Ndinu Mtumiki Wokhulupirika
“Mwiniwake wa inuyo si inu.”—1 AKOR. 6:19.
1. Kodi anthu ambiri amaona bwanji ukapolo?
PAFUPIFUPI zaka 2,500 zapitazo, wolemba masewero wina wa ku Greece analemba kuti: “Palibe munthu amene amafuna kukhala kapolo.” Ngakhalenso masiku ano, anthu ambiri akhoza kugwirizana ndi mawu amenewa. Tikutero chifukwa akapolo ambiri amaponderezedwa ndipo ali mu ukaidi. Iwo amagwira ntchito ndiponso kudzipereka kuti ambuye awo, omwe akuwapondereza, azipeza phindu osati iwowo.
2, 3. (a) Kodi Khristu amaona bwanji akapolo ake okhulupirika, kapena kuti atumiki ake? (b) Kodi tikambirana mafunso ati onena za atumiki oyang’anira nyumba?
2 Ngakhale zili choncho, Yesu ananena kuti ophunzira ake adzakhala atumiki odzichepetsa, kapena kuti akapolo. Koma ukapolo wa Akhristu oona si wonyozeka kapena wopondereza. Tikutero chifukwa Yesu amawadalira komanso kuwalemekeza. Pa nkhaniyi, tiyeni tione zimene Yesu ananena za “kapolo” wina. Khristu atatsala pang’ono kufa, analosera kuti adzapereka ntchito kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mat. 24:45-47.
3 N’zochititsa chidwi kuti nayenso Luka analemba za kapoloyu koma anagwiritsa ntchito mawu oti “mtumiki woyang’anira nyumba.” (Werengani Luka 12:42-44.) Masiku ano, Akhristu okhulupirika ambiri sali m’gulu la mtumiki wokhulupirika limeneli. Koma Malemba amasonyeza kuti anthu onse amene amatumikira Mulungu ali ngati atumiki oyang’anira nyumba. Kodi maudindo awo ndi otani? Nanga ayenera kuwaona bwanji maudindowo? Kuti tiyankhe mafunsowa, tiyeni tikambirane maudindo amene atumiki akale anali nawo.
MAUDINDO A ATUMIKI AKALE
4, 5. Kodi atumiki akale ankapatsidwa maudindo otani? Perekani zitsanzo.
4 Kalekale anthu ankakonda kusankha kapolo amene ndi wokhulupirika kuti akhale mtumiki woyang’anira nyumba ndiponso ntchito za mbuye wake. Mtumikiyu ankakhala ndi mphamvu zoyang’anira zinthu za m’nyumba, ndalama ndiponso atumiki anzake. Mwachitsanzo, Eliezere anali mtumiki yemwe Abulahamu anamupatsa udindo woyang’anira zinthu zake zonse. N’kuthekanso kuti Abulahamu anatumiza iyeyo ku Mesopotamiya kuti akasankhire mwana wake Isaki mkazi. Umenewutu unali udindo waukulu kwambiri.—Gen. 13:2; 15:2; 24:2-4.
5 Yosefe, yemwe anali mdzukulu wa Abulahamu, ankayang’anira nyumba ya Potifara. (Gen. 39:1, 2) Patapita nthawi, nayenso Yosefe anakhala ndi mtumiki wake yemwe anamupatsa udindo ‘woyang’anira nyumba yake.’ Mtumikiyu ndi amene anakonza zochereza abale 10 a Yosefe. Komanso ndi mtumiki ameneyu yemwe Yosefe anamuuza kuti akonze zoti abale akewo aoneke ngati anaba kapu yasiliva. Choncho tikhoza kuona kuti atumiki akalewo ankapatsidwa udindo waukulu.—Gen. 43:19-25; 44:1-12.
6. Kodi akulu achikhristu ali ndi maudindo osiyanasiyana otani?
6 Patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo analemba kuti oyang’anira achikhristu ndi ‘atumiki a Mulungu.’ (Tito 1:7) Oyang’anira ali ndi udindo woweta “gulu la nkhosa za Mulungu” choncho amapereka malangizo ndiponso kutsogolera m’mipingo. (1 Pet. 5:1, 2) Koma sikuti oyang’anira onse amakhala ndi udindo wofanana. Mwachitsanzo, masiku ano oyang’anira achikhristu ambiri amatumikira mu mpingo umodzi. Koma oyang’anira oyendayenda amatumikira mipingo yambiri. Ndipo abale amene ali m’Komiti ya Nthambi amayang’anira mipingo yonse ya m’gawo la nthambi yawo. Komabe oyang’anira onsewa ayenera kusamalira udindo wawo mokhulupirika ndipo onse ‘adzayankha mlandu’ kwa Mulungu.—Aheb. 13:17.
7. Kodi tikudziwa bwanji kuti kwenikweni Akhristu onse ali ngati atumiki oyang’anira nyumba?
7 Koma nanga bwanji za Akhristu okhulupirika ambiri amene si oyang’anira? Polembera kalata Akhristu onse m’madera osiyanasiyana, mtumwi Petulo anati: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana monga oyang’anira [kapena kuti atumiki oyang’anira nyumba] abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene wakusonyeza m’njira zosiyanasiyana.” (1 Pet. 1:1; 4:10) Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu, Mulungu wapatsa tonsefe maluso kapena mphatso zimene tingagwiritse ntchito pothandiza Akhristu anzathu. Choncho onse amene amatumikira Mulungu ndi atumiki ndipo ali ndi udindo wolemekezeka ndiponso wofunika.
NDIFE A MULUNGU
8. Kodi ndi mfundo yofunika iti imene tiyenera kukumbukira?
8 Tsopano tiyeni tione mfundo zitatu zimene ife, monga atumiki oyang’anira nyumba, tiyenera kukambirana. Mfundo yoyamba ndi yakuti: Tonse ndife a Mulungu ndipo tidzayankha mlandu kwa iye. Pajatu Paulo analemba kuti: “Mwiniwake wa inuyo si inu, pakuti munagulidwa pa mtengo wokwera,” womwe ndi nsembe ya magazi a Khristu. (1 Akor. 6:19, 20) Popeza kuti ndife a Yehova, tiyenera kumvera malamulo ake, omwe si olemetsa. (Aroma 14:8; 1 Yoh. 5:3) Komanso ndife akapolo a Khristu. Mofanana ndi atumiki akale, timakhala ndi ufulu wambiri koma ufulu wake uli ndi malire. Tiyenera kutsatira malangizo amene timapatsidwa posamalira maudindo athu. Kaya tili ndi udindo wotani, tiyenera kukumbukira kuti ndife atumiki a Mulungu ndiponso a Khristu.
9. Kodi Yesu anapereka fanizo liti losonyeza mmene zinthu zimakhalira pakati pa mbuye ndi kapolo wake?
9 Yesu anatithandiza kumvetsa mmene zinthu zimakhalira pakati pa mbuye ndi kapolo wake. Pa nthawi ina, iye analankhula ndi ophunzira ake za kapolo amene anabwera kunyumba atagwira ntchito tsiku lonse. Yesu anafunsa ophunzira akewo ngati pali mbuye amene anganene kwa kapolo wakeyo kuti: “Fika kutebulo kuno msanga udzadye.” Yesu anasonyeza kuti sangatero ayi. Koma mbuyeyo amanena kuti: “Ndikonzere chakudya chamadzulo, uvale epuloni ndi kunditumikira kufikira nditamaliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso udye ndi kumwa.” Kodi Yesu anafotokoza bwanji mfundo ya fanizoli? Iye anati: “Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”—Luka 17:7-10.
10. N’chiyani chimasonyeza kuti Yehova amayamikira zimene timachita pomutumikira?
10 N’zoona kuti Yehova amayamikira zimene timachita pomutumikira. Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Yehova satipempha kuchita zinthu zimene sitingakwanitse. Zonse zimene amatipempha kuchita zimatithandiza komanso sizikhala zolemetsa kwenikweni. Koma malinga ndi fanizo la Yesu lija, kapolo sachita zinthu zodzikondweretsa kapena kuika zofuna zake patsogolo. Choncho mfundo ndi yakuti, pamene tinadzipereka kwa Mulungu, tinasankha kuika zofuna zake patsogolo nthawi zonse. Kodi zimenezi si zoona?
ZIMENE YEHOVA AMAFUNA KUTI TONSE TIZICHITA
11, 12. Monga atumiki, kodi tiyenera kuchita chiyani, nanga tiyenera kupewa chiyani?
11 Mfundo yachiwiri imene tiyenera kukumbukira ndi yakuti: Monga atumiki, tonse timayendera mfundo zofanana. Ndi zoona kuti mu mpingo wachikhristu pali maudindo ena amene amaperekedwa kwa anthu ochepa. Koma pali maudindo ambiri amene tonsefe tili nawo. Mwachitsanzo, tonse monga ophunzira a Khristu ndiponso Mboni za Yehova, tiyenera kukondana. Yesu ananena kuti anthu adzadziwa Akhristu oona chifukwa chakuti amakondana. (Yoh. 13:35) Koma tiyenera kukondanso anthu amene si Akhristu anzathu. Tonsefe tiyenera kuyesetsa kuchita zimenezi.
12 Tiyeneranso kukhala ndi khalidwe labwino. Tifunika kupewa makhalidwe amene Mawu a Mulungu amaletsa. Paulo analemba kuti: “Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akor. 6:9, 10) Komabe timadziwa kuti kutsatira mfundo zolungama za Mulungu kumafuna kuti tichite khama. Tikamatero, timapindula m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, zimatithandiza kukhala ndi thanzi labwino, kugwirizana ndi ena ndiponso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Werengani Yesaya 48:17, 18.
13, 14. Kodi Akhristu onse ali ndi udindo wotani? Nanga tiyenera kuuona bwanji?
13 Tiyeneranso kukumbukira kuti atumiki akale ankagwira ntchito. Ifenso tili ndi ntchito yofunika kugwira. Tapatsidwa mphatso ya mtengo wapatali ya kudziwa choonadi. Mulungu amafuna kuti choonadi chimenechi tiziuza anthu ena. (Mat. 28:19, 20) Paulo analemba kuti: “Chotero anthu azitha kuona kuti ndife atumiki a Khristu ndi oyang’anira zinsinsi zopatulika za Mulungu.” (1 Akor. 4:1) Paulo anazindikira kuti monga mtumiki, anafunika kuyang’anira mosamala “zinsinsi zopatulika.” Anafunikanso kuuza anthu ena za zinsinsi zimenezi mokhulupirika, monga analamulira Ambuye Yesu Khristu.—1 Akor. 9:16.
14 Tikamauza anthu ena choonadi, timasonyeza kuti timawakonda. Komabe zinthu zimasiyanasiyana pa moyo wa Akhristu. Sikuti onse angachite zofanana mu utumiki. Yehova amadziwa zimenezi. Koma chofunika n’chakuti tonse tizichita zonse zimene tingathe pomutumikira. Tikamachita zimenezi modzipereka, timasonyeza kuti timakonda Mulungu ndiponso anthu ena.
KUKHALA OKHULUPIRIKA N’KOFUNIKA KWAMBIRI
15-17. (a) N’chifukwa chiyani mtumiki ayenera kukhala wokhulupirika? (b) Kodi Yesu anapereka fanizo liti losonyeza zimene zimachitikira munthu wosakhulupirika?
15 Mfundo yachitatu ndi yogwirizana kwambiri ndi mfundo ziwiri zimene takambiranazi. Mfundo yake ndi yakuti: Tiyenera kukhala okhulupirika ndiponso odalirika. Mtumiki akhoza kukhala ndi makhalidwe ena abwino kapena maluso ambiri koma ngati si wokhulupirika ndiponso wodalirika kwa mbuye wake ndiye kuti ndi wopanda pake. Kuti munthu akhale mtumiki wabwino ndiponso wothandiza, ayenera kukhala wokhulupirika. Musaiwale kuti Paulo analemba kuti: “Chofunika kwa woyang’anira [kapena kuti mtumiki woyang’anira nyumba] ndicho kukhala wokhulupirika.”—1 Akor. 4:2.
16 Timadziwa kuti tikakhala okhulupirika, tidzadalitsidwa. Koma ngati tikhala osakhulupirika, sitidzalandira madalitso. Tikhoza kuona zimenezi m’fanizo la Yesu lonena za matalente. Akapolo amene anali okhulupirika ‘anachita malonda’ ndi ndalama za mbuye wawo ndipo iye anawathokoza ndi kuwadalitsa kwambiri. Koma kapolo wosadalirika amene sanachite chilichonse ndi ndalama za mbuye wake anamuweruza kuti ndi “woipa,” “waulesi” ndiponso “wopanda pake.” Ndiyeno anamulanda talente imene anamupatsa ija n’kumuponya kunja.—Werengani Mateyu 25:14-18, 23, 26, 28-30.
17 Pa nthawi ina, Yesu anasonyeza zimene zimachitikira munthu wosakhulupirika. Iye anati: “Munthu wina anali wolemera ndipo anali ndi mtumiki woyang’anira nyumba yake. Mtumiki ameneyu ena anamuneneza kwa bwana wakeyo kuti anali kumusakazira chuma. Choncho anamuitana ndi kumuuza kuti, ‘Ndamva zoipa zimene ukuchita. Pita ukalembe lipoti la mmene wagwirira ntchito yoyang’anira nyumba ino udzandipatse, pakuti supitiriza kuyendetsa ntchito za panyumba pano.’” (Luka 16:1, 2) Popeza kapoloyu anasakaza chuma cha bwana wake, bwanayu anamuchotsa ntchito. Fanizoli lili ndi phunziro lofunika kwambiri kwa ife. Tiziyesetsa kukhala okhulupirika pa utumiki wathu.
KODI NDI NZERU KUDZIYEREKEZERA NDI ENA?
18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudziyerekezera ndi ena?
18 Aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuchita bwanji pa udindo wanga monga mtumiki?’ Koma si bwino kudziyerekezera ndi anthu ena. Baibulo limatilangiza kuti: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake, osati modziyerekezera ndi munthu wina.” (Agal. 6:4) M’malo moyerekezera zimene timachita ndi zimene anthu ena amachita, tingachite bwino kuganizira zimene ifeyo tingakwanitse. Zimenezi zingatithandize kupewa kudzikuza komanso kukhumudwa. Pamene tikudzifufuza, tiyeneranso kukumbukira kuti zinthu zimasintha pa moyo. Zinthu ngati matenda, ukalamba kapena maudindo ena zingatilepheretse kuchita zambiri ngati kale. Koma n’kuthekanso kuti mwina panopa tingawonjezere zimene tikuchita. Ngati zili choncho, mungachite bwino kuyesetsa kuchita zimenezi.
19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ngati sitikulandira udindo winawake?
19 Tiyeneranso kuganizira za maudindo amene tili nawo komanso amene timafuna kukhala nawo. Mwachitsanzo, m’bale angamafune kukhala mkulu mu mpingo kapena kupatsidwa nkhani pa misonkhano ikuluikulu. N’zoona kuti ndi bwino kuyesetsa kuti tiyenerere maudindo ngati amenewa, koma sitiyenera kukhumudwa ngati tikuona kuti sakubwera mofulumira. Mwina pa zifukwa zina, zomwe sitingathe kuzidziwa, pangatenge nthawi kuti tipatsidwe maudindo ena. Musaiwale kuti Mose ankaoneka kuti ndi wokonzeka kutsogolera Aisiraeli kutuluka mu Iguputo. Koma anayenera kuyembekeza zaka 40 kuti achite zimenezi. Izi zinamupatsa nthawi yokwanira yoti akhale ndi makhalidwe ofunika kuti athe kutsogolera anthu ouma khosi ndi opanduka amenewo.—Mac. 7:22-25, 30-34.
20. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yonatani?
20 N’kutheka kuti sitidzapatsidwa n’komwe udindo winawake. Izi n’zimene zinachitikira Yonatani. Iye anali mwana wa Sauli choncho anayenera kukhala mfumu yotsatira ya Isiraeli. Koma Mulungu anasankha Davide, yemwe anali wamng’ono kwambiri, kuti adzakhale mfumu. Kodi Yonatani anatani atadziwa zimenezi? Iye anavomereza ndipo anathandiza Davide mpaka kufika poika moyo wake pa chiswe. Anauza Davide kuti: “Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.” (1 Sam. 23:17) Kodi mwaiona mfundo yake pamenepa? Yonatani anavomereza zimene zinachitikazi ndipo sanachitire nsanje Davide ngati mmene bambo wake anachitira. M’malo mosirira maudindo amene anthu ena apatsidwa, tiziyesetsa kusamalira maudindo amene ifeyo tili nawo. Sitiyenera kukayikira kuti m’dziko latsopano, Yehova adzaonetsetsa kuti zinthu zonse zabwino zimene atumiki ake amalakalaka zidzakwaniritsidwa.
21. Kodi tiyenera kuona bwanji udindo wathu monga atumiki?
21 Tisaiwale kuti monga atumiki okhulupirika si ife akapolo oponderezedwa kapena ozunzidwa. Koma tili ndi udindo wolemekezeka ndipo tapatsidwa ntchito imene sidzachitikanso. Ntchito imeneyi ndi yolalikira uthenga wabwino m’masiku otsiriza ano. Koma tikamagwira ntchito imeneyi, timakhalanso ndi ufulu wambiri chifukwa timatha kusankha tokha mmene timasamalirira maudindo athu. Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala atumiki okhulupirika. Tiyeni tiziona kuti ndi mwayi wa mtengo wapatali kwambiri kutumikira Yehova, yemwe ndi wamkulu m’chilengedwe chonse.