Landirani Chilango cha Yehova Nthawi Zonse
“Usapeputse mwambo wa Yehova.”—MIYAMBO 3:11.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kulandira chilango cha Mulungu?
MFUMU SOLOMO ya Isiraeli wakale ikupatsa aliyense wa ife chifukwa chomveka cholandirira chilango cha Mulungu. Solomo akuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.” (Miyambo 3:11, 12) Inde, Atate wanu wa kumwamba amakupatsani inuyo chilango chifukwa chakuti amakukondani.
2. Kodi tanthauzo la “mwambo” n’chiyani, ndipo munthu angalangidwe m’njira zotani?
2 Mawu akuti “mwambo” akunena za kulanga, kudzudzula, kulangiza, ndi kuphunzitsa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Palibe kulanga kumene kumamveka kosangalatsa panthawiyo, komatu kumakhala kowawa. Koma pambuyo pake, kwa aja amene aphunzitsidwa nako, kumabala chipatso cha mtendere, ndicho chilungamo.” (Aheberi 12:11) Kulandira ndi kutsatira chilango cha Mulungu, kungakuthandizeni kutsatira njira yolungama ndipo mapeto ake mungayambe kugwirizana kwambiri ndi Yehova, Mulungu woyera. (Salmo 99:5) Mungalandire chilango kudzera mwa okhulupirira anzanu, m’zimene mumaphunzira pamisonkhano yachikhristu, ndiponso powerenga Mawu a Mulungu ndi mabuku a “mdindo wokhulupirika.” (Luka 12:42-44) Muyenera kuyamikira kwambiri ngati mwasonyezedwa mbali ina imene mukufunikira kukonza. Koma kodi ndi chilango chotani chimene munthu angafunikire akachita tchimo lalikulu?
Chimene Ena Amachotsedwera
3. Kodi munthu amachotsedwa akatani?
3 Atumiki a Mulungu amaphunzira Baibulo ndi mabuku achikhristu. Amakambirana mfundo za Yehova pamisonkhano yawo ya mpingo, yadera, ndi yachigawo. Choncho Akhristu amadziwa zimene Yehova amawayembekezera kuchita. Munthu amachotsedwa mu mpingo pokhapokha ngati sanalape pamene wachita tchimo lalikulu.
4, 5. Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Malemba chochotsa munthu mu mpingo chimene chafotokozedwa pano, nanga n’chifukwa chiyani mpingo unalimbikitsidwa kum’bwezeretsa mwamunayo?
4 Tiyeni tione chitsanzo cha m’Malemba cha munthu amene anachotsedwa. Mpingo wa ku Korinto unalekerera “dama [limene] ngakhale amitundu [sanali kuchita]. Akuti mwamuna wina [ankakhala] ndi mkazi wa atate wake.” Paulo analimbikitsa Akorinto kuti ‘am’pereke munthu ameneyu kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe, kotero kuti mzimuwo ungapulumutsidwe.’ (1 Akorinto 5:1-5) Atachotsedwa ndi kuperekedwa kwa Satana, munthu wochimwayo anakhalanso mbali ya dziko la Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Kuchotsedwa kwake kunachotsanso khalidwe loipa mu mpingo ndipo kunateteza “mzimu” wa mpingo, kapena kuti mtima wake wabwino woopa Mulungu.—2 Timoteyo 4:22; 1 Akorinto 5:11-13.
5 Pasanadutse nthawi yaitali kwambiri, Paulo analimbikitsa Akhristu ku Korinto kubwezeretsa munthu wochimwa uja. Chifukwa chiyani? Mtumwiyo anati, kuti ‘Satana asawachenjerere.’ Mwachionekere, mwamuna wochimwa uja anali atalapa ndi kuyeretsa moyo wake. (2 Akorinto 2:8-11) Akorinto akanati akane kum’bwezeretsa munthu wolapayo, Satana akanawachenjerera m’njira yakuti iwo akanakhala ankhanza ndi osakhululuka, zimene Mdyerekezi anali kufuna kuti iwo achite. Iwo ayenera kuti ‘anam’khululukira ndi kum’tonthoza’ mwamuna wolapayo pasanadutse nthawi yaitali.—2 Akorinto 2:5-7.
6. Kodi kuchotsa munthu mu mpingo kumathandiza chiyani?
6 Kodi kuchotsa munthu mu mpingo kumathandiza chiyani? Kumathandiza kuti dzina loyera la Yehova lisatonzedwe ndipo kumateteza mbiri yabwino ya anthu ake. (1 Petulo 1:14-16) Kuchotsa mu mpingo munthu wochimwa amene sanalape kumalimbikitsa anthu kuti azitsatira mfundo za Mulungu ndipo kumateteza mpingo kuti ukhalebe woyera mwauzimu. Ndiponso kungathandize munthu wosalapayo kuzindikira kulakwa kwake.
Kulapa N’kofunika
7. Kodi chinachitika n’chiyani kwa Davide atalephera kuulula machimo ake?
7 Ambiri akachita tchimo lalikulu, amalapadi ndipo sachotsedwa mu mpingo. Koma sikuti n’zophweka kuti munthu alapedi. Taganizirani za Mfumu Davide ya Isiraeli, imene inalemba Salmo 32. Nyimboyi imasonyeza kuti kwa nthawi ndithu Davide sanaulule machimo ake aakulu amene mwina anachita mokhudzana ndi Bateseba. Mapeto ake, kuzunzika mtima ndi machimo akewo kunathetsa nyonga yake, monga mmene kutentha kwa m’chilimwe kumaumitsira mtengo wauwisi. Davide anavutika m’thupi ndipo anasowa mtendere, koma ‘ataulula machimo ake, Yehova anam’khululukira.’ (Salmo 32:3-5) Kenako Davide anaimba kuti: “Wodala munthuyu Yehova samuwerengera mphulupulu zake.” (Salmo 32:1, 2) Mtima wake unakhaladi m’malo Mulungu atamuchitira chifundo!
8, 9. Kodi kulapa kumaonekera bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kuti munthu wochotsedwa abwezeretsedwe?
8 Apa n’zoonekeratu kuti munthu wochimwa ayenera kulapa ngati akufuna kuti achitiridwe chifundo. Koma kuchita manyazi kapena kuopa kudziwika sindiko kulapa ayi. “Kulapa” kumatanthauza “kusintha maganizo ako” pa khalidwe loipalo, chifukwa cha chisoni. Munthu wolapa amakhala ndi “mtima wosweka” ndipo amafuna “kukonza cholakwacho” ngati n’kotheka.—Salmo 51:17; 2 Akorinto 7:11.
9 Kulapa n’kofunika kwambiri kuti munthu abwezeretsedwe mu mpingo wachikhristu. Sikuti munthu wochotsedwa amangom’landira mumpingo pakadutsa nthawi yakutiyakuti ayi. Asanabwezeretsedwe, mtima wake ufunika kusintha kwambiri. Ayenera kuzindikira kukula kwa tchimo lake ndi chitonzo chimene iye anabweretsa pa Yehova ndiponso pa mpingo. Wochimwayo ayenera kulapa, kupemphera ndi mtima wonse kuti akhululukidwe, ndi kutsatira mfundo zolungama za Mulungu. Popempha kuti abwezeretsedwe, ayenera kutha kupereka umboni wakuti walapa ndipo ‘akuchita ntchito zosonyeza kulapa.’—Machitidwe 26:20.
N’chifukwa Chiyani Kuulula Tchimo N’kofunika?
10, 11. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuyesa kubisa tchimo?
10 Ena amene achimwa angaganize kuti: ‘Mwina ndikauza aliyense za tchimo langa, angandifunse mafunso ochititsa manyazi ndipo angandichotse mu mpingo. Koma ndikabisa, ndipewa zonsezi ndipo palibe aliyense mu mpingo amene adzadziwa.’ Kuganiza kotereku n’kulephera kuzindikira mfundo zina zofunika kwambiri. Mfundo zake ziti?
11 Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.” Ngakhale zili choncho, amalanga anthu ake “pamlingo woyenera.” (Eksodo 34:6, 7; Yeremiya 30:11, NW) Mukachita tchimo lalikulu, zingatheke bwanji kuti Mulungu akuchitireni chifundo ngati mukuyesa kubisa tchimo lanulo? Yehova amakhala akudziwa, ndipo samangonyalanyaza tchimolo.—Miyambo 15:3; Habakuku 1:13.
12, 13. Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu akuyesa kubisa tchimo?
12 Ngati mwachita tchimo lalikulu, kuulula kungakuthandizeni kukhalanso ndi chikumbumtima chabwino. (1 Timoteyo 1:18-20) Koma ngati mulephera kuulula, chikumbumtima chanu chingaipe ndipo mungayambe kumachimwirachimwira. Kumbukirani kuti mukachimwa, sikuti mwangochimwira munthu mnzanu kapena mpingo ayi. Mwachimwira Mulungu. Wamasalmo anaimba kuti: “Yehova, mpando wachifumu wake uli m’Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake. Yehova ayesa wolungama mtima [“ndi woipa,” NW].”—Salmo 11:4, 5.
13 Yehova sadalitsa munthu aliyense amene amabisa tchimo lalikulu n’kuyesa kukhalabe mumpingo woyera wachikhristu. (Yakobe 4:6) Ndiye ngati mwachimwa ndipo mukufuna kuchita chabwino, musazengereze kuulula ndi mtima wonse zimene mwachita. Apo ayi, chikumbumtima chanu chizikuimbani mlandu, makamaka mukamawerenga kapena kumva uphungu wokhudzana ndi milandu yaikulu ngati wanuwo. Bwanji ngati Yehova angakuchotsereni mzimu wake, ngati mmene anachitira ndi Mfumu Sauli? (1 Samueli 16:14) Mzimu wa Mulungu utakuchokerani, mungafike mpaka pochita tchimo loopsa kwambiri.
Akhulupirireni Abale Anu Okhulupirika
14. Kodi n’chifukwa chiyani munthu amene wachimwa ayenera kutsatira uphungu wa pa Yakobe 5:14, 15?
14 Ndiye kodi munthu wochimwa amene walapa, ayenera kuchita chiyani? “Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo am’pempherere, am’pake mafuta m’dzina la Yehova. Ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamuutsa.” (Yakobe 5:14, 15) Kupita kwa akulu ndi njira imodzi imene munthuyo ‘angabalire zipatso zosonyeza kulapa.’ (Mateyo 3:8) Amuna okhulupirika ndi achikondi amenewa ‘adzam’pempherera ndi kum’paka mafuta m’dzina la Yehova.’ Monga mafuta oziziritsa bala, uphungu wa m’Baibulo umene iwo amapereka umakhala wotonthoza kwa aliyense amene walapadi.—Yeremiya 8:22.
15, 16. Kodi akulu achikhristu amatsatira bwanji chitsanzo chimene Mulungu anapereka malinga ndi zolembedwa pa Ezekieli 34:15, 16?
15 Yehova, M’busa wathu, anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha chikondi pamene anamasula Ayuda ku ukapolo wa ku Babulo mu 537 B.C.E. ndiponso pamene anamasula Isiraeli wauzimu ku “Babulo Wamkulu” mu 1919 C.E. (Chivumbulutso 17:3-5; Agalatiya 6:16) Atachita zimenezi, anakwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa . . . Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira tchika yothyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo.”—Ezekieli 34:15, 16.
16 Yehova anadyetsa nkhosa zake zophiphiritsa, kuzigonetsa zili zotetezeka, ndi kufunafuna zotayika. Nawonso abusa achikhristu amaonetsetsa kuti nkhosa za Mulungu zikudya bwino mwauzimu ndipo n’zotetezeka. Akulu amafunafuna nkhosa zimene zasochera n’kusiya mpingo. Mofanana ndi mmene Mulungu ‘analukira tchika yothyoka mwendo,’ oyang’anira ‘amalukira tchika’ nkhosa zimene zapwetekedwa ndi zonena za munthu wina kapena zimene zadzipweteka zokha. Ndipo mofanana ndi mmene Mulungu ‘analimbitsira yodwala,’ akulu amathandiza amene adwala mwauzimu, mwina chifukwa chakuti achimwa.
Mmene Abusa Amathandizira
17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchedwa kupita kwa akulu kuti atithandize mwauzimu?
17 Akulu amatsatira ndi mtima wonse uphungu wakuti: ‘Pitirizaninso kuchita chifundo . . . , koma ndi mantha.’ (Yuda 23) Akhristu ena achita tchimo lalikulu mwa kuchita chiwerewere. Koma ngati ali olapadi, angayembekeze kusamalidwa mwachifundo ndiponso mwachikondi ndi akulu amene ali okonzeka kuwathandiza mwauzimu. Paulo ananena za amuna amenewa kuphatikizapo iyenso, kuti: “Sikuti ndife olamulira chikhulupiriro chanu, koma ndife antchito anzanu kuti mukhale ndi chimwemwe.” (2 Akorinto 1:24) Choncho, musachedwe kupita kwa iwo kuti akuthandizeni mwauzimu.
18. Kodi akulu amachita bwanji ndi okhulupirira anzawo amene alakwa?
18 Ngati mwachita tchimo lalikulu, n’chifukwa chiyani muyenera kudalira akulu? Chifukwa chakuti iwo kwenikweni ali abusa a gulu la nkhosa za Mulungu. (1 Petulo 5:1-4) Kulibe m’busa amene amamenya mwana wa nkhosa wofatsa amene akulira chifukwa choti wadzipweteka. Choncho, akulu akamathandiza okhulupirira anzawo amene alakwa, saganiza kwambiri zoti munthu wolakwayu tim’patsa chilango chanji ayi, koma amaganiza kwambiri za tchimolo ndi thandizo lauzimu limene angapereke kuti am’pulumutse ngati kuli kotheka. (Yakobe 5:13-20) Akulu ayenera kuweruza mwachilungamo ndi ‘kusamalira gulu la nkhosa mwachikondi.’ (Machitidwe 20:29, 30; Yesaya 32:1, 2) Mofanana ndi Akhristu ena onse, akulu ayenera ‘kuchita cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu.’ (Mika 6:8) Makhalidwe amenewa n’ngofunika kwambiri pogamula nkhani zokhudza moyo ndi utumiki wopatulika wa “nkhosa za pabusa [pa Yehova].”—Salmo 100:3.
Mofanana ndi abusa akale, akulu achikhristu ‘amalukira tchika’ nkhosa za Mulungu zimene zathyoka
19. Kodi akulu achikhristu amayesa kuwongolera munthu wina ndi mtima wotani?
19 Abusa achikhristu amaikidwa ndi mzimu woyera ndipo amayesetsa kutsogoleredwa ndi mzimuwo. Ngati “munthu wapatuka panjira osazindikira,” amuna oyenerera mwauzimuwo amayesa “kumuwongolera munthu woteroyo ndi mzimu wachifatso.” (Agalatiya 6:1; Machitidwe 20:28) Mofatsa komanso motsatira kwambiri mfundo za Mulungu, akulu amayesa kuwongola maganizo ake, ngati mmene dokotala wachifundo amabwezerera fupa lothyoka m’malo mwake bwinobwino pofuna kuti munthuyo asamve ululu kwambiri koma kuti athandizike pa vuto lakelo. (Akolose 3:12) Popeza kuti akuluwo amadalira pemphero ndi Malemba kuti aone ngati angam’chitire chifundo, zogamula zawo zimagwirizana ndi mmene Mulungu akuonera nkhaniyo.—Mateyo 18:18.
20. Kodi ndi liti pamene pangafunikire kulengeza ku mpingo kuti uje wadzudzulidwa?
20 Ngati ambiri akudziwa za tchimolo kapena ngati tchimolo lidzadziwike ndithu, pangakhale poyenera kulengeza ku mpingo pofuna kuteteza mbiri ya mpingowo. Chilengezo chimaperekedwanso ngati mpingo ukufunikira kudziwa. Nthawi imene munthu wodzudzulidwa kaamba ka mlandu wachiweruzo akuchira mwauzimu, amakhala ngati munthu amene anadzipweteka uja yemwe akuchira, woti sangachite zinthu zambiri chifukwa cha kupwetekako. Kwa nthawi yakutiyakuti, zingakhale zothandiza kuti munthu wolapayo asamapereke ndemanga pamisonkhano koma azingomvetsera basi. Akulu angakonze zoti munthu wina aziphunzira naye Baibulo n’cholinga choti am’thandize kulimba pambali imene ali wofooka kuti akhalenso ‘wolimba m’chikhulupiriro.’ (Tito 2:2) Amachita zonsezi chifukwa cha chikondi, osati kuti akhaulitse wolakwayo ayi.
21. Kodi nkhani zina zokhudza kulakwa zingasamalidwe bwanji?
21 Akulu angapereke thandizo lauzimu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, tinene kuti m’bale amene kale anali ndi vuto la kumwa, wamwa mowa kwambiri kamodzi kapena kawiri ali yekha kunyumba. Kapena amene anasiya kalekale kusuta fodya, wasuta fodya kamodzi kapena kawiri chifukwa chakuti wafooka kwa kanthawi. Ngakhale kuti wapemphera ndipo akukhulupirira kuti Mulungu wamukhululukira, ayenera kupita kwa mkulu kuti amuthandize kuti tchimo lakelo lisakhale chizolowezi. Mkulu mmodzi kapena awiri angasamalire nkhani imeneyo. Komabe, mkuluyo kapena akuluwo ayenera kudziwitsa woyang’anira wotsogolera, popeza kuti pangakhale zina zimene zingafunikire kuziona.
Pitirizani Kulandira Chilango cha Mulungu
22, 23. N’chifukwa chiyani muyenera kupitiriza kulandira chilango cha Mulungu?
22 Kuti Mkhristu aliyense ayanjidwe ndi Mulungu, ayenera kulabadira chilango cha Yehova. (1 Timoteyo 5:20) Choncho, labadirani chilango chilichonse chimene mumalandira mukamawerenga Malemba ndi mabuku achikhristu kapena mukamamvera uphungu woperekedwa pa misonkhano ya mpingo, misonkhano yadera, ndi yachigawo ya anthu a Yehova. Khalani maso pochita chifuniro cha Yehova. Mukatero, chilango cha Mulungu chidzakuthandizani kukhala ndi linga lolimba lauzimu limene lingakutetezeni ku uchimo.
23 Kulandira chilango cha Mulungu kudzakuthandizani kukhalabe m’chikondi chake. N’zoona kuti ena achotsedwa mu mpingo wachikhristu, koma zimenezi sizingakuchitikireni ngati ‘mutchinjiriza mtima wanu’ ndi ‘kuyenda monga munthu wanzeru.’ (Miyambo 4:23; Aefeso 5:15) Koma ngati panopa ndinu wochotsedwa, bwanji osayamba kuchita zomwe mungathe kuti mubwezeretsedwe? Mulungu akufuna kuti onse amene anadzipereka kwa iye azimulambira mokhulupirika ndiponso “mokondwera mtima.” (Deuteronomo 28:47) Mungachite zimenezi kosatha ngati nthawi zonse mulandira chilango cha Yehova.—Salmo 100:2.