Kodi N’zotheka Kukondana Mpaka Kalekale?
“Kuyaka [kwa chikondi] kuli ngati kuyaka kwa moto. Chikondicho ndi lawi la Ya.”—NYIMBO 8:6.
1, 2. (a) Kodi mfundo za m’Nyimbo ya Solomo zingathandize ndani? (b) N’chifukwa chiyani tikuyankha choncho? (Onani chithunzi pamwambapa.)
MKULU wina atangomaliza kukamba nkhani ya ukwati ankayang’anitsitsa banja latsopanolo likuvina ku phwando la ukwati. Mwamuna ndi mkaziyo ankayang’anizana monyandirana. Aliyense pa phwandolo ankaoneratu kuti akukondana kwambiri. Koma mkuluyo ankadzifunsa kuti: ‘Kodi banja limeneli likhalitsa? Kodi chikondi chawo chipitirira kapena chiyamba kuchepa zaka zikamadutsa?’ Kunena zoona, zimakhala zosangalatsa ngati mwamuna ndi mkazi wake amakondanabe ngakhale kuti akukumana ndi mavuto ena. Koma masiku ano mabanja ambiri akutha. Izi zimatichititsa kudzifunsa kuti: ‘Kodi n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azikondana mpaka kalekale?’
2 Ngakhale nthawi ya Mfumu Solomo, anthu ambiri sankakondana kwenikweni. Pofotokoza mmene zinalili pa nthawiyo, Solomo analemba kuti: “Pa anthu 1,000, ndapezapo mwamuna mmodzi yekha wowongoka mtima, koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi wowongoka mtima. Zimene ndapeza n’zakuti, Mulungu woona anapanga anthu owongoka mtima, koma anthuwo asankha njira zina zambirimbiri.” (Mlal. 7:26-29) Akazi amitundu ina olambira Baala anasokoneza kwambiri mu Isiraeli moti zinali zovuta kuti Solomo apeze mwamuna kapena mkazi wakhalidwe labwino.a Koma ndakatulo imene Solomo analemba zaka 20 asanalembe mawu amenewa, imasonyeza kuti n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi akhale ndi chikondi chenicheni. Ndakatuloyi imafotokoza bwino chikondichi komanso zimene anthu amachita pochisonyeza. Kaya tili pa banja kapena ayi, tikhoza kuphunzira zambiri m’Nyimbo ya Solomo.
N’ZOTHEKA KUKHALA NDI CHIKONDI CHENICHENI
3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azikondana mpaka kalekale?
3 Werengani Nyimbo ya Solomo 8:6. Lembali likufotokoza kuti chikondi ndi “lawi la Ya.” Mawu amenewa ndi oyenera chifukwa chakuti Yehova ndi amene anayambitsa chikondi ngati chimenechi. Iye anapanga munthu m’chifaniziro chake, choncho anthu amatha kukondana. (Gen. 1:26, 27) Mulungu anapereka Hava kwa Adamu ndipo Adamuyo anasangalala kwambiri moti ananena ndakatulo. Hava anapangidwa kuchokera ku nthiti ya Adamu ndipo Adamuyo ayenera kuti ankamukonda kwambiri. (Gen. 2:21-23) Popeza Yehova analenga anthu kuti azikondana n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azikondana mpaka kalekale.
4, 5. Fotokozani mwachidule nkhani ya mu Nyimbo ya Solomo.
4 Nyimbo ya Solomo imafotokoza bwino kwambiri chikondi chenicheni chimene mwamuna ndi mkazi angakhale nacho. Nyimboyi ndi yonena za mtsikana wochokera m’mudzi wa Sunemu, kapena kuti Sulemu, ndi mnyamata wina amene anali m’busa. Imafotokoza kuti anthu awiriwa ankakondana kwambiri. Ndiyeno mtsikanayu ankalondera munda umene unali pafupi ndi msasa wa Mfumu Solomo. Mfumuyi itaona kuti mtsikanayo anali wokongola kwambiri inamuitanitsa. Koma zinali zoonekeratu kuti mtsikanayo ankakonda kwambiri m’busayo. Solomo anayesetsa kumukopa koma iye anasonyeza kuti ankalakalaka kukhala ndi mnyamata amene ankamukondayo. (Nyimbo 1:4-14) Ndiyeno mnyamatayo anapeza njira yolowera m’msasamo ndipo analankhulana mawu achikondi ndi mtsikanayo.—Nyimbo 1:15-17.
5 Solomo anabwerera ku Yerusalemu limodzi ndi mtsikanayo ndipo m’busayo anawatsatira. (Nyimbo 4:1-5, 8, 9) Zonse zimene Solomo anachita pokopa mtsikanayo zinangopita pachabe. (Nyimbo 6:4-7; 7:1-10) Kenako mfumuyo inalola kuti mtsikanayo abwerere kwawo. Ndiyeno nyimboyo imatha ndi mawu a mtsikanayo opempha kuti mnyamata amene ankamukondayo abwere msanga “ngati insa.”—Nyimbo 8:14.
6. N’chifukwa chiyani zimavuta kudziwa amene akulankhula mu Nyimbo ya Solomo?
6 Nyimbo ya Solomo ndi yabwino ndipo Baibulo limanena kuti ndi “nyimbo yokoma kwambiri.” (Nyimbo 1:1) Koma zimavuta kudziwa amene akulankhula chifukwa chakuti Solomo sanalembe olankhulawo. N’kutheka kuti sanawatchule pofuna kuti nyimboyo ndiponso ndakatulo yake ikhale yokoma kwambiri. Komabe timatha kudziwa anthu amene akulankhula chifukwa cha zimene akunena.
“CHIKONDI CHIMENE UMANDISONYEZA CHIMAPOSA VINYO”
7, 8. Fotokozani mawu ena osonyeza chikondi amene ali m’Nyimbo ya Solomo.
7 Nyimbo ya Solomo imafotokoza mawu achikondi amene mtsikanayu ndi m’busa uja ankauzana. Zimene zalembedwazo n’zimene anthu ankachita kuderalo zaka 3,000 zapitazo. Choncho masiku ano tingadabwe nazo komabe tikhoza kumvetsa mmene ankamvera mumtima mwawo. Mwachitsanzo, mnyamatayo anati maso a mtsikanayo ndi okongola “ngati maso a njiwa.” (Nyimbo 1:15) Nayenso mtsikanayo anati maso a mnyamatayo ndi okongola ngati njiwa zenizenizo. (Werengani Nyimbo ya Solomo 5:12.) Apa ankatanthauza kuti mbali yakuda ya maso a mnyamatayo inali ngati njiwa ndipo mbali yoyera inkaoneka ngati mkaka umene njiwazo zinkasambiramo.
8 Koma sikuti anthuwa ankangochemerera maonekedwe okha. Mwachitsanzo, mnyamatayo ananenanso za mawu a mtsikanayo. (Werengani Nyimbo ya Solomo 4:7, 11.) Iye anati milomo yake “imangokhalira kukha uchi wapachisa.” Anatchula za uchi wapachisa chifukwa umakhala wokoma kuposa umene wapitidwa mphepo. Ndipo pamene ananena kuti “uchi ndi mkaka zili kuseri kwa lilime” lake, ankatanthauza kuti mawu ake ndi abwino ndiponso okoma ngati uchi ndi mkaka. Choncho pamene m’busayo anauza mtsikanayo kuti “ndiwe wokongola paliponse, . . . ndipo mwa iwe mulibe chilema chilichonse,” sankangonena za maonekedwe ake okha.
9. (a Kodi anthu okwatirana ayenera kusonyezana chikondi chotani? (b) Kodi kusonyezana chikondi m’banja n’kofunika bwanji?
9 Atumiki a Yehova saona ukwati ngati pangano la bizinezi. Amaona kuti mwamuna ndi mkazi amafunika kukondana kwambiri. Koma kodi chikondi chawo chiyenera kukhala chotani? Paja chikondi chilipo chamitundumitundu. Pali china chimene anthu amachisonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Yoh. 4:8) China n’chimene anthu amasonyezana chifukwa choti ali pachibale. China n’chimene munthu amasonyeza mnzake wapamtima. (Yoh. 11:3) Ndipo china n’chimene chimakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi. (Miy. 5:15-20) Ndiyeno chikondi chimene tikunena kuti Akhristu okwatirana azisonyezana chiyenera kukhala cha mitundu yonseyi. Koma munthu sangadziwe zoti amakondedwa ngati sasonyezedwa chikondicho. Choncho si bwino kutanganidwa kwambiri mpaka kusowa mpata wosonyezana chikondi. Anthu akamasonyezana chikondi, banja limakhala losangalala komanso lotetezeka. M’mayiko ena, makolo ndi amene amasankhira ana awo mwamuna kapena mkazi ndipo anawo amalowa m’banja asakudziwana bwinobwino. Choncho akamayamba kudziwana bwino ayenera kusonyezana chikondi. Izi zikhoza kuthandiza kuti ubwenzi wawo ulimbe.
10. Kodi kukumbukira chikondi chimene wina anakusonyezani kumathandiza bwanji?
10 Kusonyezana chikondi m’banja kulinso ndi ubwino wina. Solomo analonjeza mtsikana uja kuti amupangira zokongoletsa “zagolide zokhala ndi mikanda yasiliva.” Iye ankamuchemereranso kuti anali “wokongola ngati mwezi wathunthu, wosadetsedwa ngati dzuwa lowala.” (Nyimbo 1:9-11; 6:10) Koma mtsikanayo anakhalabe wokhulupirika kwa m’busa uja. Kodi n’chiyani chinkamulimbikitsa pamene anasiyanitsidwa ndi mnyamatayo? Iye ankalimba mtima akakumbukira mmene mnyamatayo ankamusonyezera chikondi. (Werengani Nyimbo ya Solomo 1:2, 3.) Iye ankaona kuti chikondi chake ‘chinkaposa vinyo’ amene amasangalatsa mtima ndipo dzina lake linkamukhazika mtima m’malo ngati ‘amuthira pamutu mafuta onunkhira bwino.’ (Sal. 23:5; 104:15) Munthu amakonda kwambiri mnzake ngati amakumbukira chikondi chimene anamusonyeza. Choncho anthu amene ali pa banja ayenera kusonyezana chikondi nthawi ndi nthawi.
‘MUSAYESE KUDZUTSA CHIKONDI MPAKA PAMENE CHIKONDICHO CHIFUNIRE’
11. Kodi Akhristu amene sali pa banja angaphunzire chiyani pa zimene mtsikana uja ananena?
11 Nyimbo ya Solomo ili ndi mfundo zimene zingathandizenso Akhristu amene sali pa banja, makamaka amene akufuna kukhala pa banja. Mtsikana uja sankakonda Solomo ndipo analumbiritsa akazi a kunyumba yachifumu kuti: “Musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.” (Nyimbo 2:7; 3:5) Si bwino kungoyamba chibwenzi ndi munthu wina aliyense amene wapezeka. Mkhristu amene akufuna kukhala pa banja angachite bwino kudikira mpaka atapeza munthu amene angamukonde kwambiri.
12. N’chifukwa chiyani mtsikana uja ankakonda kwambiri m’busayo?
12 N’chifukwa chiyani mtsikana uja ankakonda m’busayo? N’zoona kuti mnyamatayo anali wooneka bwino ngati “mbawala,” manja ake anali ngati ‘agolide’ ndipo miyendo yake inali yamphamvu ngati “zipilala zamiyala ya mabo.” Koma sikuti mnyamatayo anangokhala wamphamvu ndi wooneka bwino basi. Mtsikanayo ankadziwa kuti mnyamatayo ankakonda Yehova ndipo anali ndi makhalidwe abwino. M’pake kuti ankamuona kuti anali ngati “mtengo wa maapozi pakati pa mitengo ya m’nkhalango.”—Nyimbo 2:3, 9; 5:14, 15.
13. N’chifukwa chiyani m’busayo ankakonda kwambiri mtsikana uja?
13 N’zoona kuti mtsikanayo analinso wokongola kwambiri. Paja Solomo anakopeka naye ngakhale kuti pa nthawiyo anali ndi “mafumukazi 60, adzakazi 80 ndi atsikana osawerengeka.” Koma mtsikanayo ankadziona ngati “duwa lonyozeka la m’chigwa cha m’mphepete mwa nyanja.” Iye anali wodzichepetsa kwambiri ndipo ankakonda Yehova. N’chifukwa chake m’busayo ankamuona ngati “duwa pakati pa zitsamba zaminga.”—Nyimbo 2:1, 2; 6:8.
14. Kodi Akhristu amene akufuna kukhala pa banja angaphunzire chiyani m’Nyimbo ya Solomo?
14 M’Mawu a Mulungu muli malangizo osapita m’mbali akuti Akhristu ayenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Mkhristu amene akufuna kukhala pa banja sayenera kuyamba chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira koma mtumiki wa Yehova wokhulupirika. Kuti banja liziyenda bwino komanso lizitumikira Yehova mogwirizana, anthu onse ayenera kukonda Mulungu ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Choncho ngati mukufuna kukhala pa banja, muyenera kutsanzira m’busayu ndi mtsikanayo n’kumayang’ana makhalidwe amenewa.
MKWATIBWI WANGA “ALI NGATI MUNDA WOTCHINGIDWA NDI MPANDA”
15. Kodi Akhristu amene sali pa banja angaphunzire chiyani kwa mtsikanayu?
15 Werengani Nyimbo ya Solomo 4:12. N’chifukwa chiyani m’busa uja ananena kuti mtsikana wake anali ngati “munda wotchingidwa ndi mpanda”? Mpanda umachititsa kuti anthu asalowe m’munda mwachisawawa koma azidzera pakhomo limene limakhomedwa. Mtsikana wa m’nyimboyi anali ngati munda umenewu chifukwa chakuti sankalola kukopana ndi amuna ena koma ankakonda m’busa yekhayu. Iye sanakopeke ndi zimene mfumu ija inkachita. Apa anasonyeza kuti ali ngati “khoma” osati “chitseko” chimene chimangotsegukatseguka. (Nyimbo 8:8-10) Akhristu amene sali pa banja ayeneranso kukondana ndi munthu amene adzakwatirane naye yekha.
16. Kodi Akhristu amene ali pa chibwenzi angaphunzire chiyani m’Nyimbo ya Solomo?
16 Tsiku lina kutacha bwino, m’busayo anapempha kuti apite koyenda ndi mtsikanayu koma azichimwene ake sanalole. M’malomwake anamuuza kuti azikalondera munda wa mpesa. Sikuti ankamukayikira kuti akachita zoipa. Iwo ankafuna kuteteza mlongo wawoyo kuti asapezeke pamalo amene angayesedwe. (Nyimbo 1:6; 2:10-15) Akhristu amene ali pa chibwenzi ayenera kusamalanso kuti asachite zosayenera. Choncho si bwino kukhala awiriwiri kwaokha. N’zoona kuti akhoza kusonyezana chikondi moyenerera koma si bwino kukhala pamalo amene angayesedwe.
17, 18. Kodi kukambirana Nyimbo ya Solomo kwakuthandizani bwanji?
17 Akhristu ambiri akamalowa m’banja amakhala akukondana kwambiri. Koma tiyenera kukumbukira kuti Yehova ndi amene anayambitsa ukwati ndipo suyenera kutha. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti chikondi, chomwe chimatchedwa “lawi la Ya,” chiziyakabe.—Maliko 10:6-9.
18 Pofuna kulowa m’banja, ndi bwino kufufuza munthu amene tingamukonde ndi mtima wonse ndipo chikondi chake chiyenera kukhala ngati moto wosazimitsika. Kaya mukufuna kulowa m’banja kapena mwalowa kale, taona kuti n’zotheka kukhala ndi chikondi chenicheni chomwe ndi “lawi la Ya.”—Nyimbo 8:6.