CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Sankhani Mwanzeru Munthu Wokwatirana Naye
Solomo anachita zinthu mopanda nzeru pokwatira akazi amene ankalambira milungu yonyenga (1Mf 11:1, 2; w18.07 18 ¶7)
Pang’ono ndi pang’ono, akazi a Solomo anamuchititsa kuti asiye kulambira Yehova (1Mf 11:3-6; w19.01 15 ¶6)
Yehova anakwiyira kwambiri Solomo (1Mf 11:9, 10; w18.07 19 ¶9)
Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu amene akufuna kulowa m’banja kuti, akwatire kapena akwatiwe “mwa Ambuye.” (1Ak 7:39) Komabe, kubatizidwa pakokha sikungapangitse munthu kukhala woyenera. Kodi munthu amene mukufuna kukwatirana nayeyo, adzakuthandizani kutumikira Yehova ndi mtima wonse? Kodi wasonyeza kuti amakonda Yehova kwa nthawi ndithu? Musanatsimikize zokwatirana ndi munthu winawake, muzikhala ndi nthawi yokwanira kuti mumudziwe bwino.