu anauza asilikaliwo kuchokapo, akumati: “Mboni za Yehova sizimakwiya ndi msonkho.”
4 Mboni za ku Nigeriazo zinali ndi mbiri yabwino ya kukhala mogwirizana ndi mawu a Paulo awa: ‘Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.’ (Aroma 13:6) Pamene Yesu adapereka lamulo lakuti, ‘Patsani kwa Kaisara zake za Kaisara,’ iye ankalankhula za kukhoma msonkho. (Mateyu 22:21) Maulamuliro akudziko amapereka misewu, chitetezo cha apolisi, malaibulale, dongosolo la zoyendera ndi zamtengatenga, sukulu, mapositi ofesi, ndi zina zambiri. Timazigwiritsira ntchito zinthu zimenezi kaŵirikaŵiri. Nkoyenerera kuti tizikhomere misonkho.
‘Perekani kwa Anthu Onse Mangawa Awo’
5. Kodi mawu akuti “perekani kwa anthu onse mangawa awo” amatanthauzanji?
5 Paulo akupitiriza kuti: ‘Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu.’ (Aroma 13:7) Liwu lakuti “onse” limaphatikizapo ulamuliro uliwonse wakudziko umene uli mtumiki wa anthu wa Mulungu. Palibe wosiidwapo. Ngakhale ngati tikukhala pansi pa dongosolo landale limene ifeyo mwaumwini sitimalikonda, timakhomabe misonkho. Ngati kumene timakhalako zipembedzo zimapatulidwa pa kukhoma msonkho, mipingo ingatenge mwaŵiwu. Ndipo mofanana ndi nzika zina, Akristu angagwiritsire ntchito makonzedwe alamulo alionse amene apangidwa kuchepetsako misonkho imene amaikhoma. Koma palibe Mkristu amene ayenera kupeŵa kukhoma misonkho mopanda lamulo.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:41; 17:24-27.
6, 7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhoma misonkho ngakhale ngati ndalamazo zimagwiritsidwa ntchito kulipirira chinachake chimene sitimagwirizana nacho kapena ngakhale ngati olamulira atizunza?
6 Komabe, bwanji ngati msonkhowo ukuwoneka kukhala wosalungama. Kapena bwanji ngati ndalama zina za msonkhozo zikugwiritsiridwa ntchito kuchilikiza chinachake chimene sitimagwirizana nacho, monga ngati kuchotsa mimba kwaulere, malo osungira mwazi, kapena maprogramu amene amawombana ndi malingaliro athu a uchete? Ife timakhomabe misonkho yathu yonse. Uli ulamulirowo umene uyenera kukhala ndi thayo la mmene umagwiritsirira ntchito ndalama za msonkhozo. Ife sitinatumidwe kuweruza ulamuliro. Mulungu ndiye “Woweruza wa dziko lapansi,” ndipo m’nthaŵi yake, iye adzaŵerengera maboma ponena za mmene anaugwiritsirira ntchito ulamuliro wawo. (Salmo 94:2; Yeremiya 25:31) Kufikira zimenezo zitachitika, tidzapitiriza kukhoma misonkho yathu.
7 Kodi bwanji ngati olamulira atizunza? Ife tikhomebe misonkho yathu chifukwa cha mautumiki a tsiku ndi tsiku amene amaperekedwa. Ponena za Mboni zovutika ndi chizunzo m’dziko lina la mu Afirika, Examiner ya ku San Francisco inati: “Inu mungathe kuziona izo kukhala nzika zopereka chitsanzo. Izo zimakhoma misonkho mwakhama, kusamalira odwala, kumenyana ndi kusadziŵa kuŵerenga ndi kulemba.” Inde, Mboni zozunzidwazo zinakhoma misonkho yawo.
“Kuopa” ndi “Ulemu”
8. Kodi ndi “kuopa” kotani kumene timapereka kwa olamulira?
8 “Kuopa” kwa pa Aroma 13:7 sikuopa kwamantha koma, mmalo mwake, ulemu kaamba ka ulamuliro wakudziko, kuopa kuswa lamulo lake. Ulemu umenewu umaperekedwa chifukwa cha udindo woloŵetsedwamo, osati nthaŵi zonse chifukwa cha munthu wokhala paudindowo. Baibulo, polankhula mwaulosi za wolamulira Wachiroma Tiberiyo, linamutcha iye “munthu woluluka.” (Danieli 11:21) Koma iye ndiye anali wolamulira, ndipo motero, Mkristu anafunikira kumuopa ndi kumpatsa ulemu.
9. Kodi ndinjira zina ziti zimene timaperekera ulemu ku maulamuliro a anthu?
9 Ponena za ulemu, timatsatira lamulo la Yesu lakusapereka maina aulemu ozikidwa pa maudindo achipembedzo. (Mateyu 23:8-10) Koma ponena za maulamuliro akudziko, timakhala achimwemwe kuwaitana ndi dzina laulemu lirilonse limene lingafunikire kuwapatsa ulemu. Paulo anagwiritsira ntchito liwu lakuti “Womvekatu” polankhula kwa abwanamkubwa Achiroma. (Machitidwe 26:25) Danieli anatcha Nebukadinezara “mbuye wanga.” (Danieli 4:19) Lerolino, Akristu angagwiritsire ntchito mawu akuti “Ambuye” kapena “Wolemekezeka.” Iwo angaimirire pamene woweruza aloŵa m’chipinda cha milandu kapena kuwerama mwaulemu pamaso pa wolamulira ngati umenewo ndiwo mwambo.
Kugonjera Kochepa
10. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti pali malire ku zimene ulamuliro wa anthu ungafune kwa Mkristu?
10 Popeza kuti Mboni za Yehova zimagonjera ku ulamuliro wa anthu, kodi nchifukwa ninji Franz Reiter ndi ena ambiri anavutika monga mmene anachitiramo? Chifukwa chakuti kugonjera kwathu nkochepa, ndipo ulamuliro nthaŵi zonse sumazindikira kuti pali malire oikiridwa ndi Baibulo ku zimene ungafune. Ngati ulamuliro ufuna chinachake chimene chimalakwira chikumbumtima chophunzitsidwa Chachikristu, uwo ukupyola malire oikiridwa ndi Mulungu. Yesu anasonyeza ichi pamene ananena kuti: ‘Patsani . . . kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.’ (Mateyu 22:21) Pamene Kaisara afuna za Mulungu, tiyenera kuzindikira kuti Mulungu ndiye ali woyambirira.
11. Kodi ndilamulo lamakhalidwe abwino liti limene limasonyeza kuti pali malire ku zimene ulamuliro wa anthu ungafune limene limavomerezedwa mofala?
11 Kodi kaimidwe kameneka nkopotozeka kapena kachinyengo? Ayi ndithu. Kwenikweni, iko kali mbali ina ya lamulo lamakhalidwe abwino lozindikiridwa ndi mitundu yambiri yotsungula. M’zaka za zana la 15, munthu wina wotchedwa Peter von Hagenbach anazengedwa mlandu woyambitsa ulamuliro wankhalwe m’dera la ku Ulaya limene iye ankalamulira. Kudzichinjiriza kwake kwakuti iye ankangotsatira malamulo a mbuye wake, Wolamulira wa ku Burgundy, kunakanidwa. Kunena kumeneku kwakuti munthu wochita nkhanzayo sali woŵerengeredwa ngati akungotsatira malamulo a ulamuliro waukulu kwapangidwa nthaŵi zambiri chiyambire nthaŵiyo—makamaka ndi apandu a nkhondo ya Nazi pamaso pa Khoti la Mitundu Yonse mu Nuremberg. Kudzinenerako kwakanidwa kaŵirikaŵiri. Khoti la Mitundu Yonse linanena motere m’chiweruzo chake: “Anthu ali ndi mathayo a mitundu yonse amene amapyola mathayo a kumvera koperekedwa ndi boma limodzi.”
12. Kodi nziti zimene ziri zina za zitsanzo Zamalemba za atumiki a Mulungu amene anakana kumvera zofuna zosalingalira za olamulira?
12 Atumiki a Mulungu nthaŵi yonse azindikira kuti chigonjero chimene iwo amachipereka mowona mtima ku maulamuliro aakulu chiri ndi polekezera. Pafupifupi ndi nthaŵi imene Mose anabadwa mu Igupto, Farao analamulira anamwino aŵiri Achihebri kupha ana aamuna onse obadwa kumene Achihebri. Komabe, anamwinowo anasunga anawo amoyo. Kodi iwo adalakwa kusamvera Farao? Ayi, iwo ankatsatira chikumbumtima chawo chopatsidwa ndi Mulungu, ndipo Mulungu anawadalitsa chifukwa cha chimenecho. (Eksodo 1:15-20) Pamene Israyeli anali muukapolo m’Babulo, Nebukadinezara analamula kuti nduna zake, kuphatikizapo Ahebri awa, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, agwade pamaso pa chifano chimene anachiimika m’chigwa cha Dura. Ahebri atatuwo anakana. Kodi iwo adali olakwa? Ayi, popeza kuti kulabadira lamulo la mfumulo kukanatanthauza kusamvera lamulo la Mulungu.—Eksodo 20:4, 5; Danieli 3:1-18.
“Kumvera Mulungu Monga Wolamulira”
13. Kodi Akristu oyambirira anapereka chitsanzo chotani m’nkhani ya chigonjero chochepa kwa maulamuliro aakulu?
13 Mofananamo, pamene olamulira Achiyuda analamula Petro ndi Yohane kuleka kulalikira za Yesu, iwo anayankha kuti: “Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu.” (Machitidwe 4:19; 5:29) Iwo sakadakhala chete. Magazini akuti The Christian Century akusimba za kaimidwe kena kolimba mtima kamene Akristu oyambirira anakatenga pamene akunena kuti: “Akristu oyambirira sanatumikire m’magulu ankhondo. Roland Bainton akunena kuti ‘kuyambira kumapeto kwa nyengo ya Chipangano Chatsopano mpaka ku zaka khumi za A.D. 170-180 palibe umboni uliwonse wakuti Akristu anali m’gulu lankhondo’ (Christian Attitudes Toward War and Peace [Abingdon, 1960], mas. 67-8). . . . Swift akunena kuti Justin Martyr ‘amachilingalira kukhala chinthu chodziŵikiratu kuti Akristu amapeŵa machitidwe achiwawa.’”
14, 15. Kodi ndiati amene ali ena a malamulo amakhalidwe abwino a m’Baibulo amene analamulira kumvera kochepa kwa Akristu oyambirira ku maulamuliro a anthu?
14 Kodi nchifukwa ninji Akristu oyambirira sanatumikire monga asilikali? Mosakaikira, aliyense wa iwo anaphunzira mosamalitsa Mawu a Mulungu ndi malamulo napanga chosankha chake chaumwini pamaziko a chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Baibulo. Iwo anali auchete, “siali a dziko lapansi,” ndipo uchete wawo umawaletsa kutenga mbali m’mikangano ya dziko lino. (Yohane 17:16; 18:36) Kuwonjezera apa, iwo nga Mulungu. (2 Timoteo 2:19) Kutaya miyoyo yawo mu imfa chifukwa cha Boma kukanatanthauza kupatsa Kaisara zake za Mulungu. Ndiponso, iwo anali mbali ya ubale wa mitundu yonse womangidwa pamodzi ndi chikondi. (Yohane 13:34, 35; Akolose 3:14; 1 Petro 4:8; 5:9) M’chikumbumtima chabwino iwo sakanamenya nkhondo ndi kuthekera kwa kupha Mkristu mnzawo.
15 Kuwonjezera pa chimenechi, Akristu sakakhalamo ndi phande m’zikumbukiro zofala zachipembedzo, monga ngati kulambira wolamulira. Monga chotulukapo, iwo anawonedwa kukhala “anthu achilendo ndi owopsa, ndipo anthu ena onsewo anawakaikira iwo.” (Still the Bible Speaks, lolembedwa ndi W. A. Smart) Ngakhale kuti Paulo analemba kuti Akristu ayenera kupereka ‘kuopa kwa eni ake a kuwaopa,’ iwo sanaiwale kuopa kwawo kwakukulu, kapena ulemu kwa Yehova. (Aroma 13:7; Salmo 86:11) Yesu iyemwini anati: “Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m’gehena.”—Mateyu 10:28.
16. (a) Kodi ndi m’mbali ziti mmene Akristu ayenera kusanthula mosamalitsa chigonjero chawo ku maulamuliro aakulu? (b) Kodi bokosi lapatsamba 27 likufotokozanji mwafanizo?
16 Monga Akristu, timayang’anizana ndi zitokoso zofananazo lerolino. Sitingakhale ndi mbali mu mtundu wamakono uliwonse wa kulambira mafano—kaya kukhale kuchitira fano kapena chiphiphiritso m’chitidwe wakulambira kapena kupanga ndemanga za chipulumutso kwa munthu kapena gulu. (1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Ndipo mofanana ndi Akristu oyambirira, sitingagonjeretse uchete wathu Wachikristu.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:4.
‘Chifatso ndi Ulemu Wakuya’
17. Kodi Petro anapereka uphungu wotani kwa awo ovutika chifukwa cha chikumbumtima?
17 Mtumwi Petro analemba za kaimidwe kathu kolimbamtima nati: ‘Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.’ (1 Petro 2:19) Inde, ndichisomo kwa Mulungu pamene Mkristu achilimika mosasamala kanthu za chizunzo, ndipo pali phindu lowonjezereka kuti chikhulupiriro cha Mkristuyo chimalimbitsidwa ndi kuyengedwa. (Yakobo 1:2-4; 1 Petro 1:6, 7; 5:8-10) Petro analembanso kuti: ‘Komatu ngati mukamva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhaŵa; koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakufunsa chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso ndi ulemu wakuya.’ (1 Petro 3:14, 15) Uphungu wothandizadi!
18, 19. Kodi mkhalidwe wa ulemu wakuya ndi kulingalira ungathandize motani ngati olamulira aika malire ku ufulu wathu wa kulambira?
18 Pamene chizunzo chibuka chifukwa chakuti olamulira sakumvetsetsa kaimidwe Kachikristu kapena chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko anenera Mboni za Yehova molakwa kwa olamulira, kupereka zifukwa zenizeni kwa olamulira kungatulukepo kuchepetsedwa kwa chitsenderezo. Pokhala ndi chifatso ndi ulemu wakuya, Mkristu sabwezera mwakuthupi kwa ozunzawo. Komabe, iye amagwiritsira ntchito njira iriyonse ya lamulo imene iripo kuchinjiriza chikhulupiriro chake. Kenaka iye amasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova.—Afilipi 1:7; Akolose 4:5, 6.
19 Ulemu wakuya umatsogozanso Mkristu kuchita zimene angathe, kumvera ulamuliro popanda kulakwira chikumbumtima chake. Mwachitsanzo, ngati misonkhano yampingo yaletsedwa, Akristu adzapeza njira zina zosawonekera kwambiri kuti apitirize kudya pagome la Yehova. Wolamulira Wamkulukulu, Yehova Mulungu, akutiuza kupyolera mwa Paulo kuti: ‘Tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena.’ (Ahebri 10:24, 25) Koma kusonkhana koteroko kungachitidwe mochenjera. Ngakhale ngati anthu ochepa okha ndiwo apezekapo, tingakhale ndi chidaliro kuti Mulungu amadalitsa makonzedwe oterowo.—Yerekezerani ndi Mateyu 18:20.
20. Ngati kulalikidwa kwapoyera kwa mbiri yabwino kwaletsedwa, kodi Akristu angachite motani ndi mkhalidwewo?
20 Mofananamo, maulamuliro ena aletsa kulalikidwa kwapoyera kwa mbiri yabwino. Akristu okhala pansi pa uyang’aniro wawo amakumbukira kuti, kupyolera mwa Yesu iyemwiniyo, Wolamulira Wamkulukuluyo anati: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Chotero, iwo amamvera Wolamulira Wamkulukuluyo mosasamala kanthu za zomwe zingawachitikire. Kumene kunali kotheka, atumwiwo analalikira poyera ndi kunyumba ndi nyumba, koma pali njira zina zowafikira anthu, monga ngati umboni wamwamwaŵi. (Yohane 4:7-15; Machitidwe 5:42; 20:20) Kaŵirikaŵiri olamulira samaloŵereramo m’ntchito yolalikira ngati Baibulo lokha ndilo likugwiritsidwa ntchito—chimene chikugogomezera kufunika kwa Mboni zonse kukhala zophunzitsidwa bwino kukambitsirana za m’Malemba. (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:2, 17.) Mwakukhala olimba mtima, komabe aulemu, Akristu kaŵirikaŵiri angapeze njira yomvera Yehova popanda kuputa mkwiyo wa maulamuliro aakulu.—Tito 3:1, 2.
21. Ngati Kaisara sakufuna kuleka chizunzo chake, kodi Akristu angasankhe kuchita chiyani?
21 Komabe, nthaŵi zina olamulira samafuna kuleka kuzunza Akristu. Pamenepo, m’chikumbumtima choyera, tingangopirira m’kuchita zabwino. Franz Reiter wachichepereyo anayang’anizana ndi chosankha ichi: kugonjeretsa chikhulupiriro chake kapena kufa. Popeza kuti iye sakadaleka kulambira Mulungu, molimba mtima anasankhapo kufa. Usiku wake womalizira asanafe, Franz anawalembera amayi ake motere: “Ndidzanyongedwa mmawa m’mamawa. Ndiri ndi nyonga yochokera kwa Mulungu, monga momwedi zinakhalira ndi Akristu onse okhulupirika akumbuyoku . . . Ngati mudzachirimika kufikira imfa, tidzawonananso m’chiukiriro.”
22. Kodi tiri ndi chiyembekezo chotani, ndipo kodi pakali pano tiyenera kupitiriza kumachitanji?
22 Tsiku lina anthu onse adzakhala pansi pa lamulo limodzi lokha, lija la Yehova Mulungu. Kufikira nthaŵi imeneyo, tiyenera kulabadira ndi chikumbumtima chabwino makonzedwe a Mulungu ndi kusungabe kugonjera kwathu kochepa ku maulamuliro aakulu pamene tikumvera Mfumu Ambuye Yehova m’zinthu zonse.—Afilipi 4:5-7.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi nchiti chomwe chiri chifukwa chachikulu chokhalira wogonjera ku maulamuliro aakulu?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuzengereza pokhoma misonkho yoikidwa ndi Kaisara?
◻ Kodi tiyenera kupereka ulemu wotani kwa olamulira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kugonjera kwathu kwa Kaisara kuli kochepa chabe?
◻ Ngati tikuzunzidwa chifukwa chakuti Kaisara akufuna zake za Mulungu, kodi tiyenera kuchita motani?
[Bokosi patsamba 27]
Ulemu, osati kulambira
Mmawa wina mkati mwa kalasi, Terra, Mboni ya Yehova yachichepere ya ku Canada, anawona kuti mphunzitsi wake anatenga wophunzira mnzake kunka naye kunja kwa kalasi kwa mphindi zochepa. Mwamsanga pambuyo pake, mphunzitsiyo anampempha Terra mwakachetechete kutsagana nawo ku ofesi ya mphunzitsi wamkulu wapasukulupo.
Pamene anafika kumeneko, Terra anaona mbendera ya Canada itayalidwa pa desiki la mphunzitsi wamkulu wapasukulupo. Mphunzitsiyo anauza Terra kulavulira pa mbenderayo! Iye anati popeza kuti Terra samaimba nyimbo yafuko kapena kupereka sawatcha ku mbendera, panalibe chifukwa chimene angakanire kuchita chinthu choterocho. Terra anakana, akumalongosola kuti ngakhale kuti Mboni za Yehova sizimalambira mbendera, izo zimailemekeza.
Atabwerera m’kalasimo, mphunzitsiyo analengeza kuti wangopanga kufufuza. Iye anatenga ophunzira aŵiri pa nthaŵi zosiyana kunka ku ofesi ya mphunzitsi wamkulu wapasukulupo nawauza kulavulira pa mbenderayo. Woyambayo amakhalamo ndi phande m’miyambo yautundu, koma analavulira pa mbendera pamene anauzidwa kutero. Mosiyana, Terra samaimba nyimbo yafuko kapena kupereka sawatcha ku mbendera; komabe, iye anakana kunyazitsa mbendera mwanjira imeneyi. Mphunzitsiyo anasonyeza kuti Terra ndiye anasonyeza ulemu woyenerera.—1990 Yearbook of Jehovah’s Witnesses.
[Mawu a Chithunzi patsamba 23]
French Embassy Press & Information Division
USSR Mission to the UN