Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’makalata a ku Korinto
MTUMWI Paulo ali ndi nkhawa kwambiri ndi moyo wauzimu wa mpingo wa ku Korinto. Iye wamva kuti pali magawano pakati pa abale kumeneko. Iwo akulekerera khalidwe lachiwerewere. Komanso mpingowo walembera kalata Paulo, kufunsa nkhani zina ndi zina. Choncho cha mu 55 C.E., Paulo akulembera Akorinto kalata yoyamba. Panthawiyi iye ali ku Efeso, paulendo wake wachitatu waumishonale.
Kalata yachiwiri, yomwe zikuoneka kuti inalembedwa patadutsa miyezi yochepa atalemba yoyamba, inali ndi malangizo owonjezereka. Zochitika za ku Korinto, mkati ndi kunja kwa mpingo, zikufanana m’njira zambiri ndi zimene zikuchitika masiku ano. Choncho, uthenga wa m’makalata a Paulowa ndi wofunika kwambiri kwa ife.—Aheb. 4:12.
‘KHALANI MASO, CHIRIMIKANI, KHALANI AMPHAMVU’
Paulo akulangiza kuti: “Muzilankhula chinthu chimodzi.” (1 Akor. 1:10) Palibe ‘maziko ena alionse kupatulapo Yesu Khristu,’ pamene pangamangidwe makhalidwe achikhristu. (1 Akor. 3:11-13) Ponena za munthu wadama wa mumpingowu, Paulo akuti: “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.” (1 Akor. 5:13) Iye akuti: “Thupi silochitira dama, koma ndi la Ambuye.”—1 Akor. 6:13.
Poyankha ‘za zimene iwo analemba,’ Paulo akupereka uphungu wothandiza wokhudza ukwati ndi kukhala osakwatira. (1 Akor. 7:1) Atafotokoza mfundo yachikhristu ya umutu, kufunika kwa dongosolo pamisonkhano yachikhristu ndiponso atatsimikizira zakuti akufa adzauka, Paulo akupereka malangizo awa: “Khalani maso, chirimikani m’chikhulupiriro, pitirizani kuchita chamuna, khalani amphamvu.”—1 Akor. 16:13.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:21—Kodi Yehova amagwiritsadi ntchito ‘nkhani yopusa’ kuti apulumutse okhulupirira? Ayi, satero. Komabe, popeza kuti ‘dziko mwa nzeru zake silitha kum’dziwa Mulungu,’ zimene iye amagwiritsa ntchito kuti apulumutse anthu zimaoneka zopusa ku dzikoli.—Yoh. 17:25.
5:5—Kodi ‘kum’pereka munthu [woipa] kwa Satana kuti thupilo liwonongedwe, kotero kuti mzimuwo upulumutsidwe,’ kumatanthauza chiyani? Munthu amene amachita machimo aakulu koma osalapa akachotsedwa mumpingo, amakhalanso mbali ya dziko la Satana loipali. (1 Yoh. 5:19) N’chifukwa chake akunenedwa kuti waperekedwa kwa Satana. Kuchotsedwa kwakeko kumawononga kapena kuti kuchotsa mumpingo khalidwe lake loipa, ndipo kumateteza mzimu kapena kuti maganizo a mpingowo.—2 Tim. 4:22.
7:33, 34—Kodi “zinthu za dziko” zimene mwamuna wokwatira kapena mkazi wokwatiwa amada nazo nkhawa ndi ziti? Paulo akunena za zinthu zofunika pamoyo wa tsiku ndi tsiku zimene Akhristu okwatira afunika kuda nazo nkhawa. Zinthuzi ndi monga, chakudya, zovala ndiponso nyumba, koma sizikuphatikizapo zinthu zoipa za dzikoli, zimene Akhristu amapeweratu.—1 Yoh. 2:15-17.
11:26—Kodi mwambo wokumbukira imfa ya Yesu uyenera kuchitika kangati ndiponso “mpaka” liti? Paulo sanali kunena kuti mwambo wa imfa ya Yesu uzichitika pafupipafupi. Liwu la Chigiriki limene lamasuliridwa kuti “nthawi zonse,” limatanthauza “pamene” kapena “nthawi iliyonse imene.” Choncho, Paulo anali kunena kuti nthawi iliyonse imene Akhristu odzozedwa adya zizindikiro za pa Chikumbutso, kamodzi pachaka pa Nisani 14, ndiye kuti ‘akulengeza imfa ya Ambuye.’ Iwo amachita zimenezi “mpaka iye adzafike,” kutanthauza kuti mpaka iye atawalandira kumwamba mwa kuwaukitsa kwa akufa.—1 Ates. 4:14-17.
13:13—Kodi n’chifukwa chiyani chikondi chimaposa chikhulupiriro ndi chiyembekezo? Pamene “zinthu zoyembekezeredwa” zikwaniritsidwa, ndipo “chiyembekezo chotsimikizika” cha zinthuzo chikwaniritsidwa, mbali zina za chikhulupiriro ndi chiyembekezocho zimatha. (Aheb. 11:1) Motero chikondi ndi chachikulu kuposa chikhulupiriro ndi chiyembekezo chifukwa chakuti chikondicho chimakhalapo kosatha.
15:29—Kodi “kubatizidwa kuti akhale akufa” kumatanthauza chiyani? Paulo sanali kutanthauza kuti anthu amoyo ayenera kubatizidwa m’malo mwa amene anafa asanabatizidwe. Apa Paulo akunena za kumizidwa kwa Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera, m’moyo wosunga umphumphu mpaka imfa yawo ndi kuuka kwawo, n’kukakhala ndi moyo monga mizimu.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:26-31; 3:3-9; 4:7. Kudzitama koyenerera mwa Yehova, osati mwa ife eni, kumalimbikitsa umodzi mumpingo.
2:3-5. Mwina n’zotheka kuti Paulo ankakayikira ngati angawafike pa mtima omvera ake panthawi imene anali kulalikira ku Korinto, mzinda umene unali likulu la maphunziro ndi nzeru za Chigiriki. Komabe, sanalole chofooka chilichonse kapena mantha amene anali nawo kumulepheretsa kuchita utumiki umene Mulungu anamupatsa. Ifenso tikakumana ndi zinthu zosazolowereka, tisamalole zimenezi kutilepheretsa kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tiyenera kudalira Yehova ndi mtima wathu wonse ngati Paulo.
2:16. Kukhala ndi “maganizo a Khristu” kumatanthauza kudziwa mmene iye amaganizira, kuganiza mmene iye amaganizira, kudziwa bwino umunthu wake wonse, ndi kutsatira chitsanzo chake. (1 Pet. 2:21; 4:1) Ndiyetu m’pofunika kwambiri kuti tiziphunzira bwinobwino za moyo ndi utumiki wa Yesu.
3:10-15; 4:17. Tiyenera kumaonetsetsa luso lathu la kuphunzitsa ndi kupanga ophunzira kuti lili bwanji, kenako n’kumaliwongolera. (Mat. 28:19, 20) Ngati sitiphunzitsa mwaluso, wophunzira wathu angagwe atakumana ndi mavuto oyesa chikhulupiriro chake, ndipo zimenezi zingatipweteke kwambiri motero kuti ngakhale titapulumuka, tidzakhala ‘ngati tapulumuka m’moto.’
6:18. ‘Kuthawa dama’ sikumangotanthauza kupewa mitundu yosiyanasiyana ya por·neiʹa, koma kumatanthauzanso kupewa zolaula, khalidwe lonyansa, kukonda kuganizira za kugonana, kukopana, kapena china chilichonse chimene chingatsogolere ku dama.—Mat. 5:28; Yak. 3:17.
7:29. Anthu okwatirana sayenera kuika chidwi chawo chonse pa mnzawoyo mpaka kuika zinthu za Ufumu pamalo achiwiri m’moyo wawo.
10:8-11. Yehova anakwiya kwambiri pamene Aisiraeli anang’ung’udza potsutsa Mose ndi Aroni. Choncho, n’chinthu chanzeru kupewa kukhala ndi chizolowezi chong’ung’udza.
16:2. Tingamapereke mokhazikika ndalama zopititsa patsogolo zinthu za Ufumu ngati timakonzekera pasadakhale ndiponso ngati timachita zimenezo mwadongosolo.
‘PITIRIZANI KUWONGOKA’
Paulo akuuza Akorinto kuti ayenera ‘kukhululukira ndi mtima wonse ndiponso kutonthoza’ munthu wolakwa amene analangidwa uja popeza walapa. Ngakhale kuti iwo anamva chisoni chifukwa cha kalata yake yoyamba, Paulo akunena kuti iye akukondwera chifukwa chakuti ‘chisoni chimene iwo anamvacho chinawachititsa kulapa.’—2 Akor. 2:6, 7; 7:8, 9.
Paulo akulimbikitsa Akorinto kuti ‘monga akusefukira m’chilichonse, asefukirenso pa kupereka.’ Atayankha otsutsa, iye akupereka malangizo omaliza kwa onse kuti: “Pitirizani kukondwera, kuwongoka, kutonthozedwa, kukhala ndi maganizo ogwirizana, ndi kukhala mwamtendere.”—2 Akor. 8:7; 13:11.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:15, 16—N’chifukwa chiyani ifeyo tili “fungo la Khristu lonunkhira bwino”? Chifukwa chakuti timatsatira zimene Baibulo limanena ndiponso timafalitsa uthenga wake. Ngakhale kuti “fungo” limeneli lingakhale lonunkha kwa anthu osalungama, ndi fungo lonunkhira bwino kwa Yehova ndi anthu amitima yabwino.
5:16—Kodi zikutheka bwanji kuti Akhristu odzozedwa ‘saona munthu mwa kuthupi’? Iwo saona anthu malinga ndi mmene amaonekera, kutanthauza kuti sakondera ena chifukwa cha chuma, khungu, fuko kapena dziko limene amachokera. Chachikulu kwa iwo ndi ubale wawo wauzimu ndi okhulupirira anzawo.
11:1, 16; 12:11—Kodi Paulo analidi wodzikweza kwa Akorinto? Ayi, si choncho. Komabe kwa ena, mwina anaoneka ngati wodzitama ndi wodzikweza chifukwa cha zimene iye anakakamizika kunena poteteza utumwi wake.
12:1-4—Kodi ndani amene “anakwatulidwa kukalowa m’paradaiso”? Popeza kuti Baibulo silifotokoza za munthu wina aliyense amene anaona masomphenya amenewo, ndipo mawuwa Paulo anawanena atangomaliza kufotokoza mfundo zoteteza utumwi wake, iye ayenera kuti anali kunena zimene iyeyo anakumana nazo. Zikuoneka kuti zimene mtumwiyu anaona m’masomphenyawo, ndi paradaiso wauzimu amene mpingo wachikhristu ukusangalala naye mu “nthawi ya chimaliziro.”—Dan. 12:4.
Zimene Tikuphunzirapo:
3:5. Vesili likutiuza mfundo yakuti Yehova amayeneretsa bwino Akhristu kaamba ka utumiki kudzera m’Mawu ake, mzimu woyera, ndi mbali ya padziko lapansi ya gulu lake. (Yoh. 16:7; 2 Tim. 3:16, 17) Choncho ndi bwino kuphunzira mwakhama Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo, kusasiya kupempherera mzimu woyera, ndiponso kupezeka nthawi zonse pamisonkhano yachikhristu ndi kutenga nawo mbali.—Sal. 1:1-3; Luka 11:10-13; Aheb. 10:24, 25.
4:16. Popeza kuti Yehova amakonza ‘munthu wathu wa mkati kukhala watsopano tsiku ndi tsiku,’ tiyenera kugwiritsa ntchito nthawi zonse zinthu zimene Yehova wapereka pofuna kutithandiza, osalola kuti tsiku lithe popanda kuchita zinthu zauzimu.
4:17, 18. Kukumbukira kuti “chisautso n’chakanthawi ndipo n’chopepuka” kungatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova tikakumana ndi mavuto.
5:1-5. Apa Paulo akufotokoza bwino kwambiri maganizo amene Akhristu odzozedwa ali nawo pa chiyembekezo chawo chokakhala ndi moyo kumwamba.
10:13. Tiyenera kulalikira m’gawo la mpingo wathu lokha, pokhapokha titachita kuuzidwa kukathandiza ku dera limene kuli kusowa kwakukulu.
13:5. Kuti ‘tidziyese tokha kuti tione ngati tili m’chikhulupiriro,’ tiyenera kuonetsetsa ngati khalidwe lathu likugwirizana ndi zimene timaphunzira m’Baibulo. Kuti ‘tidzidziwe tokha motsimikiza kuti ndife otani,’ tiyenera kuona kuti moyo wathu wauzimu ndi wokhwima motani, ndiponso kuti ‘luntha lathu la kuzindikira’ ndi lakuthwa motani, komanso kuchuluka kwa ntchito zathu za chikhulupiriro. (Aheb. 5:14; Yak. 1:22-25) Mwa kutsatira uphungu wothandiza wa Paulo umenewu, tingapitirize kuyenda m’njira ya choonadi.
[Chithunzi pamasamba 26, 27]
Kodi mawu akuti “nthawi zonse pamene mudya mkate umenewu ndi kumwa za m’chikho chimenechi,” amatanthauza chiyani?—1 Akor. 11:26