Tsatirani Chitsanzo cha Yesu cha Kudzipereka Kwaumulungu
“Movomerezeka chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu chimenechi nchachikulu: ‘Iye [Yesu] anawonekera m’thupi.’”—1 TIMOTEO 3:16, “NW.”
1. (a) Kodi ndi funso lotani limene linakhala losayankhidwa kwa zaka zoposa 4,000? (b) Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene yankho linaperekedwera?
LINALI funso limene linakhala losayankhidwa kwa zaka zoposa 4,000. Chiyambire nthaŵi imene munthu woyamba, Adamu, analephera kusunga umphumphu, funso linali lakuti: Kodi ndimotani mmene kudzipereka kwaumulungu kungasonyezedwere pakati pa mtundu wa anthu? Pomalizira pake, m’zaka za zana loyamba C.E., yankho linaperekedwa ndi kudza kwa Mwana wa Mulungu ku dziko lapansi. M’lingaliro lirilonse, mawu, ndi kachitidwe, Yesu Kristu anasonyeza chigwirizano chake chaumwini kwa Yehova. Mwakutero, iye anavundukula ‘chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu,’ kusonyeza njira imene anthu odzipatulira ayenera kusungira kudzipereka koteroko.—1 Timoteo 3:16, NW.
2. Polondola kudzipereka kwaumulungu, kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira chitsanzo cha Yesu?
2 Polondola kudzipereka kwaumulungu monga Akristu odzipatulira, obatizidwa, timachita bwino ‘kulingalira’ chitsanzo cha Yesu. (Ahebri 12:3) Chifukwa ninji? Kaamba ka zifukwa ziŵiri. Choyamba, chitsanzo cha Yesu chingatithandize kukulitsa kudzipereka kwaumulungu. Yesu anadziŵa Atate wake bwino lomwe kuposa wina aliyense. (Yohane 1:18) Ndipo Yesu anatsanzira mosamalitsa njira ndi mikhalidwe ya Yehova kotero kuti anati: “Iye amene wandiona Ine waona Atate.” (Yohane 14:9) Kupyolera mwa moyo ndi uminisitala za Yesu, tingamvetsetse mozama mikhalidwe yabwino ya Yehova, mwakutero kulimbitsa chigwirizano chathu chaumwini kwa Mlengi wathu wachikondi. Chachiŵiri, chitsanzo cha Yesu chingatithandize m’kusonyeza kudzipereka kwaumulungu. Iye anakhazikitsa chitsanzo changwiro chakhalidwe losonyeza kudzipereka kwaumulungu. Mwakutero tingachite bwino kulingalira mmene ‘tingavalire Kristu,’ uko ndiko kuti, kumtenga monga chitsanzo chathu, kutsanzira chitsanzo chake.—Aroma 13:14.
3. Kodi programu yathu yaumwini ya kuphunzira Baibulo iyenera kuphatikizapo chiyani, ndipo nchifukwa ninji?
3 Sizonse zimene Yesu ananena ndi kuchita zimene zinasungidwa mwakulembedwa. (Yohane 21:25) Chotero, zinthu zimene zinalembedwa pansi pa chitsogozo chaumulungu ziyenera kukhala zosangalatsadi kwa ife. Chotero programu ya phunziro Labaibulo laumwini iyenera kuphatikizapo kuŵerenga zolembedwa za Uthenga Wabwino wa moyo wa Yesu. Koma ngati kuŵerenga koteroko kuti kutipindulitse m’kulondola kwathu kudzipereka kwaumulungu, tiyenera kutenga nthaŵi kusinkhasinkha moyamikira zimene taŵerenga. Tiyeneranso kukhala ogalamuka kuwona mopyola zodziŵikiratu.
Make Mbuu, Mwana Mbuu
4. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Yesu anali munthu waubwenzi ndi wachifundo chakuya? (b) Kodi ndi chiyambi chotani chimene Yesu anatenga pochita ndi ena?
4 Lingalirani chitsanzochi. Yesu anali munthu waubwenzi ndi wachifundo. Wonani pa Marko 10:1, 10, 13, 17, ndi 35 kuti anthu a misinkhu yonse ndi ziyambi anampeza kukhala wofikirika. Pa zochitika zambiri, iye ananyamula ana. (Marko 9:36; 10:16) Kodi nchifukwa ninji anthu, ngakhale ana, sanatekeseke ndi Yesu? Chifukwa cha chikondwerero chake chowona, chenicheni mwa iwo. (Marko 1:40, 41) Zimenezi zinawonekera m’chakuti anali woyamba kufikira ena ofuna thandizo. Mwakutero, timaŵerenga kuti ‘anawona’ mkazi wamasiye wa ku Nayini amene mwana wake wakufa ananyamulidwa. Iye ‘anayandikira’ naukitsa mnyamatayo, ndipo palibe paliponse pamene pakunena kuti winawake anampempha kuchita zimenezo. (Luka 7:13-15) Iye anachiritsanso mkazi wopunduka ndi mwamuna wambulu popanda kupemphedwa kuchita zimenezo.—Luka 13:11-13; 14:1-4.
5. Kodi zolembedwa zimenezi za uminisitala wa Yesu zikutiphunzitsanji ponena za mikhalidwe ndi njira za Yehova?
5 Pamene muŵerenga za zochitika zoterozo, imani ndi kudzifunsa kuti: ‘Popeza kuti Yesu anatsanzira mwangwiro Atate ake, kodi zochitika zimenezi zikundiuzanji ponena za mikhalidwe ndi njira za Yehova?’ Ziyenera kutitsimikizira kuti Yehova ali Mulungu waubwenzi ndi chifundo chakuya. Ukulu wa chikondwerero chomangirira chimenechi m’banja la anthu unamfulumiza kukhala woyamba m’kuchita nawo. Iye sanafunikire kukokosedwa kuti apereke Mwana wake “dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28; Yohane 3:16) Iye amafunafuna mwaŵi wa “kukondwera nawo” awo amene adzamtumikira chifukwa cha chikondi. (Deuteronomo 10:15) Mongadi mmene Baibulo likunenera kuti: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudziwonetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”—2 Mbiri 16:9.
6. Kodi nchiyani chimene chimatulukapo pamene tisinkhasinkha pa ubwenzi ndi chifundo cha Yehova monga zinasonyezedwa ndi Mwana wake?
6 Kusinkhasinkha pa ubwenzi ndi chifundo cha Yehova mwanjira imeneyi, monga zasonyezedwa ndi Mwana wake, kudzakhudza mtima wanu, kuudzaza ndi chiyamikiro chachikulu chamikhalidwe Yake yabwino yosangalatsa. Izinso, zidzakukokerani kwa iye. Mudzafulumizidwa kumfikira mwaufulu m’pemphero nthaŵi zonse ndiponso pansi pa mikhalidwe iriyonse. (Salmo 65:2) Kudzalimbitsa chigwirizano chanu chaumwini kwa iye.
7. Mutasinkhasinkha pa ubwenzi ndi chifundo cha Yehova, kodi muyenera kudzifunsa chiyani, ndipo nchifukwa ninji?
7 Ngakhale ndi tero, kumbukirani kuti kudzipereka kwaumulungu kumaphatikizapo zoposa kudzimva kwa kulambira. Monga mmene katswiri wa Baibulo R. Lenski akudziŵitsira, “kumaphatikizapo ulemu wathu wonse, mkhalidwe wakulambira ndi machitidwe otulukamo.” (Kanyenye ngwathu.) Chotero pambuyo posinkhasinkha pa ubwenzi ndi chifundo cha Yehova monga momwe zasonyezedwa ndi Yesu, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimotani mmene ndingakhalire ngati Yehova m’zinthu zimenezi? Kodi ena amandipeza kukhala wofikirika?’ Ngati ndinu kholo, muyenera kukhala wofikirika kwa ana anu. Ndipo ngati ndinu mkulu mu mpingo, ndithudi muyenera kukhala wofikirika. Pamenepa, kodi nchiyani chimene chingakupangeni kukhala wofikirika kwambiri? Ubwenzi ndi chifundo chakuya. Muyenera kukulitsa chikondwerero chowona mtima, chenicheni mwa ena. Pamene mumasamaliradi ena ndipo muli wofunitsitsa kudzipereka inu eni mmalo mwawo, iwo adzadziŵa zimenezi ndi kudzimva okokeredwa kwa inu.
8. (a) Kodi nchiyani chimene muyenera kukumbukira pamene mukuŵerenga zolembedwa za Baibulo za Yesu? (b) Kodi tikuphunziranji ponena za Yehova kuchokera ku zolembedwa zosonyezedwa m’mawu am’munsi?
8 Chotero pamene mukuŵerenga zolembedwa za Baibulo za Yesu, kumbukirani kuti mungaphunzire zambiri ponena za Yehova monga munthu kuchokera ku zinthu zimene Yesu ananena ndi kuchita.a Ndipo pamene chiyamikiro chanu cha mikhalidwe ya Mulungu, chonga chimene Yesu anasonyeza, chikufulumizani kukhala wofanana Naye, mukupereka umboni wa kudzipereka kwaumulungu.
Kusonyeza Kudzipereka Kwaumulungu Kulinga kwa Ziŵalo za Banja
9, 10. (a) Kodi chikondi ndi kudera nkhaŵa kwa Yesu kaamba ka amayi ake, Mariya, zinasonyezedwa motani pa mphindi zochepa zokha asanamwalire? (b) Mwachiwonekere, kodi nchifukwa ninji Yesu anaikizira chisamaliro cha Mariya kwa mtumwi Yohane ndipo osati kwa mmodzi wa abale ake akuthupi?
9 Moyo ndi uminisitala za Yesu Kristu zimavumbula zambiri ponena za mmene kudzipereka kwaumulungu kuyenera kusonyezedwera. Chitsanzo chokhudza mtima chalembedwa pa Yohane 19:25-27, pamene timaŵerenga kuti: “Koma [pamtengo wozunzirapo, NW] anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Mariya, mkazi wa Kleopa, ndi Mariya wa Magadala. Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda [Yohane], alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu! Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amayi wako. Ndipo kuyambira ola lomweli wophunzirayo ananka naye kwawo.”
10 Tangolingalirani zimenezo! Mphindi zochepa zokha asanapereke moyo wake wapadziko lapansi, chikondi ndi kudera nkhaŵa kwa Yesu zinamfulumiza kuikizira chisamaliro cha amayi ake, Mariya, (mwachiwonekere amasiye tsopano) kwa mtumwi wokondedwa Yohane. Koma kodi nchifukwa ninji Yohane ndipo osati mmodzi wa abale akuthupi a Yesu? Chifukwa chakuti Yesu anali wodera nkhaŵa osati ndi zosoŵa zakuthupi zokha za Mariya, koma makamaka ndi ubwino wauzimu. Ndipo mtumwi Yohane (mwinamwake msuwani wa Yesu) anatsimikizira kukhala wokhulupirika, pamene kuli kwakuti palibe umboni wakuti abale a Yesu akuthupi anali okhulupirira pa nthaŵiyo.—Mateyu 12:46-50; Yohane 7:5.
11. (a) Molingana ndi Paulo, kodi ndimotani mmene Mkristu angasonyezere kudzipereka kwaumulungu m’nyumba mwake? (b) Kodi nchifukwa ninji Mkristu weniweni amasamalira makolo okalamba?
11 Tsopano, kodi kumeneku kunali kuwonetsa kotani kwa kudzipereka kwaumulungu? Mtumwi Paulo akulongosola kuti: “Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu. Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera [makolo ndi agogo awo, NW]; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” (1 Timoteo 5:3, 4) Paulo akunena kuti kulemekeza makolo a wina mwakupereka zinthu zakuthupi pamene kufunika, kuli chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu. Motani? Yehova, Myambitsi wa kakonzedwe ka banja, akulamula ana kulemekeza makolo awo. (Aefeso 3:14, 15; 6:1-3) Chotero, Mkristu weniweni amazindikira kuti kusamalira thayo labanja lotelolo kumasonyeza osati chikondi chokha kwa makolo a wina komanso ulemu kwa Mulungu ndi chimvero ku malamulo ake.—Yerekezerani ndi Akolose 3:20.
12. Kodi ndimotani mmene mungasonyezere kudzipereka kwaumulungu kwa makolo okalamba, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala cholinga?
12 Pamenepa, kodi ndimotani mmene mungasonyezere kudzipereka kwaumulungu kulinga kwa ziŵalo za banja? Zimenezi zikaphatikizapo kupanga makonzedwe a kusamalira zosoŵa zauzimu ndi zakuthupi za makolo okalamba, monga mmene Yesu anachitira. Kulephera kuchita tero kukasonyeza kusoŵeka kwa kudzipereka kwaumulungu. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 3:2, 3, 5.) Mkristu wodzipatulira amapereka kwa makolo osoŵa osati kokha chifukwa cha chifundo kapena thayo koma chifukwa chakuti amakonda banja lake, ndipo amazindikira ukulu umene Yehova amaika pa kusamalira thayo loterolo. Chotero, kusamalira kwake makolo okalamba kuli chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu.b
13. Kodi ndimotani mmene tate Wachikristu angasonyezere kudzipereka kwaumulungu kulinga kwa banja lake?
13 Kudzipereka kwaumulungu kungasonyezedwe panyumba m’njira zina. Mwachitsanzo, tate Wachikristu ali ndi thayo la kupereka zinthu mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwauzimu kaamba ka banja lake. Chotero, kuwonjezera pa kupereka chirikizo lakuthupi, iye mwachikondi amakonzekera phunziro labanja Labaibulo lokhazikika. Amandandalitsa nthaŵi ya kugaŵana mokhazikika mu utumiki wakumunda ndi banja lake. Iye amakhala wachikatikati, akumazindikira kufunika kwawo kwa kupumula ndi zosangulutsa. Ndipo mwanzeru amaika zoyambirira, osalola ntchito za mpingo kumpangitsa kunyalanyaza banja lake. (1 Timoteo 3:5, 12) Kodi nchifukwa ninji amachita zonsezi? Osati kokha chifukwa cha thayo koma chifukwa cha chikondi kaamba ka banja lake. Iye amazindikira kufunika kumene Yehova amaika pa kusamalira banja la wina. Mwakukwaniritsa thayo lake monga mwanuna ndi tate, iye akuchita kudzipereka kwaumulungu.
14. Kodi ndimotani mmene mkazi Wachikristu angasonyezere kudzipereka kwaumulungu m’nyumba?
14 Nawonso akazi Achikristu ali ndi thayo la kusonyeza kudzipereka kwaumulungu panyumba. Motani? Baibulo likuti mkazi ayenera ‘kugonjera’ kwa mwamuna wake ndipo ayenera kukhala ndi “ulemu waukulu” kwa iye. (Aefeso 5:22, 33, NW) Ngakhale ngati mwamuna wake sali wokhulupirira, iye ayenera kukhala ‘wogonjera’ kwa iye. (1 Petro 3:1) Mkazi Wachikristu amasonyeza kugonjera kwamkazi mwakuchilikiza mwamuna wake m’zosankha zimene amapanga malinga ngati zimenezi siziwombana ndi malamulo a Mulungu. (Machitidwe 5:29) Ndipo kodi nchifukwa ninji amalandira thayo limeneli? Osati kokha chifukwa chakuti amakonda mwamuna wake koma makamaka chifukwa chakuti amazindikira kuti “kuyenera kwa Ambuye”—kuti kali kakonzedwe ka Mulungu ka banja. (Akolose 3:18) Kugonjera kwake kodzifunira kwa mwamuna wake kuli kasonyezedwe kake ka kudzipereka kwaumulungu.
“Ndinadzera Ichi”
15. Kodi ndim’njira yowonekera yotani imene Yesu anasonyezera kudzipereka kwaumulungu?
15 Njira imodzi yodziŵika kwambiri ya Yesu yosonyezera kudzipereka kwaumulungu inali mwa ‘kulalikira mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu.’ (Luka 4:43, NW) Pambuyo pa ubatizo wake mu Yordano mu 29 C.E., Yesu anathera zaka zitatu ndi theka zotsatira wotanganitsidwa ndi ntchito yofunika koposa imeneyi. “Ndinadzera ichi,” iye analongosola tero. (Marko 1:38; Yohane 18:37) Koma kodi ndimotani mmene kumeneku kunaliri kusonyeza kudzipereka kwaumulungu?
16, 17. (a) Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yesu kukhala wotanganitsidwa mokulira ndi kulalikira ndi kuphunzitsa? (b) Kodi nchifukwa ninji uminisitala wa Yesu wa kulalikira ndi kuphunzitsa unali chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu?
16 Kumbukirani kuti kudzipereka kwaumulungu kumaphatikizapo kukhala ndimoyo m’njira imene imakondweretsa Mulungu chifukwa chakuti mumamkonda ndi kuyamikira mwakuya mikhalidwe yake yosangalatsa. Pamenepa, kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yesu kuthera zaka zake zomalizira pa dziko lapansi ali wotanganitsidwa ndi kulalikira ndi kuphunzitsa? Kodi kunali kungodzimva wofunikira kuchita ntchito yake kapena thayo? Palibe chikaikiro chakuti anali wodera nkhaŵa ndi anthu. (Mateyu 9:35, 36) Ndipo anazindikira kotheratu kuti kudzozedwa kwake ndi mzimu woyera kunamuika ndi kumpatsa ntchito ya kuchita utumiki wake. (Luka 4:16-21) Komabe, zolinga zake zinazamirapo.
17 “Ndikonda Atate,” Yesu anawauza mosabisa atumwi ake pa usiku wake womalizira pano pa dziko lapansi. (Yohane 14:31) Chikondi chimenecho n’chozikidwa pa chidziŵitso chozama, chenicheni cha mikhalidwe ya Yehova. (Luka 10:22) Atasonkhezeredwa ndi mtima wofulumizidwa ndi chiyamikiro chozama, Yesu anapeza chisangalalo m’kuchita chifuniro cha Mulungu. (Salmo 40:8) Chinali “chakudya” chake—chofunikira kwenikweni kaamba ka moyo, chokoma kwambiri. (Yohane 4:34) Iye anakhazikitsa chitsanzo changwiro cha “kufuna choyamba ufumu” m’malo modziika poyamba. (Mateyu 6:33, NW) Chotero kusonyezedwa kwa kudzipereka kwake kwaumulungu sikunasonyezedwe kokha ndi zimene anachita kapena mmene anazichitira mu uminisitala wake wa kulalikira ndi kuphunzitsa koma chifukwa chimene anazichitira.
18. Kodi nchifukwa ninji kukhala ndi phande mu uminisitala sikuli kwenikwenidi chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu?
18 Kodi ndimotani mmene tingatsanzirire chitsanzo cha “chitsanzo” chathu Yesu, m’zimenezi? (1 Petro 2:21) Onse amene amavomereza ku chiitano cha Yesu chakuti “ukadze kuno, unditsate ine” ali ndi ntchito yaumulungu ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Luka 18:22; Mateyu 24:14; 28:19, 20) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti mwakukhala ndi phande m’kulengeza mbiri yabwino, tikulondola kudzipereka kwaumulungu? Osati kwenikweni. Ngati tingadziloŵetse mu uminisitala wosakangalika kapena woyerekezera, kapena kotero kuti tikondweretse ziŵalo za banja kapena ena, siungalingaliridwe konse kukhala ‘machitidwe a kudzipereka kwaumulungu.’—2 Petro 3:11, NW.
19. (a) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chifukwa choyamba cha zimene timachita mu uminisitala? (b) Kodi nchiyani chimene chimatulukapo pamene tafulumizidwa ndi chikondi chakuya kaamba ka Mulungu?
19 Mofanana ndi Yesu, zolinga zathu ziyenera kukhala zozama. Yesu anati: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse [malingaliro, zikhumbo, ndi kudzimva kwamkati kwa munthu], ndi moyo wako wonse [moyo wanu ndi umunthu wanu wonse], ndi nzeru zako zonse [mphamvu zanu za nzeru], ndi mphamvu yako yonse.” Ku izi, mlembi wozindikira anawonjezera kuti: “Ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.” (Marko 12:30, 33, 34) Chotero siziri kokha zimene timachita zimene ziri zofunika komanso chifukwa chimene timazichitira. Chikondi chozama kaamba ka Mulungu chimene chimalowetsamo mbali iriyonse chiyenera kukhala chifukwa choyamba cha zimene timachita mu uminisitala. Pamene ziri tero, sitidzakhutira ndi kukhala ndi phande kwapakamwa, koma tidzafulumizidwa kusonyeza kuzama kwa kudzipereka kwathu kwaumulungu mwakuchita zoposa. (2 Timoteo 2:15) Panthaŵi imodzimodziyo, pamene chikondi cha Mulungu chiri chisonkhezero chathu, sitidzakhala osuliza, kuyerekeza uminisitala wathu ndi wa ena.—Agalatiya 6:4.
20. Kodi ndimotani mmene tingapindulire mokwanira kuchokera ku chitsanzo cha Yesu cha kulondola kudzipereka kwaumulungu?
20 Tingakhale oyamikira chotani nanga kuti Yehova wativumbulira chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu! Mwakuphunzira mosamalitsa zimene Yesu ananena ndi kuchita ndikukalimira kumutsanzira, tidzathandizidwa kukulitsa ndi kusonyeza kudzipereka kwaumulungu ku mlingo wokwanira. Yehova adzatidalitsa molemera pamene tikutsatira chitsanzo cha Yesu m’kulondola kudzipereka kwaumulungu monga Akristu odzipatulira, obatizidwa.—1 Timoteo 4:7, 8.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka zitsanzo zina zowonjezereka, lingalirani zimene tikuphunzira ponena za Yehova m’zolembedwa zotsatirazi: Mateyu 8:2, 3; Marko 14:3-9; Luka 21:1-4; ndi Yohane 11:33-36.
b Kaamba ka kalongosoledwe kokwanira ka zimene zimaloŵetsedwamo m’kusonyeza kudzipereka kwaumulungu kulinga kwa makolo okalamba, onani Nsanja ya Olonda ya June 1, 1987, masamba 13-18.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Polondola kudzipereka kwaumulungu, kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira chitsanzo cha Yesu?
◻ Kodi tikuphunziranji ponena za Yehova kuchokera ku ubwenzi ndi chifundo chosonyezedwa ndi Yesu?
◻ Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kudzipereka kwaumulungu kulinga kwa ziŵalo za banja?
◻ Kuti uminisitala wathu ukhale chisonyezero cha kudzipereka kwaumulungu, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala cholinga chathu?
[Chithunzi patsamba 21]
Tate Wachikristu ali ndi thayo la kupereka zinthu kaamba ka banja lake mwakuthupi, mwamaganizo, ndi mwauzimu
[Chithunzi patsamba 23]
‘Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire . . . kubwezera makolo ndi agogo awo.’