Kukhala Mwamuna ndi Mkulu—Kulinganiza Mathayowo
‘Woyang’anira akhale mwamuna wa mkazi mmodzi.’—1 TIMOTEO 3:2.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji kusakwatira kwa ansembe sikuli kwa m’Malemba?
M’ZAKA za zana loyamba, Akristu okhulupirika anasamala za kulinganiza mathayo awo osiyanasiyana. Pamene mtumwi Paulo ananena kuti Mkristu amene akhala wosakwatira “achita [bwino] koposa,” kodi anatanthauza kuti mwamuna woteroyo ndiye ali woyeneretsedwa bwino kutumikira monga woyang’anira mumpingo wachikristu? Kodi iye kwenikweni anali kupanga umbeta kukhala chiyeneretso cha kukhala mkulu? (1 Akorinto 7:38) Kusakwatira kuli chiyeneretso cha atsogoleri achipembedzo achikatolika. Koma kodi kusakwatira kwa ansembe kuli kwa m’Malemba? Matchalitchi a Eastern Orthodox amalola ansembe awo a pa parishi kukwatira, koma osati abishopu awo. Kodi zimenezo nzogwirizana ndi Baibulo?
2 Atumwi 12 a Kristu, ziŵalo za maziko a mpingo wachikristu, anali amuna okwatira. (Mateyu 8:14, 15; Aefeso 2:20) Paulo analemba kuti: “Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa [Petro]?” (1 Akorinto 9:5) New Catholic Encyclopedia imavomereza kuti “lamulo la kusakwatira linayambidwa ndi tchalitchi” ndi kuti “atumiki a NT [Chipangano Chatsopano] sanali oletsedwa kukwatira.” Mboni za Yehova zimatsatira chitsanzo cha m’Malemba m’malo mwa kutsatira lamulo la tchalitchi.—1 Timoteo 4:1-3.
Ukulu ndi Ukwati Zimayendera Pamodzi
3. Kodi ndi maumboni a m’Malemba otani amene amasonyeza kuti oyang’anira achikristu angakhale amuna okwatira?
3 M’malo mofuna kuti amuna oikidwa monga oyang’anira akhale osakwatira, Paulo analembera Tito kuti: “Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe m’Krete, kuti ukalongosole zosoŵa, nukaike akulu [Chigiriki, pre·sbyʹte·ros] m’midzi yonse, monga ndinakulamulira; ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nawo ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mawu. Pakuti woyang’anira [Chigiriki, e·piʹsko·pos, kumene kwachokera liwu lakuti “bishopu”] ayenera kukhala wopanda chirema, ngati mdindo wa Mulungu.”—Tito 1:5-7.
4. (a) Kodi timadziŵa motani kuti ukwati suli chiyeneretso cha oyang’anira achikristu? (b) Kodi mbale wosakwatira amene ali mkulu ali ndi mwaŵi wotani?
4 Kumbali inayo, ukwati suli chiyeneretso cha m’Malemba chokhalira mkulu. Yesu anali mbeta chikhalire. (Aefeso 1:22) Paulo, woyang’anira wachitsanzo chabwino kwambiri mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba, anali wosakwatira panthaŵiyo. (1 Akorinto 7:7-9) Lerolino, alipo Akristu osakwatira ambiri amene akutumikira monga akulu. Umbeta wawo uyenera kuwapatsa nthaŵi yokulirapo yochitira mathayo awo monga oyang’anira.
‘Mwamuna Wokwatira Ali Wogaŵanika’
5. Kodi ndi mfundo ya m’Malemba yotani imene abale okwatira ayenera kuizindikira?
5 Pamene mwamuna wachikristu akwatira, ayenera kudziŵa kuti akusenza mathayo atsopano amene adzafuna nthaŵi yake ndi maganizo ake. Baibulo limati: “Mwamuna wosakwatira amadera nkhaŵa zinthu za Ambuye, mmene angapezere chiyanjo cha Ambuye. Koma mwamuna wokwatira amadera nkhaŵa zinthu za dziko, mmene angapezere chiyanjo cha mkazi wake, ndipo amakhala wogaŵanika.” (1 Akorinto 7:32-34, NW) Kodi amakhala wogaŵanika m’lingaliro lotani?
6, 7. (a) Kodi ndi njira imodzi yotani mwa imene mwamuna wokwatira amakhalira “wogaŵanika”? (b) Kodi ndi uphungu wotani umene Paulo akupereka kwa Akristu okwatira? (c) Kodi zimenezi zingasonkhezere motani chosankha cha mwamuna cha kulandira gawo la kuntchito?
6 Choyamba, mwamuna amathedwa ulamuliro wa pathupi lake. Paulo anamveketsa zimenezi bwino lomwe kuti: “Mkazi alibe ulamuliro wa pathupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pathupi la iye yekha, koma mkazi ndiye.” (1 Akorinto 7:4) Ena amene akuganiza zokwatira angalingalire kuti zimenezi sizofunikira kwambiri chifukwa chakuti kugonana sikudzakhala chinthu chachikulu muukwati wawo. Komabe, popeza kudzisungira kwa munthu asanaloŵe mu ukwati kuli chofunika cha m’Malemba, Akristu samadziŵa kwenikweni zofunika za kugonana za mnzawo wa muukwati wamtsogolo.
7 Paulo akusonyeza kuti ngakhale okwatirana amene ‘asumika maganizo awo pa zinthu za mzimu’ ayenera kulingalira za zofunika za kugonana za wina ndi mnzake. Iye anapereka uphungu kwa Akristu a ku Korinto kuti: “Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma [chi]modzimodzinso mkazi kwa mwamuna. Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthaŵi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.” (Aroma 8:5; 1 Akorinto 7:3, 5) Nzachisoni kuti pakhala zochitika za chigololo pamene uphungu umenewu sunatsatiridwe. Chifukwa cha zimenezi, Mkristu wokwatira ayenera kupenda zinthu mosamalitsa asanavomereze gawo la kuntchito limene lidzamulekanitsa ndi mkazi wake kwa nthaŵi yaitali. Iye salinso ndi ufulu wodziyendera umene anali nawo akali mbeta.
8, 9. (a) Kodi Paulo anatanthauzanji pamene ananena kuti Akristu okwatira “amadera nkhaŵa zinthu za dziko”? (b) Kodi Akristu okwatira ayenera kudera nkhaŵa za kuchitanji?
8 Kodi ndi m’lingaliro lotani limene tinganenere kuti amuna achikristu okwatira, kuphatikizapo akulu, “amadera nkhaŵa zinthu za dziko [koʹsmos]”? (1 Akorinto 7:33) Nkoonekeratu kuti Paulo sanali kulankhula za zinthu zoipa za dzikoli, zimene Akristu onse oona ayenera kupeŵa. (2 Petro 1:4; 2:18-20; 1 Yohane 2:15-17) Mawu a Mulungu amatilangiza ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi [ko·smi·kosʹ], ndi kukhala ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’—Tito 2:12.
9 Chotero, Mkristu wokwatira “amadera nkhaŵa zinthu za dziko” m’lingaliro lakuti iye ayenera kusamala za zinthu za masiku onse za moyo wa muukwati. Zimenezi zimaphatikizapo, kupeza nyumba, chakudya, zovala, zosangulutsa—limodzinso ndi nkhaŵa zina zambiri ngati pali ana. Koma ngakhale okwatirana opanda ana, kuti ukwati wawo ukhale wachipambano, onse aŵiri mwamuna ndi mkazi ayenera kudera nkhaŵa za “kupeza chiyanjo” cha wina ndi mnzake. Zimenezi nzofunika kwambiri kwa akulu achikristu pamene akulinganiza mathayo awo.
Amuna Abwino Amakhalanso Akulu Abwino
10. Kuti Mkristu ayeneretsedwe kukhala mkulu, kodi abale ake ndi anthu akunja ayenera kukhala okhoza kuonanji?
10 Pamene kuli kwakuti ukwati suli chiyeneretso chokhalira mkulu, ngati mwamuna wachikristu akwatira, asanavomerezedwe kuikidwa monga mkulu, ayenera kusonyeza umboni wa kuyesayesa kwake kukhala mwamuna wabwino ndi wachikondi, pamene akuchita umutu woyenera. (Aefeso 5:23-25, 28-31) Paulo analemba kuti: “Ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino. Ndipo kuyenera woyang’anira akhale wopanda chirema, mwamuna wa mkazi mmodzi.” (1 Timoteo 3:1, 2) Kuyenera kukhala koonekeratu kuti mkulu akuyesayesa kwenikweni kukhala mwamuna wabwino, kaya mkazi wake ndi Mkristu mnzake kapena ayi. Ndipo ngakhale anthu akunja kwa mpingo ayenera kuona kuti iye akusamalira bwino mkazi wake ndi mathayo ake ena. Paulo anawonjezera kuti: “Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa Mdyerekezi.”—1 Timoteo 3:7.
11. Kodi mawu akuti “mwamuna wa mkazi mmodzi” amatanthauzanji, motero kodi ndi kusamala kotani kumene akulu ayenera kuchita?
11 Ndithudi, mawu akuti “mwamuna wa mkazi mmodzi” akuchotserapotu mitala iliyonse, koma amatanthauzanso kukhulupirika kwa muukwati. (Ahebri 13:4) Akulu makamaka ayenera kusamala kwambiri pamene akuthandiza alongo mumpingo. Ayenera kupeŵa kukhala okha pamene akuchezera mlongo wofunikira uphungu ndi chitonthozo. Iwo angachite bwino kupita ndi mkulu wina, mtumiki wotumikira, kapena ngakhale mkazi wawo ngati ili chabe nkhani ya kucheza kopereka chilimbikitso.—1 Timoteo 5:1, 2.
12. Kodi ndi malongosoledwe otani amene akazi a akulu ndi atumiki otumikira ayenera kuyenerana nawo?
12 Ndiponso, pamene ankandandalika ziyeneretso za akulu ndi atumiki otumikira, mtumwi Paulo anaperekanso uphungu kwa akazi a awo olingaliridwa kuikidwa pa mathayo amenewo. Analemba kuti: “Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadyerekeza, odzisunga, okhulupirika m’zonse.” (1 Timoteo 3:11) Mwamuna wachikristu angachite zambiri kuthandiza mkazi wake kukwaniritsa zofotokozedwazo.
Mathayo a m’Malemba Kulinga kwa Mkazi
13, 14. Ngakhale ngati mkazi wa mkulu sali Mboni inzake, kodi nchifukwa ninji iye ayenera kukhalabe naye ndi kukhala mwamuna wabwino?
13 Ndithudi, uphungu umenewu woperekedwa kwa akazi a akulu ndi atumiki otumikira umasonyeza kuti akazi oterowo ali Akristu odzipatulira. Kaŵirikaŵiri, ndi mmene zilili mmenemu chifukwa chakuti Akristu ayenera kukwatira kokha “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Koma bwanji za mbale amene anali wokwatira kale wosakhulupirira pamene iye anapatulira moyo wake kwa Yehova, kapena amene mkazi wake apanduka osati chifukwa cha iye?
14 Zimenezi, mwa izo zokha, sizingamletse kukhala mkulu. Ndiponso sizingamlole kupatukana ndi mkazi wake chabe chifukwa chakuti sagwirizana naye pa zimene amakhulupirira. Paulo anapereka uphungu wakuti: “Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka.” (1 Akorinto 7:27) Iye anapitiriza kunena kuti: “Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. Koma ngati wosakhulupirayo achoka, achoke. M’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere. Pakuti udziŵa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? kapena udziŵa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?” (1 Akorinto 7:12, 15, 16) Ngakhale ngati mkazi wake sali Mboni, mkulu ayenera kukhala mwamuna wabwino.
15. Kodi ndi uphungu wotani umene mtumwi Petro akupereka kwa amuna achikristu, ndipo pangakhale zotulukapo zotani ngati mkulu asonyeza kukhala mwamuna wonyalanyaza thayo lake?
15 Kaya mkazi wake ndi wokhulupirira mnzake kapena ayi, mkulu wachikristu ayenera kudziŵa kuti mkazi wake amafunikira chisamaliro chake chachikondi. Mtumwi Petro analemba kuti: “Momwemonso amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” (1 Petro 3:7) Mwamuna amene alephera dala kusamalira zosoŵa za mkazi wake amaika pangozi unansi wake ndi Yehova; akhoza kudzitsekera njira yake kwa Yehova monga “ndi mtambo kuti pemphero . . . lisapyolemo.” (Maliro 3:44) Zimenezi zingamchititse kulandidwa mathayo monga woyang’anira wachikristu.
16. Kodi ndi mfundo yaikulu yotani imene Paulo akupereka, ndipo akulu ayenera kuziona motani zimenezo?
16 Monga momwe taonera, mfundo yaikulu ya Paulo ndiyo yakuti pamene mwamuna akwatira, amathedwa mlingo wina wa ufulu umene anali nawo monga mbeta umene unamulola ‘kutsata chitsatire Ambuye, popanda chocheukitsa.’ (1 Akorinto 7:35) Malipoti amasonyeza kuti akulu ena okwatira nthaŵi zina aganiza mosayenera pa mawu ouziridwa a Paulo. Pokhumba kuchita zimene iwo okha amaganiza kuti ndizo zimene akulu abwino ayenera kuchita, anganyalanyaze mathayo awo monga mwamuna. Ena kumakhala kowavuta kukana thayo la mumpingo, ngakhale pamene kuli koonekeratu kuti zimenezo zingafooketse mkhalidwe wauzimu wa akazi awo. Iwo amasangalala ndi zabwino za muukwati, koma kodi alinso ofunitsitsa kukwaniritsa mathayo omwe amadza ndi zimenezo?
17. Kodi nchiyani chimene chachitika kwa akazi, ndipo zimenezi zikanapeŵedwa motani?
17 Ndithudi, kukhala ndi changu monga mkulu nkoyamikirika. Komabe, kodi Mkristu amakhala wolinganizika bwino ngati posamalira mathayo ake mumpingo, amanyalanyaza mathayo ake a m’Malemba kulinga kwa mkazi wake? Pamene kuli kwakuti amafuna kuchirikiza a mumpingo, mkulu wolinganizika bwino amasamalanso za mkhalidwe wauzimu wa mkazi wake. Akazi a akulu ena afooka kuuzimu, ndipo ena ‘asweka’ mwauzimu. (1 Timoteo 1:19) Pamene kuli kwakuti mkazi ali ndi thayo la kukonza chipulumutso cha mwini yekha, nthaŵi zina vuto lauzimu lingapeŵedwe ngati mkuluyo ‘alera ndi kusunga’ mkazi wake, “monganso Kristu eklesia.” (Aefeso 5:28, 29) Kuti akhale otsimikiza, akulu ayenera ‘kudzichenjera okha, ndi gulu lonse.’ (Machitidwe 20:28) Ngati ali okwatira, zimenezi zimaphatikizapo akazi awo.
“Chisautso m’Thupi”
18. Kodi mbali zina za “chisautso” chimene Akristu okwatira amakumana nacho nzotani, ndipo zimenezi zingayambukire motani ntchito za mkulu?
18 Mtumwiyo analembanso kuti: “Ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m’thupi, ndipo ndikulekani.” (1 Akorinto 7:28) Paulo anakhumba kuleka awo amene anali okhoza kutsanzira chitsanzo chake cha kukhala mbeta ndi kumasuka ku nkhaŵa zimene mosapeŵeka zimafika ndi ukwati. Ngakhale kwa okwatirana opanda ana, nkhaŵa zimenezi zimaphatikizapo matenda kapena mavuto a zandalama limodzinso ndi mathayo a m’Malemba kulinga kwa makolo okalamba a wina wa mu ukwati. (1 Timoteo 5:4, 8) Mwa njira yopereka chitsanzo chabwino, mkulu ayenera kukwaniritsa mathayo ameneŵa, ndipo nthaŵi zina zimenezi zidzayambukira zochita zake monga woyang’anira wachikristu. Ubwino wake ngwakuti akulu ambiri akuchita bwino pa kukwaniritsa mathayo a m’banja ndi a mumpingo omwe.
19. Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati: “Akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe”?
19 Paulo anawonjezera kuti: “Yafupika nthaŵi, kuti tsopano iwo akukhala nawo akazi akhalebe monga ngati alibe.” (1 Akorinto 7:29) Ndithudi, kuona zimene anali atalemba kale m’chaputala chimenechi kwa Akorinto, nkoonekeratu kuti sanatanthauze kuti Akristu okwatira ayenera kunyalanyaza akazi awo mwa njira zina. (1 Akorinto 7:2, 3, 33) Iye anasonyeza zimene anatanthauza, pamene analemba kuti: “Iwo akuchita nalo dziko lapansi, [akhale] monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.” (1 Akorinto 7:31) Nzoonekeratu kwambiri tsopano kuposa m’tsiku la Paulo kapena m’tsiku la mtumwi Yohane kuti, “dziko lapansi lipita.” (1 Yohane 2:15-17) Chifukwa chake, Akristu amene amazindikira kufunika kwa kudzimana motsanzira Kristu sangamwerekere kotheratu m’zisangalalo ndi mwaŵi wa muukwati.—1 Akorinto 7:5.
Akazi Odzimana
20, 21. (a) Kodi nkudzimana kotani kumene akazi achikristu ambiri akukuchita mofunitsitsa? (b) Kodi nchiyani chimene mkazi ayenera kuyembekezera kwa mwamuna wake, ngakhale ngati ali mkulu?
20 Monga momwe akulu amachitira modzimana kuti apindulitse ena, akazi ambiri a akulu ayesayesa kulinganiza mathayo awo a muukwati ndi zinthu za Ufumu. Zikwi zambiri za akazi achikristu ali osangalala kugwirizana ndi amuna awo kuti awathandize kusenza mathayo awo monga oyang’anira. Yehova amawakonda kaamba ka chimenechi, ndipo amadalitsa mzimu wabwino umene amasonyeza. (Filemoni 25) Ngakhale ndi choncho, uphungu wa Paulo wolinganizika bwino umasonyeza kuti akazi a oyang’anira akhoza moyenerera kuyembekezera amuna awo kupereka kwa iwo nthaŵi yokwanira bwino ndi chisamaliro. Lili thayo la m’Malemba kwa akulu okwatira kupereka nthaŵi yokwanira kwa akazi awo kuti alinganize bwino mathayo awo monga mwamuna ndi woyang’anira.
21 Koma bwanji ngati kuwonjezera pa kukhala mwamuna, mkulu wachikristuyo alinso tate? Zimenezi zimakulitsirako mathayo ake ndipo zimamtsegulira mbali inanso ya uyang’aniro, imene tidzapenda m’nkhani yotsatira.
Kubwereramo
◻ Kodi ndi maumboni a m’Malemba otani amene amasonyeza kuti woyang’anira wachikristu akhoza kukhala mwamuna wokwatira?
◻ Ngati mkulu wosakwatira akwatira, kodi ayenera kudziŵanji?
◻ Kodi ndi m’njira zotani zimene Mkristu wokwatira “amadera nkhaŵa zinthu za dziko”?
◻ Kodi akazi ambiri a oyang’anira amasonyeza motani mzimu wabwino wa kudzimana?
[Chithunzi patsamba 17]
Ngakhale kuti mkulu amakhala wochulukidwa ndi zochita zateokrase, ayenera kupatsa mkazi wake chisamaliro chachikondi