Kodi Mumaona Anthu Ofooka Mmene Yehova Amawaonera?
“Ziwalo za thupi zimene zimaoneka ngati zofooka ndizo zofunika.”—1 AKOR. 12:22.
1, 2. N’chifukwa chiyani Paulo anatha kumvetsa anthu ofooka?
NTHAWI zina tonsefe timafooka. Mwachitsanzo, tikadwala chimfine kapena chifuwa tingafooke n’kuvutika kugwira ntchito za tsiku ndi tsiku. Koma nanga mungamve bwanji ngati mwafooka kwa nthawi yaitali osati kwa mlungu umodzi kapena iwiri yokha? Zimenezi zikachitika, mungafune kuti anthu azikumvetsani.
2 Nayenso mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto, mumpingo komanso kunja kwa mpingo, amene anamufooketsa. Nthawi zina, iye ankamva ngati sangapirirenso. (2 Akor. 1:8; 7:5) Paulo ankaganizira mavuto amene ankakumana nawo monga Mkhristu ndipo ananena kuti: “Ndani ali wofooka, ine osakhalanso wofooka?” (2 Akor. 11:29) Paulo anayerekeza anthu mumpingo ndi ziwalo zosiyanasiyana za thupi ndipo anati: “Ziwalo za thupi zimene zimaoneka ngati zofooka ndizo zofunika.” (1 Akor. 12:22) Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa? N’chifukwa chiyani tiyenera kuona anthu amene amaoneka ngati ofooka mmene Yehova amawaonera? Nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji?
KODI YEHOVA AMAONA BWANJI ANTHU OFOOKA?
3. N’chiyani chingachititse kuti tiziipidwa ndi abale ndi alongo amene amafuna kuthandizidwa?
3 M’dzikoli anthu amakonda kupikisana ndipo amayesetsa kuti azionekabe ngati achinyamata komanso amphamvu. Anthu ambiri amangochita zimene akuona kuti zingawathandize ndipo saganizira anthu ofooka. Mwina ife sitisangalala ndi zimenezi koma mosazindikira tingayambe kutengera maganizo amenewa. Izi zingatichititse kuti tiyambe kuipidwa ndi abale ndi alongo amene amafuna kuthandizidwa pafupipafupi. Kodi tingatani kuti tiziona anthu oterewa mmene Yehova amawaonera?
4, 5. (a) Kodi fanizo la pa 1 Akorinto 12:21-23 limatithandiza bwanji kuona anthu ofooka mmene Yehova amawaonera? (b) Kodi chimachitika n’chiyani tikamathandiza anthu ofooka?
4 Fanizo limene Paulo analemba m’kalata yake yoyamba yopita kwa Akorinto lingatithandize kudziwa mmene Yehova amaonera anthu ofooka. Mu chaputala 12, Paulo ananena kuti ziwalo zimene timaganiza kuti n’zosaoneka bwino komanso zofooka zili ndi ntchito yake. (Werengani 1 Akorinto 12:12, 18, 21-23.) Anthu ena amene amakhulupirira kuti tinasintha kuchokera ku zinyama amatsutsa mfundo imeneyi. Koma panopa, asayansi atulukira kuti ziwalo zina zimene anthu ankaganiza kuti n’zopanda ntchito zimagwira ntchito zina zofunika.a Mwachitsanzo, anthu ankaganiza kuti chala chaching’ono chakuphazi n’chopanda ntchito. Koma panopa atulukira kuti chimathandiza kuti tizitha kuima komanso kuyenda bwino.
5 Fanizo la Pauloli likusonyezeratu kuti munthu aliyense mumpingo ndi wofunika. Satana amanyoza ndiponso kuderera anthu koma Yehova amaona kuti mtumiki wake aliyense, ngakhale amene amaoneka ngati wofooka, ndi ‘wofunika’ kwambiri. (Yobu 4:18, 19) Mfundo imeneyi iyenera kutikumbutsa kuti ndife ofunika kwambiri mumpingo ndiponso m’gulu lonse la Yehova. Kodi mukukumbukira nthawi imene munathandiza m’bale kapena mlongo wachikulire kuti adutse bwinobwino malo enaake? Mwina munkayenda nawo pang’onopang’ono eti? Kunena zoona, munthu umamva bwino ukathandiza ena chonchi. Zimathandiza kuti ukhale wosangalala, woleza mtima, wachikondi komanso womvetsa zinthu. (Aef. 4:15, 16) Atate wathu wachikondi amasangalala akaona kuti anthu mumpingo akulemekeza aliyense mosaganizira zofooka zake. Zimasonyezeratu kuti anthuwo ndi oganiza bwino komanso achikondi.
6. Kodi nthawi zina Paulo ankagwiritsa ntchito bwanji mawu oti ‘ofooka’ ndi “olimba”?
6 M’kalata yake yopita kwa Akorinto, chochititsa chidwi n’chakuti Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti “zofooka” posonyeza mmene anthu osakhulupirira ankaonera Akhristu pa nthawiyo. Anagwiritsanso ntchito mawu oti “wofooka” ponena za mmene iyeyo ankamvera. (1 Akor. 1:26, 27; 2:3) Paulo anatchulanso za anthu “olimba” koma sananene zimenezi n’cholinga choti Akhristuwo adzimve kuti ndi ofunika kuposa anzawo. (Aroma 15:1) M’malomwake, ankafuna kulimbikitsa anthu amene akhala Akhristu kwa nthawi yaitali kuti azilezera mtima Akhristu atsopano.
KODI TIYENERA KUSINTHA MMENE TIMAWAONERA?
7. N’chiyani chingachititse kuti tisamathandize anthu ovutika?
7 Tikamathandiza anthu ovutika timakhala tikutsanzira Yehova ndipo iye amasangalala nafe. (Sal. 41:1; Aef. 5:1) Komabe nthawi zina sitiona moyenera anthuwo ndipo sitingafune kuwathandiza. Kapena mwina timachita manyazi chifukwa chosadziwa zimene tinganene kwa anthu amene akuvutika ndipo timangowapewa. Mlongo wina dzina lake Cynthia,b yemwe mwamuna wake anamusiya, ananena kuti: “Zimapweteka kwambiri ngati abale ndi alongo akukupewa kapena ngati sakuchita zimene umayembekezera kwa anzako apamtima. Ukamakumana ndi mavuto umafuna kuti anzako asamakutalikire.” Davide ankadziwa mmene zimapwetekera anthu akamakupewa.—Sal. 31:12.
8. N’chiyani chingatithandize kuti tiziwamvetsa bwino abale athu?
8 Tikhoza kumvetsa bwino abale athu tikamakumbukira zimene iwo akupirira. Ena mwa iwo akudwala, ena ali pabanja ndi munthu wosakhulupirira ndipo ena akuvutika kwambiri ndi nkhawa. Mwina tsiku lina ifenso tidzakumana ndi mavuto omwewo. Aisiraeli ali ku Iguputo anali osauka ndiponso ofooka. Ndiyeno asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, anakumbutsidwa kuti ‘asamaumire mtima’ abale awo ovutika. Yehova ankafuna kuti iwo asamanyoze anthu osauka koma aziwathandiza.—Deut. 15:7, 11; Lev. 25:35-38.
9. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati munthu wina wakumana ndi mavuto? Perekani chitsanzo.
9 Tiyenera kulimbikitsa anthu amene akukumana ndi mavuto osati kuwaweruza kapena kuwakayikira. (Yobu 33:6, 7; Mat. 7:1) Tiyerekezere kuti munthu wachita ngozi pamsewu n’kufika naye kuchipatala. Kodi madokotala amayamba kufufuza ngati wachititsa ngozi ndi iyeyo? Ayi, koma amayamba mwamsanga kumuthandiza. N’chimodzimodzinso ndi Mkhristu mnzathu amene wafooka chifukwa chokumana ndi mavuto. Tiyenera kuyamba mwamsanga kumulimbikitsa.—Werengani 1 Atesalonika 5:14.
10. Kodi anthu ooneka ngati ofooka angakhale bwanji “olemera m’chikhulupiriro”?
10 Kuganizira kwambiri zimene abale athu akukumana nazo kungatithandize kuona zofooka zawo m’njira yoyenera. Mwachitsanzo, taganizirani za alongo amene akhala akutsutsidwa ndi amuna awo kwa zaka zambiri. Iwo akhoza kuoneka ofooka komabe amasonyeza chikhulupiriro cholimba komanso kupirira. Kodi mumamva bwanji mukamaona mlongo amene akulera yekha ana akubwera ku misonkhano limodzi ndi anawo? Kodi mumamuyamikira chifukwa cha chikhulupiriro chake ndiponso khama lake? Nanga mumamva bwanji mukaona achinyamata amene akukhala okhulupirika ngakhale kuti amakumana ndi mayesero kusukulu? Kukhala odzichepetsa kungatithandize kuzindikira kuti anthu amene amaoneka ngati ofooka angakhale “olemera m’chikhulupiriro” mofanana ndi anthu amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendera.—Yak. 2:5.
TIZIWAONA MMENE YEHOVA AMAWAONERA
11, 12. (a) N’chiyani chingatithandize kuona anthu ofooka mmene Yehova amawaonera? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita ndi Aroni?
11 Kuona mmene Yehova ankachitira zinthu ndi atumiki ake kungatithandize kuti tiziona anthu ofooka mmene iye amawaonera. (Werengani Salimo 130:3.) Tiyerekeze kuti inuyo munali ndi Mose pa nthawi imene Aroni anapanga fano la mwana wang’ombe. Kodi mukanamva bwanji pamene Aroni ankafotokoza zifukwa zake zosamveka? (Eks. 32:21-24) Nanga mukanamva bwanji kuona Aroni akutsatira maganizo a Miriamu n’kumatsutsa Mose chifukwa chokwatira mkazi wamtundu wina? (Num. 12:1, 2) Kapena kodi mukanamva bwanji pamene Aroni ndi Mose sanalemekeze Yehova, pa nthawi imene Yehovayo anapereka madzi kwa anthu pa Meriba?—Num. 20:10-13.
12 Pa zonse zimene Aroni anachitazi, Yehova akanatha kumulanga nthawi yomweyo. Koma iye anadziwa kuti Aroni sanali munthu woipa ndipo si amene ankayambitsa mavutowo. Zikuoneka kuti Aroni ankalakwitsa zinthu chifukwa cha kupanikizika kapena kutsatira zimene anthu ena ankafuna. Koma iye ankavomereza kulakwa kwake ndipo sankatsutsana ndi ziweruzo za Yehova. (Eks. 32:26; Num. 12:11; 20:23-27) Yehova ankaganizira kwambiri chikhulupiriro cha Aroni ndiponso mtima wake wolapa. Patapita zaka zambirimbiri, anthu ankakumbukirabe kuti Aroni ndi ana ake anali anthu oopa Yehova.—Sal. 115:10-12; 135:19, 20.
13. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tiyambe kuona anthu ofooka mmene Yehova amawaonera?
13 Kuti tiyambe kuona anthu ofooka mmene Yehova amawaonera tiyenera kudzifufuza. (1 Sam. 16:7) Mwachitsanzo, kodi timamva bwanji ngati wachinyamata wina sakusankha bwino zosangalatsa kapena akuoneka kuti amachita zinthu mosasamala? M’malo momuimba mlandu, tingachite bwino kuganizira zimene tingachite kuti timuthandize. Tiyeni tiziyesetsa kuthandiza anzathu. Tikatero tidzakhala anthu omvetsa zinthu komanso achikondi.
14, 15. (a) Kodi Yehova anamuona bwanji Eliya pa nthawi imene anafooka? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Eliya?
14 Kuganiziranso zimene Yehova anachita ndi atumiki ake amene anafooka kungatithandizenso kuti tisinthe maganizo athu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene anachita ndi Eliya. Iye analimba mtima polimbana ndi aneneri 450 a Baala koma atamva kuti Yezebeli akufuna kumupha anachita mantha n’kuthawa. Atayenda mtunda wamakilomita 150 anafika ku Beere-seba n’kulowa m’chipululu. Iye atatopa chifukwa choyenda mtunda wautali pa dzuwa, anakhala pansi pa kamtengo kenakake n’kupempha Mulungu kuti ‘achotse moyo wake.’—1 Maf. 18:19; 19:1-4.
15 Kodi Yehova anamva bwanji pamene ankaona mtumiki wake padzikoli atafooka chonchi? Kodi anamuona ngati wosafunika chifukwa chakuti pa nthawiyo anali wokhumudwa komanso wamantha? Ayi ndithu. M’malomwake, anamutumizira mngelo kuti akamuthandize. Kawiri konse mngeloyu analimbikitsa Eliya kuti adye. Anachita zimenezi kuti ‘mtunda umene ankafuna kuyenda usamukulire.’ (Werengani 1 Mafumu 19:5-8.) Yehova anamvetsera zimene mneneri wake ananena ndiponso anamupatsa zofunika asanamuuze zina zoti achite.
16, 17. Kodi tingatsanzire bwanji zimene Yehova anachitira Eliya?
16 Kodi tingatsanzire bwanji Mulungu wathu wachikondi? Tisamafulumire kupereka malangizo. (Miy. 18:13) Choyamba tiyenera kusonyeza kuti tikumvetsa mavuto a anthu amene akudziona kuti ndi osafunika chifukwa cha zimene akukumana nazo. (1 Akor. 12:23) Tikatero tidzatha kuwathandiza mogwirizana ndi mavuto awo.
17 Chitsanzo ndi Cynthia amene tamutchula kale uja. Pamene mwamuna wake anachoka, iye ndi ana ake aakazi awiri ankada nkhawa kwambiri. Kodi abale ndi alongo ena anatani? Mlongoyu anati: “Titangowaimbira foni n’kuwauza zimene zachitika, anafika pasanathe mphindi 45. Nawonso ankalira ndipo sanatisiye tokha masiku oyambirira. Pa nthawiyo tinkalephera kudya ndipo tinkangokhalira kudandaula moti anatitenga kuti tikakhale kwawo kwa kanthawi.” Izi zikungotikumbutsa zimene Yakobo analemba. Iye anati: “Ngati m’bale kapena mlongo ali waumphawi ndipo alibe chakudya chokwanira pa tsikulo, koma wina mwa inu n’kunena kuti: ‘Yendani bwino, mupeze zovala ndi zakudya za tsiku lililonse,’ koma osamupatsa zimene thupi lake likusowazo, kodi pali phindu lanji? Momwemonso chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.” (Yak. 2:15-17) Abale ndi alongowa anathandiza kwambiri Cynthia ndi ana ake moti patangopita miyezi 6 anayamba upainiya wothandiza.—2 Akor. 12:10.
ZIMATHANDIZA ANTHU AMBIRI
18, 19. (a) Kodi tingathandize bwanji anthu amene afooka? (b) Fotokozani ubwino wothandiza anthu ofooka.
18 Mwina mukudziwa kuti zimatenga nthawi kuti munthu apezenso mphamvu atadwala kwambiri. Mkhristu amene wafooka chifukwa chokumana ndi mavuto aakulu angatengenso nthawi kuti ayambe kutumikira Yehova mwakhama. N’zoona kuti Mkhristuyo ayenera kulimbitsa chikhulupiriro chake pophunzira Baibulo, kupemphera ndiponso kuchita zinthu zina zokhudza kulambira. Koma funso n’kumati, Kodi tidzalezera mtima Mkhristu mnzathuyo? Komanso pamene iye akuyesetsa kupezanso mphamvu, kodi tidzapitiriza kumusonyeza chikondi? Kodi tidzayesetsa kuthandiza anthu amene afooka kudziwa kuti ndi ofunika komanso kuti timawakonda?—2 Akor. 8:8.
19 Tisaiwale kuti kupatsa kumabweretsa chimwemwe, choncho tikamathandiza abale athu timakhala osangalala. Timaphunziranso kukhala anthu omvetsa ndiponso oleza mtima. Izi zikhoza kuthandizanso kuti anthu onse mumpingo azikondana. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikamachita zimenezi, timatsanzira Yehova yemwe amaona aliyense kukhala wamtengo wapatali. Tonsefe tilidi ndi zifukwa zomveka zotichititsa kumvera malangizo akuti: “Muthandize ofookawo.”—Mac. 20:35.
a Charles Darwin, amene ankakhulupirira zoti tinasintha kuchokera ku zinyama, analemba m’buku lake kuti anthufe tili ndi ziwalo zina zomwe “n’zopanda ntchito.” Munthu winanso wotsatira zimene Darwin ankaphunzitsa ananena kuti pali ziwalo zambiri m’thupi zimene n’zosafunika.
b Dzina lasinthidwa.