Kuyamikira Kaamba ka Abale Athu
“Ndi chiyanjo chosanyenga chaubale . . . ,kondanani wina ndi mnzake kwenikweni kuchokera mu mtima..”—1 PETRO 1:22, NW.
1. Nchiyani chimene chinakhutiritsa anthu ambiri kuti Mboni za Yehova zimachita Chikristu chowona?
CHIKONDI chiri chizindikiritso cha Chikristu chowona. Mkati mwa chakudya chotsirizira chimene Yesu anagawana ndi atumwi ake, iye anagogomezera chimenechi, akumanena kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Anthu ambiri choyamba anakhala okhutiritsidwa kuti Mboni za Yehova zikuchita Chikristu chowona pamene anapezeka pa msonkhano pa Nyumba ya Ufumu kapena ku msonkhano waukulu. Iwo anawona chikondi chikugwira ntchito, ndipo chifukwa cha ichi anadziŵa kuti anali pakati pa ophunzira owona a Kristu.
2. Nchiyani chimene mtumwi Paulo akunena kulinga ku chikondi, chizindikiritso chapadera cha Chikristu?
2 Tonsefe timasangalala kuti chizindikiro chapadera chimenechi cha Chikristu chenicheni chiri chowonekera pakati pa anthu a Yehova lerolino. Ngakhale ndi tero, mofanana ndi Akristu oyambirira, timazindikira kuti tifunikira kufunafuna njira zina mokhazikika zosonyezera chiyamikiro kaamba ka abale athu. Paulo analemba ku mpingo mu Tesalonika kuti: “Koma Ambuye akukuliteseni inu, nakuchulukitseni m’chikondano wina kwa mnzake.” (1 Atesalonika 3:12) Ndimotani mmene tingawonjezekere m’chikondi chathu kaamba ka wina ndi mnzake?
Chikondi ndi Chiyanjo Chaubale
3. Mkuwonjezera ku kutsogoza moyo woyera, nchiyani chimene mtumwi Petro ananena kuti chinali choyenera kaamba ka Akristu?
3 M’kalata ya chisawawa yolembedwera ku mipingo ya Chikristu mu Asia Minor, mtumwi Petro analemba kuti: “Popeza mwayeretsa moyo wanu [kapena, miyoyo] pa kumvera chowonadi ndi [Chiyanjo chaubale, NW] chosanyenga [phi-la-del-phi’a], mukondane [mtundu wa a-ga-pa’o] kwenikweni kuchokera mu mtima.” (1 Petro 1:22) Petro akusonyeza kuti sichiri chowkwanira kuyeretsa miyoyo yathu. Chimvero chathu ku chowonadi, kuphatikizapo lamulo latsopano, chiyenera kutulukapo m’chiyanjo chaubale chosanyenga ndi chikondi chenicheni kaamba ka wina ndi mnzake.
4. Ndi mafunso otani amene tifunikira kufunsa, ndipo nchiyani chimene Yesu ananena m’chigwirizano ndi ichi?
4 Kodi chikondi chathu ndi chiyamikiro kaamba ka abale athu chiri chokhoterera kulongosoledwa kokha kwa awo omwe timkonda? Kodi timakhoterera kukhala owolowa manja kulinga kwa awa, tikumanyalanyaza zophophonya zawo, pamene tikukhala ofulumira kuzindikira zolakwa ndi zolephera za ena kwa amene sitimadzimva oyandikira mwachibadwa? Yesu ananena kuti: “Ngati muwakonda [mtundu wa a-ga-pa’o] akukondana ndi inu, mphoto yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?”—Mateyu 5:46.
5. Ndi kusiyana kotani kumene wophunzira wa Baibulo akupanga pakati pa liwu la Chigriki lotanthauza “chikondi” ndi lija lotanthauza “chiyanjo”?
5 M’bukhu lake New Testament Words, Profesa William Barclay akupanga ndemanga zotsatirazi pa liwu la Chigriki lotembenuzidwa “chiyanjo” ndi lolongosoledwa kukhala “chikondi”: “Pali kutentha kwachikondi ponena za mawu amenewa [phi-li’a, kutanthauza “chiyanjo,” ndi verebu yofanana nalo phi-le’o]. Iwo amatanthatuza kuyang’ana pa winawake ndi cholinga chachikondi. . . . Mawu ofala kwenikweni a C[hipangano] C[chatsopano] kaamba ka chikondi ali nauni agape ndi verebu agapan . . . Philia linali liwu lokondeka, koma ilo motsimikirzirika linali liwu la kutentha ndi kuyandikira kwathithithi ndi chiyanjo. . . . Agape limachita ndi maganizo: ilo siliri kokha lingaliro lomwe limabuka palokha m’mitima yathu; liri prinsipulo pa limene timakhala mwadala. Agape imachita kwakukulukulu ndi zofuna. Iko kuli kugonjetsa, kulakika, ndi kufikiritsa. Palibe ndi mmodzi yense mwachibadwa amene anakonda mdani wake. Kukonda mdani wa wina kuli kugonjetsa zikhoterero zathu zonse zachibadwa ndi zolinga. Agape ameneyu . . . ali m’chenicheni mphamvu ya kukonda zosakondeka, kukonda anthu amene sitimawakonda.”
6. (a) Ndi mafunso ofufuza otani omwe tifunikira kudzifunsa ife eni? (b) Mogwirizana ndi Petro, nchifukwa ninji sitifunikira kulekezera chiyanjo chathu chaubale kwa awo omwe timakonda mwachibadwa?
6 Pa chodzikanira chakuti Malemba amalola kukhala kwathu ndi malingaliro otentha kaamba ka abale ena kuposa ena, kodi tiri okhoterera ku kulinganiza kudziŵa kwathu? (Yohane 19:26; 20:2) Kodi timaganizira kuti tingalongosole “chikondi” chosafikapo, cholingaliridwa kwa ena chifukwa chakuti tifunikira kutero, pamene tikusungirira chiyanjo chaubale chotentha kaamba ka awo amene timakokedwerako? Ngati ndi tero, taphonya nsonga ya kulangiza kwa Petro. Sitinayeretse mokwanira miyoyo yathu ndi chimvero chathu ku chowonadi, popeza Petro akunena kuti: “Tsopano popeza kuti ndi chimvero ku chowonadi mwayeretsa miyoyo yanu kufikira mutadzimva ndi chiyanjo chenicheni kulinga kwa abale anu a Chikristu, kondanani wina ndi mnzake ndi mtima wonse ndi mphamvu zanu zonse.”—1 Peter 1:22, The New English Bible.
“Chiyanjo Chaubale Chosanyenga”
7, 8. Nchiyani chomwe chiri chiyambi cha liwu lotembenuzidwa “chosanyenga,” chotero nchifukwa ninji Petro anagwiritsira ntchito kalongosoledweka?
7 Mtumwi Petro akunena ngakhale mowonjezereka. Iye akunena kuti chiyanjo chathu chaubale chifunikira kukhala chosanyenga. Liwu lotembenuzidwa “chosanyenga” limabwera kuchokera ku liwu la Chigriki lotanthauza kusemphana ndi chenicheni lomwe linagwiritsiridwa ntchito kaamba ka oseŵera pa pulatiformu omwe analankhula ndi nkhope zawo zitaphimbidwa ndi zinyawu. Ichi chinawatheketsa iwo kusintha umunthu m’mbali zosiyanasiyana mkati mwa kuseŵerako. Liwulo kenaka linatenga lingaliro lophiphiritsira la kunyenga, kubisa, kapena kuyerekeza.
8 Kodi ndimotani mmene timadzimverera mkati mozama mwa mitima yathu kulinga kwa ena a abale ndi alongo mu mpingo? Kodi timawapatsa iwo moni pa misonkhano ndi kumwetulira kokakamizidwa, mwamsanga kupenya kwina kapena kungopitirira? Moipirakobe, kodi timayesera kupewa ngakhale kuwapatsa iwo moni? Ngati ndi tero, nchiyani chomwe chinganenedwe ponena za “kumvera kwathu ku chowonadi” chomwe chikanayenera kuyeretsa miyoyo yathu ku mlingo wa kudzimva achiyanjo chotsimikizirika kulinga kwa Akristu anzathu? Mwa kugwiritsira ntchito liwu lakuti “chosanyenga,” Petro akunena kuti chiyanjo chathu kaamba ka abale athu sichiyenera kvalidwa kaamba ka kuwonetsera. Chiyenera kukhala chenicheni, chochokera mu mtima.
“Kwenikweni Kuchokera mu Mtima”
9, 10. Nchiyani chimene Petro anatanthauza pamene ananena kuti tiyenera kukondana wina ndi mnzake “kwenikweni,” kapena “motambasuka”?
9 Petro akuwonjezera kuti: “mukondane kwenikweni [m’chenicheni, “motambasuka”] kuchokera mu mtima.” Ichi sichimafunikira kutambasula mtima kuti tisonyeze chikondi kwa awo amene timakonda mwachibadwa ndi amene amavomereza. Koma Petro akutiuza ife kukondana wina ndi mnzake “motambasuka.” Chitalongosoledwa pakati pa Akristu, chikondi cha a-ga’pe sichiri kokha luntha, chikondi cholingalirika, chonga ngati chimene tingakhale nacho kaamba ka adani athu. (Mateyu 5:44) Icho chiri chikondi chenicheni ndipo chimafunikira kuyesayesa. Icho chimaphatikizapo kutambasula mitima yathu, kuikulitsira iyo kunja kotero kuti ingakute anthu amene sitimakonda nthaŵi zonse.
10 Mu Linguistic Key to the Greek New Testament, Fritz Rienecker akuchitira ndemanga pa liwu lotembenuzidwa “kwenikweni,” kapena “motambasuka,” mu 1 Petro 1:22. Iye akulmeba kuti: “lingaliro lokulira liri lija la kufunitsitsa, changu (kuchita chinthu osati mopepuka . . . koma monga mmene zinaliri ndi kuvutikira) (Hort).” Kuvutikira kumatanthauza, pakati pa zinthu zina, “kutambasuka ku mlingo wokulira.” Chotero kukondana wina ndi mnzake kwenikweni kuchokera mu mtima kumatanthauza kudziikizako ife eni mokwanira m’kuyesayesa kwathu kwa kukhala ndi chiyanjo chaubale kaamba ka anzathu Achikirstu onse. Kodi ena a abale ndi alongo athu ali opsyinjika m’chiyanjo chathu chachikondi? Ngati ndi tero, tifunikira kukulitsa.
“Kulitsani”
11, 12. (a) Ndi uphungu wotani umene mtumwi Paulo anapereka kwa Akristu mu Korinto? (b) Ndimotani mmene Pualo anakhazikitsira chitsanzo chabwino m’mbaliyi?
11 Mtumwi Paulo mwachiwonekere anamva kufunika kaamba ka ichi mu mpingo wa ku Korinto. Iye analembera Akristu kumeneko kuti: “Mkamwa mwathu m’motseguka kwa inu, Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa. Simupsyinjika mwa ife, koma mupsyinjika mumtima mwanu. Ndipo kukhale chibwezero chomwechi—ndinena monga ndi ana anga—mukulitsidwe inunso.”—2 Akorinto 6:11-13.
12 Kodi ndimotani mmene tingakulitsire mitima yathu kuti tiphatikize abale ndi along athu onse? Paulo anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’mbaliyi. Iye m’chenicheni anafunafuna zabwino mwa abale ake, ndipo anawakumbukira iwo osati kaamba ka zolephera zawo koma kaamba ka mikhalidwe yawo yabwino. Mutu wotsirizira wa kalata yake kwa Akristu mu Roma umasonyeza chimenechi. Tiyeni tisanthule Aroma mutu 16 ndi kuwona mmene umwunikirira mkhalidwe weniweni wa Paulo kulinga kwa abale ndi alongo ake.
Kuyamikira Kotentha
13. Ndimotani mmene Paulo analongosolera chiyamikiro chake kaamba ka Febe, ndipo nchifukwa ninji?
13 Paulo analemba kalata yake kwa Aroma kuchokera ku Korinto chifupifupi chaka cha 56 C.E., mkati mwa ulendo wake wachitatu wa umishonale. Iye mwachiwonekere anaikiza zolembazo kwa mkazi Wachikristu wotchedwa Febe, chiwalo cha mpingo wapafupi wa Kenkreya, yemwe ankapita ku Roma. (Ŵerengani maversi 1, 2.) Dziŵani kutentha kumene iye akumuyamikirira mkaziyo kwa abale mu Roma. M’njira ina kapena inzake, iye anachirikiza Akristu ambiri, kuphatikizapo Paulo, mwinamwake mkati mwa kuyenda kwawo kodutsa doko la nyanja lotanganitsidwa la Kenkreya. Pokhala wochimwa wopanda ungwiro, mofanana ndi anthu ena onse, Febe mosakaikira anali ndi zofooka zake. Koma m’malo mochenjeza mpingo wa ku Roma molimbana ndi zophophonya za Febe, Paulo anawalangiza iwo “kumlandira iye mwa Ambuye popeza ali woyenera oyera.” Ndi mkhalidwe wabwino, weniweni chotani nanga!
14. Ndi zinthu zabwino zotani zimene Paulo ananena ponena za Priskila ndi Akula?
14 Kuchokera pa versi 3 mapaka versi 15, Paulo akutumiza moni kwa Akristu oposa 20 otchulidwa ndi maina ndi kwa ena ambiri otchulidwa mmodzi ndi mmodzi kapena monga gulu. (Ŵerengani maversi 3, 4.) Kodi mungakhoze kuzindikira chiyanjo chaubale chimene Paulo anadzimva kaamba ka Priska (kapena, Priskila; yerekezani ndi Machitidwe 18:2) ndi Akula? Aŵiriwa anadziwunikira iwo eni ku ngozi kaamba ka Paulo. Tsopano iye akupatsa moni antchito anzakewa ndi chiyamikiro ndipo anawatumizira iwo chisonyezero cha chiyamikiro m’malo mwa mipingo ya Akunja. Ndimotani nanga mmene Akula ndi Priskila angakhale analimbikitsidwira ndi moni wochokera mu mtima ameneyu!
15. Ndimotani mmene Paulo anasonyezera kuolowa manja kwake ndi kuzichepetsa pamene anapatsa moni Androniko ndi Yuniya?
15 Paulo anakhala Mkristu wodzipereka mwachiwonekere mkati mwa chaka chimodzi kapena ziŵiri za imfa ya Kristu. Panthaŵi imene iye analemba kalata yake kwa Aroma, iye anali atagwiritsiridwa ntchito ndi Kristu monga mtumwi wotchuka kwa amitundu kwa zaka zambiri. (Machitidwe 9:15; Aroma 1:1; 11:13) Komabe, onani kuolowa manja kwake ndi kudzichepetsa. (Ŵerengani versi 7.) Iye anapatsa moni Androniko ndi Yuniya monga “omveka mwa atumwi [otumizidwa]” ndipo anavomereza kuti iwo anali atatumikira Kristu kwa nthaŵi yaitali kuposa mmene iye anachitira. Palibe kuthekera kulikonse kwa nsanje yochepera pamenepo!
16. (a) Ndi m’kalongosoledwe kachikondi kotani kamene Paulo analankhulira za Akristu ena okhala mu Roma? (b) Nchifukwa ninji tingatsimikizire kuti moni ameneyu anali zitsanzo za “chiyanjo chaubale chosanyenga”?
16 Timadziŵa zochepera kapena osati chirichonse za Akristu oyambirira oterowo onga ngati Epeneto, Ampliato, ndi Staku. (Ŵerengani maversi 5, 8, 9.) Koma kokha mwanjira imene Paulo anawapatsira moni atatu onsewo, tingakhale otsimikiza kuti anali amuna okhulupirika. Anadzikondetsa iwo eni kwa Paulo kotero kuti iye anatcha aliyense wa iwo “wokondedwa wanga.” Paulo analinso ndi mawu achikondi kaamba ka Apele ndi Rufo, akumalozera kwa iwo aliyense payekha monga “wovomerezedwayo mwa Kristu,” ndi “wosankhidwayo mwa Ambuye.” (Ŵerengani maversi 10, 13.) Ndi zowonjezera zabwino chotani nanga zomwe tifunikira kupereka kwa Akristu aŵiri amenewa! Ndipo kudziŵa kulunjika kwa Paulo, tinagakhale otsimikizira kuti iko sikunali chizolowezi wamba. (Yerekezani ndi 2 Akorinto 10:18.) Mwangozi, Paulo sanaiwale kupereka moni kwa amayi a Rufo.
17. Ndimotani mmene Paulo analongosolera chiyamikiro chozama kaamba ka alongo ake?
17 Chimenecho chimatibweretsa ife ku kuyamikira kwa Paulo kaamba ka alongo ake. M’kuwonjezera ku amayi a Rufo, Paulo anatchula akazi ena Achikirstu osachepera pa asanu ndi mmodzi. Tawona kale mmene analankhulira mwachikondi za Febe ndi Priskila. Koma dziŵani chiyanjo chaubale chotentha chimene iye anayanja nacho Mariya, Trufena, Trufosa, ndi Persida. (Ŵerengani maversi 6,12.) Wina angadzimve kuti mtima wake unapita kwa alongo ogwira ntchito mwamphamvuwa omwe “anachita ntchito zambiri” kaamba ka abale awo. Ndi chomangirira chotani nanga mmene ichi chiriri kuwona kuyamikira kochokera mu mtima kwa Paulo kaamba ka abale ndi alongo ake, mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwawo!
Osakaikira Zolinga za Abale Athu
18. Ndimotani mmene tingayesere kutsatira Paulo, koma nchiyani chimene chingakhale choyenerera?
18 Bwanji osatsatira Paulo ndi kuyesera kupeza chinachake chabwino chonena ponena za mbale ndi mlongo aliyense mu mpingo? Kwa ena, simudzakhala ndi vuto mpang’ono pomwe. Kwa ena, chingatenge kufufuza kochepera. Bwanji osayesera kuthera nthaŵi ina ndi iwo ndi cholinga chofuna kuwadziŵa iwo bwino lomwe? Inu motsimikizirika mudzapeza mikhalidwe yokondeka mwa iwo, ndipo, ndani yemwe adziŵa, iwo angayambe kukuyamikirani inu mowonjezereka kuposa kale.
19. Nchifukwa ninji sitifunikira kukaikira zolinga za abale athu, ndipo ndimotani mmene Yehova amatikhazikitsira chitsanzo chabwino chachikondi?
19 Sitifunikira kukaikira zolinga za abale athu. Onse a iwo amakonda Yehova; kupanda apo sakanapereka miyoyo yawo kwa iye. Ndipo nchiyani chomwe chimawaletsa iwo kubwerera ku dziko, kutsatira njira zake zopita mopepuka? Chiri chikondi chawo kaamba ka Yehova, chilungamo chake, ndi Ufumu wake pansi pa Kristu. (Mateyu 6:33) Koma onsewo, m’njira zosiyanasiyana, afunikira kumenyera zolimba kuti akhale okhulupirika. Yehova amawakonda iwo kaambaka chimenechi. (Miyambo 27:11) Iye amawalandira iwo monga atumiki ake mosasamala kanthu za zolakwa zawo ndi zolephera. Ichi pokhala tero, kodi ife ndani kuti tilephere kuwaika iwo m’chiyanjo chathu chachikondi? ?—Aroma 12:9, 10; 14:4.
20. (a) Mogwirizana ndi kalata ya Paulo kwa Aroma, ndi ati okha omwe tifunikira kukhala okaikira, ndipo ndi chitsogozo cha yani chomwe tingatsatire mopepuka m’chigwirizano ndi ichi? (b) Kupanda apo, ndimotani mmene tiyenera kulingalira abale athu onse?
20 Okha amene Paulo anatichenjeza ife kukhala okaikira ali “iwo akuchita zopatutsana ndi zopunthwitsa,” ndi awo omwe amachita “motsutsana ndi chiphunzitso munachiphunzira.” Paulo akutiuza ife kuyang’anira oterewa ndi kuwapewa. (Aroma 16:17) Akulu a mu mpingo adzakhala atayesera kuwathandiza amenewa. (Yuda 22, 23) Chotero tingadalire pa akulu kutidziŵitsa ife ngati ena ake afunikira kupewedwa. Kupanda apo, tiyenera kulingalira abale athu onse monga ofunikira chiyanjo chathu chaubale chosanyenga, ndipo tiyenera kuphunzira kuwakonda iwo kwenikweni kuchokera mu mtima.
21, 22. (a) Nchiyani chmene chiri kutsogolo kwathu? (b) Ndi mikhalidwe yotani yomwe ingabuke, chotero nchiyani chomwe chiri chofulumira kuchita? (c) Nchiyani chomwe chidzalingaliridwa m’nkhani yotsatira?
21 Satana, ziwanda zake, ndi dongosolo lake lonse la kudziko la zinthu ali otsutsana nafe. Har–Magedo iri kutsogolo kwathu. Iyo idzayambitsidwa ndi kuwukira kwa Gogi wa Magogi. (Ezekieli, mitu 38, 39) Panthaŵi imeneyo, tidzafunikira abale athu kuposa ndi kalelonse. Tingadzadzipeze ife eni tikufunika thandizo la aja enieniwo amene sitimawayamikira mwachindunji. Kapena amenewa angakhale m’kusowa kwenikweni kwa chithandizo chathu. Tsopano iri nthaŵi ya kukulitsa ndi kuwonjezera chiyamikiro chathu kaamba ka abale athu onse.
22 Kuyamikira kaamba ka abale athu kumaphatikizapo, ndithudi, ulemu woyenera kaamba ka akulu a mu mpingo. M’mbaliyi, akulu iwo eniwo ayenera kukhala chitsanzo chabwino mwakusonyeza chiyamikiro choyenera osati kokha kaamba ka abale onse komanso kaamba ka akulu anzawo. Mbali imeneyi ya nkhaniyi idzalingaliridwa m’nkhani yotsatira.
Nsonga kaamba ka Kubwereramo
□ Nchiyani chomwe chiri chizindikiro chapadera cha Chikristu chowona?
□ Nchifukwa ninji ponse paŵiri chikondi ndi chiyanjo chaubale ziri zoyenera?
□ Ndimotani mmene tingakondanirane wina ndi mnzake “kwenikweni,” kapena “motambasuka”?
□ Mu Aroma mutu 16, ndimotani mmene Paulo anasonyezera chiyamikiro kaamba ka abale ndi alonga ake?
□ Nchifukwa ninji sitifunikira kukhala okaikira zolinga za abale athu?
[Chithunzi patsamba 12]
Yeserani kupeza mikhalidwe yokondeka mwa awo omwe simuwakonda mwachibadwa