Kodi Tiyenera Kuchitanji Kuti Tipulumutsidwe?
TSIKU lina munthu wina anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo oŵerengeka kodi?” Kodi Yesu anayankha motani? Kodi iye anati: ‘Tangondivomereza ine monga Ambuye ndi Mpulumutsi wako, ndipo udzapulumutsidwa’? Ayi! Yesu anati: “Yesetsani kuloŵa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kuloŵamo, koma sadzakhoza.”—Luka 13:23, 24.
Kodi Yesu analephera kuyankha funso la munthuyo? Ayi, munthuyo sanafunse kuti kudzakhala kovuta motani kupulumutsidwa; anafunsa ngati anthu adzakhala oŵerengeka. Chotero Yesu anangosonyeza kuti anthu oŵerengeka kwambiri kusiyana ndi amene munthu angaganize ndiwo adzayesetsa kuti alandire dalitso labwino kwambiri limeneli.
‘Koma si zimene ndinauzidwa,’ oŵerenga ena angatsutse. Iwo angagwire mawu Yohane 3:16 yemwe amati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike koma akhale nawo moyo wosatha.” Komabe, tikuyankha kuti: ‘Nanga, kodi nchiyani chimene tiyenera kukhulupirira? Kuti Yesu analikodi? Inde. Kuti ndiye Mwana wa Mulungu? Eetu! Ndipo popeza Baibulo limatcha Yesu “Mphunzitsi” ndi “Ambuye,” kodi sitiyeneranso kukhulupirira zimene anaphunzitsa, kumumvera, ndi kumtsatira?’—Yohane 13:13; Mateyu 16:16.
Kutsatira Yesu
Ehe, apa ndipo pali vuto! Anthu ambiri amene anauzidwa kuti “anapulumutsidwa” samafuna kumtsatira Yesu kapena kumumvera. Kwenikweni, mtsogoleri wina wachipembedzo wachiprotesitanti analemba kuti: “Ndithudi, chikhulupiriro chathu mwa Kristu chiyenera kupitiriza. Koma lingaliro lakuti nchofunika koposa, kapena kuti chiyenera kutero zivute zitani, silimachirikizidwa konse m’Baibulo.”
Zosiyana ndi zimenezo, Baibulo limatchula machitachita oipa ofala pakati pa anthu ena amene amaganiza kuti “anapulumutsidwa.” Ponena za wina amene apitiriza ndi njira zotero, linalangiza Akristu kuti: “Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” Inde Mulungu safuna anthu oipa kuipitsa mpingo wake wachikristu!—1 Akorinto 5:11-13.
Choncho, kodi kutsatira Yesu kumatanthauzanji, ndipo tingakuchite motani? Eya, kodi Yesu anachitanji? Kodi anali ndi makhalidwe oipa? wadama? chidakwa? wabodza? Kodi anali wosaona mtima pamalonda? Ayi! ‘Koma,’ mungafunse, ‘kodi ndiyenera kuchotsa zinthu zonsezo m’moyo wanga?’ Kuti mupeze yankho, onani Aefeso 4:17 mpaka 5:5. Samanena kuti Mulungu adzatilandira ife ngakhale titachita zinthu zotani. M’malo mwake, amatiuza kukhala osiyana ndi amitundu amene “sazindikiranso kanthu konse, . . . koma simunaphunzira Kristu chotero . . . Muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale . . . Wakubayo asabenso . . . Dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima . . . Pakuti ichi muchidziŵe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe choloŵa mu ufumu wa Kristu ndi Mulungu.”
Kodi tikutsatira Yesu ngati sitiyesa mpang’ono pomwe kutsanzira chitsanzo chake? Kodi sitifunikira kulimbikira kuchititsa moyo wathu kukhala wofanana kwambiri ndi wa Kristu? Anthu amene amanena monga trakiti lina lachipembedzo kuti: “Idzani kwa Kristu tsopano—monga momwe mulili” samaganiza za funso limenelo nthaŵi zambiri, ngati amatero nkomwe.
Mmodzi wa ophunzira a Yesu anachenjeza kuti anthu osapembedza anali “kusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu Yesu Kristu.” (Yuda 4) Kwenikweni, kodi ndi motani mmene ife tingasandutsire chifundo cha Mulungu “chikhale chilakolako chonyansa”? Tingachite zimenezo mwa kuganiza kuti nsembe ya Kristu imakwirira machimo adala amene timafuna kupitiriza kuchita m’malo mwa machimo akupanda ungwiro kwaumunthu amene tikuyesetsa kuwasiya. Kunena zoona sitingafune kuvomereza zimene ananena mmodzi wa alaliki otchuka kwambiri a ku America kuti munthu safunikira “kusintha, kuleka zoipa, kapena kulapa.”—Siyanitsani ndi Machitidwe 17:30; Aroma 3:25; Yakobo 5:19, 20.
Chikhulupiriro Chimasonkhezera Ntchito
Anthu ambiri auzidwa kuti “kukhulupirira Yesu” kumachitika kamodzi kwatha ndi kuti chikhulupiriro chathu sichiyenera kukhala cholimba kwambiri kuti chitisonkhezere kumvera. Koma Baibulo limatsutsa zimenezo. Yesu sananene kuti anthu amene amayamba kuyenda panjira yachikristu amapulumutsidwa. M’malo mwake, anati: “Iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.” (Mateyu 10:22) Baibulo limafanizira njira yathu yachikristu ndi liŵiro, chipulumutso monga mphotho yake. Ndipo limatiuza kuti: “Thamangani, kuti mukalandire.”—1 Akorinto 9:24.
Chotero, “kuvomereza Kristu” kumafuna zambiri kuposa kungovomereza madalitso amene nsembe yopambana ya Yesu imapereka. Pamafunika kumvera. Mtumwi Petro akunena kuti chiweruzo chiyambira “panyumba ya Mulungu,” nawonjezera: ‘Koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera uthenga wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?’ (1 Petro 4:17) Choncho tiyenera kuchita zambiri kuposa kungomva ndi kukhulupirira. Baibulo limati tiyenera ‘kukhala akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga [tokha].’—Yakobo 1:22.
Mauthenga Ake a Yesu
Buku la Baibulo la Chivumbulutso lili ndi mauthenga ochokera kwa Yesu, otumizidwa kumipingo yachikristu yoyambirira isanu ndi iŵiri kupyolera mwa Yohane. (Chivumbulutso 1:1, 4) Kodi Yesu ananena kuti popeza anthu a mipingo imeneyi anali ‘atamvomereza’ kale, basi zimenezo zinali zokwanira? Ayi. Anayamikira ntchito zawo ndi chipiriro ndipo analankhula za chikondi chawo, chikhulupiriro, ndi utumiki wawo. Koma anati Mdyerekezi adzawayesa ndi kuti adzafupidwa “yense wa [iwo] monga mwa ntchito [zawo].”—Chivumbulutso 2:2, 10, 19, 23.
Chotero Yesu anafotokoza kudzipereka koposeratu kuja kumene anthu anadziŵa pamene anauzidwa kuti chipulumutso chawo “chinachitika kale” pamene ‘anangomvomereza’ iye pamsonkhano wachipembedzo. Yesu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha ine, adzaupeza.”—Mateyu 16:24, 25.
Kudzikana ife tokha? Kutsata Yesu kosaleka? Zimenezo zingafune khama. Zingasinthe moyo wathu. Koma, kodi Yesu ananenetsadi kuti ena a ife ‘tidzataya ndi moyo wathu’ womwe—kufa chifukwa cha iye? Inde, chikhulupiriro chotero chimadza kokha ndi chidziŵitso cha zinthu zazikulu zimene munthu angadziŵe mwa kuphunzira Mawu a Mulungu. Chinasonyezedwa patsiku limene Stefano anaponyedwa miyala ndi anthu oyaluka maganizo ndi chipembedzo amene ‘sanathe kuilaka nzeru ndi mzimu umene analankhula nawo.’ (Machitidwe 6:8-12; 7:57-60) Ndipo chikhulupiriro chotero chinasonyezedwa m’nthaŵi yathu ndi Mboni za Yehova mazana ambiri zimene zinafa m’misasa yachibalo ya Nazi m’malo mwa kuswa chikumbumtima chawo chophunzitsidwa Baibulo.a
Kukangalika kwa Akristu
Tiyenera kugwiritsa chikhulupiriro chathu chachikristu chifukwa, mosiyana ndi zimene mungamve kumatchalitchi ena kapena pamaprogramu achipembedzo apawailesi yakanema, Baibulo limati tikhoza kugwa. Limasimba za Akristu amene anasiya “njira yolunjika.” (2 Petro 2:1, 15) Chotero tifunikira ‘kugwira ntchito yake ya chipulumutso chathu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’—Afilipi 2:12; 2 Petro 2:20.
Kodi umu ndi mmene Akristu a m’zaka za zana loyamba, anthu amene anamvadi Yesu ndi atumwi ake akuphunzitsa, anamvera nkhaniyi? Inde. Anadziŵa kuti anafunikira kuchita kanthu kena. Yesu anati: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyu 28:19, 20.
Patapita milungu ingapo kuchokera pamene Yesu ananena zimenezo, anthu 3,000 anabatizidwa tsiku limodzi lokha. Chiŵerengero cha okhulupirira chinawonjezeka msanga kufika 5,000. Amene anakhulupirira anaphunzitsanso ena. Pamene anabalalika chifukwa cha chizunzo, zinangowathandiza kufalitsa uthenga wawo. Baibulo limati “iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mawuwo” osati atsogoleri angapo okha. Chotero, patapita zaka 30, mtumwi Paulo anakhoza kulemba kuti uthenga wabwino unali ‘utalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’—Machitidwe 2:41; 4:4; 8:4; Akolose 1:23.
Paulo sanatembenuze anthu, monga amachita alaliki ena a pa TV, mwa kunena kuti: ‘Vomereza Yesu tsopano lino, ndipo udzakhala wopulumutsidwa kosatha.’ Ndipo sanadzidalire monga mtsogoleri wina wachipembedzo wachimereka amene analemba kuti: “Pamene ndinali mnyamata, . . . ndinali kale wopulumutsidwa.” Patapita zaka 20 kuchokera pamene Yesu mwiniyo anasankha Paulo kupereka uthenga wachikristu kwa amitundu, mtumwi ameneyu wakhama pantchito analemba kuti: “Ndipump[h]untha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:27; Machitidwe 9:5, 6, 15.
Chipulumutso chili mphatso yaulere yochokera kwa Mulungu. Si chinthu chimene tingapeze chifukwa cha zochita zathu. Komabe chimafuna kuti ife tiyesetse. Ngati wina wakupatsani mphatso yamtengo wapatali ndipo simunasonyeze chiyamikiro chachikulu mwa kuinyamula ndi kupita nayo, kusoŵa kwanu chiyamikiro mwina kungasonkhezere wokupatsaniyo kuipereka kwa wina. Chabwino, kodi mwazi wamoyo wa Yesu Kristu uli ndi mtengo wotani? Ndiwo mphatso yaulere, koma tiyenera kuiyamikira kwambiri.
Akristu oona ali mumkhalidwe wopulumuka mwanjira yakuti ali ndi chiyanjo cha Mulungu. Monga gulu, chipulumutso chawo nchotsimikizirika. Aliyense payekha, ayenera kukwaniritsa zofunika za Mulungu. Komabe, tingalephere, pakuti Yesu anati: “Ngati wina sakhala mwa ine, watayika kunja monga nthambi, nafota.”—Yohane 15:6.
“Mawu a Mulungu Ali Amoyo”
Kukambitsirana kotchulidwa poyamba m’nkhani yoyambirira kunachitika pafupifupi zaka 60 zapitazo. Johnny amakhulupirirabe kuti chipulumutso chimadza kokha mwa Yesu Kristu, koma amazindikira kuti tiyenera kuchikalimira. Iye ali wotsimikiza kuti Baibulo limasonyeza kwenikweni kumene chiyembekezo cha munthu chingapezeke ndi kuti tiyenera kuphunzira buku labwinolo, kukhudzidwa mtima nalo, ndi kulilola kutisonkhezera kuchita ntchito zachikondi, chikhulupiriro, kukoma mtima, kumvera, ndi kupirira. Ana ake wawalera kufikira pa kukhulupirira zinthu zimodzimodzi, ndipo tsopano akukondwa kuwaona iwo akuleranso ana awo mwanjira imodzimodziyo. Amati bwenzi aliyense anali ndi chikhulupiriro chotero, ndipo amachita zonse zotheka kuchikhomereza m’mitima ndi m’maganizo a ena.
Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Akhoza kusintha moyo wanu. Akhoza kukusonkhezerani kuchita ndi mtima wonse ntchito za chikondi, chikhulupiriro, ndi kumvera. Koma muyenera kuchita zambiri kuposa ‘kungovomereza’ m’maganizo zimene Baibulo limanena. Liphunzireni ndipo lolani mtima wanu kusonkhezeredwa nalo. Iloleni nzeru yake kukutsogolerani. Mboni za Yehova zodzipereka pafupifupi 5,000,000 m’maiko oposa 230 zimapereka maphunziro a Baibulo apanyumba aulere. Kuti mudziŵe zimene mungaphunzire paphunziro lotero, lemberani ofalitsa magazini ano. Chikhulupiriro ndi nyonga yauzimu zimene mudzapeza mudzakondwera nazo!
[Mawu a M’munsi]
a M’buku lake lakuti The Nazi State and the New Religions: Five Case Studies in Non-Conformity, Dr. Christine E. King anasimba kuti: “Mboni [ya Yehova] yachijeremani imodzi mwa ziŵiri zilizonse inaponyedwa m’ndende, imodzi mwa zinayi inataya moyo wake.”
[Bokosi patsamba 7]
Chifukwa Ninji Tiyenera ‘Kulimbanatu Chifukwa cha Chikhulupiriro’?
Buku la Baibulo la Yuda linalembedwa kwa “oitanidwa, . . . osungidwa ndi [“kaamba ka,” NW] Yesu Kristu.” Kodi limanena kuti popeza iwo ‘anavomereza Yesu,’ chipulumutso chawo chinali chotsimikizirika? Ayi, Yuda anauza Akristu amenewo ‘kulimbanatu chifukwa cha chikhulupiriro.’ Anawauza zifukwa zitatu zochitira zimenezo. Choyamba, Mulungu ‘anapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m’dziko la Aigupto,’ koma ambiri a iwo anagwa pambuyo pake. Chachiŵiri, ngakhale angelo anapanduka nakhala ziŵanda. Chachitatu, Mulungu anawononga Sodomu ndi Gomora chifukwa cha chisembwere chonyansa chimene chinachitika m’midzi imeneyo. Yuda akutchula nkhani za m’Baibulo zimenezi monga “chitsanzo.” Inde, ngakhale okhulupirira “osungidwa kaamba ka Yesu Kristu” ayenera kusamala kuti asagwe pachikhulupiriro choona.—Yuda 1-7.
[Bokosi patsamba 8]
Kodi Zolondola Nziti?
Baibulo limati: “Timuyesa munthu wolungama chifukwa cha chikhulupiriro, wopanda ntchito za lamulo.” Limanenanso kuti: “Munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.” Kodi zolondola nziti? Kodi timayesedwa olungama chifukwa cha chikhulupiriro kapena ntchito?—Aroma 3:28; Yakobo 2:24.
Yankho lolondola la m’Baibulo nlakuti zonse ziŵiri nzolondola.
Kwa zaka mazana ambiri Chilamulo chimene Mulungu anapereka kupyolera mwa Mose chinafuna kuti olambira achiyuda apereke nsembe zakutizakuti, kusunga masiku amadyerero, ndi kutsatira zofunika ponena za zakudya ndi zinthu zina. “Ntchito za lamulo” zotero, kapena kungoti “ntchito,” sizinali zofunikanso Yesu atapereka nsembe yangwiro.—Aroma 10:4.
Koma choonadi chakuti ntchito zimenezi zochitidwa pansi pa Chilamulo cha Mose zinaloŵedwa m’malo ndi nsembe yopambana ya Yesu sichinatanthauze kuti tiyenera kunyalanyaza malangizo a Baibulo. Ilo limati: “Koposa kotani nanga mwazi wa Kristu . . . udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa [zakale], kukatumikira Mulungu wamoyo?”—Ahebri 9:14.
Kodi ndi motani mmene ‘timatumikirira Mulungu wamoyo’? Pakati pa zinthu zina, Baibulo limatiuza kulimbana ndi ntchito za thupi, kukaniza makhalidwe oipa a dziko, ndi kupeŵa misampha yake. Limati: “Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro,” tayani “tchimoli limangotizinga,” ndipo ‘thamangani mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera Woyambira ndi Womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu.’ Ndipo Baibulo limatilangiza ‘kusalema ndi kukomoka m’moyo wathu.’—1 Timoteo 6:12; Ahebri 12:1-3; Agalatiya 5:19-21.
Sitimapeza chipulumutso mwa kuchita zinthu zimenezi, pakuti palibe munthu amene akhoza kuchita zonse zofunika kuti ayenerere dalitso lalikulu limenelo. Komabe, sitimayenerera mphatso yaikulu imeneyi ngati tilephera kusonyeza chikondi chathu ndi kumvera mwa kuchita zinthu zimene Baibulo limati Mulungu ndi Kristu amafuna ife kuchita. Popanda ntchito zosonyeza chikhulupiriro chathu, kunena kwathu kuti tikutsatira Yesu kudzakhala kopereŵera kwambiri, pakuti Baibulo limanena zomveka kuti: “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.”—Yakobo 2:17.
[Chithunzi patsamba 7]
Phunzirani Baibulo ndi kusonkhezeredwa nalo