Kupambana Chiyeso cha Kukhulupirika
‘Muvale umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo [chenicheni ndi kukhulupirika, NW].’—AEFESO 4:24.
1. Kodi nchifukwa ninji tili ndi mangawa akukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu?
KUPAMBANA chiyeso cha kukhulupirika kuli ndi mbali zambiri. Mbali yofunika koposa ndiyo kupambana chiyeso cha kukhulupirika kulinga kwa Yehova Mulungu. Inde, polingalira za amene Yehova ali ndi zimene watichitira, ndipo chifukwa cha kudzipatulira kwathu kwa iye, tili ndi mangawa akukhala okhulupirika kwa iye. Kodi timasonyeza motani kukhulupirika kulinga kwa Yehova Mulungu? Njira yoyamba ndiyo mwa kukhala okhulupirika pa mapulinsipulo olungama a Yehova.
2, 3. Kodi ndi kugwirizana kotani kumene kulipo pakati pa kukhulupirika ndi chilungamo?
2 Kuti tipambane chiyesocho, tiyenera kulabadira mawu opezeka pa 1 Petro 1:15, 16 akuti: “Monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti ine ndine woyera mtima.” Kukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu kudzatichititsa kumumvera iye nthaŵi zonse, tikumagwirizanitsa malingaliro athu, mawu, ndiponso zochita zathu ndi chifuniro chake choyera. Kumatanthauza kusunga chikumbumtima chokoma, monga momwe timalamulidwira pa 1 Timoteo 1:3-5 kuti: “Chitsiriziro cha chilamuliro [kusaphunzitsa ziphunzitso zosiyana kapena kusamala nkhani zachabe] ndicho chikondi chochokera mumtima woyera ndi m’chikumbumtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga.” Zoona, palibe aliyense wa ife amene ali wangwiro, koma tiyenera kuyesayesa kuchita zonse zotheka, si choncho kodi?
3 Kukhulupirika kulinga kwa Yehova kudzatiletsa kunyalanyaza mwadyera mapulinsipulo olungama. Inde, kukhulupirika kudzatiletsa kukhala munthu wina mkati ndi munthu winanso kunja. Wamasalmo anali kuganiza za kukhulupirika pamene anaimba kuti: “Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu: muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliwope dzina lanu.” (Salmo 86:11) Kukhulupirika kumafuna chimene moyenerera chatchedwa “kumvera malamulo osatheka kusungitsidwa ndi wina.”
4, 5. Kukhulupirika kudzatichititsa kukhala osamala kuwopera kuti tingachitenji?
4 Kukhulupirika kulinga kwa Yehova Mulungu kudzatiletsanso kuchita chilichonse chimene chingadzetse chitonzo pa dzina lake ndi Ufumu wake. Mwachitsanzo, Akristu aŵiri anavutana kwambiri nthaŵi ina kwakuti mosayenerera anasankha kupita kukhoti lakudziko. Woweruza anafunsa kuti, ‘Kodi nonse aŵirinu ndinu Mboni za Yehova?’ Mwachionekere iye sanamvetsetse zimene iwo anali kuchita m’khoti. Chitonzo chake kukula! Kukhulupirika kulinga kwa Yehova Mulungu kukanachititsa abalewo kulabadira chilangizo cha mtumwi Paulo chakuti: “Koma pamenepo pali chosoŵa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?” (1 Akorinto 6:7) Ndithudi, njira ya kukhulupirika kulinga kwa Yehova Mulungu ndiyo kulola kutayikidwa kanthu kena kuposa kudzetsa chitonzo pa Yehova ndi gulu lake.
5 Kukhulupirika kulinga kwa Yehova Mulungu kumafunanso kusagonja pa kuwopa munthu. “Kuwopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.” (Miyambo 29:25) Motero, sitimagonja poyang’anizana ndi chizunzo, koma timatsatira chitsanzo choperekedwa ndi Mboni za Yehova m’dziko lomwe kale linali Soviet Union, ku Malaŵi, ku Ethiopia, ndi m’maiko ena ambirimbiri.
6. Kukhulupirika kudzatiletsa kuyanjana ndi yani?
6 Ngati tili okhulupirika kwa Yehova Mulungu, tidzapeŵa kupanga mabwenzi ndi onse amene ali adani ake. Nchifukwa chake wophunzira Yakobo analemba kuti: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Tifunika kukhala ndi kukhulupirika kumene Mfumu Davide anasonyeza pamene anati: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nawo chisoni [“sindinyansidwa nawo,” NW] iwo akuukira inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: ndiwayesa adani.” (Salmo 139:21, 22) Sitifunika kumacheza ndi ochimwa dala alionse, pakuti tilibe nawo chochita. Kodi kukhulupirika kulinga kwa Mulungu sikudzatiletsa kucheza ndi mdani aliyense wotero wa Yehova, kaya maso ndi maso kapena kupyolera pawailesi yakanema?
Kukhalira Mbali Yehova
7. Kukhulupirika kudzatithandiza kuchitanji kulinga kwa Yehova, ndipo Elihu anachita motani zimenezi?
7 Kukhulupirika kudzatisonkhezera kukhalira mbali Yehova Mulungu. Elihu alidi chitsanzo chabwino kwambiri pa zimenezo! Yobu 32:2, 3 amatiuza kuti: “Adapsa mtima Elihu . . . Adapasa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu. Adapsa mtima pa mabwenzi ake atatu omwe, pakuti anasoŵa pomyankha; koma [iwo anafika ponena kuti Mulungu ali woipa, NW].” M’machaputala 32 mpaka 37 a Yobu, Elihu akukhalira mbali Yehova. Mwachitsanzo, anati: “Mundilole pang’ono, ndidzakuuzani, pakuti ndili nawonso mawu akunenera Mulungu. . . . Ndidzavomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama. . . . Sawachotsera wolungama maso ake.”—Yobu 36:2-7.
8. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhalira mbali Yehova?
8 Kodi nchifukwa ninji tifunika kukhalira mbali Yehova? Lerolino, Mulungu wathu Yehova amachitiridwa mwano m’njira zambirimbiri. Anthu amanena kuti iye kulibe, kuti ali mbali ya Utatu, kuti amazunza anthu kwamuyaya m’helo woyaka moto, kuti akuyesa mwamphwayi kutembenuza dziko, kuti sasamala za anthu, ndi zina zotero. Timasonyeza kukhulupirika kwathu kwa iye mwa kumkhalira mbali ndi kusonyeza kuti Yehova alikodi; kuti ndi Mulungu wanzeru, wolungama, wamphamvuyonse, ndi wachikondi; kuti ali ndi nthaŵi ya kalikonse; ndi kuti ikafika nthaŵi yake, adzathetsa kuipa konse ndi kusandutsa dziko lonse lapansi paradaiso. (Mlaliki 3:1) Zimenezi zimafuna kuti tigwiritsire ntchito mpata uliwonse kuchitira umboni dzina la Yehova ndi Ufumu wake.
Kukhulupirika ku Gulu la Yehova
9. Kodi ndi pankhani zotani zimene ena asonyezerapo kusakhulupirika kwawo?
9 Tsopano tafika pankhani ya kukhala wokhulupirika ku gulu looneka la Yehova. Ndithudi, tili ndi mangawa akukhala okhulupirika kwa ilo, kuphatikizapo kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” mwa amene mpingo wachikristu umadyetsedwa mwauzimu. (Mateyu 24:45-47) Tinene kuti m’zofalitsa za Watch Tower mwatuluka chinthu chimene sitikumvetsetsa kapena sitikuvomereza pakali pano. Kodi tidzatani? Kukhumudwa ndi kuchoka m’gulu? Ndi zimene ena anachita pamene Nsanja ya Olonda, zaka zambiri zapitazo, inati pangano latsopano lidzagwira ntchito m’Zaka Chikwi. Ena anakhumudwa ndi zimene Nsanja ya Olonda inanena pankhani ya uchete. Aja amene anakhumudwa ndi nkhani zimenezi akanakhala okhulupirika ku gulu ndi kwa abale awo, akanayembekeza kuti Yehova amveketse nkhani zimenezi, zimene anachita kumene panthaŵi yake. Chotero, kukhulupirika kumaphatikizapo kuyembekezera moleza mtima kufikira chidziŵitso china chitafalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.
10. Kukhulupirika kudzatiletsa kuchita chidwi ndi chiyani?
10 Kukhulupirika ku gulu looneka la Yehova kumatanthauzanso kusagwirizana konse ndi ampatuko. Akristu okhulupirika samachita chidwi ndi zimene anthu otero amanena. Zoona, aja amene Yehova Mulungu akugwiritsira ntchito kutsogoza ntchito yake padziko lapansi sali angwiro. Koma kodi Mawu a Mulungu amatiuza kuchitanji? Kusiya gulu la Mulungu? Iyayi. Kukonda abale kuyenera kutikhalitsa okhulupirika kwa ilo, ndipo tiyenera kupitiriza ‘kukondana kwenikweni kuchokera kumtima.’—1 Petro 1:22.
Kukhulupirika Kulinga kwa Akulu Okhulupirika
11. Kukhulupirika kudzatithandiza kupeŵa kalingaliridwe kati koipa?
11 Pamene china chimene chikutivuta kumvetsetsa chanenedwa kapena kuchitidwa mumpingo, kukhulupirika kudzatiletsa kuweruziratu zinthu ndipo kudzatithandiza kuona kuti mwina imeneyo yangokhala nkhani yodalira pa kaonedwe ka munthu. Kodi sikuli bwino kusumika maganizo pa mikhalidwe yabwino ya akulu oikidwa ndi okhulupirira anzathu ena kuposa pa zophophonya zawo? Inde, tifunika kupeŵa kalingaliridwe konse koipa koteroko, pakuti kali mbali ya kusakhulupirika! Kukhulupirika kudzatithandizanso kumvera chilangizo cha Paulo cha ‘kusachitira mwano munthu aliyense.’—Tito 3:1, 2.
12, 13. Kodi ndi ziyeso zapadera ziti zimene akulu amayang’anizana nazo?
12 Kukhulupirika kumapereka ziyeso zapadera kwa akulu. Chimodzi cha ziyesozo ndicho nkhani ya kusunga chinsinsi. Wina mumpingo angauze mkulu nkhani yachinsinsi. Kukhulupirika kulinga kwa iyeyo kudzaletsa mkulu kuswa pulinsipulo la kusunga chinsinsi. Adzalabadira chilangizo chopezeka pa Miyambo 25:9 chakuti: “Osaulula zinsinsi za mwini.” Zimenezo zikutanthauza kuti sayenera kutero ndi kwa mkazi wake yemwe!
13 Akulu alinso ndi ziyeso zina za kukhulupirika zimene afunika kupambana. Kodi iwo adzakhala okondweretsa anthu, kapena kodi molimba mtima ndi mwachifatso adzathandiza aja ofunikira kuwongolera, ngakhale ngati ali achibale awo enieni kapena mabwenzi? Kukhulupirika ku gulu la Yehova kudzachititsa ife amene tili akulu kuyesa kuthandiza aliyense wofunikira thandizo lauzimu. (Agalatiya 6:1, 2) Ngakhale kuti tiyenera kukhala okoma mtima, kukhulupirika kudzatichititsa kulankhula mosapita m’mbali kwa mkulu mnzathu, monga momwedi Paulo analankhulira mosapita m’mbali kwa mtumwi Petro. (Agalatiya 2:11-14) Komanso, oyang’anira afunika kukhala osamala, kuti mwa kuchita mopanda nzeru kapena kusonyeza tsankho kapena mwa njira ina kugwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wawo, angachititse aja omwe akuwayang’anira kuvutika pa kukhulupirika kwawo ku gulu la Mulungu.—Afilipi 4:5.
14, 15. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingayese kukhulupirika kwa amene ali mumpingo?
14 Palinso mbali zina pankhani ya kupambana chiyeso cha kukhulupirika ku mpingo ndi akulu ake. Ngati muli mikhalidwe yovuta mumpingo, imatipatsa mpata wa kusonyeza kukhulupirika kwathu kulinga kwa Yehova ndi aja amene akumuimira. (Onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 1987, masamba 15-17.) Pamene wina wachotsedwa, kukhulupirika kumafuna kuti tichirikize akulu, osati kuti pambuyo pake tiziyesa kuona ngati panali zifukwa zokwanira zochitira zimenezo.
15 Kukhulupirika ku mpingo kumafunanso kuti tizichirikiza misonkhano yonse isanu mlungu ndi mlungu malinga ndi mikhalidwe yathu ndi kukhoza kwathu. Kukhulupirika kumafuna kuti tisamangopezekapo chabe nthaŵi zonse komanso kukonzekera ndi kupereka ndemanga zomangirira pamene mpata ulola.—Ahebri 10:24, 25.
Kukhulupirika mu Ukwati
16, 17. Kodi ndi ziyeso zotani za kukhulupirika zimene Akristu okwatirana amayang’anizana nazo?
16 Kodi nkwayaninso kumene tili ndi mangawa akukhala wokhulupirika? Ngati ndife okwatira, chifukwa cha malumbiro athu a ukwati, tiyenera kupambana chiyeso cha kukhala wokhulupirika kwa mnzathu wa muukwati. Kukhulupirika kulinga kwa mnzathu kudzatipeŵetsa kulakwitsa zinthu mwa kukhala wabwino kwambiri kwa akazi ena kapena amuna ena kuposa mmene tilili kwa mkazi wathu kapena mwamuna wathu. Kukhulupirika kulinga kwa mnzathu kumafunanso kuti tisauze akunja zofooka kapena zophophonya za mnzathu. Nkwapafupi kudandaula kwa ena kuposa kulimbikira kusunga njira zolankhulana zili chitsegukire pakati pathu ndi mnzathu, zimene tiyenera kuchita mogwirizana ndi Lamulo la Chikhalidwe. (Mateyu 7:12) Kwenikweni, mkhalidwe wa ukwati umayesa kwambiri kukhulupirika kwathu kwachikristu.
17 Kuti tipambane chiyeso chimenechi cha kukhulupirika, sitiyenera kungopeŵa liwongo la khalidwe lonyansa koma tiyeneranso kutetezera maganizo athu ndi mtima. (Salmo 19:14) Mwachitsanzo, ngati mitima yathu yonyenga imalakalaka zokondweretsa ndi chisangalalo, nkwapafupi kwambiri kwa ife kuchoka pa kukhumbira wamba kufika pa kukhumbitsa kwadyera. Akumalimbikitsa kukhulupirika muukwati, Mfumu Solomo akulangiza amuna mophiphiritsira ‘kumwa madzi m’chitsime chawo.’ (Miyambo 5:15) Ndipo Yesu anati: “Yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Amuna amene amakonda kuyang’ana zamaliseche amakhala pangozi ya kukopeka kuchita chigololo, motero akumanyengeza akazi awo ndi kukhala osakhulupirika kwa iwo. Mwa njira imodzimodziyo, mkazi wokondetsa maprogramu opitirizabe a pa TV ochita ndi nkhani zachigololo angakopeke kukhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake. Komabe, mwa kukhaladi okhulupirika kwa mnzathu, timalimbitsa chomangira cha ukwati, ndipo timathandizana pakuyesayesa kwathu kukondweretsa Yehova Mulungu.
Zotithandiza Kukhala Okhulupirika
18. Kodi ndi kuzindikira chiyani kumene kudzatithandiza kukhala okhulupirika?
18 Kodi nchiyani chimene chidzatithandiza kupambana chiyeso cha kukhulupirika pambali zinayi izi: kukhulupirika kulinga kwa Yehova, ku gulu lake, ku mpingo, ndi kwa mnzathu wa muukwati? Chithandizo chimodzi ndicho kuzindikira kuti kupambana chiyeso cha kukhulupirika kumagwirizana ndi kutsimikiziritsa uchifumu wa Yehova. Inde, mwa kukhalabe okhulupirika timasonyeza kuti timaona Yehova monga Mfumu ya Chilengedwe Chonse. Motero tingakhalenso ndi ulemu waumwini ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano la Yehova. Tingadzithandize kukhala okhulupirika mwa kulingalira zitsanzo zabwino za kukhulupirika, kuyambira kwa Yehova kufikira kwa aja otchulidwa m’Baibulo ndi m’zofalitsa zathu za Watch Tower, kuphatikizapo a m’nkhani za mu Yearbook.
19. Kodi chikhulupiriro chili ndi mbali yotani pa kukhala kwathu okhulupirika?
19 Chikhulupiriro cholimba mwa Yehova Mulungu ndi kuwopa kusamkondweretsa zidzatithandiza kupambana chiyeso cha kukhulupirika. Timalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi kumuwopa mwa kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndi mwa kuchita utumiki wachikristu. Zimenezi zidzatithandiza kuchita mogwirizana ndi chilangizo cha Paulo cholembedwa pa Aefeso 4:23, 24: ‘Mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo [chenicheni ndi kukhulupirika, NW].’
20. Koposa zonse, kodi ndi mkhalidwe uti umene udzatithandiza kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi kwa ena onse amene tili nawo mangawa akukhala wokhulupirika?
20 Kuzindikira mikhalidwe ya Yehova kumatithandiza kukhala okhulupirika. Koposa zonse, chikondi chopanda dyera kwa Atate wathu wakumwamba ndi chiyamiko kaamba ka zonse zomwe watichitira, kumkonda iye ndi mtima wathu wonse ndi moyo ndi nzeru ndi mphamvu zathu zonse kudzatithandiza kukhala okhulupirika kwa iye. Ndiponso, kukhala ndi chikondi chimene Yesu anati chidzadziŵikitsa otsatira ake kudzatithandiza kukhala okhulupirika kwa Akristu onse mumpingo ndi m’banja mwathu. Kuzitchula mwanjira ina, kwenikweni ili nkhani ya kukhala wadyera kapena wopanda dyera. Kusakhulupirika kumatanthauza kukhala wadyera. Kukhulupirika kumatanthauza kusakhala wadyera.—Marko 12:30, 31; Yohane 13:34, 35.
21. Kodi nkhani ya kupambana chiyeso cha kukhulupirika ingafotokozedwe motani mwachidule?
21 Mwachidule: Kukhulupirika ndiko mkhalidwe wapamwamba wosonyezedwa ndi Yehova Mulungu, ndi Yesu Kristu, ndipo ndi atumiki oona onse a Yehova. Kuti tikhale ndi unansi wabwino ndi Yehova Mulungu, tiyenera kupambana chiyeso cha kukhulupirika kulinga kwa iye mwa kukwaniritsa zofunika zake zolungama, mwa kusayanjana konse ndi adani ake, ndi mwa kukhalira mbali Yehova pochitira umboni wolinganizidwa ndi wamwamwaŵi. Tiyeneranso kupambana chiyeso cha kukhala okhulupirika ku gulu looneka la Yehova. Tiyenera kukhala okhulupirika ku mipingo yathu ndi okhulupirika kwa anzathu a muukwati. Mwa kupambana bwinobwino chiyeso cha kukhulupirika, tidzakhala tikutengamo mbali m’kutsimikiziritsa uchifumu wa Yehova, ndipo tidzakhala kumbali yake m’nkhaniyo. Motero tidzapeza chiyanjo chake ndipo tidzalandira mphotho ya moyo wosatha. Zimene mtumwi Paulo ananena pa kudzipereka kwaumulungu zinganenedwenso pa kupambana chiyeso cha kukhulupirika. Iko kupindula ponse paŵiri moyo uno ndi womwe ulinkudza.—Salmo 18:25; 1 Timoteo 4:8.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene tingapambanire chiyeso cha kukhulupirika kulinga kwa Mulungu?
◻ Kodi kukhulupirika ku gulu la Yehova kumafunanji kwa ife?
◻ Kodi akulu angapambane motani chiyeso cha kukhulupirika?
◻ Kodi ndi chiyeso chotani cha kukhulupirika chimene Akristu okwatira ayenera kupambana?
◻ Kodi ndi mikhalidwe yotani imene idzatithandiza kupambana chiyeso cha kukhulupirika?
[Chithunzi patsamba 17]
Kukhulupirika kulinga kwa amene ali mumpingo kudzaletsa akulu kuvumbula nkhani zachinsinsi
[Zithunzi patsamba 18]
Kukhala wokhulupirika kwa mnzanu kumalimbitsa chomangira ukwati